Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

 Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Kodi kugula nyumba ya chipembedzo china n’kuisintha kukhala Nyumba ya Ufumu n’kuphatikiza zikhulupiriro?

Nthaŵi zambiri, Mboni za Yehova zimapeŵa kuchita zimenezi ndi zipembedzo zina. Komabe, kugula nyumba koteroko sikungakhale kuphatikiza zikhulupiriro. Kungangoonedwa monga malonda omwe achitika ndipo atha. Sikuti mpingo wa Mboni za Yehova wa kumaloko ukatero ndiye kuti ukugwirira ntchito limodzi ndi chipembedzo china kuti amange nyumba yoti onse azilambiriramo.

Nanga kodi kuphatikiza zikhulupiriro n’kutani malinga ndi mmene Yehova amaonera? Taonani malangizo a mtumwi Paulo aŵa: “Musakhale omangidwa m’goli ndi osakhulupira osiyana; pakuti chilungamo chigawana bwanji ndi chosalungama? Kapena kuunika kuyanjana bwanji ndi mdima? Ndipo Kristu avomerezana bwanji ndi Beliyali? Kapena wokhulupira ali nalo gawo lanji pamodzi ndi wosakhulupira? Ndipo chiphatikizo chake n’chanji ndi kachisi wa Mulungu ndi wa mafano? . . . Chifukwa chake, Tulukani pakati pawo, ndipo patukani, ati Ambuye, ndipo musakhudza kanthu kosakonzeka; ndipo Ine ndidzalandira inu.” (2 Akorinto 6:14-17) Kodi Paulo anatanthauza chiyani pamene anati ‘kugawana’ ndi “kuyanjana”?

Mwachionekere, kugawana kumene Paulo ananena ndiko kulambira ndiponso kuchita zinthu zauzimu limodzi ndi olambira mafano ndi osakhulupirira. Iye anachenjeza Akorinto kuti apeŵe “kulandirako . . . ku gome la ziŵanda.” (1 Akorinto 10:20, 21) Motero, kuphatikiza zikhulupiriro ndiko kulambira limodzi kapena kuchitira limodzi zinthu zauzimu ndi a zipembedzo zina. (Eksodo 20:5; 23:13; 34:12) Pogula nyumba imene ankagwiritsa ntchito a chipembedzo china, cholinga ndicho kungopezapo nyumbayo kuti ikhale Nyumba ya Ufumu. Isanayambe kugwiritsidwa ntchito ngati Nyumba ya Ufumu, imayeretsedwa kuti pasakhalenso zizindikiro zilizonse za kulambira konyenga. Ikasinthidwa motero, imapatuliridwa kwa Yehova n’cholinga chomulambiriramo basi. Palibe kuyanjana kapena kugawana pakati pa kulambira koona ndi konyenga.

Pokambirana za kugula nyumbayo, m’pofunika kuchepetsa kukumanakumana ndi a chipembedzo chinacho ndipo nkhani zokambirana ziyenera kukhala zokhudza kugula nyumbayo basi. Anthu a mumpingo wachikristu ayenera kukumbukira chenjezo la Paulo lakuti asakhale “omangidwa m’goli ndi osakhulupira.” Ngakhale sitimadziona kuti ndife apamwamba kuposa anthu a zikhulupiriro zina, timapeŵa kuchitira nawo zinthu limodzi kapena kutengeka kuti tiloŵe chipembedzo chawo. *

Nanga bwanji pankhani yoti mpingo uchite lendi nyumba ya chipembedzo china? Kuchita lendi nthaŵi zambiri kumachititsa kukumanakumana ndi a chipembedzo china komwe n’kofunika kupeŵa. Ngakhale kuchita lendi nyumba yoteroyo kuti igwiritsidwe ntchito kamodzi chabe, bungwe la akulu liyenera kulingalira mfundo zotsatirazi: Kodi padzakhala mafano ndi zizindikiro zina zachipembedzo mkati kapena kunja kwa nyumbayo? Kodi anthu m’deralo adzaona bwanji kugwiritsa ntchito kwathu nyumbayo? Kodi ena mumpingo sakhumudwa chifukwa chogwiritsa ntchito nyumbayo? (Mateyu 18:6; 1 Akorinto 8:7-13) Akulu afunika kupenda mfundo zimenezi ndiyeno n’kusankha chochita. Ayeneranso kuganizira chikumbumtima chawo ndi cha anthu mumpingo posankha zoti agule ndi kusintha nyumba yoteroyo kuti ikhale Nyumba ya Ufumu.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 6 Onani Nsanja ya Olonda ya April 15, 1999, masamba 28 ndi 29, kuti muone mfundo zokhudza kuchita zinthu moyenera ndi magulu amene Yehova sawayanja.

[Chithunzi patsamba 27]

Nyumba iyi imene inali sunagoge anaigula n’kuisintha kukhala Nyumba ya Ufumu