Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Misonkhano ya Mayiko mu 2003

Misonkhano ya Mayiko mu 2003

Misonkhano ya Mayiko mu 2003

LOŴERUKA pa October 6, 2001, msonkhano wapachaka wa mamembala a Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania unachitika mu mzinda wa Jersey City, ku New Jersey, U.S.A. Msonkhanowo utatha, mamembalawo pamodzi ndi alendo awo anasangalala ndi pulogalamu yapadera. Tsiku lotsatira, pamisonkhano yowonjezera imene inachitikira m’mizinda inayi ku Canada ndi ku United States, a m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova analengeza zotsatirazi itatha nkhani yawo yomaliza:

“Pamene tikuganizira za m’tsogolo, n’kofunika kwambiri kuti anthu a Mulungu onse asaleke kusonkhana kwawo pamodzi. Mtumwi Paulo analangiza kuti zimenezi, pamodzi ndi kulimbikitsana, ziyenera kuchitika koposa monga tikuona kuti tsiku lalikulu ndi loopsa la Yehova likuyandika. (Ahebri 10:24, 25) Mogwirizana ndi lamulo la m’Malemba limeneli, tikuyembekeza kudzakhala ndi misonkhano yachigawo m’madera onse a dziko lapansi chaka chamaŵa [2002]. Ndiyeno m’chaka cha 2003, ngati Yehova alola, tingadzakhale ndi misonkhano yapadera ya mayiko m’madera ena a dziko lapansi. Tsopano ndi nthaŵi yogalamuka ndiponso kukhala tcheru, kuona mmene zinthu zikuchitikira m’dzikoli.”

Ngakhale kuti kusatsimikizirika kwa zinthu ndiponso nkhaŵa zikukulirakulira pamene dongosolo lino likuyandikira mapeto ake, ntchito ya anthu a Mulungu iyenera kupita patsogolo. Uthenga wabwino wa Ufumu, kuphatikizapo uthenga wochenjeza wa m’Baibulo, uyenera kulalikidwa kwa anthu a mtundu uliwonse, fuko, ndi manenedwe, kuwauza kuti ‘aope Mulungu ndi kum’patsa ulemerero pakuti nthaŵi ya chiweruzo chake yafika.’ (Chivumbulutso 14:6, 7) Motero, malinga ndi chifuniro cha Atate wathu wakumwamba ndi kukoma mtima kwake, misonkhano ya mayiko ikukonzedwa kuti idzachitike m’madera osiyanasiyana pa dziko lonse m’chaka cha 2003.

Poyamba, misonkhano imeneyi ikukonzedwa kuti idzachitike m’mizinda ingapo ku North America ndipo kenako ku Ulaya ngakhale kuti zimenezi sizinatsimikizike kwenikweni. Pakadzapita nthaŵi pang’ono mu 2003, adzakhala akukonza zoti nthumwi zina zipite ku mizinda ingapo ya ku Asia; ndipo chakumapeto kwa chakachi, ena adzapita ku Africa, South America, ndi ku madera a panyanja ya Pacific. Nthambi zina adzazipempha kutumiza nthumwi zoŵerengeka kuti zipite ku malo a msonkhano omwe adzawauze, motero sizidzatheka kuitana aliyense kuti apite ku misonkhanoyi. Komabe, zidzakhala zolimbikitsa kukhala ndi nthumwi zochepa zoimira mayiko osiyanasiyana pa malo alionse a msonkhano.

Mipingo ya Mboni za Yehova idziŵitsidwa posachedwapa zinthu zina zokhudza misonkhano imeneyi. Nthambi ya kumene nthumwi zoitanidwa zidzachokera idzauza nthumwizo za masiku ake enieni ndi mizinda imene adzapite. Motero, tikukupemphani kuti musalembe kalata kapena kufunsa za nkhani imeneyi pakalipano.

Amene adzasankhidwa kukhala nthumwi adzakhala anthu okhawo amene ndi Mboni zodzipatulira zobatizidwa amene adzakhala zitsanzo zabwino ndi kusonyeza chikondi chaubale kwa abale a dziko limene iwo akupita. Nawonso amene adzalandire alendoŵa adzakhala ndi mwayi wowalandira ndi manja aŵiri ndi kuwachereza ndi mtima wonse. (Ahebri 13:1, 2) Zimenezi zidzachititsa kuti pakhale ‘kutonthozana [“kulimbikitsana,” NW].’ (Aroma 1:11, 12) Nthambi zimene adzazipempha kutumiza nthumwi ku dziko kapena mayiko amene adzawauze zidzafotokoza ndondomeko yonse ya makonzedwe ameneŵa.

Misonkhano yachigawo ya masiku atatu ya 2003 adzaikonza kuti ichitike m’mayiko ambiri monga mwa nthaŵi zonse. Mwa kusonkhana pamodzi, tonse tidzakhala ndi mwayi womvetsera, kuphunzira, ndi kulimbikitsidwa. (Deuteronomo 31:12; 1 Akorinto 14:31) Zimenezi zidzachititsa anthu a Mulungu onse kukhala ndi mwayi ‘wolaŵa ndi kuona kuti Yehova ndiye wabwino.’ (Salmo 34:8) Pa misonkhano yonse ya mayiko, ndiponso pa misonkhano yambiri yachigawo, padzakhala amishonale, omwe ena mwa iwo adzalankhulapo.

M’chaka chino cha 2002, tikhala ndi Misonkhano Yachigawo yakuti “Olengeza Ufumu Achangu,” imene idzatilimbikitsa kulalikira kwambiri. Mosakayika, pamene tikutero chikhumbo chathu chofuna kudziŵa zimene Yehova watikonzera chaka chamaŵa chidzakula. Zimenezi zidzatithandiza ‘kudikira ndi kukhala okonzeka’ poganizira nthaŵi zoŵaŵitsa ndiponso zapadera zino.​—Mateyu 24:42-44.