Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

 Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Kodi n’kololeka kuti mtumiki wachikristu akambe nkhani pa maliro a munthu wodzipha yekha?

Mtumiki wachikristu aliyense angasankhe yekha ngati angakambe nkhani ali ndi chikumbumtima chabwino pa maliro a munthu amene akuoneka kuti wadzipha yekha. Posankha zoti achite, ayenera kuganizira mafunso otsatiraŵa: Kodi Yehova amaona bwanji kudzipha? Kodi munthuyo wadzipha dala? Kodi kuvutika maganizo n’kumene kwam’chititsa kudzipha? Kodi anthu m’deralo amaona bwanji kudzipha?

Ife monga Akristu, timasamala kwambiri mmene Yehova amaonera kudzipha. Yehova amaona moyo wa munthu kukhala wamtengo wapatali ndiponso wopatulika. (Genesis 9:5; Salmo 36:9) Mulungu sasangalala ndi munthu wodzipha yekha mwadala. (Eksodo 20:13; 1 Yohane 3:15) Malinga ndi mfundo imeneyi, kodi ndiye kuti pa maliro a munthu amene wadzipha yekha sangakambepo nkhani ya maliro?

Taganizirani nkhani ya Mfumu Sauli ya Israyeli. Atazindikira kuti sapulumuka pa nkhondo yake yomaliza yolimbana ndi Afilisti, “Sauli anatenga lupanga lake naligwera,” m’malo moti adani ake amuphe mwachipongwe. Afilisti atapeza mtembo wake, anaupachika pa linga la ku Betisani. Anthu a ku Jabezi Gileadi atamva zimene Afilisti anachita, anakachotsa mtembowo n’kuutentha. Ndiyeno anatenga mafupa ake n’kuwaika m’manda. Ndiponso anasala kudya kwa masiku asanu ndi aŵiri, womwe unali mwambo wolira maliro wa Aisrayeli. (1 Samueli 31:4, 8-13; Genesis 50:10) Davide, wodzozedwa wa Yehova atamva zimene anthu a ku Jabezi Gileadi anachita, anati: “Mudalitsike ndi Yehova inu, popeza munachitira chokoma ichi mbuye wanu Sauli, ndi kumuika. Ndipo tsopano Yehova achitire inu chokoma ndi choonadi.” (2 Samueli 2:5, 6) Baibulo silinena kuti anthu a ku Jabezi Gileadi analakwa chifukwa chochita zimene tingati mwambo wa maliro pa maliro a Mfumu Sauli. Yerekezerani zimenezi ndi anthu amene maliro awo sanaikidwe chifukwa cha zolakwa zawo. (Yeremiya 25:32, 33) Mtumiki wachikristu angalingalire nkhani ya Sauli poona ngati angakambe nkhani pa maliro a munthu wodzipha yekha.

Mtumikiyo ayeneranso kuganizira cholinga cha nkhani ya maliro. Mboni za Yehova, mosiyana ndi anthu amene amakhulupirira kuti moyo sufa, sizikamba nkhani ya maliro ndi maganizo olakwika oti alengeze kuti womwalirayo wapita kudziko lina. Cholinga chachikulu cha nkhaniyo sichakuti imuthandize womwalirayo ayi, koma kuti itonthoze anamalira ndi kupereka umboni kwa anthu amene afika pa malirowo wonena za mmene akufa alili. (Mlaliki 9:5, 10; 2 Akorinto 1:3-5) Chifukwa china chachikulu chokambira nkhani ya maliro ndicho kuthandiza anthu amene alipowo kusinkhasinkha za kufupika kwa moyo. (Mlaliki 7:2) Kodi zolinga zimenezi zikwaniritsidwa ngati akamba nkhaniyo pamaliro a munthu wodzipha yekha?

N’zoona kuti ena angaganize kuti munthuyo wadzipha dala, akudziŵa kuti akuchimwira Yehova. Koma kodi n’zotheka nthaŵi zonse kutsimikizira kuti maganizo amenewo ndi oona? Kodi zingakhale kuti zinangochitika mwangozi? Ena amene amafuna kudzipha amasintha maganizo n’kuleka osadzipha. Munthu akamwalira sangalape chifukwa cha zimene anachita.

Mfundo ina yofunika kuiganizira ndiyo kuvutika maganizo komwe kumachititsa ambiri kudzipha. Ameneŵa angatchedwedi anthu odzipha okha. Ena ataŵerengera anapeza kuti anthu 90 mwa  anthu 100 alionse amene amadzipha amakhala ndi vuto la maganizo kapena kukondetsa mankhwala osokoneza bongo. Kodi Yehova adzakhululukira anthu odzipha okha amene anali ndi mavuto a maganizo? Sitingathe kuweruza kuti womwalirayo anachita tchimo losakhululukidwa pamaso pa Yehova kapena ayi. Mtumiki wachikristu angaganizire vuto la womwalirayo komanso matenda amene anadwalapo pamene akuganizira ngati angakambe nkhani pa maliro a munthuyo.

Palinso mfundo ina yofunika kuiganizira: Kodi anthu a m’deralo amaona bwanji kudzipha ndiponso kumwalira kwa munthuyo? Imeneyi ndi mfundo imene makamaka akulu afunika kuiganizira, popeza ayenera kuonetsetsa kuti mbiri ya mpingo wa Mboni za Yehova m’deralo isaipe. Akulu angaganize zoti asakambe nkhani ya maliroyo kwa anthu onse kapena ku Nyumba ya Ufumu malinga ndi mmene anthu ambiri amaonera kudzipha m’deralo, ndiponso makamaka mmene munthu womwalirayo wadziphera.

Komabe, ngati mtumiki wachikristu wapemphedwa kukamba nkhani pa malirowo, mwina angaganize zoti atero, koma payekha osati moimira mpingo. Ngati waganiza kutero, ayenera kusamala kuti asafotokoze mwatchutchutchu kuti munthuyo adzaukitsidwa kapena ayi. Yehova ndi amene akudziŵa zimene womwalirayo angayembekezere ndipo palibe amene anganene kuti munthuyo adzauka kapena ayi. Mtumikiyo angotsindika pa mfundo zoona za m’Baibulo pankhani ya imfa ndi kutonthoza anamalira.