Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

 Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Kodi “khamu lalikulu” limene Yohane anaona likuchita utumiki wopatulika m’kachisi wa Yehova, linkachitira m’bwalo liti la kachisiyo?​—Chivumbulutso 7:9-15.

Sikulakwitsa kunena kuti khamu lalikulu limalambira Yehova mu limodzi la mabwalo a padziko lapansi a kachisi wake wamkulu wauzimu, makamaka limene likufanana ndi bwalo lakunja la kachisi wa Solomo.

Mmbuyomo, tinkanena kuti Bwalo la Akunja lomwe linaliko m’nthaŵi ya Yesu ndilo likuimira khamu lalikulu mwauzimu. Komabe, kafukufuku wasonyeza kuti zimenezo sizoona pazifukwa zisanu. Choyamba, si mbali zonse za kachisi wa Herode zomwe zili ndi chochiimira m’kachisi wamkulu wauzimu wa Yehova. Mwachitsanzo, kachisi wa Herode anali ndi Bwalo la Akazi ndi Bwalo la Israyeli. Amuna ndi akazi ankaloŵa m’Bwalo la Akazi, koma amuna okha ndiwo ankawalola kuloŵa m’Bwalo la Israyeli. Mosiyana ndi zimenezo, amuna ndi akazi amalambira pamodzi m’bwalo la padziko lapansi la kachisi wauzimu wa Yehova. (Agalatiya 3:28, 29) Choncho, palibe chimene Bwalo la Akazi ndi Bwalo la Israyeli zikuimira m’kachisi wauzimu.

Chachiŵiri, pa pulani yomwe Mulungu anapereka ya kachisi wa Solomo kapena kachisi yemwe Ezekieli anaona m’masomphenya panalibe Bwalo la Akunja. Ndipo ngakhale kachisi yemwe Zerubabele anamumanganso analibe Bwalo la Akunja. Choncho, palibe chifukwa chonenera kuti Bwalo la Akunja lili ndi choliimira m’kachisi wamkulu wauzimu wolambiriramo yemwe Yehova wakonza, makamaka poganiziranso mfundo yotsatira yachitatu.

Chachitatu, Bwalo la Akunja analimanga ndi Mfumu Herode ya Edomu pofuna kudzilemekeza ndiponso pofuna kuyanjana ndi Roma. Herode anayamba kukonzanso kachisi wa Zerubabele mwinamwake m’ma 18 kapena 17 B.C.E. Buku lotanthauzira mawu a m’Baibulo lakuti The Anchor Bible Dictionary limanena kuti: “Ulamuliro wa Kumadzulo [Roma] pofuna kusonyeza mphamvu monga ulamuliro wa padziko lonse unafuna kuti kachisiyo akhale wamkulu kuposa akachisi a m’mizinda ya kummaŵa.” Komabe, mulingo wa kukula kwa kachisiyo anali atauika kale. Buku lomweli limati: “Ngakhale kuti kachisi weniweniyo anayenera kukhala wofanana ndendende kukula kwake ndi kachisi wakaleyo [yemwe anamanga Solomo ndi Zerubabele], Phiri la Kachisi linali ndi malo oti atha kuwonjezera kukula kwake. Motero, Herode anakuza malo a kachisiyo mwakuwonjezera mbali yomwe tsopano amaitcha Bwalo la Akunja. Ndiyeno kodi nyumba yomwe anaimanga mwa njira imeneyi, ingaimire bwanji kachisi wauzimu yemwe Yehova wakonza?

Chachinayi, pafupifupi aliyense​—akhungu, opunduka ndiponso Akunja osadulidwa​—anali kuloŵa m’Bwalo la Akunja. (Mateyu 21:14, 15) N’zoona kuti bwaloli linkagwiradi ntchito yake kwa Akunja ambiri osadulidwa omwe ankafuna kupereka zopereka kwa Mulungu. Ndipo munali m’bwalo limeneli mmene Yesu nthaŵi zambiri anali kulankhula kwa anthu ndipo kaŵiri konse anathamangitsa osinthitsa ndalama komanso amalonda, akumawauza kuti anyazitsa nyumba ya Atate wake. (Mateyu 21:12, 13; Yohane 2:14-16) Komabe, buku lakuti The Jewish Encyclopedia limati: “Bwalo la kunja limeneli kwenikweni silinali mbali ya Kachisi. Ndipo dothi lake silinali lopatulika ayi. Aliyense anali kuloŵa m’bwalo limeneli.”

Chachisanu, buku lakuti A Handbook on the Gospel of Matthew lomwe analemba Barclay  M. Newman ndi Philip C. Stine, limanena kuti, liwu lachigiriki (hi·e·ron’) lomwe analimasulira kuti “kachisi” lomwenso analigwiritsa ntchito ponena za Bwalo la Akunja, limatanthauza malo onse pamene panali kachisiyo, osati Kachisi weniweniyo ayi. Mosiyana ndi liwu limeneli, liwu lina lachigiriki (na·os’) lomwe analimasulira kuti “kachisi” m’masomphenya omwe Yohane anaona khamu lalikulu, lili ndi tanthauzo lachindunji. Liwuli nthaŵi zambiri akaligwiritsa ntchito m’nkhani yonena za kachisi wa ku Yerusalemu, limatanthauza Malo Opatulikitsa, kachisi weniweniyo, kapena bwalo la kachisi.

A khamu lalikulu amakhulupirira nsembe ya dipo ya Yesu. Iwo ali oyera mwauzimu popeza “anatsuka zovala zawo, naziyeretsa m’mwazi wa Mwanawankhosa.” Choncho, amayesedwa olungama akumayembekezera kukhala mabwenzi a Mulungu ndi kupulumuka chisautso chachikulu. (Yakobo 2:23, 25) Iwo m’njira zambiri amafanana ndi otembenukira ku Chiyuda a mu Israyeli amene ankatsatira pangano la chilamulo ndiponso kulambira pamodzi ndi Aisrayeli.

N’zoona kuti otembenukira ku Chiyuda sankatumikira m’bwalo la m’kati kumene ansembe ankagwirako ntchito yawo. N’chimodzimodzinso a khamu lalikulu. Iwo sali m’bwalo lam’kati la kachisi wamkulu wauzimu wa Yehova. Bwalo lam’kati limeneli, limaimira mkhalidwe wangwiro ndi wolungama wa “ansembe oyera” a Yehova akadali pano padziko lapansi. (1 Petro 2:5) Koma monga momwe mkulu wakumwamba anauzira Yohane, khamu lalikulu lili m’kachisi mwenimwenimo, osati kunja kwa kachisi, m’bwalo lophiphiritsa lotchedwa Bwalo la Akunja ayi. Ndi mwayitu waukulu zedi umenewu! Ndipotu mwayi umenewu ukuonetsa poyera kufunika koti aliyense azikhala woyera mwauzimu ndiponso m’makhalidwe nthaŵi zonse!

[Chithunzi patsamba 31]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Kachisi wa Solomo

1. Malo Opatulikitsa

2. Bwalo Lam’kati

3. Bwalo Lakunja

4. Masitepe opita ku Bwalo la Kachisi