Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

 Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Kodi n’koyenera kupemphera kwa Mulungu popanda kunena mawu akuti “m’dzina la Yesu”?

Baibulo limasonyeza kuti Akristu amene akufuna kupemphera kwa Yehova ayenera kuchita zimenezo m’dzina la Yesu. Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine.” Anawonjezeranso kuti: “Chimene chilichonse mukafunse m’dzina langa, ndidzachichita, kuti Atate akalemekezedwe mwa Mwana. Ngati mudzapempha kanthu m’dzina langa, ndidzachita.”​—Yohane 14:6, 13, 14.

Potchula za udindo wapadera umene Yesu ali nawo, buku lakuti Cyclopedia of Biblical, Theological, and Ecclesiastical Literature limati: “Pemphero liyenera kupita kwa Mulungu yekha basi, kudzera mwa Yesu Kristu monga Mkhalapakati. Motero, mapembedzero onse opita kwa oyera mtima kapena angelo ali opanda phindu ndipo n’kuchitira Mulungu mwano. Kulambira cholengedwa chilichonse, kaya n’chapamwamba motani, n’kulambira mafano ndipo ndi koletsedwa kotheratu m’chilamulo chopatulika cha Mulungu.”

Bwanji ngati wina zinthu zitamuyendera bwino anena kuti “Zikomo kwambiri Yehova” popanda kuwonjezera mawu akuti “m’dzina la Yesu”? Kodi kutero kungakhale kulakwa? Ayi. Tiyerekeze kuti Mkristu wakumana ndi ngozi yadzidzidzi n’kufuula kuti: “Ndithandizeni, Yehova!” Mulungu sangakane kuthandiza chifukwa chakuti mtumiki wake sananene kuti “m’dzina la Yesu.”

Komabe, tiyenera kudziŵa kuti kungofuula kwa Mulungu pakokha sikutanthauza kupemphera. Mwachitsanzo, Kaini ataweruzidwa ndi Yehova chifukwa cha kupha mbale wake Abele, anati: “Kulangidwa kwanga n’kwakukulu kosapiririka. Taonani, mwandiingitsa ine lero lomwe padziko; ndi pankhope panu ndidzabisika; ndipo ndidzakhala wothaŵathaŵa ndi woyendayenda pa dziko lapansi; ndipo kudzatero kuti onse akundipeza adzandipha.” (Genesis 4:13, 14) Ngakhale kuti Kaini analankhula kwa Yehova, iye anali kudandaula chifukwa cha zotsatira zopweteka za uchimo.

Baibulo limatiuza kuti: “Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo odzichepetsa.” Kulankhula ndi Wam’mwambamwamba mopanda ulemu ngati kuti iye ndi munthu wamba kungasonyeze kusadzichepetsa. (Yakobo 4:6; Salmo 47:2; Chivumbulutso 14:7) Kungakhalenso kupanda ulemu ngati tidziŵa zimene Mawu a Mulungu amanena za udindo wa Yesu ndiyeno mwadala n’kupemphera popanda kutchula Yesu Kristu.​—Luka 1:32, 33.

Zimenezi sizikutanthauza kuti Yehova amafuna kuti tizichita mwambo winawake popemphera. Chofunika kwambiri ndicho mmene mtima wa munthu ulili. (1 Samueli 16:7) M’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino, mkulu wa asilikali achiroma dzina lake Korneliyo, ‘anapemphera kwa Mulungu kosaleka.’ Korneliyo, yemwe anali Wakunja wosadulidwa, sanali wodzipatulira kwa Yehova. Ngakhale ayenera kuti sanapemphere m’dzina la Yesu, mapemphero ake ‘anakwera nakhala chikumbutso pamaso pa Mulungu.’ Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti ‘woyesa mitima,’ anaona kuti Korneliyo anali “munthu wopembedza ndi wakuopa Mulungu.” (Machitidwe 10:2, 4; Miyambo 17:3) Atadziŵa za “Yesu wa ku Nazarete,” Korneliyo analandira mzimu woyera ndipo anakhala wophunzira wa Yesu wobatizidwa.​—Machitidwe 10:30-48.

Pomaliza, munthu sangagamule kuti ndi mapemphero ati amene Mulungu amawamva. Ngati Mkristu nthaŵi ina alankhula kwa Mulungu ndiyeno n’kuiwala kunena kuti “m’dzina la Yesu,” palibe chifukwa choti azivutika maganizo kuti walakwa. Yehova amadziŵa bwinobwino zofooka zathu ndipo amafuna kutithandiza. (Salmo 103:12-14) Tingakhale ndi chidaliro kuti ngati tikhulupirira “Mwana wa Mulungu . . . ngati tipempha kanthu monga mwa chifuniro chake, atimvera.” (1 Yohane 5:13, 14) Komabe Akristu oona, makamaka akamaimira ena m’pemphero la pagulu, amazindikira udindo umene Yesu ali nawo pa zolinga za Yehova malinga ndi mmene Malemba amafotokozera. Ndipo amayesetsa kulemekeza Yesu mwa kupemphera kwa Mulungu kudzera mwa iye.