Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kulemekeza Mulungu Kumapiri a ku Philippines

Kulemekeza Mulungu Kumapiri a ku Philippines

 Kulemekeza Mulungu Kumapiri a ku Philippines

Mwalondola, ngati mukuganiza kuti Philippines ndi dziko la pazisumbu. Komatu ndi dzikonso la mapiri ochititsa kaso. Kwa Mboni za Yehova, kulalikira m’mizinda ndiponso m’zigwa kwakhala kosavuta ndiponso kopindulitsa kwambiri. Komabe, mmenemu si mmene zinthu zilili kumapiri.

MAPIRI akuluakulu, okongola ndi ochititsa kaso a dziko limeneli amasiyana kwambiri ndi magombe a nyanja okhala ndi mchenga, matanthwe a korali, midzi ya asodzi, ndiponso mizinda yapiringupiringu m’malo a thyathyathya a zisumbuzi. Mapiriŵa amapangitsanso kuti ntchito yolalikira “uthenga wabwino” wa Ufumu wa Mulungu ikhale yovuta.​—Mateyu 24:14.

Zisumbu za Philippines zili pamalo pomwe panakumana matanthwe aakuluakulu aŵiri mwa matanthwe omwe ali pansi penipeni pa dziko lapansili. Kutentha kwa pansi pa matanthweŵa kunachititsa kuti nthaka ichite zigwembe zomwe zinapangitsa kuti pa zisumbu zikuluzikulu za Philippines pakhale mitandadza ya mapiri osongoka. Zisumbu zoposa 7,100 zopanga dziko la Philippines zili chakumadzulo kwa dera lam’nyanja yamchere ya Pacific, kumene ziphalaphala zotentha zochoka pansi panthaka zimaphulika kaŵirikaŵiri. Chotero, pa zisumbuzi pamaphulikaphulika ziphalaphala zotentha, zomwe zachititsanso kuti Philippines likhale dziko la mapirimapiri. Zigwembezigwembe zimenezi zachititsa kuti anthu a kumapiriŵa atalikirane ndi anthu ena. Kufikira anthu ameneŵa n’kovuta chifukwa chakuti misewu yabwino yoti n’kudutsa galimoto ndi yochepa kwambiri.

Ngakhale kuti kuli zopinga zimenezi, Mboni za Yehova zimadziŵa kufunika kofikira “anthu onse.” (1 Timoteo 2:4) Chotero Mboni za ku Philippines zatsatira mzimu wa pa Yesaya 42:11, 12: “Okhala m’Sela aimbe, akuwe kuchokera pamwamba pa mapiri. Apereke ulemerero kwa Yehova, anene matamando ake m’zisumbu.”

Khama loyesayesa kulalikira kwa anthu okhala m’mapiri linayamba zaka zoposa 50 zapitazo. Nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse itatha amishonale anathandiza kupititsa patsogolo ntchitoyi. Anthu ambiri okhala m’dzikoli analandira choonadi cha Baibulo, ndipo nawonso anathandiza kufalitsa choonadichi ku midzi ya m’mapiri. Zimenezi zinabala zipatso zabwino kwambiri.  Mwachitsanzo, m’mapiri a Cordillera Central, omwe ali kumpoto pachisumbu cha Luzon, muli ofalitsa uthenga wabwino oposa 6,000. Ambiri mwa ofalitsaŵa ndi mbadwa za komweko, monga mafuko a Ibaloi, Ifugao, ndi Kalinga.

Komabe m’mapiriŵa mudakali malo ena ovuta kufikako. Anthu okhala kumeneko sanaiŵalidwe. Kodi ena mwa anthuwo afikiridwa motani, ndipo iwo achitapo zotani?

Chikhulupiriro Chenicheni Chiloŵa M’malo mwa Miyambo

Anthu a mtundu wa Tingiyani ndiwo amakhala m’dera la mapiri m’chigawo cha Abra pachisumbu cha kumpoto cha Luzon. Dzina lakuti Tingiyani mwinamwake linachokera ku liwu la chinenero cha Chimalaya chachikale lakuti, tinggi, limene limatanthauza “phiri.” Zikuwayeneradi kwambiri! Atingiyani amadzitchanso kuti Aitinegi. Chinenero chawo nachonso amachitcha dzina lomweli. Iwo amakhulupirira mulungu wotchedwa Kabuniyani, ndipo amakhulupirira kwambiri zamalodza. Mwachitsanzo, amati ndi tsoka ngati munthu amene akukonza ulendo winawake ayetsemula. Ayenera kuyembekezera kwa maola angapo kuti tsokalo lichoke.

M’chaka cha 1572, Aspanya anabwera ndi Chikatolika, koma analephera kuphunzitsa Atingiyani Chikristu chenicheni. Anthu omwe anakhala Akatolika anapitirizabe kukhulupirira Kabuniyani ndipo ankatsatira miyambo ya makolo awo. Anthu ameneŵa anayamba kudziŵa zolondola za m’Baibulo koyamba m’ma 1930 Mboni za Yehova zitayamba kulalikira uthenga wa Ufumu m’mapiriwo. Kuyambira nthaŵi imeneyo, Atingiyani ambiri oona mtima anayamba kulemekeza Yehova “kuchokera pamwamba pa mapiri.”

Mwachitsanzo, a Lingbaoan anali mfumu yolemekezeka kwambiri m’deralo ndipo ankachita miyambo ya Atingiyani. “Ndinkatsatira mokhulupirika miyambo ya Atingiyani. Munthu akaphedwa, tinkavina gule tikaika maliro, ndipo tinkaimba mabelu. Tinkaperekanso nsembe za nyama. Tinkakhulupirira Kabuniyani, ndipo sindinkadziŵa Mulungu wofotokozedwa m’Baibulo.” Zonsezi  zinali kuchitika ngakhale kuti iwo ankadziŵika kuti anali Mkatolika.

Atumiki a Mboni za Yehova anapita kukalalikira m’deralo. Anakumana ndi a Lingbaoan ndi kuwalimbikitsa kuŵerenga Baibulo. Iwo akukumbukira kuti: “Baibulo ndi lomwe linandikhutiritsa maganizo kuti Yehova ndi Mulungu woona.” Kenako a Lingbaoan anaphunzira Baibulo ndi Mboni, ndipo anasankha kutumikira Mulungu woona. Anasiya zomwe ankachita kale, kuphatikizaponso ufumu, zomwe zinakhumudwitsa wansembe wa m’deralo ndiponso anthu omwe anali anzawo a Lingbaoan. Komabe, a Lingbaoan anatsimikiza mtima kutsata choonadi chimene anali atapeza m’Baibulo. Panopo iwo ndi mkulu mu mpingo.

Mausana Asanu ndi Aŵiri ndi Mausiku Asanu ndi Limodzi

Ngakhale kuti anthu a m’madera ena a Abra amamva uthenga wabwino mobwerezabwereza, madera ena ali kutali kwambiri ndipo pamatenga nthaŵi kuti alalikilemo. Nthaŵi inayake m’mbuyomu, panakonzedwa zopita ku dera limodzi mwa maderaŵa. Gulu la Mboni 35 linayamba ulendo wokalalikira ku gawo losagaŵiridwa ku Tineg, m’chigawo cha Abra, dera lomwe mboni zinali zisanafikeko kwa zaka 27.

Ulendowu unali wapansi ndipo anayenda kwa masiku asanu ndi aŵiri. Tangoganizani! Kuwoloka milato yokola ndi zingwe ndiponso mitsinje yozama komanso kuyenda, kudutsa mitandadza ya mapiri, mutanyamula katundu woti mukagwiritse ntchito​—zonsezi n’cholinga chofuna kukalalikira uthenga wabwino kwa anthu amene saumva kaŵirikaŵiri! Mwa mausiku asanu ndi umodzi paulendowo, mausiku anayi anagona panja.

Ngakhale kuti Mboni zolimba mtima zimenezi zomwe zinali paulendowu zinatenga chakudya, izo sizikanatha kunyamula kamba wokwanira ulendo wonsewo. Koma limeneli silinali vuto chifukwa chakuti anthu ankasangalala kwambiri kusinthanitsa chakudya ndi mabuku othandizira kuphunzira Baibulo. Mbonizo zinalandira zinthu zochuluka zakumunda, nsomba, ndi nyama ya mbaŵala. Ngakhale kuti panali zovuta zina ndi zina, gululo linati: “Kudzipereka kwathu kunafupidwa ndi chimwemwe chodzala tsaya chomwe tinapeza.”

M’masiku asanu ndi aŵiriwo, atumiki ameneŵa analalikira m’midzi khumi, nagaŵira mabuku 60, magazini 186, mabulosha 50, ndi mathirakiti ambiri. Anasonyeza mmene maphunziro a Baibulo amachitikira kwa anthu m’magulu 74. M’tauni ya Tineg, atapemphedwa ndi akuluakulu a tauniyo ndiponso anthu ena otchuka, anachita msonkhano wa mpingo pomwe panafika anthu 78. Ambiri mwa amene anafika pamsonkhanowo anali aphunzitsi ndi apolisi. Tikukhulupirira kuti Atingiyani ambiri ayamba nawo ‘kuimba’ ndi kutamanda Yehova kuchokera pamwamba pa mapiri.

Zinthu Zabwino Kuposa Golidi

Kum’mwera kwenikweni kwa dziko la Philippines kuli zisumbu zina kumene Aspanya anapezako golidi. Pamenepa ndi pamene panayambira dzina lakuti Mindoro, chidule cha mawu a Chispanya akuti mina de oro, kapena kuti “mgodi wa golidi.” Komabe, pa zisumbupo tsopano pakupezeka zinthu zabwino kuposa golidi zomwe ndi anthu amene akufuna kutumikira Yehova, Mulungu woona.

Nzika pafupifupi 125,000 zotchedwa Amangiyani zimakhala m’nkhalango m’katikati mwa Mindoro, kutali ndi kumene mitundu ina ya anthu imakhala. Salira zambiri m’moyo mwawo, nthaŵi zambiri amangodzikhalira osaonana ndi anthu akumadera ena, ndipo ali ndi chinenero chawochawo. Ambiri mwa anthu ameneŵa amalambira  mizimu, ndipo amakhulupirira milungu yambiri ndiponso malaulo.

Nthaŵi zina, akasoŵa chakudya kapena zinthu zina zofunika pamoyo, Amangiyani ena amapita kugombe kukafuna ntchito. Ndi momwe zinalili ndi Pailing, yemwe amachokera ku gulu lina la Amangiyani lotchedwa Batangani. Anakulira m’nkhalango za mapiri, ndipo anali kutsatira zikhulupiriro ndiponso kuchita nawo miyambo ya Abatangani. Anthu ambiri kumeneko anali kuvala mateŵera basi. Pofuna kuti akolole chakudya chochuluka, mwa mwambo wa Abatangani, pamafunika kuti anthu opembedza aphe nkhuku, magazi ake adonthere m’madzi kwinaku akupemphera.

Pailing sakutsatanso miyambo imeneyo. Chifukwa? Atapita kumadera a kuchigwa, anapeza ntchito m’mabanja a Mboni za Yehova. Limodzi mwa mabanjawo linagwiritsa ntchito mpata umenewo ndi kuuza Pailing za choonadi cha Baibulo. Pailing anasangalala kwambiri ndipo anakonda kuphunzira za cholinga cha Yehova pa anthu ndi dziko lapansi. Mabanjawo analinganiza zoti iye apite ku sukulu ya pulayimale, komanso kuti aphunzire Baibulo. Ali ndi zaka 24, Pailing anabatizidwa monga mmodzi wa Mboni za Yehova. Pamene amakwanitsa zaka 30, n’kuti ali m’chaka chachiŵiri cha maphunziro a ku sekondale, ndipo anapanga sukuluyo kukhala gawo lake lolalikiramo. Tsopano amamutcha kuti Rolando (dzina limene limapezeka kumadera a kuchigwa).

Mutakumana ndi Rolando, mungamuone kuti ndi mtumiki wotchena bwino akumwetulira, yemwe akutumikira monga mlaliki wa nthaŵi zonse ndiponso monga mtumiki wotumikira mu mpingo wina pa chisumbu cha Mindoro. Posachedwapa Rolando anapita kwawo kumapiri, osati n’cholinga chokachita nawo miyambo ya Abatangani, koma n’cholinga chokawagaŵira choonadi cha m’Baibulo chopatsa moyo.

Ofunitsitsa Kukhala ndi Nyumba ya Ufumu

Chigawo cha Bukidnon​—kutanthauza kuti “Anthu a Kumapiri” m’chinenero cha Chisebuyano​—chili pa chisumbu cha kum’mwera cha Mindanao. M’dera limeneli muli mapiri, maphompho, zigwa za mitsinje, ndiponso zitunda zathyathyathya. Nthaka yake yachonde imalola bwino nanadzi, chimanga, khofi, mpunga, ndi nthochi. Ku Bukidnon kumakhala anthu ozoloŵera kukhala m’mapiri, Atalaandigi ndi Ahigaononi. Anthu ameneŵanso akufunika kuphunzira za Yehova. Posachedwapa, kufupi ndi mzinda wa Talakag, mwayi umenewu, wophunzira za Yehova, unatseguka mochititsa chidwi kwambiri.

Mboni zomwe zimapita ku madera okwera ameneŵa zimaona kuti ndi kozizira koma zimalandiridwa mwansangala kwambiri. Anthu a kumeneko ankati amakhulupirira Mulungu Wamphamvuyonse, Atate, koma sankadziŵa dzina lake. Popeza nthaŵi zambiri ankakhala ali m’nkhalango, aka kanali koyamba kukumana ndi Mboni za Yehova. Anadziŵa dzina la Mulungu, ndiponso cholinga chake chosangalatsa kwambiri chokhudzana ndi Ufumu. Anthuwo anasangalala, motero Mbonizo zinakonza zokawachezeranso kumudzi wawo.

Anapitako maulendo angapo. Zimenezi zinapangitsa kuti anthu a m’deralo apereke malo a “nyumba” ya Mboni za Yehova. Mbonizo zinalandira malowo mosangalala. Malowo anali pamwamba pa phiri lalitali kwambiri m’deralo ndipo munthu akaima pamenepo amatha kuona msewu bwinobwino. Nyumbayo anaimanga ndi mitengo, nsungwi, ndi masamba a kanjedza. Ntchito yomanga nyumba imeneyi inatenga miyezi itatu ndi masiku khumi. Kumaso kwake anaika chikwangwani chooneka bwino chakuti “Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova.” Tangoganizani, Nyumba ya Ufumu kumangidwa mpingo usanakhazikitsidwe!

Kuyambira nthaŵi imeneyo, mbale wina yemwe ndi mkulu mu mpingo yemwenso ndi mtumiki wa nthaŵi zonse anasamukira ku deralo, limodzinso ndi mtumiki wotumikira wina. Iwo pamodzi ndi Mboni za m’madera akufupi, anagwira ntchito mwakhama n’cholinga chokhazikitsa mpingo. Izi zinatheka mu August wa 1998. Mpingo waung’ono umene anaukhazikitsawo ukugwiritsa ntchito Nyumba ya Ufumu imeneyi, kuthandiza anthu a kumapiri kuphunzira choonadi cha Baibulo.

Ndithudi, Yehova wagwiritsa ntchito kwambiri atumiki ake ofunitsitsa ku Philippines kufalitsa choonadi cha Ufumu ngakhale m’mapiri movuta kufikamo. Zimatikumbutsa Yesaya 52:7, amene amati: “Akongolatu pamapiri mapazi a iye amene adza ndi uthenga wabwino.”

[Mapu patsamba 11]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

ABRA

MINDORO

BUKIDNON

[Mawu a Chithunzi]

Dziko Lapansi: Mountain High Maps® Copyright © 1997 Digital Wisdom, Inc.

[Zithunzi patsamba 10]

Kulalikira kumapiri kumafuna kuyenda kwa maola angapo kudutsa dera la zigwembezigwembe

[Chithunzi patsamba 10]

Ubatizo mu mtsinje wa m’phiri