Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Dziko la Maganizo Opotoka Pankhani ya Kukhulupirika

Dziko la Maganizo Opotoka Pankhani ya Kukhulupirika

 Dziko la Maganizo Opotoka Pankhani ya Kukhulupirika

LACHISANU lina madzulo mumzinda wa Tel Aviv, ku Israel, mnyamata wina analoŵa pagulu la achinyamata anzake omwe anali kunja kwa nyumba ina yosangalaliramo usiku. Posakhalitsa bomba linaphulika ndipo linanyenyeratu gulu lonselo.

Munthu winanso wophulitsa mabomba opha adani pamodzi ndi iye yemwe anali atadzipha ndiponso kupha achinyamata ena 19. “Ziwalo za anthu zinangoti balala! Onsewo anali achinyamata, ang’ono ndithu. Ha, sindinaonepo zoopsa ngati zimenezo,” anatero dokotala wina pouza atolankhani.

M’buku lake lakuti The Lancet, Thurstan Brewin analemba kuti: “Ndi makhalidwe omweŵa omwe aliyense amawafuna, monga kukhulupirika . . . , omwe angayambitse nkhondo komanso kuchititsa nkhondoyo kukhala yovuta kuithetsa.” Inde, kuyambira pa nkhondo zapakati pa Matchalitchi Achikristu ndi Asilamu mpaka pa kupulula anthu kochita kukonza dala kwa chipani cha Nazi ku Germany, anthu apha anzawo chifukwa chofuna kukhala okhulupirika.

Anthu Ovutika ndi Kusakhulupirika Akuchuluka

Palibe angakane kuti kukhulupirika konyanyira n’kowononga, komanso kuti kusakhulupirika kungabweretse chipwirikiti pakati pa anthu. Kukhala wokhulupirika kumatanthauza kuchita zinthu mosazembera munthu wina kapena mosanyenga ndiponso kumaphatikizapo kukhalabe wolimba wosagonja pa chiyeso chilichonse choti uchite zinthu zosonyeza kusakhulupirika. Ngakhale kuti anthu ambiri amanena kuti amafuna kukhulupirika kotereku, ambiri akuvutika ndi kusakhulupirika kwadzaoneni m’mabanja, m’mene kukhulupirika kumafunika kwambiri. Chiŵerengero cha mabanja osudzulana chikukwera kwambiri chifukwa cha dyera lopambanitsa, mavuto a tsiku ndi tsiku, komanso chiwerewere chomwe chafala kwambiri. Mofanana ndi achinyamata omwe anafa ndi bomba ku Tel Aviv, nthaŵi zambiri ana osalakwa ndiwo amavutika ndi kusakhulupirika m’banja.

Lipoti lina linati: “Nthaŵi zambiri maphunziro a mwana ndiwo amasokonezeka ngati banja lasokonezeka chifukwa chakuti makolo asudzulana, kupatukana, kapena ngati m’banjalo muli kholo limodzi.” Ana aamuna amene akuleredwa ndi mayi yekha ndiwo ali pangozi yokhala osaphunzira, kudzipha, ndiponso kuphwanya malamulo. Chaka chilichonse ku United States, ana wani miliyoni makolo awo amasudzulana. Ngati m’dzikolo titatenga ana onse omwe abadwa kwa makolo okwatirana m’chaka chimodzi, pafupifupi theka la ana onsewo makolo awo adzakhala atasudzulana aliyense wa iwo asanakwanitse zaka 18. Ziŵerengero zikusonyeza kuti zinthu n’zomvetsanso chisoni kwambiri kwa ana ambiri m’mayiko ena padziko lonse.

 Kodi Kukhala Okhulupirika N’kosatheka?

Kusakhulupirika pa chikhalidwe komwe kwafala kwambiri masiku ano kumachititsa mawu a Mfumu Davide kukhala oyenera kuposa kale lonse. Iye anati: “Pulumutsani, Yehova; pakuti wofatsa wasoŵa; pakuti okhulupirika achepa mwa ana a anthu.” (Salmo 12:1) N’chifukwa chiyani kusakhulupirika kwafala motere? Polemba m’magazini ya Time, Roger Rosenblatt, anati: “Ngakhale kuti kukhulupirika ndi khalidwe lapamwamba, ambiri amachita mantha monyanyira, kudzikayikira, kuchita zinthu mwadyera, ndi kuti n’kufuna zinthu zosatheka kuyembekezera kuti anthu ofooka ife tikhale okhulupirika.” Pofotokoza za nthaŵi yomwe tikukhala ino, Baibulo linanena mosapita m’mbali kuti: “Anthu adzakhala odzikonda okha, . . . osayera mtima [“osakhulupirika,” NW], opanda chikondi chachibadwidwe.”​—2 Timoteo 3:1-5.

Popeza taona mmene kukhulupirika kapena kusakhulupirika kumakhudzira kaganizidwe ndiponso zochita za munthu, tifunse kuti: ‘Kodi tiyenera kukhala okhulupirika kwa ndani?’ Taonani zomwe nkhani yotsatirayi ikunena pa funso limeneli.

[Mawu a Chithunzi patsamba 3]

Chithunzi chili pamwamba: © AFP/​CORBIS