Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Chinthu Choposa Chuma cha Aigupto

Chinthu Choposa Chuma cha Aigupto

 Chinthu Choposa Chuma cha Aigupto

MOSE ndi mmodzi mwa anthu akuluakulu m’mbiri yakale. Mabuku anayi a Baibulo, kuyambira Eksodo mpaka Deuteronomo​—pafupifupi onseŵa amakamba zimene Mulungu anachita ndi Aisrayeli pamene Mose anali kulamulira. Iye anawatsogolera kutuluka ku Igupto, anali mkhalapakati wa pangano la Chilamulo, ndipo anatsogolera Aisrayeli mpaka ku malire a Dziko Lolonjezedwa. Mose anakulira m’nyumba ya Farao, ndipo kenako anapatsidwa ulamuliro pa anthu a Mulungu, ndiponso anali mneneri, woweruza, ndi mlembi wouziridwa ndi Mulungu. Ngakhale anali ndi maudindo onseŵa, iye anali “wofatsa woposa anthu onse.”​—Numeri 12:3.

Zambiri zimene Baibulo limanena zokhudza Mose ndi zomwe zinachitika m’zaka 40 zomalizira za moyo wake, kuyambira nthaŵi imene Israyeli anachoka ku ukapolo mpaka kufa kwa Mose ali ndi zaka 120. Kuyambira ali ndi zaka 40 mpaka 80, anali mbusa ku Midyani. Koma buku lina limati, zaka 40 zoyambirira za moyo wake, kuyambira pamene anabadwa mpaka pamene anathaŵa ku Igupto “ziyenera kuti ndizo mbali yosangalatsa kwambiri ya moyo wake, komano ndi imene sidziŵika.” Koma kodi tingadziŵepo chiyani pa zomwe zinachitika m’nthaŵi imeneyi? Kodi moyo umene Mose anakulira unakhudza motani moyo umene anadzakhala? Kodi ndi zochitika zotani zimene zinali kumukhudza? Kodi anakumana ndi mavuto otani? Ndipo kodi tingaphunzire chiyani pa zonsezi?

Ukapolo ku Igupto

Buku la Eksodo limasimba kuti Farao anayamba kuwaopa Aisrayeli a mu Igupto chifukwa chakuti anali kuchulukana kwambiri. Poganiza kuti ‘akuwachenjerera,’ Farao anayesa kuchepetsa chiŵerengero chawo mwa kuwagwiritsa ntchito yaukapolo mwankhanza, kuuza akapitawo kuti aziwakwapula, kunyamula katundu wolemera, kukumba dothi, ndiponso kuumba njerwa zimene aliyense amayenera kuumba tsiku lililonse.​—Eksodo 1:8-14; 5:6-18.

Chithunzi cha momwe moyo unalili ku Igupto, kumene kunabadwira Mose chikugwirizana ndendende ndi zimene mbiri imanena. Zomwe analemba pa gumbwa kalekale ndiponso zomwe analemba pa manda ena ake, zimafotokoza kuti m’ma 2000 B.C.E., kapena nthaŵiyi isanafike, akapolo ankaumba njerwa ku Igupto. Nduna zoyang’anira kuumba njerwako zinali ndi akapolo ambiri omwe  zinkawaika m’magulu a anthu 6 mpaka 18 ndiponso kuika woyang’anira pa gululo. Ankakumba dothi loumbira njerwa ndiponso kukanyamula udzu kupita nawo kumene amaumbira njerwazo. Anthu amitundu yosiyanasiyana ankatunga madzi, ndipo ankagwiritsa ntchito makasu posakaniza dothi ndi udzuwo. Ankaumba njerwa zambiri pogwiritsa ntchito chikombole cha makona anayi. Ndiyeno antchitowo ankanyamula goli lokhala ndi mabasiketi onyamuliramo njerwa zimene zauma ndi dzuŵa kupita nazo kumene akazigwiritse ntchito, nthaŵi zina njira imene ankadutsa inali yotsetsereka. Aigupto oyang’anira, ankagwira ntchito yawo chokhala pansi kapena kuyenda pang’onopang’ono kwinaku atanyamula ndodo.

Chikalata china chakale chimatchula kuti antchito 602 anaumba njerwa 39,118, kutanthauza kuti munthu m’modzi amaumba njerwa pafupifupi 65 asanasinthane ndi wina. Ndipo chikalata cha m’ma 1200 B.C.E., chimati: “Amuna amamaliza . . . kuumba njerwa zimene akufunika kuumba tsiku lililonse.” Zonsezi zikufanana kwambiri ndi ntchito imene buku la Eksodo limatchula kuti Aisrayeli anali kugwira.

Kuwazunza kumeneko sikunachepetse chiŵerengero cha Ahebri. Komano, “monga momwe [Aigupto] anawasautsiramo, momwemo anachuluka . . . Ndipo anavutika chifukwa cha ana a Israyeli.” (Eksodo 1:10, 12) Ndiyeno, choyamba Farao analamula azamba achihebri kupha makanda amuna onse a Aisrayeli kenako analamula anthu ake onse kuchitanso zomwezo. Mu nthaŵi yovuta imeneyi Yokobedi ndi Amramu anabala mwana wamwamuna wokongola, dzina lake Mose.​—Eksodo 1:15-22; 6:20; Machitidwe 7:20.

Anamubisa, Anamupeza, Ndipo Anamulera

Makolo a Mose sanamvere lamulo la Farao loti aphe ana ndipo anabisa mwana wawoyo. Kodi anachita zimenezo ngakhale kuti panali azondi ndiponso anthu ena ofufuza makanda m’makomo? Sitikudziŵa bwinobwino. Mulimonse mmene zinalili, patatha miyezi itatu makolo a Mose sakanamubisanso. Choncho mayi wake, mothedwa nzeru analuka kabokosi kagumbwa ndi kukamata phula kuti musaloŵe madzi, ndipo anaikamo mwanayo. Tingati, Yokobedi anamverabe mawu a Farao ngakhale kuti anachita zosiyana ndi zimene iye amafuna kwenikweni zoti mwana aliyense wa mwamuna wa Ahebri am’ponye m’mtsinje wa Nile. Ndiyeno Miriamu, mlongo wamkulu wa Mose, anaima chapafupi kumayang’anira kabokosiko.​—Eksodo 1:22–2:4.

Sitikudziŵa ngati Yokobedi anali ndi cholinga chakuti mwana wamkazi wa Farao adzapeze Mose akabwera ku mtsinjeko kudzasamba, koma zimenezi n’zimene zinachitika. Mwana wamkazi wa mfumuyo anazindikira kuti mwanayo anali wa Ahebri. Kodi iye anachita chiyani? Kodi iye momvera atate ake, analamula kuti mwanayo aphedwe? Ayi, anachita monga momwe amayi ambiri amachitira mwachibadwa. Anachita chifundo.

Miriamu anafika pafupi ndi mwana wa mfumuyo. Ndipo anafunsa kuti, ‘Ndipite kodi  kukakuitanirani woyamwitsa wa Ahebri, akuyamwitsireni mwanayo?’ Ena amaona kuti zimene zinachitika pankhaniyi n’zimene simungayembekezere kuti zichitike. Zomwe anachita mlongo wa Mose n’zosiyana ndi zimene anachita Farao, amene anapangana ndi aphungu ake kuti ‘awachenjerere’ Ahebri. Inde, zinali zotsimikizirika kuti Mose akhala wamoyo pamene mwana wamkazi wa mfumu anavomereza zimene mlongo wake wa Mose ananena. Mwana wamkazi wa Farao nati, “Pita,” ndipo nthaŵi yomweyo Miriamu anakatenga mayi ake. Zotsatira zake zinali zakuti, Yokobedi ndi amene anamulemba ntchito yolera mwana wake yemwe motetezedwa ndi banja lachifumu, zomwe simungayembekezere kuti zingachitike.​—Eksodo 2:5-9.

Chifundo cha mwana wamkazi wa Farao chikusiyana ndi nkhanza za atate ake. Sikuti sanadziŵe kapena ananamizidwa za mwanayo ayi. Chisoni chochokera pansi pamtima chinamulimbikitsa kutenga mwanayo. Ndiponso kuvomereza mfundo yokaitana mayi wachihebri kuti aziyamwitsa mwanayo kumasonyeza kuti analibe mtima woipa wa atate wake.

Kuleredwa ndi Kuphunzira

Yokobedi “anatenga mwanayo, nam’yamwitsa. Ndipo atakula mwanayo, anapita naye kwa mwana wamkazi wa Farao, ndipo iye anakhala mwana wake.” (Eksodo 2:9, 10) Baibulo silimanena kuti Mose anakhala nthaŵi yaitali motani ndi makolo ake om’berekawo. Ena amaganiza kuti mwina anakhala nawo mpaka atasiya kuyamwa​—zaka ziŵiri kapena zitatu​—koma n’kutheka kuti panapita nthaŵi yaitalipo ndithu. Eksodo amangonena kuti ‘anakula’ ndi makolo ake, zimene zingatanthauze zaka zosadziŵika kwenikweni. Mulimonse mmene zinalili, mosakayikira Amramu ndi Yokobedi anagwiritsa ntchito nthaŵi imeneyo kuuza mwana wawoyo kuti ndi m’Hebri ndiponso kumuphunzitsa za Yehova. Zinali kudzadziŵika m’tsogolo kuti makolo ake anakhomerezadi kwambiri chikhulupiriro ndi kukonda chilungamo mwa Mose.

Atapita kwa mwana wamkazi wa Farao, Mose anaphunzira “nzeru zonse za Aaigupto.” (Machitidwe 7:22) Zimenezi zingatanthauze kuti Mose anaphunzira zonse zofunika kuti akhale mu ofesi ya boma. Maphunziro ambiri a Aigupto anali Masamu, zomangamanga, ndiponso maluso ena ndi sayansi. Mwina, banja lachifumu linkafuna kuti aphunzire chipembedzo cha Aigupto.

Mwina Mose anaphunzira maphunziro ake apaderaŵa pamodzi ndi ana ena abanja lachifumu. Ena amene anaphunzira maphunziro apamwambawa ndi “ana a anthu olamulira mayiko ena amene amawatumiza kapena kuwatengera ku ukapolo ku Igupto kuti ‘akaphunzire’ ndiyeno akalamulire monga atumiki” okhulupirika a Farao. (limatero buku lakuti The Reign of Thutmose IV, lomwe analemba Betsy M. Bryan) Sukulu zamkaka zimene ana achifumu ankaphunzira zinkathandiza achinyamata kudzakhala nduna. * Zimene anazilemba mu nthaŵi ya Ufumu Wapakati wa Aigupto ndi Ufumu Watsopano zimasonyeza kuti atumiki ambiri a Farao ndiponso maofesala aboma apamwamba, kaya ndi aakulu, ankagwiritsabe ntchito dzina laulemu lakuti “Mwana wa Sukulu ya Mkaka.”

Kukhala m’nyumba ya mfumu kunaika Mose pachiyeso. Moyo wake unali wamwanaalirenji, wabwino, ndiponso anali wolamulira. Komanso zinali zosavuta kutengera makhalidwe oipa. Kodi Mose akanatani? Kodi akanakhala wokhulupirika kwa ndani? Kodi analidi wolambira Yehova, mbale wa Ahebri amene anali kuzunzidwa, kapena anakomedwa  ndi zimene Aigputo osakhulupirirawo anam’chitira?

Chosankha Chofunika

Mose ali ndi zaka 40, ‘anatuluka kukapenya akatundu a abale ake,’ ngakhale kuti panthaŵiyi akanakhala ali m’Igupto weniweni. Zimene anachita zimasonyeza kuti sikuti ankangofuna kukawaona ayi; ankafunitsitsa kuwathandiza. Ataona Mwaigupto akumenya Mhebri, iye analoŵera ndewuyo, ndi kupha munthu wankhanzayo. Zimene anachitazo zinasonyeza kuti anali kuganizira abale ake. Mwachionekere munthu amene anamuphayo anali nduna ndipo anaipha ikugwira ntchito yake. Aigupto ankaona kuti Mose anali ndi zifukwa zonse zokhalira wokhulupirika kwa Farao. Koma chinalimbikitsanso Mose chinali kukonda chilungamo, khalidwe limene anaonetsanso tsiku lotsatira pamene analetsa Mhebri amene amamenya mnzake popanda chifukwa. Mose anafuna kumasula Ahebri ku ukapolo wankhanza, koma Farao atamva za kupanduka kwa Mose anafuna kumupha ndipo Mose anakakamizika kuthaŵira ku Midyani.​—Eksodo 2:11-15; Machitidwe 7:23-29. *

Nthaŵi imene Mose ankafuna kumasula anthu a Mulungu inali yosagwirizana ndi ya Yehova. Komabe, zochita zake zinasonyeza chikhulupiriro. Ahebri 11:24-26 amati: “Ndi chikhulupiriro Mose, atakula msinkhu, anakana kutchedwa mwana wake wa mwana wamkazi wa Farao; nasankhula kuchitidwa zoipa pamodzi ndi anthu a Mulungu, kosati kukhala nazo zokondweretsa za zoipa nthaŵi.” Chifukwa? Chifukwa chakuti ‘anaŵerengera chitonzo cha Kristu chuma choposa zolemera za Aigupto; pakuti anapenyerera chobwezera cha mphoto.’ Kugwiritsa ntchito mawu akuti “Kristu” m’njira yapaderayi, kutanthauza “wodzozedwa,” kukumuyenera Mose chifukwa chakuti, m’kupita kwa nthaŵi Yehova anamupatsa ntchito yapadera.

Tangolingalirani! Mose analeredwa m’moyo umene unali wa ana achifumu a ku Igupto okha. Udindo wake, unali woti akanakhala pantchito yabwino ndi yosangalatsa kwambiri, koma anakana zonsezi. Anaona kuti moyo m’nyumba ya Farao wankhanzayo, sunali wogwirizana ndi kukonda Yehova ndi chilungamo. Kuzindikira ndi kulingalira zimene Mulungu analonjeza atate wake Abrahamu, Isake, ndi Yakobo kunathandiza Mose kusankha kuyanjidwa ndi Mulungu. Choncho, Yehova anagwiritsa ntchito Mose pantchito yofunika kwambiri yokwaniritsa cholinga Chake.

Tonse timafunika kusankha zinthu zimene zili zofunika kwambiri. Monga Mose, mwina mukufunika kusankha zinthu zovuta kwambiri. Kodi mungasiye zinthu zina zimene munazoloŵera kuchita ngakhale zitakhala zovuta kwambiri kuzisiya? Kapena kodi mungasiye zinthu zimene zikuchita kuonekeratu kuti n’zaphindu ngakhale zitakhala zochuluka kwambiri? Ngati n’zimene mukufuna kusankha, kumbukirani kuti Mose anaona ubwenzi ndi Yehova kukhala wofunika kwambiri kuposa chuma chonse cha Aigupto, ndipo sanadandaule.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 17 Maphunziro ameneŵa angafanane ndi amene Danieli ndi anzake aja anaphunzira kuti akagwire ntchito za boma ku Babulo. (Danieli 1:3-7) Yerekezani ndi buku la Samalani Ulosi wa Danieli!, mutu 3, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 20 Zoti Mose anali wokonda chilungamo zikuonekeranso pa zimene anachita kumene anathaŵira. Iye anathandiza abusa achikazi amene analibe wowathandiza kwa m’Midyani wankhanza.​—Eksodo 2:16, 17.

[Bokosi patsamba 11]

Ntchito Yoyamwitsa Mwana

Mwachibadwa, amayi amayamwitsa ana awo. Komabe, m’magazini ya Journal of Biblical Literature, katswiri wina wamaphunziro, Brevard Childs, anati, “nthaŵi zina mabanja achifumu [kufupi ndi Kum’mawa] anali kulemba ntchito mayi woyamwitsa mwana. Izi zinali kuchitikanso ngati mayi amwanayo akulephera kudyetsa mwanayo kapena sakudziŵika. Mayiyu anali ndi udindo wolera ndi kuyamwitsa mwanayo kwa nthaŵi imene agwirizana.” Malembo ambiri a pagumbwa amati ntchito yoyamwitsa ana inayambira ku Near East kalekale. Makalata ameneŵa akutsimikizira kuti zimenezi zinalidi zofala mu nthaŵi ya ulamuliro wa Chisumeriya mpaka kumapeto kwa ulamuliro wa Chihelene ku Igupto. Nkhani zimene zimapezeka m’makalata ameneŵa ndi zimene amakambirana anthu amene akugwira ntchito yoyamwitsa mwanayo, utali umene agwirizana kulera mwanayo, malamulo antchitoyo, mitundu ya zakudya, ndalama zimene wantchitoyo adzalipire akapanda kuchita zimene agwirizanazo, malipiro ake, ndi momwe azim’lipirira. Childs anati, nthaŵi zambiri, “ntchito yoyamwitsa ana imatenga zaka zoposa ziŵiri kapena zitatu. Mayiyu amayamwitsira mwanayo kunyumba kwake, koma nthaŵi zina ankapita naye mwanayo kwa mwini wake kuti akamuone.”

[Zithunzi patsamba 9]

Kuumba njerwa ku Igupto sikunasinthe kwenikweni monga ankachitira m’nthaŵi ya Mose, malinga ndi momwe chithunzi chakale chikusonyezera

[Mawu a Chithunzi]

Chithunzi chapamwambacho: Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.; chili munsicho: Erich Lessing/​Art Resource, NY