Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Misonkhano Imene Imafulumiza ku Chikondano ndi Ntchito Zabwino

Misonkhano Imene Imafulumiza ku Chikondano ndi Ntchito Zabwino

 “Idzani Kuno kwa Ine, . . . Ndipo Ine Ndidzakupumulitsani Inu”

Misonkhano Imene Imafulumiza ku Chikondano ndi Ntchito Zabwino

KUCHOKERA ku Toronto mpaka ku Tokyo, ndiponso kuchokera ku Moscow mpaka ku Montevideo, Mboni za Yehova miyandamiyanda pamodzi ndi anzawo zimakhamukira ku malo awo olambirira, kangapo mlungu uliwonse. Ena mwa anthu ameneŵa ndi amuna apabanja ogwira ntchito molimba, omwe amakhala atatopa chifukwa chogwira ntchito tsiku lonse; akazi okwatiwa otakataka panyumba pamodzi ndi ana awo; achinyamata amphamvu omwe anali kusukulu tsiku lonse; okalamba amene amayenda pang’onopang’ono chifukwa cha zotsinatsina m’thupi; akazi amasiye ndi ana amasiye olimba mtima ndiponso anthu ovutika maganizo omwe akufuna chilimbikitso.

Mboni za Yehova zimenezi zimagwiritsa ntchito zoyendera zosiyanasiyana monga sitima zothamanga kwambiri, abulu, sitima zing’onozing’ono zoyenda pansi pa nthaka ndiponso magalimoto akuluakulu. Ena amawoloka mitsinje yomwe muli ng’ona zambiri pamene ena amalimbana ndi piringupiringu wochititsa mantha wa magalimoto a m’mizinda ikuluikulu. N’chifukwa chiyani anthu onseŵa amalimbikira chotere?

Chifukwa chachikulu n’chakuti kupezeka ndiponso kuchita nawo misonkhano yachikristu ndi njira yofunika kwambiri yolambirira Yehova Mulungu. (Ahebri 13:15) Mtumwi Paulo anatchulanso chifukwa china. Iye analemba kuti: ‘Tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino, osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, . . . komatu tidandaulirane, ndiko koposa monga momwe muona tsiku lilikuyandika.’ (Ahebri 10:24, 25) Paulo pamenepa anagwirizana ndi wamasalmo Davide yemwe anaimba kuti: “Ndinakondwera mmene ananena nane, Tiyeni ku nyumba ya Yehova.”​—Salmo 122:1.

N’chifukwa chiyani Akristu amakondwera kupezeka pa misonkhano yawo? Chifukwa chakuti amene amafika pamisonkhano sangokhala oonerera. M’malo mwake, misonkhano imawapatsa mwayi wodziŵana ndi ena. Misonkhanoyi makamaka imakhalanso nthaŵi yabwino yopatsa osati kungolandira. Imakhalanso nthaŵi yofulumizana kusonyeza chikondi ndiponso kugwira nawo ntchito zabwino. Izi zimathandiza kuti misonkhano ikhale yolimbikitsa kwambiri. Komanso, misonkhano yachikristu ndi njira imodzi yomwe Yesu amakwaniritsira lonjezo lake lakuti: “Idzani kuno kwa Ine, . . . ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu.”​—Mateyu 11:28.

 Malo Opeza Chilimbikitso ndi Chikondi

Mboni za Yehova zili ndi zifukwa zomveka zoonera misonkhano yawo kukhala yopatsa mpumulo. Chifukwa choyamba n’chakuti pamisonkhanoyo, “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” amapereka chakudya chauzimu panthaŵi yake. (Mateyu 24:45) Misonkhano imathandizanso kwambiri kuti atumiki a Yehova akhale ndi luso ndi changu pophunzitsa Mawu a Mulungu. Kuwonjezera pamenepo, ku Nyumba ya Ufumu kumapezeka mabwenzi achikondi, oganizira ena, ndiponso osamala omwe ali okonzeka komanso ofunitsitsa kuthandiza ndi kulimbikitsa ena panthaŵi ya mavuto.​—2 Akorinto 7:5-7.

Zimenezi n’zimene zinachitikira Phillis, mkazi wamasiye yemwe mwamuna wake anamwalira pamene ana ake aakazi aŵiri anali ndi zaka wina zisanu ndi winayo zisanu ndi zitatu. Pofotokoza mmene misonkhano yachikristu yamulimbikitsira pamodzi ndi ana akewo, iye anati: “Zinali zolimbikitsa kupita ku Nyumba ya Ufumu chifukwa okhulupirira anzathu nthaŵi zonse ankasonyeza chikondi chawo ndi kutiganizira mwa kutikumbatira, kutiuza mfundo za m’Malemba, kapena kutigwira chanza mwamphamvu. Anali malo amene ndinkafuna kumangokhalako nthaŵi zonse.”​—1 Atesalonika 5:14.

Marie atamuchita opaleshoni yaikulu, dokotala wake anamuuza kuti adzatenga pafupifupi milungu isanu ndi umodzi kuti apeze bwino. Milungu yoyambirira ya nthaŵiyo, Marie sankapita ku misonkhano. Dokotala wake anazindikira kuti iye sanali kusangalala monga kale. Atadziŵa kuti sanapite kumisonkhano, dokotalayo anamulimbikitsa kutero. Marie anayankha kuti mwamuna wake amene anali wosiyana naye chipembedzo, sakanamulola kupita ku misonkhano poona kuti sanali kupeza bwino. Choncho, dokotalayo analemba kalata yamalangizo “yom’lamula” Marie kuti azipita ku Nyumba ya Ufumu kuti anzake azikamulimbikitsa. Atachita zimenezi, Marie ananena kuti: “N’tachita nawo msonkhano umodzi, ndinayamba kupezako bwino. Ndinayamba kudya, ndinagona usiku wonsewo, sindinafunikire kumwa pafupipafupi mankhwala ochepetsa ululu, ndipo ndinayambanso kumwetulira!”​—Miyambo 16:24.

Anthu ena amaona chikondi chomwe chimakhala pamisonkhano yachikristu. Wophunzira wina wamkazi wapakoleji anasankha kufufuza Mboni za Yehova n’cholinga chofuna kulemba nkhani yokhudza phunziro lake la sayansi ya chikhalidwe cha anthu. Pa za misonkhano ya Mboni, iye m’nkhani yakeyo analemba kuti: “Kundilandira kwawo ndi manja aŵiri . . . [kunali] kochititsa chidwi kwambiri. .  . . Khalidwe laubwenzi la Mboni za Yehova linali loonekera bwino kwambiri ndipo ndilo ndinaona kukhala chinthu chapadera kwambiri pa msonkhanowo.”​—1 Akorinto 14:25.

M’dziko lamavutoli, mpingo wachikristu ndiwo malo opezako chilimbikitso chauzimu. Ndiwo malo amtendere ndiponso achikondi. Mwa kupezeka pa misonkhano mudzadzionera nokha kuti mawu a wamasalmo ndi oona. Iye anati: “Onani, n’kokoma ndi kokondweretsa ndithu kuti abale akhale pamodzi!”​—Salmo 133:1.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 25]

KUKWANIRITSA CHOSOŴA CHAPADERA

Kodi anthu osamva angapindule motani ndi misonkhano yachikristu? Mboni za Yehova padziko lonse zikukhazikitsa mipingo ya zinenero zolankhula ndi manja. Zaka 13 zapitazi, mipingo ya zinenero zolankhula ndi manja yokwana 27 ndiponso timagulu 43 zinakhazikitsidwa ku United States. Tsopano m’mayiko ena osachepera 40, muli mipingo yotereyi pafupifupi 140. Mabuku achikristu akupangidwa pa mavidiyo m’zinenero zolankhula ndi manja zokwana 13.

Mpingo wachikristu umapereka mwayi wotamanda Yehova kwa anthu osamva. Odile, mkazi yemwe kale anali Mkatolika ku France, yemwenso ankadwala maganizo ndipo ankafuna kudzipha, akuthokoza kwambiri chifukwa cha maphunziro a Baibulo omwe analandira ku misonkhano yachikristu. Iye anati: “Ndinayamba kupezanso bwino ndiponso kusangalala ndi moyo. Koma koposa zonse, ndinapeza choonadi. Moyo wanga tsopano uli ndi cholinga.”