Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Nyumba ya Ufumu Ilandira Mendulo Yaulemu

Nyumba ya Ufumu Ilandira Mendulo Yaulemu

 Olengeza Ufumu Akusimba

Nyumba ya Ufumu Ilandira Mendulo Yaulemu

UNDUNA wa Zosamalira Malo m’dziko la Finland unasankha chaka cha 2000 kukhala “Chaka Chokongoletsa Malo.” Mmodzi wa akuluakulu amene ankayendetsa zimenezi ananena kuti “mutu wachaka chinowu womwe ukunena za kukongoletsa malo cholinga chake n’kukumbutsa tonse mmene malo obiriŵira amakhudzira moyo wathu watsiku ndi tsiku ndiponso thanzi lathu.”

Pa January 12, 2001, ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Finland inalandira kalata yochokera ku Bungwe la Makampani Okongoletsa Malo m’dzikolo. Kalatayo inanena kuti Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova ku Tikkurila yalandira nawo mendulo yaulemu chifukwa cha malo ake okongola ndiponso otchetchedwa bwino. Kalatayo inanenanso kuti “malowo amakhala okongola mochititsa kaso zedi m’nthaŵi youma ngakhalenso yamvula.”

Mendulo yaulemuyo anaipereka kwa Mboni za Yehova pamwambo womwe unachitikira ku Hotela ya Rosendahl mumzinda wa Tampere ku Finland. Pamwambowo panali akatswiri 400 a ntchito zosiyanasiyana komanso anthu a bizinesi. Bungwe la Makampani Okongoletsa Malo ku Finland linatulutsanso chikalata chomwe anachifalitsa m’zofalitsira nkhani zosiyanasiyana. Chikalatacho chinati: “M’madera osiyanasiyana m’dziko lino, Nyumba za Ufumu za Mboni za Yehova zimakhala zokongola kwambiri pafupifupi nthaŵi zonse ndipo anazimanga bwino zedi. Aliyense wodutsa pafupi ndi nyumbazi amachita chidwi kwambiri ndi mmene amasamalira malowo. Nyumba ya Ufumu ya ku Tikkurila ndi imodzi mwa malo okongola kwambiri otereŵa. Nyumba yeniyeniyo ndiponso malo ake ndi za bata komanso zokongola zedi.”

Ku Finland kuli Nyumba za Ufumu zokwana 233 ndipo zambiri mwa nyumbazi zili ndi malo okongola kwambiri. Komabe, chomwe chimachititsa maloŵa kukhala okongola kwambiri n’chakuti ndi malo a kulambira koona ndiponso ophunzirirako Baibulo. Kwa Mboni za Yehova zoposa sikisi miliyoni padziko lonse, Nyumba ya Ufumu ndi malo awo apamtima kaya ikhale ndi zinthu zofunika kapena yaing’ono. N’chifukwa chake amalimbikira kuisamalira bwino kwambiri. Nonse muli olandiridwa ndi manja aŵiri ku Nyumba za Ufumu zakwanuko!