Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Anthu Onse Amene Tinkakhala Nawo Pafupi Anapita Kuti Anthuni?

Kodi Anthu Onse Amene Tinkakhala Nawo Pafupi Anapita Kuti Anthuni?

 Kodi Anthu Onse Amene Tinkakhala Nawo Pafupi Anapita Kuti Anthuni?

“Anthu masiku ano alibe nawo ntchito anthu amene amakhala nawo pafupi.”​—Anatero Benjamin Disraeli, yemwe anali m’tsogoleri wa Angelezi m’ma 1800.

ANTHU okalamba a ku Cuba ali ndi njira yawo yotukulira moyo, monga: kugwirizana kwa anthu okhala moyandikana, kapena kupanga magulu a agogo, monga momwe eni ake amanenera. Malinga ndi lipoti la 1997, pafupifupi munthu m’modzi mwa anthu okalamba asanu a ku Cuba ali m’gulu limeneli. M’maguluŵa ndi mmene amapeza ubwenzi, chilimbikitso ndi thandizo lenileni lofunika kuti akhalebe ndi moyo wabwino. Magazini ya World-Health inati: “Nthaŵi iliyonse madokotala a mabanja okhala m’dera limodzi akafuna anthu oti awathandize kuchita ndaŵala ya katemera, ku magulu a anthu okalamba n’komwe amapeza anthu ofunitsitsa kuthandiza.”

Komabe, n’zachisoni kuti madera ambiri padziko lapansi alibe anthu achikondi chonchi m’dera lawo. Mwachitsanzo, talingalirani, nkhani yomvetsa chisoni ya Wolfgang Dircks, yemwe ankakhala pamdadada wina kumadzulo kwa Ulaya. Zaka zingapo zapitazo, magazini ya The Canberra Times inati ngakhale kuti mabanja 17 amene ankakhala pamdadada umene Wolfgang amakhala anadziŵa kuti iye sakuoneka, “palibe ndi m’modzi yemwe amene anaganiza zoimba belu la kunyumba kwake.” Ndiyeno eninyumbayo ataloŵa mnyumbamo, “anapeza mafupa okhaokha ali kutsogolo kwa TV.” Pa miyendo ya mafupawo panali buku losonyeza mapulogalamu a pa TV a pa December 5, 1993. Wolfgang anali atafa zaka zisanu zapitazo. Umenewu ndi umboni womvetsa chisoni kwambiri wakuti anthu okhala moyandikana sakuganizirana ndi kukondana. N’zosadabwitsa kuti wolemba nkhani wina analemba m’magazini yotchedwa The New York Times Magazine kuti dera limene amakhala, lakhala “dera la alendo,” monganso mmene alili madera ena ambiri. Kodi ndi mmenenso zilili m’dera lanu?

N’zoona kuti madera ena a kumidzi anthu amachezerana bwinobwino ndiponso madera ena a m’tauni anthu amayesetsa kukonda kwambiri anthu amene amakhala nawo pafupi. Komabe, anthu ambiri a m’tauni amaona kuti ndi osungulumwa ndiponso osatetezeka m’dera lawo lomwe. Amasungulumwa chifukwa  chosadziŵana ndi anthu amene akukhala nawo pafupi. Kodi zimatheka bwanji?

Kusadziŵana ndi Anthu Okhala Nawo Pafupi

Ndi zoona kuti ambirife tili ndi anthu amene tayandikana nawo kwambiri. M’khichini mukamatuluka utsi, kulira kwa wailesi, kulongolola kwa ana, chitseko chikakhala chosatseka, ndiponso phokoso pothyola nkhuni, zonsezi ndi zizindikiro zakuti pali anthu pafupi nafe. Komabe, ubwenzi weniweni sukhalapo ngati anthu oyandikana sadziŵana kapena amanyalanyazana chifukwa chotanganidwa ndi zochitika m’moyo. Anthu angaone kuti palibe chifukwa chochezera ndi anthu amene akukhala nawo pafupi kapena kukhudzidwa mwa njira ina iliyonse ndi zimene zikuwachitikira. Nyuzipepala ya ku Australia yotchedwa Herald Sun inati: “Anthu oyandikana sadziŵana n’komwe, choncho sakhudzidwa ndi zimene zikuwachitikira anzawowo. Masiku ano si vutonso kupeŵa kapena kupatula anthu amene sakuwasangalatsa kucheza nawo.”

Zimenezi n’zosadabwitsa. M’dziko lino limene anthu ndi “odzikonda okha,” anthu okhala moyandikana akukumana ndi zotsatira zake zamoyo umenewu. (2 Timoteo 3:2) Chifukwa cha zimenezi, kusungulumwa ndiponso kudzipatula n’kofala. Chotsatira cha kudzipatula ndicho kusakhulupirira ena, makamaka ngati m’dera mwachuluka chiwawa ndi upandu. Ndiyeno mwamsanga, kusakhulupirirana kumachititsa anthu kusachitirana chifundo.

Mulimonse momwe zilili m’dera lanulo, simungakane kuti anthu abwino okhala nawo pafupi ndi ofunika. Zinthu zambiri zimayenda bwino ngati anthu achita zinthu mogwirizana. Anthu abwino okhala nawo pafupi angakhalenso aphindu. Nkhani yotsatirayi ifotokoza momwe zingakhalire choncho.