Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Chimene Tingaphunzirepo pa Mbiri ya Aroma

Chimene Tingaphunzirepo pa Mbiri ya Aroma

 Chimene Tingaphunzirepo pa Mbiri ya Aroma

“NGATI ndinalimbana ndi zilombo ku Efeso monga mwa munthu.” Ena amaganiza kuti mawu ameneŵa, a pa 1 Akorinto 15:32, amatanthauza kuti mtumwi Paulo anam’patsa chilango chomenyana ndi munthu wina m’bwalo la maseŵera la Aroma. Kaya anamenyanadi kapena ayi, chodziŵika n’chakuti m’mabwalo amaseŵera panthaŵiyo sichinali chachilendo anthu kumenyana mpaka wina atafa. Kodi mbiri imatiuza chiyani za m’mabwalo a maseŵera ameneŵa ndiponso zimene zinkachitika kumeneko?

Monga Akristu, timafuna kukhala ndi chikumbumtima chogwirizana ndi maganizo a Yehova, chimene chingatithandize kuganiza bwino posankha zochita, pankhani za maseŵera a masiku ano. Mwachitsanzo, onani maganizo a Mulungu pankhani ya chiwawa, m’mawu aŵa: “Usachitire nsanje munthu wachiwawa; usasankhe njira yake iliyonse.” (Miyambo 3:31) Akristu oyambirira ankawalangiza zimenezi kuti ziwatsogolere pamene anthu ambiri m’nthaŵi yawo ankasangalala ndi maseŵera omenyana achiroma. Pamene tikupenda  zimene zinkachitika m’maseŵerawo, tiyeni tione zimene Akristu lerolino akuphunzirapo pankhaniyi.

Anthu aŵiri okonzekera kumenyana mogwiritsa ntchito zida aloŵa m’bwalo la maseŵera lachiroma. Atangoyamba kutemana ndi lupanga pa zishango, khamu la anthu likuchemerera munthu amene limamukonda. Imeneyi ndi ndewu yafumbi. Mosakhalitsa, wina akuponya zida zake pansi ndi kugwada chifukwa chakuti wapwetekedwa ndipo kuti sangathe kupitiriza. Akuchita zimenezi kusonyeza kuti wagonja ndipo akupempha kuti am’chitire chifundo. Anthu akukuwa kwambiri. Anthu ena m’gululo akufuula kuti am’chitire chifundo munthuyo, ena akuti aphedwe. Aliyense akuyang’ana mfumu. Iyo ikamvetsera zimene khamulo likufuna, ikhoza kumasula munthu amene wagonjayo kapena ingasonyeze chizindikiro choti aphedwe.

Aroma ankasangalala kwambiri kuonerera maseŵera omenyana. Mungadabwe kumva kuti ndewu zimenezi poyambirira zinkachitika pamaliro a anthu otchuka kwambiri. Pali chikhulupiriro chakuti maseŵerawa anawayambitsa ndi anthu a ku Osikani kapena Saminayiti, komwe masiku ano kumatchedwa chigawo chapakati cha Italy. Anthuŵa anali kupereka anthu nsembe pofuna kusangalatsa mizimu ya anthu akufa. Zochitika zimenezi ankati ndi munus, kapena “mphatso” (zikakhala zambiri ankati, munera). Mbiri ikuti maseŵera oyambirira a mtunduwu ku Roma anachitika mu 264 B.C.E. pamene magulu atatu a anthu aŵiriaŵiri anamenyana mumsika wa ng’ombe. Pamaliro a Marcus Aemilius Lepidus, panachitika ndewu 22 za anthu aŵiriaŵiri. Pamaliro a Publius Licinius, magulu 60 a anthu aŵiriaŵiri anamenyana. Mu 65 B.C.E., Julius Caesar anatumiza magulu 320 a anthu aŵiriaŵiri kukamenyana m’bwalo la maseŵera.

Wolemba mbiri Keith Hopkins anati, “mwambo wa maliro wa anthu otchuka ankaugwiritsa ntchito pa zolinga zandale, ndipo maseŵera apamaliro oterewa anali okhudza ndale . . . chifukwa chakuti anthu omwe ankakonda maseŵeraŵa anali nzika zoyenerera kuchita nawo chisankho. Maseŵeraŵa ankasangalatsa kwambiri popeza ankakhudza mipikisano ya mafumu otchuka kwambiri pa ndale.” Mu ulamuliro wa Augustus (kuyambira 27 B.C.E. mpaka 14 C.E.) munera zinali mphatso zapamwamba​—zosangalatsira anthu wamba​—zimene maofesala olemera a boma ankapereka polimbikitsa ntchito yawo yandale.

Oseŵera Ndiponso Maphunziro Awo

Mungafunse kuti, ‘Kodi ankamenyanawo ndani?’ Anali akapolo, anthu olakwa amene awaweruza kuti aphedwe, asilikali amene agwidwa ukapolo, kapena anthu wamba ongofuna kusangalala kapena kutchuka ndiponso chuma. Onse ankawaphunzitsa m’sukulu zangati ndende. Buku lakuti Giochi e spettacoli (Maseŵera ndi Zionetsero) limanena kuti anthu omenyanaŵa akamaphunzira “alonda ankawayang’anira nthaŵi zonse ndipo ankalandira chilango chokhwima, malamulo oipa kwambiri, ndipo makamaka zilango zinali zankhanza . . . Kaŵirikaŵiri zimenezi zinkapangitsa anthuŵa kudzipha, kupanduka, ndi kuukira.” Sukulu yaikulu ya Aroma yophunzitsa anthu kumenya inali ndi tizipinda ta munthu mmodzimmodzi tokwana pafupifupi 1000. Munthu aliyense ankamuphunzitsa kukhala katswiri pa mbali inayake. Ena ankamenya pogwiritsa ntchito zida zodzitetezera, zishango, ndi malupanga. Ena ankagwiritsa ntchito ukonde ndiponso mikondo ya mano atatu. Komabe ena ankaphunzira kumenyana ndi nyama m’maseŵera ena otchuka, otchedwa kusaka. Kapena kodi Paulo anali kunena za maseŵera ameneŵa?

Anthu amene ankakonza maseŵera ameneŵa ankapempha thandizo kwa anthu amalonda amene ankalemba anthu a zaka zoyambira 17 kapena 18 ndi kuwaphunzitsa kumenya. Malonda ogulitsa anthu anali a ndalama kwabasi. Chionetsero china chimene Talajani anachita pokondwera kuti asilikali  apambana nkhondo anali ndi anthu 10,000 ndi nyama 11,000.

Zochitika M’bwalo la Maseŵera

Nthaŵi ya m’maŵa ku bwalo la maseŵera inali nthaŵi ya maseŵera otchedwa kusaka. Nyama za kuthengo za mitundu yonse ankazikakamiza kuloŵa m’bwalomo. Anthu oonerera ankasangalala ng’ombe ikamamenyana ndi chimbalangondo. Nthaŵi zambiri ankazimanga pamodzi nyamazi kuti zimenyane mpaka ina ife, ndiyeno yotsalayo ankaipha ndi mlenje. Maseŵera ena otchuka ankamenyanitsa mikango ndi njuzi, kapena njobvu ndi chimbalangondo. Alenje ankasonyeza luso lawo pa kupha nyama zakunja zomwe ankazibweretsa m’dziko lawolo, mosasamala kanthu kuti amawononga ndalama zochuluka motani. Nyamazi zinali monga akambuku, zipembere, mvuwu, akadyamsonga, afisi, ngamila, mimbulu, nkhumba, ndi agwape.

Zimene zinkachitika pamaseŵera osakawo zinkasangalatsa anthu kwambiri. M’bwalomo ankaikamo miyala, madzi, ndi mitengo kuti muoneke ngati m’nkhalango. M’mabwalo ena, nyama zinkaoneka ngati zabwera mwamatsenga kuchokera pansi ndiponso kumwamba. Khalidwe lachilendo la nyama linkawonjezera kuti zinthu zikhale zosangalatsa, koma zimene zinapangitsa maseŵera a kusaka kukhala osangalatsa kwambiri zinali nkhanza zimene anthu ankachita.

Kenako anthu akupha ndi amene ankaloŵa m’bwalomo. Ankayesetsa kuchita zimenezi ngati kuti zikuchitikadi. Maseŵera ena oyerekezera zimene zinachitika anali kuonetsa anthu oseŵerawo akufadi.

Madzulo, magulu osiyanasiyana a anthu omenyana onyamula zida zosiyanasiyana ndiponso ophunzitsidwa maluso osiyanasiyana ankamenyana. Ena mwa amene ankatulutsa mitembo ankavala monga mulungu wa kumidima.

Mmene Zinkakhudzira Anthu Oonerera

Anthu oonerera sankakhutira ndi zimene aona, choncho anthu omenyana omwe akuchita ulesi anali kuwakwapula ndi ndondo ndiponso zitsulo zotentha kuti azimenyana kwambiri. Khamu la anthu linkafuula kuti: “N’chifukwa chiyani akuopa kumenyedwa? N’chifukwa chiyani akumenya monyengerera? Bwanji akuopa kufa? M’kwapuleni kuti apse mtima ayambe kumenya! Asiyeni abwezerane, amenyane ndi lupangalo atavula malaya!” Nduna ina ya boma yachiroma dzina lake Seneca, inalemba kuti panthaŵi yopuma ankalengeza kuti: “Pakhala kupha anthu panthaŵi yopuma ino, kuti pakhalebe zosangalatsa panthaŵiyi!”

N’zosadabwitsa kuti, Seneca akuti anapita kunyumba “ali wankhanza kwambiri komanso woipa mtima.” Mawu oona a munthu woonerera ameneyu, akufunika kuti tiwalingalire mofatsa. Kodi maseŵera ena amasiku ano, anthu oonerera zingawakhudze mofananamo, kukhala “ankhanza kwambiri ndi oipa mtima”?

Ena angati ndi amwayi popeza amabwerera kwawo ali bwinobwino. Pamene munthu wina amene ankaonerera maseŵerawa ananena zoseketsa zokhudza mfumu Domitani, mfumuyo inam’kokapo pampando  wake ndipo inamuponya kwa agalu. Chifukwa chakuti panalibe anthu olakwa oti awaphe, Caligula analamula kuti khamu lina la anthu aligwire ndi kuliponya ku nyama zolusa. Ndipo makina a m’bwalolo akapanda kugwira bwino ntchito yake momwe mfumu Klaudiyo ankafunira, iye ankalamula okonza makinawo kuti akamenyane m’bwalo la maseŵera.

Okondetsetsa maseŵera ankayambitsanso mavuto ndi zipolowe. Bwalo la maseŵera la kumpoto kwa Roma linagwa, ndipo anthu ambirimbiri akuti anafa. Chipolowe chinaulika pa maseŵera ena ku Pompeii mu 59 C.E. Tasitasi anati kumenyana pakati pa anthu okhala kumeneko ndi anthu a m’tauni yoyandikana nayo kunayamba ndi kunyozana, kenako kugendana, mapeto ake anamenyana ndi malupanga. Anthu ambiri anadulidwa ziwalo kapena kuvulazidwa ndipo ambiri anaphedwa.

Phunziro Lomveka Bwino

Chionetsero cha posachedwapa (Sangue e arena, “Magazi ndi Mchenga”) ku bwalo lalikulu la maseŵera la Colosseum ku Rome chinafanana ndi maseŵera a munera a makedzana. Chinaonetsa mbali zina za vidiyo yosonyeza ng’ombe zikumenyana, anyamata ankhonya ophunzitsidwa bwino, mpikisano wa magalimoto ndi njinga zamoto, anthu akuchita maseŵera omenyana mosaletseka, ndiponso zipolowe za anthu openyerera. Pomaliza chionetserocho, anaonetsa mmene bwalo la Colosseum limaonekera ukakhala mu mlengalenga. Kodi mukuganiza kuti anthu oonerera pamapeto pake ankati chiyani? Kodi ndi anthu angati amene anatengapo phunziro?

Masiku ano kumenyanitsa agalu, atambala, ng’ombe, ndiponso maseŵera achiwawa ndi zofala m’mayiko ena. Pa mpikisano wa magalimoto ndi njinga anthu amaika miyoyo pachiswe n’cholinga chosangalatsa anthu. Ndipo tangolingalirani za mapulogalamu a pa TV. Kafukufuku amene anachitika m’dziko lina la azungu anasonyeza kuti mwana amene amaonera TV, pamene azidzafika zaka khumi n’kutheka kuti adzakhala ataonera anthu pafupifupi 10,000 akuphedwa ndiponso maseŵera achiwawa pafupifupi 100,000.

Tertullian, wolemba nkhani wa m’ma 200 C.E., anati, kusangalala ndi maseŵeraŵa “sikugwirizana ndi chipembedzo choona ndiponso kumvera ndi mtima wonse Mulungu woona.” Iye ankaona anthu opita ku maseŵerawo kuti amathandiza anthu amene amapha anzawowo. Bwanji lerolino? Aliyense angadzifunse kuti, ‘Kodi ndimasangalala ndi maseŵera okhetsa magazi, opha anthu, kapena achiwawa pa TV kapena pa Intaneti?’ Ndi bwino kukumbukira kuti Salmo 11:5 limati: “Yehova ayesa wolungama mtima: Koma moyo wake umuda woipa ndi iye wakukonda chiwawa.”

[Bokosi patsamba 28]

Kumenyana N’cholinga “Chosangalatsa Akufa”

Ponena za chiyambi cha maseŵera omenyana, Tertullian, wolemba nkhani wa m’ma 200 C.E., anati: “Anthu akale ankaganiza kuti mwa kuchita maseŵera ameneŵa anali kutumikira akufa. Iwo ankakometsera maseŵerawo mwa kusonyeza njira zatsopano zankhanza. Kale, pokhulupirira kuti mizimu ya akufa imasangalala ndi magazi a anthu, pamaliro ankakonda kupereka nsembe akapolo kapena akapolo onyozeka kwambiri amene anawagula. Ndiyeno anaganiza kuti ndi bwino kubisa kusalemekeza kwawo zinthu zopatulika mwa kumachita zimenezi monga maseŵera. Choncho anthu ogwidwawo akaphunzitsidwa kwambiri kumenya ndi zida zimene anali nazo panthaŵiyo​—ankawaphunzitsa kuphedwa​—ndiyeno patsiku la maliro anali kukawaphera kumanda. Choncho anthu nthaŵi imeneyo ankasangalala kufa mochita kuphedwa. Ichi ndicho chiyambi cha munus. Koma patapita nthaŵi pang’ono zochitikazi zinapita patsogolo moti kutukuka kwa chikhalidwe kunali kuyendera limodzi ndi zochitika za nkhanzazi, popeza holide yopanda nyama zolusa zothandiza kukhadzula matupi a anthu ankaiona kuti siyosangalatsa. Chimene anali kupereka posangalatsa akufa ndicho ankati mwambo wa maliro.”

[Chithunzi patsamba 27]

Chisoti ndiponso zotetezera miyendo zimene amavala kale pomenyana

[Zithunzi patsamba 29]

Akristu akale ankaona kuti maseŵera achiwawa sanali abwino. Kodi inunso mumatero?

[Mawu a Chithunzi]

Nkhonya: Dave Kingdon/​Index Stock Photography; ngozi ya galimoto: AP Photo/​Martin Seppala

[Mawu a Chithunzi patsamba 26]

Phoenix Art Museum, Arizona/​Bridgeman Art Library