Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kupindula ndi Kukoma Mtima kwa Yehova

Kupindula ndi Kukoma Mtima kwa Yehova

 Kupindula ndi Kukoma Mtima kwa Yehova

“Wokhala nazo nzeru . . . azindikire zachifundo za [“kukoma mtima kwa,” NW] Yehova.”​—SALMO 107:43.

1. Kodi liwu la Chihebri lotembenuzidwa kuti “kukoma mtima” analigwiritsa ntchito liti koyamba m’Baibulo, ndipo ndi mafunso ati okhudza khalidwe limeneli amene tikambirane?

ZAKA pafupifupi 4,000 zapitazo, Loti, mwana wa mphwake wa Abrahamu, anauza Yehova kuti: “Munakuza chifundo chanu.” (Genesis 19:19) Aŵa ndi malo oyamba m’Baibulo pamene pamapezeka liwu la Chihebri limene mu New World Translation of the Holy Scriptures analitembenuza kuti “kukoma mtima.” Yakobo, Naomi, Davide ndi atumiki ena a Mulungu anatchulanso khalidwe la Yehova limeneli. (Genesis 32:10; Rute 1:8; 2 Samueli 2:6) Ndipotu, liwu lakuti “kukoma mtima” limapezeka maulendo pafupifupi 250 mu New World Translation of the Holy Scriptures. Koma kodi kukoma mtima kwa Yehova n’chiyani? Kodi iye anakomera mtima ndani kalelo? Ndipo kodi timapindula bwanji ndi khalidwe limeneli masiku ano?

2. N’chifukwa chiyani liwu la Chihebri limene alimasulira kuti “kukoma mtima” n’lovuta kufotokoza, ndipo njira ina yabwino yolimasulira ndi iti?

2 M’Malemba, mawu a “kukoma mtima” amamasulira liwu la Chihebri limene tanthauzo lake ndi lozama kwambiri moti zinenero zambiri zilibe liwu limodzi limene lingapereke tanthauzo lake lonse. Motero, mawu akuti “chifundo,” ‘zokoma,’ ndi ‘ufulu,’ opezeka m’malemba ogwidwa m’Baibulo la Chicheŵa la Revised Nyanja (Union) Version,  * m’nkhani ino ndi yotsatira, ndiponso mawu akuti “chikondi,” ndi “kukhulupirika” safotokoza mokwanira tanthauzo lonse la liwulo. Komabe, Baibulo la New World Translation of the Holy Scriptures limamasulira bwino liwu la Chihebrilo kukhala “kukoma mtima,” limene limakhudza zochuluka ndipo silisiyana kwambiri ndi tanthauzo la liwulo.​—Eksodo 15:13; Salmo 5:7.

Kusiyana Kwake ndi Chikondi ndi Kukhulupirika

3. Kodi kukoma mtima kumasiyana bwanji ndi chikondi?

3 Mawu a kukoma mtima ndi ogwirizana ndi mawu akuti chikondi ndi kukhulupirika. Komabe, kukoma mtima kumasiyana ndi makhalidwe ameneŵa m’njira zofunika kwambiri. Taonani mmene kukoma mtima kumasiyanirana ndi chikondi. Munthu angathe kukonda zinthu kapena maganizo ena ake. Baibulo limanena za ‘kukonda vinyo ndi mafuta’ ndiponso ‘kukonda nzeru.’ (Miyambo 21:17; 29:3) Koma munthu amakomera mtima anthu anzake basi, osati maganizo ena ake kapena zinthu zopanda moyo. Mwachitsanzo, pa Eksodo 20:6 akunena za anthu pamene akuti Yehova ‘akuwachitira chifundo anthu zikwizikwi.’

4. Kodi kukoma mtima kumasiyana bwanji ndi kukhulupirika?

4 Liwu la Chihebri limene analitembenuza kuti “kukoma mtima” lili ndi tanthauzo lokhudza mbali zambiri kusiyana ndi liwu lakuti “kukhulupirika.” M’zinenero zina, nthaŵi zambiri liwu lakuti “kukhulupirika” amaligwiritsa ntchito kusonyeza mtima umene munthu wamng’ono ayenera kukhala nawo kwa munthu wamkulu. Koma malinga ndi wofufuza wina, liwu la kukoma mtima m’Baibulo “nthaŵi zambiri limatanthauza zosemphana kwambiri ndi zimenezo: wamphamvu amakhulupirika  kwa wopanda mphamvu kapena wovutika.” N’chifukwa chake Mfumu Davide inapempha Yehova kuti: “Walitsani nkhope yanu pa mtumiki wanu: mundipulumutse ndi chifundo chanu.” (Salmo 31:16) Pano Yehova wamphamvuyo akupemphedwa kukomera mtima munthu wovutika, Davide. Popeza munthu wovutika sangalamule munthu amene ali ndi ulamuliro, waulamuliroyo amasonyeza kukoma mtima mwa kufuna kwake osati mochita kumuumiriza.

5. (a) Kodi Mawu a Mulungu amafotokoza kuti kukoma mtima kwake kumachita chiyani? (b) Kodi tikambirana mbali ziti zimene Yehova amasonyezera kukoma mtima?

5 Wamasalmo ananena kuti: “Wokhala nazo nzeru . . . azindikire zachifundo za Yehova.” (Salmo 107:43) Kukoma mtima kwa Yehova kungalanditse ndi kupulumutsa. (Salmo 6:4; 119:88, 159) Kumateteza ndiponso kumathandiza kuchepetsa mavuto. (Salmo 31:16, 21; 40:11; 143:12) N’zotheka kumasuka ku uchimo chifukwa cha khalidwe limeneli. (Salmo 25:7) Tiona popenda nkhani zina za m’Malemba ndiponso malemba ena a m’Baibulo kuti kukoma mtima kwa Yehova (1) amakusonyeza mwa kuchitapo kanthu ndiponso (2) atumiki ake okhulupirika amawakomera mtima.

Kusonyeza Kukoma Mtima Kumaoneka mwa Kulanditsa

6, 7. (a) Kodi Yehova anakuza bwanji kukoma mtima kwake kwa Loti? (b) Kodi ndi liti pamene Loti anatchula kukoma mtima kwa Yehova?

6 Mwina njira yabwino yodziŵira kuti kukoma mtima kwa Yehova kumakhudza mbali zotani ndiyo kupenda nkhani za m’Malemba zimene zikutchula khalidwe limeneli. Pa Genesis 14:1-16 tikupeza kuti magulu ankhondo a adani anatenga Loti, mwana wa mphwake wa  Abrahamu. Koma Abrahamu analanditsa Loti. Moyo wa Loti unalinso pangozi pamene Yehova anaganiza zowononga mzinda woipa wa Sodomu, kumene Loti ndi banja lake anali kukhala.​—Genesis 18:20-22; 19:12, 13.

7 Angelo a Yehova anatulutsa Loti ndi banja lake mumzindawo atangotsala pang’ono kuti auwononge. Nthaŵi imeneyo, Loti anati: “Kapolo wanu anapeza ufulu pamaso panu, ndipo munakuza chifundo chanu, chimene munandichitira ine, pakupulumutsa moyo wanga.” (Genesis 19:16, 19) Loti ponena mawu ameneŵa, anazindikira kuti Yehova anamukomera mtima mwapadera mwa kum’pulumutsa. Choncho, Mulungu anasonyeza kukoma mtima kwake mwa kulanditsa ndi kupulumutsa.​—2 Petro 2:7.

Kukoma Mtima kwa Yehova mwa Kutsogolera Kwake

8, 9. (a) Kodi mnyamata wa Abrahamu anam’patsa ntchito yotani? (b) N’chifukwa chiyani mnyamatayo anapempha Mulungu kuti am’komere mtima, ndipo n’chiyani chinachitika akupemphera?

8 Mu Genesis chaputala 24 timaŵerenga nkhani ina pamene Mulungu anasonyezanso kukoma mtima. Nkhaniyo ikusimba kuti Abrahamu anauza mnyamata wake kuti apite ku dziko la abale a Abrahamu kuti akam’pezere mkazi mwana wake Isake. (Vesi 2-4) Ntchito imeneyi inali yovuta, koma anam’limbitsa mtima kuti mthenga wa Yehova adzamutsogolera. (Vesi 7) Kenako, mnyamatayo anafika pachitsime kunja kwa “mudzi wa Nahori” (mwina ku Harana kapena malo oyandikana nawo) nthaŵi imene akazi anali kufika kudzatunga madzi. (Vesi 10, 11) Iye ataona akaziwo akufika pamenepo, anadziŵa kuti nthaŵi yofunika kwambiri kuti achite zimene anamutuma inali imeneyo. Koma kodi akanasankha bwanji mkazi woyenera?

9 Mnyamata wa Abrahamu pozindikira kuti anafunika thandizo la Mulungu, anapemphera kuti: “Yehova, Mulungu wa mbuyanga Abrahamu mundiyendetse ine bwino lero lino, mum’chitire ufulu mbuyanga Abrahamu.” (Vesi 12) Kodi Yehova akanasonyeza bwanji kukoma mtima? Mnyamatayo anapempha chizindikiro chimene chikanamuthandiza kudziŵa mkazi amene Mulungu anasankha. (Vesi 13, 14) Mkazi wina anachitadi zimene mnyamatayo anapempha kwa Yehova. Ndipotu, zinangokhala ngati kuti anamva nawo pemphero lakelo. (Mavesi 15-20) Mnyamatayo anadabwa kwambiri moti ‘ankangomuyang’ana.’ Koma panali zinthu zina zimene anafunikabe kudziŵa. Kodi mkazi wokongolayo analidi wachibale wa Abrahamu? Ndipo kodi anali asanakwatiwe? Choncho, mnyamatayo anangokhala “chete, kuti adziŵe ngati Yehova anamuyendetsa bwino kapena iyayi.”​—Mavesi 1621.

10. Kodi mnyamata wa Abrahamu anazindikira bwanji kuti Yehova anakomera mtima mbuye wake?

10 Posakhalitsa, mkaziyo anafotokoza kuti iye anali “mwana wa Betuele mwana wamwamuna wa Milika, amene anam’balira Nahori [mbale wake wa Abrahamu].” (Genesis 11:26; 24:24) Atatero, mnyamatayo anazindikira kuti Yehova anayankha pemphero lake. Anadabwa nazo kwambiri zimenezi, ndipo anaweramitsa mutu wake nati: “Ayamikike Yehova Mulungu wa mbuyanga Abrahamu amene sanasiya mbuyanga wopanda chifundo chake ndi zoona zake: koma ine Yehova wanditsogolera m’njira ya ku nyumba ya abale ake a mbuyanga.” (Vesi 27) Mwa kum’tsogolera mnyamatayo, Mulungu anakomera mtima mbuye wake, Abrahamu.

Kukoma Mtima kwa Mulungu Kumapatsa Mpumulo ndi Chitetezo

11, 12. (a) Kodi Yehova anakomera mtima Yosefe pamayesero otani? (b) Kodi Mulungu anamukomera mtima bwanji Yosefe?

11 Tsopano tiyeni tione Genesis chaputala 39. Chaputala chimenechi chikufotokoza za  Yosefe, mdzukulutuvi wa Abrahamu, amene anamugulitsa muukapolo ku Igupto. Komabe, “Yehova anali ndi Yosefe.” (Mavesi 1, 2) Ngakhale Potifara, mbuye wa Yosefe wa ku Igupto, anaona kuti Yehova anali naye Yosefeyo. (Vesi 3) Komabe, Yosefe anakumana ndi chiyeso chachikulu. Anamuimba mlandu wabodza woti anafuna kugona ndi mkazi wa Potifara ndipo anamuika m’ndende. (Mavesi 7-20) Pamene anali “m’dzenje [la ndende, NW],” “anapweteka miyendo yake ndi matangadza; anam’goneka m’unyolo.”​—Genesis 40:15; Salmo 105:18.

12 Kodi n’chiyani chinachitika nthaŵi yonse ya chiyeso chimenechi? “Yehova anali ndi Yosefe nam’chitira iye zokoma.” (Vesi 21a) Kukoma mtima kumeneku kunachititsa zinthu zosiyanasiyana moti m’kupita kwa nthaŵi Yosefe anapeza mpumulo pa mavuto ake aja. Yehova anam’patsa Yosefe “ufulu pamaso pa woyang’anira kaidi.” (Vesi 21b) Ndipo woyang’anira ndendeyo anam’patsa Yosefe udindo. (Vesi 22) Kenako, Yosefe anakumana ndi munthu amene, patapita nthaŵi, anakam’dziŵitsa kwa Farao, wolamulira wa Igupto. (Genesis 40:1-4, 9-15; 41:9-14) Ndiyeno, mfumuyo inakweza Yosefe n’kukhala wolamulira wachiŵiri m’dziko la Igupto ndipo anagwira ntchito yopulumutsa miyoyo m’dzikolo limene munagwa njala. (Genesis 41:37-55) Yosefe anayamba  kuvutika ali ndi zaka 17 ndipo anavutika kwa zaka zoposa 12. (Genesis 37:2, 4; 41:46) Koma zaka zonse zimene anavutikazo, Yehova Mulungu anamukomera mtima Yosefe mwa kum’teteza ku mavuto oopsa ndi kum’pulumutsa kuti achite ntchito yapadera pokwaniritsa cholinga cha Mulungu.

Kukoma Mtima kwa Mulungu Sikulephera

13. (a) Kodi Salmo 136 likufotokoza kuti Yehova anasonyeza bwanji kukoma mtima? (b) Kodi kukoma mtima n’kutani?

13 Yehova anakomera mtima Aisrayeli mobwerezabwereza. Salmo 136 limasimba kuti chifukwa cha kukoma mtima kwake, iye anawalanditsa, (Vesi 10-15), anawatsogolera (Vesi 16), ndiponso anawateteza. (Vesi 17-20) Mulungu wakomeranso mtima munthu aliyense payekha. Munthu amene amakomera mtima anthu anzake amatero mwa kuchita zinthu mofuna yekha kuti athandize ngati pakusoŵeka zinazake zazikulu. Buku lina lofotokoza Baibulo limanena kuti kukoma mtima “ndi kuchita zinthu zothandiza kuti moyo uyende bwino. Ndi kuchitapo kanthu pofuna kuthandiza munthu amene ali m’mavuto.” Katswiri wina anati kukoma mtima ndi “kuchitapo kanthu chifukwa cha chikondi.”

14, 15. Kodi tingatsimikize bwanji kuti Loti anali mtumiki wa Mulungu ndipo iye anamuyanja?

14 Nkhani za m’Genesis zimene takambiranazi zikutisonyeza kuti Yehova salephera kukomera mtima anthu amene amamukonda. Loti, Abrahamu, ndi Yosefe moyo wawo unali wosiyana ndipo anakumana ndi mayesero osiyana. Iwo anali anthu opanda ungwiro, koma anali atumiki a Yehova ndipo iye anawayanja, ndiponso onse anafuna kuti Mulungu awathandize. Zimalimbikitsa kudziŵa kuti Atate wathu wachikondi wakumwamba amakomera mtima anthu ngati amenewo.

15 Nthaŵi ina, Loti sanasankhe mwanzeru ndipo anakumana ndi mavuto. (Genesis 13:12, 13; 14:11, 12) Komabe, anali ndi makhalidwe abwino. Pamene angelo aŵiri a Mulungu anafika ku Sodomu, Loti anawalandira bwino. (Genesis 19:1-3) Chikhulupiriro chinam’limbikitsa kuchenjeza akamwini ake kuti Yehova watsala pang’ono kuwononga Sodomu. (Genesis 19:14) Pa 2 Petro 2:7-9 akufotokoza mmene Mulungu anaonera Loti. Timaŵerenga kuti: “[Yehova] anapulumutsa Loti wolungamayo, wolema mtima ndi mayendedwe onyansa a oipa aja (pakuti wolungamayo pokhala pakati pawo, ndi kuona ndi kumva zawo, anadzizunzira moyo wake wolungama tsiku ndi tsiku ndi ntchito zawo zosayeruzika). Ambuye adziŵa kupulumutsa opembedza poyesedwa iwo.” Inde, Loti anali munthu wolungama ndipo mmene afotokozera apa, zikusonyeza kuti iye anali wopembedza. Ifenso monga iye, Mulungu amatikomera mtima pamene  tiyenda “m’mayendedwe opatulika ndi m’chipembedzo.”​—2 Petro 3:11, 12.

16. Kodi Baibulo limafotokoza zabwino zotani zokhudza Abrahamu ndi Yosefe?

16 Nkhani ya mu Genesis chaputala 24 ikusonyeza bwinobwino kuti Abrahamu anali bwenzi lapamtima la Yehova. Vesi loyamba limati “Yehova anadalitsa Abrahamu m’zinthu zonse.” Mnyamata wa Abrahamu anati Yehova ndi “Mulungu wa mbuyanga Abrahamu.” (Mavesi 1227) Ndipo wophunzira Yakobo anati Abrahamu ‘anayesedwa wolungama’ ndipo “anatchedwa bwenzi la Mulungu.” (Yakobo 2:21-23) N’chimodzimodzinso ndi Yosefe. Chaputala 39 chonse cha Genesis chikutsindika kuti Yosefe anali bwenzi lapamtima la Yehova. (Mavesi 2, 32123) Ndiponso, wophunzira Stefano ananena za Yosefe kuti: “Mulungu anali naye.”​—Machitidwe 7:9.

17. Kodi tingaphunzire chiyani pa zitsanzo za Loti, Abrahamu, ndi Yosefe?

17 Anthu takambiranaŵa amene Mulungu anawakomera mtima, anali paubwenzi wabwino ndi Yehova Mulungu ndipo anakwaniritsa cholinga chake m’njira zosiyanasiyana. Anakumana ndi zopinga zimene sakanatha kuzithetsa mwa iwo okha. Moyo wa Loti unafunikira kuupulumutsa, mzera wa banja la Abrahamu unafunikira kupitirira, ndiponso udindo wa Yosefe unafunika kuuteteza. Yehova yekha ndi amene akanawathandiza amuna opembedza ameneŵa ndipo anachitadi zimenezo mwa kuchitapo kanthu mokoma mtima. Ifenso ngati tikufuna kuti Mulungu atikomere mtima mpaka kalekale, tifunika kukhala mabwenzi ake apamtima ndiponso tiyenera kuchitabe zimene iye amafuna.​—Ezara 7:28; Salmo 18:50.

Mulungu Amayanja Atumiki Ake

18. Kodi malemba ena a m’Baibulo akusonyeza chiyani za kukoma mtima kwa Yehova?

18 Kukoma mtima kwa Yehova ‘kwadzaza dziko lonse’ ndipo tikuthokoza kwambiri chifukwa cha khalidwe la Mulungu limeneli. (Salmo 119:64) Tikuvomera ndi mtima wonse mavume a wamasalmo akuti: “Ayamike Yehova chifukwa cha chifundo chake, ndi zodabwiza zake za kwa ana a anthu!” (Salmo 107:8, 15, 21, 31) Tikusangalala kuti Yehova akukomera mtima atumiki ake amene amawayanja, kaya payekhapayekha kapena monga gulu. Mneneri Danieli popemphera ananena kuti Yehova ndiye “Ambuye Mulungu wamkulu ndi woopsa, wakuwasungira pangano ndi chifundo iwo akukukondani, ndi kusunga malamulo anu.” (Danieli 9:4) Mfumu Davide inapemphera kuti: “Tanimphitsani chifundo chanu pa iwo akudziŵa Inu.” (Salmo 36:10) Tikuthokoza kwambiri kuti Yehova amakomera mtima atumiki ake.​—1 Mafumu 8:23; 1 Mbiri 17:13.

19. Kodi m’nkhani yotsatirayi tikambirana mafunso otani?

19 Inde, Yehova amatiyanja monga anthu ake. Timapindula ndi chikondi cha Mulungu chimene amachisonyeza kwa anthu onse, ndipo kuwonjezera pamenepo, tikupezanso madalitso apadera chifukwa cha kukoma mtima kwa Atate wathu wakumwamba. (Yohane 3:16) Timapindula ndi khalidwe la Yehova lofunika kwambiri limeneli makamaka tikasoŵa thandizo. (Salmo 36:7) Koma kodi tingatsanzire bwanji kukoma mtima kwa Yehova Mulungu? Kodi ifeyo, aliyense payekha, tikusonyeza khalidwe labwino limeneli? M’nkhani yotsatirayi, tikambirana mafunso ameneŵa pamodzinso ndi ena.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Motero paliponse pamene pakupezeka mawu ameneŵa m’Malemba amene ali m’nkhani ino ndi nkhani yotsatirayi, akutanthauza “kukoma mtima.”

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi taphunzira chiyani za liwu la Chihebri limene analitembenuza kuti “kukoma mtima”?

• Kodi kukoma mtima kukusiyana bwanji ndi chikondi ndiponso kukhulupirika?

• Kodi Yehova anasonyeza bwanji kukoma mtima kwa Loti, Abrahamu, ndi Yosefe?

• Kodi zikutilimbikitsa motani poona mmene Yehova anasonyezera kukoma mtima m’mbuyomo?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 13]

Kodi mukudziŵa mmene Mulungu anakomera mtima Loti?

[Zithunzi patsamba 15]

Yehova chifukwa cha kukoma mtima kwake anatsogolera mtumiki wa Abrahamu

[Zithunzi patsamba 16]

Yehova anakomera mtima Yosefe mwa kum’teteza