Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukukumbukira?

Kodi Mukukumbukira?

 Kodi Mukukumbukira?

Kodi mwapindula poŵerenga makope aposachedwapa a Nsanja ya Olonda? Tayesani kuyankha mafunso otsatiraŵa:

Kodi ndi pulogalamu yotani yokhudza Ulaliki wa pa Phiri yomwe mungagwiritse ntchito pochepetsa nkhaŵa?

Tsiku lililonse mungaŵerenge chimodzi mwa ziphunzitso zomwe Yesu anatchula pa ulalikiwo kapena chomwe chili m’mbali zina za Mauthenga Abwino. Mosakayika mudzakhala wachimwemwe choposerapo ndi kuchepetsa nkhaŵa mwa kusinkhasinkha chiphunzitsocho ndi kuyesetsa kuchigwiritsa ntchito pa moyo wanu.​—12/15, masamba 12-14.

Kodi akulu mumpingo ayenera kuphunzitsa atumiki otumikira kusamalira maudindo owonjezereka pa zifukwa zitatu ziti?

Chifukwa cha kuwonjezereka kwa Mboni za Yehova, pakufunika amuna amaudindo kuti athandize kusamalira obatizidwa kumene kuti afike pokhwima mwauzimu. Ukalamba kapena matenda zachititsa akulu omwe atumikira kwa nthaŵi yaitali kuchepetsa zomwe angachite. Ndipo akulu ena akusamalira maudindo ena omwe amapindulitsa mipingo yambiri, choncho sangathe kugwira ntchito zambiri mumpingo wawo monga ankachitira kale.​—1/1, tsamba 29.

Kodi anthu amakhulupirira motani milungu yomwe si yeniyeni?

Anthu ambiri amalambira milungu ya chipembedzo chawo, koma milungu imeneyi ingakhale yopanda moyo yomwe singapulumutse monga momwe mulungu wa Baala analepherera m’nthaŵi ya Eliya. (1 Mafumu 18:26, 29; Salmo 135:15-17) Ena amalambira anthu ochita zosangalatsa kapena anthu otchuka pa zamaseŵera omwe sangapereke chiyembekezo chenicheni cha zinthu zabwino m’tsogolo. Mosiyana ndi onsewo, Yehova ndi weniweni ndipo amakwaniritsa zolinga zake.​—1/15, masamba 3-5.

Kodi tingaphunzirepo chiyani pa zomwe Kaini anachita Mulungu atamuchenjeza?

Mulungu watipatsa ufulu wakudzisankhira zochita ndipo tingasankhe kuchita zabwino m’malo mochita zoipa monga momwe Kaini anachitira. Nkhani ya m’Baibuloyi ikusonyezanso kuti Yehova amaweruza anthu osalapa.​—1/15, masamba 22-3.

N’chifukwa chiyani ukhondo uli wofunika makamaka tsopano?

Chifukwa cha kusintha kwa moyo, anthu ambiri masiku ano amathera nthaŵi yochepa kukonza pa nyumba poyerekeza ndi momwe ankachitira kale. Kusasamala chakudya kapena madzi kungabweretse matenda. Kuwonjezera pa ukhondo weniweni, Baibulo limagogomeza kufunika koti tikhale aukhondo mwauzimu, m’zochita zathu, ndiponso zimene timaganiza.​—2/1, masamba 3-6.

Paulo polankhula za Mboni zomwe zinaliko Kristu asanabwere ananena kuti, izo ‘zisayesedwe zamphumphu [“zangwiro,” NW] opanda ife.” Kodi zimenezi zidzatheka bwanji? (Ahebri 11:40)

Panthaŵi ya Zaka Chikwi ikubwerayi, Kristu ndi abale ake odzozedwa kumwamba, adzakhala mafumu ndi ansembe ndipo adzagaŵa phindu la nsembe ya dipo kwa anthu oukitsidwa. Motero, anthu okhulupirika monga amene anawalemba m’chaputala 11 cha buku la Ahebri ‘adzayesedwe angwiro.’​—2/1, tsamba 23.

Kodi Paulo ankatanthauza chiyani pamene anauza Ahebri kuti: “Simunakana kufikira mwazi”? (Ahebri 12:4)

Ankatanthauza kukana mpaka imfa. Panali zitsanzo za anthu akale amene anakhulupirika mpaka imfa. Ngakhale kuti Ahebri amene Paulo anawalembera mawuŵa anali asanayesedwepo mpaka imfa, iwo anafunika kukhala okhwima mwauzimu, kulimbitsa chikhulupiriro chawo kuti athe kupirira chilichonse chomwe chingabwere.​—2/15, tsamba 29.

N’chifukwa chiyani sitiyenera kunena kuti chifundo cha Yehova chimachepetsa chilungamo chake?

M’zinenero zina mawu akuti kuchepetsa amatanthauza kufeŵetsa kapena kuletsa. Yehova ndi Mulungu wachilungamo ndiponso wachifundo. Ndipo akamasonyeza mikhalidwe iŵiriyi, yonse imagwira ntchito limodzi mogwirizana. (Eksodo 34:6, 7; Deuteronomo 32:4; Salmo 116:5; 145:9) Chilungamo cha Yehova sichifunika kuchifeŵetsa kapena kuchichepetsa pogwiritsa ntchito chifundo ayi.​—3/1 tsamba 30.

Kodi Mkristu angaumitse mtembo wa mbale wake?

Kuumitsa mtembo ndiko kukonza mtembo kuti usawonongeke. Anthu ena akale ankachita zimenezi pazifukwa za chipembedzo. Akristu oona sangaumitse mtembo pazifukwa za chipembedzo. (Mlaliki 9:5; Machitidwe 24:15) Kuumitsa mtembo n’kungochedwetsa chinthu chomwe zivute zitani chidzachitikabe. Mtembowo udzabwerera kufumbi basi. (Genesis 3:19) Koma palibe chifukwa chodera nkhaŵa ngati kuumitsa mtembo kuli kofunika mogwirizana ndi malamulo a kumaloko kapena ngati ena m’banjamo akufuna zimenezo, kapenanso ngati anthu ena ochokera kutali akufuna kudzakhala nawo pa mwambo wa malirowo.​—3/15, masamba 29-31.

Kodi ndi zitsanzo ziti za m’Baibulo zomwe zimatiphunzitsa kuti Mulungu amalandira anthu amitundu yonse?

Yehova anatumiza mneneri Yona kuti akachenjeze Anineve, ndipo Mulungu anamulimbikitsa Yona kuti avomereze kulapa kwawo. Yesu analimbikitsa kukonda Asamariya mwa zomwe ankalankhula ndi kuchita. Mtumwi Petro ndiponso mtumwi Paulo anali ndi udindo wolalikira uthenga wabwino kwa anthu omwe sanali Ayuda. Zitsanzo zimenezi zingatithandize kuona kufunika koyesetsa kuthandiza anthu amitundu yonse.​—4/1, masamba 21-4.