Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mmene Kulumala Konse Kudzathere

Mmene Kulumala Konse Kudzathere

 Mmene Kulumala Konse Kudzathere

TANGOGANIZIRANI anthu akhungu kuona, ogontha kumamva chilichonse, osalankhula kuyimba ndi chimwemwe ndi opunduka kuyenda. Zimenezi sizidzachitika chifukwa cha kupita patsogolo kwa sayansi ya zamankhwala ayi, koma Mulungu ndiye adzachitire anthu ake zimenezi. Baibulo limaneneratu kuti: “Pamenepo maso a akhungu adzatsegudwa, ndi makutu a ogontha adzatsegulidwa. Pamenepo wopunduka adzatumpha ngati nswala, ndi lilime la wosalankhula lidzaimba.” (Yesaya 35:5, 6) Koma kodi tingatsimikize bwanji kuti ulosi wodabwitsa umenewu udzakwaniritsidwa?

Choyamba, Yesu Kristu ali pano padziko lapansi anachiritsa anthu odwala matenda osiyanasiyana ndiponso olumala mosiyanasiyana. Ndipo anthu ambiri ngakhale adani ake anadzionera okha zozizwitsa zomwe iye anachita. Ndipotu, nthaŵi ina, adaniwo anafufuza kwambiri nkhani yoti Yesu wachiritsa munthu, n’cholinga chofuna kuti anthu asamukhulupirire. Koma anachita manyazi kwambiri chifukwa zomwe anachitazo zinatsimikiza kuti nkhaniyo ndi yoona. (Yohane 9:1, 5-34) Yesu atachita chozizwitsa chinanso chomwe adani ake sakanatha kuchikana, iwo anaima mitu nati: “Titani ife? chifukwa munthu uyu achita zizindikiro zambiri.” (Yohane 11:47) Komabe, anthu wamba anali ndi chidwi kwambiri ndipo ochuluka anayamba kukhulupirira Yesu.​—Yohane 2:23; 10:41, 42; 12:9-11.

Zozizwitsa za Yesu Zinali Chithunzi cha Kuchiritsa kwa Padziko Lonse

Zozizwitsa za Yesu zinachita zambiri. Zinapereka umboni wakuti Yesu anali Mesiya komanso Mwana wa Mulungu. Zinayala maziko oti tizikhulupirira zimene Baibulo linalonjeza kuti anthu omvera adzawachiritsa m’tsogolo. Ulosi wa pa Yesaya chaputala 35 womwe tautchula m’ndime yoyambirira, ndiwo ena mwa malonjezo ameneŵa. Lemba la Yesaya 33:24 limanena za umoyo wam’tsogolo wa anthu oopa Mulungu kuti: “Wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.” Komanso lemba la Chivumbulutso 21:4 limalonjeza kuti: “[Mulungu] adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo [ziyeso ndi mavuto a masiku ano] zapita.”

Anthu nthaŵi zonse amapemphera kuti maulosi ameneŵa akwaniritsidwe. Amatero akamabwereza pemphero lachitsanzo la Yesu lomwe mwa zina limati: “Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano.” (Mateyu 6:10) Inde, chifuno cha Mulungu chimaphatikizapo dziko lapansi ndi anthu. Ngakhale kuti Mulungu walola matenda  ndiponso kulumala pazifukwa, posachedwapa adzazichotsa ndipo sizidzaipitsanso “choikapo mapazi” ake mpaka kalekale.​—Yesaya 66:1. *

Kuchira Kosamva Ululu Ndiponso Kwaulere

Kaya anthu anali kudwala matenda amtundu wanji, Yesu anawachiritsa popanda kumva ululu. Anachita zimenezo mwamsanga ndiponso kwaulere. Mbiri ya kuchiritsa kumeneku inafalikira ngati moto wosazimitsika, ndipo mwamsanga “makamu ambiri a anthu anadza kwa iye, ali nawo opunduka miyendo, akhungu, osalankhula, opunduka ziŵalo, ndi ena ambiri, nawakhazika pansi pa mapazi ake: ndipo iye anawachiritsa.” Kodi anthu anatani ataona zimenezi? Nkhani ya Mateyu yemwe ankadzionera yekha zomwe zinkachitikazo, ikupitiriza kuti: “Khamulo linazizwa, pakupenya osalankhula nalankhula, opunduka ziŵalo nachira, ndi opunduka miyendo nayenda, ndi akhungu napenya, ndipo iwo analemekeza Mulungu wa Israyeli.”​—Mateyu 15:30, 31.

Dziŵani kuti anthu amene Yesu anawachiritsa sanachite kuwasankha pa gulu la anthu monga momwe amachitira onyenga pofuna kunamiza anthu. M’malo mwake, achibale ndi anzawo a odwalawo ndiwo ‘anawakhazika pansi pa mapazi a Yesu: ndipo iye anawachiritsa.’ Tiyeni tsopano tione zitsanzo zina zosonyeza mphamvu ya Yesu ya kuchiritsa.

Khungu: Yesu ali ku Yerusalemu anaona munthu wina wamwamuna amene anali “wosaona chibadwire.” Munthuyo anali kudziŵika mumzindawo monga wopemphapempha. Choncho mutha kuona mmene anthu anasangalalira atamuona munthuyo akuyendayenda koma akuona. Komabe, si onse amene anasangalala nazo. Gulu lamphamvu komanso lotchuka lachiyuda lotchedwa Afarisi linali litakwiya kwambiri chifukwa Yesu anali atalidzudzula kuti linali loipa. Motero, ena mwa Afarisiwo anali ofunitsitsa kupeza umboni wonama n’cholinga chofuna kupeza Yesu zifukwa. (Yohane 8:13, 42-44; 9:1, 6-31) Choncho, anam’funsa munthu wochiritsidwayo, ndiyeno n’kufunsa makolo ake, kenako n’kudzafunsanso munthuyo. Koma kufufuza kwawo kunangotsimikiza chozizwitsa chomwe Yesu anachita. Zimenezi zinawakwiyitsa kwambiri Afarisiwo. Munthuyo atadabwa ndi liuma la anthu achipembedzo onyengawo, anati: “Kuyambira pachiyambi sikunamveka kuti wina anatsegulira maso munthu wosaona chibadwire. Ngati uyu sanachokera kwa Mulungu, sakadakhoza kuchita kanthu.” (Yohane 9:32, 33) Atanena mawu oona ndi anzeru osonyeza chikhulupiriro ameneŵa, Afarisi “anam’taya kunja” munthuyo. Izi zikusonyeza kuti anam’chotsa m’sunagoge.​—Yohane 9:22, 34.

Kugontha: Yesu ali ku Dekapoli, chigawo chomwe chili kummaŵa kwa mtsinje wa Yordano, anthu kumeneko “anadza naye kwa Iye munthu wogontha, ndi wachibwibwi.” (Marko 7:31, 32) Yesu kuwonjezera pa kuchiritsa munthu ameneyo anasonyezanso kuti ankadziŵa bwino kwambiri vutolo ndiponso mmene munthuyo ankamvera. Anadziŵa kuti munthuyo atha kuchita manyazi pa gulu. Baibulo limatiuza kuti Yesu anamutenga munthu wogonthayo kupita naye “pa yekha” ndipo anamuchiritsa. Apanso, anthu omwe ankaona izi zikuchitika “anadabwa kwakukulukulu, nanena, Wachita Iye zonse bwino; angakhale ogontha awamvetsa, ndi osalankhula awalankhulitsa.”​—Marko 7:33-37.

Manjenje: Yesu ali ku Kapernao anthu anabwera kwa iye ndi munthu wamanjenje atagona patchika. (Mateyu 9:2) Mavesi 6 mpaka 8 amafotokoza zomwe zinachitika. “[Yesu] ananena kwa wodwalayo, Tanyamuka, nutenge tchika lako, numuke kunyumba kwako. Ndipo ananyamuka, napita kunyumba kwake. Ndipo mmene anthu a makamu anachiona, anaopa, nalemekeza Mulungu, wakupatsa anthu mphamvu yotere.” Yesu anachitanso chozizwitsa chimenechi ophunzira ake ndi adani ake akuona. Onani kuti ophunzira a Yesu ‘analemekeza Mulungu’ pa zomwe anaonazo chifukwa iwo sanasokonezeke ndi chidani kapena maganizo olakwika.

Matenda: “Ndipo anadza kwa [Yesu] wodwala khate, nam’pempha Iye, nam’gwadira, ndi kunena ndi Iye, Ngati mufuna mukhoza kundikonza. Ndipo Yesu anagwidwa chifundo, natansa dzanja nam’khudza iye, nanena naye, Ndifuna; khala  wokonzedwa. Ndipo pomwepo khate linam’choka.” (Marko 1:40-42) Onani kuti Yesu anamuchiritsa munthuyo osati monyinyirika koma chifukwa cha chifundo chenicheni. Tangoyerekezerani kuti munthu wakhateyo munali inuyo. Kodi mukanamva bwanji ngati akanakuchiritsani mwamsanga komanso popanda kumva ululu ku matenda akupha amene anawononga pang’onopang’ono thupi lanu ndiponso kuchititsa kuti anthu asamakhale nanu pamodzi? Mosakayikira mungamvetse chifukwa chomwe wakhate wina yemwe Yesu anamuchiritsa ‘anagwera nkhope yake pansi kumapazi ake, nam’yamika Iye.’​—Luka 17:12-16.

Kuvulala: Chozizwitsa chomaliza cha Yesu asanamugwire ndi kukamupachika pamtengo chinali kuchiritsa wovulala. Polimbana ndi anthu amene ankafuna kugwira Yesu, mtumwi Petro “pokhala nalo lupanga, analisolola nakantha kapolo wa mkulu wa ansembe, nam’senga khutu lake lamanja.” (Yohane 18:3-5, 10) Nkhani imeneyi m’buku la Luka imatiuza kuti Yesu “anakhudza khutu lake, nam’chiritsa.” (Luka 22:50, 51) Apanso, Yesu anachita chozizwitsa chosonyeza chifundo chimenechi mabwenzi ake komanso adani ake akuona. Panthaŵiyi, adani ake anali odzamugwirawo.

Inde, tikamaŵerenga zozizwitsa za Yesu ndi cholinga, m’pamene timaona umboni wosonyeza kuti zimenezi n’zoonadi. (2 Timoteo 3:16) Monga tanenera poyamba paja, kuphunzira koteroko kuyenera kulimbitsa chikhulupiriro chathu pa lonjezo la Mulungu lakuti adzachiritsa anthu omvera m’tsogolo. Baibulo limatanthauzira chikhulupiriro chachikristu kuti ndi ‘chikhazikitso cha zinthu zoyembekezeka, chiyesero cha zinthu zosapenyeka.’ (Ahebri 11:1) Mwachionekere Mulungu akutilimbikitsa kukhala ndi chikhulupiriro cholimba chokhala ndi umboni osati kukhulupirira m’chimbulimbuli. (1 Yohane 4:1) Tikapeza chikhulupiriro choterocho, tidzakhala olimba mwauzimu, amoyo wabwinopo ndiponso achimwemwe chochulukirapo.​—Mateyu 5:3; Aroma 10:17.

Kuchiritsa Kwauzimu Kuyenera Kuchitika Choyamba

Ambiri amene ali ndi thanzi labwino sakusangalala. Ena mpaka amafuna kudzipha chifukwa choti sakuyembekeza chilichonse chabwino m’tsogolo kapena chifukwa chakuti atopa ndi mavuto. Iwo ali olumala mwauzimu ndipo Mulungu amaona kulumala mwauzimu kumeneku kukhala koopsa kwambiri kusiyana ndi kulumala kwenikweni. (Yohane 9:41) Mosiyana ndi ameneŵa, ambiri omwe ali olumala zenizeni, monga Christian ndi Junior omwe tawatchula m’nkhani yathayi, akukhala mosangalala kwambiri. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti iwo si olumala mwauzimu ndipo chiyembekezo chawo chodalirika chochokera m’Baibulo chimawalimbikitsa kwambiri.

Yesu potchula chinthu chofunika kwambiri kwa ife anthu, anati: “Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha, koma ndi mawu onse akutuluka mkamwa mwa Mulungu.” (Mateyu 4:4) Inde, mosiyana ndi nyama, anthu amafunikira zambiri osati chakudya chenicheni chokha ayi. Popeza anthufe anatilenga “m’chifanizo” cha Mulungu, timafunika chakudya chauzimu​—kumudziŵa Mulungu ndiponso udindo wathu pa zolinga zake komanso pokwaniritsa chifuno chake. (Genesis 1:27; Yohane 4:34) Kumudziŵa Mulungu kumachititsa moyo wathu kukhala ndi cholinga ndiponso kumatilimbikitsa kumutumikira iye. Komanso kumudziŵa Mulungu ndiko maziko a moyo wosatha m’dziko lapansi la paradaiso. Yesu anati: “Moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziŵe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munamtuma.”​—Yohane 17:3.

N’zochititsa chidwi kuti anthu a m’nthaŵi ya Yesu sankamutchula kuti “Wochiritsa” koma kuti “Mphunzitsi.” (Luka 3:12; 7:40) Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti Yesu anaphunzitsa anthu za Ufumu wa Mulungu womwe ndiwo njira yokhayo yothetsera mavuto a anthu kwamuyaya. (Luka 4:43; Yohane 6:26, 27) Boma lakumwamba limeneli lomwe lili m’manja mwa Yesu Kristu lidzalamulira dziko lonse lapansi ndiponso lidzakwaniritsa malonjezo onse a m’Baibulo okhudza kubwezeretsa anthu olungama kotheratu komanso kukonzanso malo awo okhala apadziko lapansi. (Chivumbulutso 11:15) N’chifukwa chake Yesu m’pemphero lake la chitsanzo anagwirizanitsa kudza kwa Ufumu ndi kuchitika kwa chifuno cha Mulungu padziko lapansi.​—Mateyu 6:10.

 Kwa anthu ambiri olumala, kuphunzira za chiyembekezo chosangalatsa chimenechi kwawachititsa kukhala achimwemwe m’malo mokhala achisoni. (Luka 6:21) Ndipotu, Mulungu adzachita zambiri kuposa kungochotsa chabe matenda ndi kulumala. Iye adzachotsa uchimo weniweniwo womwe umachititsa kuti anthu azivutika. Inde, malemba a Yesaya 33:24 ndi Mateyu 9:2-7 omwe mawu ake tawalemba kale koyambirira kuja, amasonyeza kuti timadwala chifukwa cha uchimo. (Aroma 5:12) Choncho, uchimo akadzauchotsa, anthu adzasangalala ndi “ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu.” Mwa zina, ufulu umenewu udzatanthauza kuti anthu adzakhala ndi maganizo ndi matupi angwiro.​—Aroma 8:21.

Anthu amene ali bwinobwino angaone mwachibwanabwana kufunika kokhala ndi umoyo wabwino. Koma amene akuvutika ndi kulumala sangatero. Amadziŵa bwino kwambiri kuti thanzi labwino komanso moyo ndi zinthu zamtengo wapatali. Amadziŵanso kuti zinthu zitha kusintha mwadzidzidzi pa moyo wa munthu. (Mlaliki 9:11) Choncho, tikukhulupirira kuti olumala omwe amaŵerenga mabuku athu adzaganizirapo mofatsa kwambiri pa malonjezo abwino kwambiri a Mulungu opezeka m’Baibulo. Yesu anapereka moyo wake kuti, zivute zitani, malonjezowo adzakwaniritsidwe. Kodi kutsimikiza kungapose pamenepa?​—Mateyu 8:16, 17; Yohane 3:16.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 6 Onani bulosha lakuti Kodi Mulungu Amatisamaliradi?, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Mmenemo tafotokoza mwatsatanetsatane chifukwa chomwe Mulungu walolera kuti anthu azivutika.