Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mavuto a Anthu Adzathadi?

Kodi Mavuto a Anthu Adzathadi?

 Kodi Mavuto a Anthu Adzathadi?

LIPOTI losonyeza mmene zinthu zilili padziko lonse lochokera ku Ireland linati: “Anthu 1.5 biliyoni padziko lonse ali paumphaŵi wadzaoneni, 1.3 biliyoni amakhala ndi moyo pogwiritsa ntchito ndalama zosakwana dola imodzi ya ku United States patsiku, wani biliyoni sadziŵa kulemba ndi kuŵerenga, 1.3 biliyoni akusoŵa madzi abwino akumwa ndiponso wani biliyoni amagona ndi njala tsiku lililonse.”

Izi zikusonyeza kuti anthu alephera momvetsa chisoni kupeza njira zokhalitsa zothetsera mavuto a dzikoli. Mavutoŵa amanyanyira kumvetsa chisoni kwake podziŵa kuti namtindi mwa anthu amene awatchula mu lipotili ndi amayi ndi ana opanda chitetezo. Kodi si zomvetsa chisoni kuti ngakhale m’zaka za m’ma 2000 zino, ufulu wachibadwidwe “wa anthu osaŵerengeka umaponderezedwabe tsiku lililonse”?​—The State of the World’s Children 2000.

“Dziko Latsopano Mumbadwo Uno Wokha”

Nthambi ya bungwe la United Nations yoona za ana ya United Nations Children’s Fund yati ikukhulupirira kuti “chisoni chomwe mavutoŵa . . . abweretsa padziko lonse chingathe kuthetsedwa.” Bungweli lati, mavuto adzaoneni omwe anthu mabiliyoni ambiri akulimbana nawo panopa titha “kuwapeŵa kapena kuwathetsa.” Ndipotu, bungweli lapempha “anthu onse kuti apange dziko latsopano mumbadwo uno wokha.” Limeneli akuti lidzakhala dziko limene “simudzakhala umphaŵi, kusankhana mitundu, chiwawa ndi matenda.” Anthu onse akuti adzakhala omasuka ku zinthu zimenezi.

Anthu amene akunena zimenezi akulimba mtima chifukwa chakuti ngakhale panopa anthu othandiza anzawo sakugona tulo kugwira ntchito pofuna kuchepetsa mavuto omwe amadza chifukwa cha “nkhondo ndi masoka zomwe zikuoneka kuti sizikutha.” Mwachitsanzo, zaka 15 zapitazi, gulu la Chernobyl Children’s Project “lathandiza kuchepetsa mavuto a ana mazanamazana omwe akudwala matenda a kansa chifukwa cha utsi wa mabomba a nyukiliya.” (The Irish Examiner, April 4, 2000) Mabungwe ang’onoang’ono ndi akuluakulu othandiza anthu ovutika, akuyesetsa kuthandiza anthu osaŵerengeka omwe akuvutika chifukwa cha nkhondo ndi masoka achilengedwe.

Komabe, amene akugwira ntchitoyi akuona zinthu moyenera. Akudziŵa kuti mavuto omwe alipoŵa “afalikira kwambiri ndipo azika mizu kusiyana ndi momwe analili zaka khumi zapitazo.” David Begg yemwe ndi mkulu wa bungwe lothandiza ovutika la ku Ireland anati: “Ogwira ntchito athu, otithandiza, ndiponso mayiko opereka thandizo, anagwira ntchito yaikulu” pamene ku Mozambique kunasefukira madzi owononga. Iye anawonjezera kuti: “Koma tokha sitingakwanitse kuthana ndi masoka aakulu ngati ameneŵa.” Pa za ntchito yothandiza ovutika mu Africa, iye ananena mosabisa kuti: “Chikhulupiriro choti zinthu zidzakhala bwino changokhala ngati makandulo omwe akuzima pang’onopang’ono.” Anthu ambiri akuona kuti mawu ameneŵa akukhudzanso mmene zinthu zilili padziko lonse.

Kunena zoona, kodi tingayembekezeredi “dziko latsopano mumbadwo uno wokha” lomwe alitchula lija? Ngakhale kuti ntchito yothandiza ovutika yomwe ikuchitika panopa ndi yabwinodi, n’kwanzeru kuganizira chiyembekezo china cha dziko latsopano lolungama ndi lamtendere. Baibulo limanena za chiyembekezo chimenechi monga momwe tionere m’nkhani yotsatirayi.

 [Mawu a Chithunzi patsamba 2]

Tsamba 3, ana: Chithunzi cha UN/​DPI chimene anajambula James Bu