Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Utsogoleri wa Kristu Mumauonadi Kukhala Weniweni?

Kodi Utsogoleri wa Kristu Mumauonadi Kukhala Weniweni?

 Kodi Utsogoleri wa Kristu Mumauonadi Kukhala Weniweni?

“Ndipo musatchedwa atsogoleri, pakuti alipo mmodzi Mtsogoleri wanu, ndiye Kristu.”​—MATEYU 23:10.

1. Kodi Mtsogoleri mmodzi yekha wa Akristu oona ndi ndani?

LINALI Lachiŵiri pa Nisan 11. Yesu Kristu anali kudzaphedwa masiku atatu m’tsogolo. Umenewu unali ulendo wake womaliza kupita ku kachisi. Tsiku limeneli, Yesu anaphunzitsa khamu la anthu amene anasonkhana kumeneko ndiponso ophunzira ake mfundo yofunika kwambiri. Anati: “Musatchedwa Rabi; pakuti Mphunzitsi wanu ali mmodzi, ndipo inu nonse muli abale. Ndipo inu musatchule wina atate wanu pansi pano, pakuti alipo mmodzi ndiye Atate wanu wa Kumwamba. Ndipo musatchedwa atsogoleri, pakuti alipo mmodzi Mtsogoleri wanu, ndiye Kristu.” (Mateyu 23:8-10) Inde, Yesu Kristu ndiye Mtsogoleri wa Akristu oona.

2, 3. Kodi timapeza phindu lotani pamoyo wathu tikamamvera Yehova ndi kutsatira Mtsogoleri wathu amene anamuika?

2 Utsogoleri wa Yesu ndi wopindulitsatu kwambiri tikautsatira. Yehova Mulungu analosera za kubwera kwa Mtsogoleri ameneyu kudzera mwa mneneri wake Yesaya kuti: “Inu nonse, inu akumva ludzu, idzani kumadzi; ndi osoŵa ndalama idzani inu mugule mudye; inde idzani, mugule vinyo ndi mkaka opanda ndalama ndi opanda mtengo wake. . . . Mverani Ine mosamalitsa, nimudye chimene chili chabwino, moyo wanu nukondwere ndi zonona. . . . Taonani, ndam’pereka iye akhale mboni ya anthu, wotsogolera ndi wolamulira anthu.”​—Yesaya 55:1-4.

3 Yesaya anagwiritsa ntchito zinthu zodziŵika zamadzimadzi monga madzi, mkaka, ndi vinyo. Anatero pofuna kusonyeza mwafanizo phindu limene timapeza pamoyo wathu mwa kumvera Yehova ndi kutsatira Mtsogoleri ndi Wolamulira amene watipatsa. Zimene zimachitika n’zoti timatsitsimulidwa ngati kuti tamwa madzi ozizira tsiku lotentha ndipo ludzu lathu la choonadi ndi chilungamo limatha. Monga momwe zimakhalira kuti ana akamamwa mkaka amalimba ndipo umawathandiza kukula bwino, ifenso timalimba ndi ‘mkaka wa mawu’ ndipo umatithandiza kukula mwauzimu ndi kukhala paubwenzi wolimba ndi Mulungu. (1 Petro 2:1-3, NW) Ndipo ndani angatsutse zoti vinyo amawonjezera chimwemwe paphwando? N’chimodzimodzinso ndi kulambira Mulungu woona ndi kutsatira mapazi a Mtsogoleri wathu amene anamuika. Kumatipangitsa ‘kukondwera monsemo’ pamoyo wathu. (Deuteronomo 16:15) Motero, tonsefe, ana ndi akulu, amuna ndi akazi, tifunika tisonyeze kuti utsogoleri wa Kristu timauonadi kukhala weniweni. Koma kodi tingasonyeze bwanji pamoyo wathu wa tsiku ndi tsiku kuti Mesiya ndi Mtsogoleri wathu?

Achinyamata​—Pitirizani ‘Kukula M’nzeru’

4. (a) Kodi n’chiyani chinachitika pamene Yesu anapita ku Yerusalemu nthaŵi ya Paskha ali ndi zaka 12? (b) Kodi Yesu anali kudziŵa zotani ali ndi zaka 12 zokha?

4 Tiyeni tipende chitsanzo chimene Mtsogoleri wathu anasiyira achinyamata. Ngakhale kuti sitikudziŵa zambiri zimene zinachitika pa ubwana wa Yesu, nkhani ina imene inachitika ikuvumbula zambiri. Pamene Yesu anali ndi zaka 12, makolo ake anamutenga pa ulendo wawo wa chaka ndi chaka wopita ku Yerusalemu nthaŵi ya Paskha. Nthaŵi imeneyi, iye anatengeka m’kukambirana za m’Malemba, ndipo achibale ake ananyamuka iye n’kumusiya komweko mosadziŵa. Patapita masiku atatu makolo ake, Yosefe ndi Mariya, nkhaŵa ili bii anam’peza mu kachisi, ‘atakhala  pakati pa aphunzitsi, namva iwo, nawafunsanso mafunso.’ Ndiponso, “onse amene anamva Iye anadabwa ndi chidziŵitso chake, ndi mayankho ake.” Tangoganizani! Yesu ali ndi zaka 12, anatha kufunsa mafunso auzimu ofuna kuganiza kwambiri ndiponso anali kuyankha mwanzeru. N’zosakayikitsa kuti zimene makolo ake anamuphunzitsa n’zimene zinamuthandiza.​—Luka 2:41-50.

5. Kodi achinyamata angapende motani mmene amaonera phunziro la Baibulo la banja?

5 Mwina ndinu wachinyamata. Mosakayika, ngati makolo anu ndi atumiki odzipereka a Mulungu, nthaŵi zonse mumachita phunziro la Baibulo la banja kunyumba kwanu. Kodi mumaliona motani phunziro la banjalo? Bwanji osasinkhasinkha mafunso monga akuti: ‘Kodi ndimalimbikitsa ndi mtima wonse makonzedwe a phunziro la Baibulo m’banja lathu? Kodi ndimagwirizana ndi makonzedwewo, osachita zinthu zimene zingasokoneze nthaŵi yake?’ (Afilipi 3:16) ‘Kodi ndimatenga nawo mbali mwachangu paphunzirolo? Ngati n’koyenera, kodi ndimafunsa mafunso okhudza nkhani imene tikuphunzira ndi kufotokoza mmene tingagwiritsire ntchito zimene tikuphunzirazo? Pamene ndikupita patsogolo mwauzimu, kodi ndikukulitsa chilakolako cha “chakudya chotafuna [chimene] chili cha anthu akulu misinkhu”?’​—Ahebri 5:13, 14.

6, 7. Kodi pulogalamu yoŵerenga Baibulo tsiku ndi tsiku ingam’thandize bwanji wachinyamata?

6 Pulogalamu yoŵerenga Baibulo tsiku ndi tsiku ndi yofunikanso kwambiri. Wamasalmo anaimba kuti: “Wodala munthuyo wosayenda mu uphungu wa oipa, . . . komatu m’chilamulo cha Yehova muli chikondwerero chake; ndipo m’chilamulo chake amalingirira usana ndi usiku.” (Salmo 1:1, 2) Yoswa, yemwe anatenga malo a Mose, ‘anali kulingilira m’buku la chilamulo usana ndi usiku.’ Zimenezi zinam’thandiza kuchita zinthu mwanzeru ndipo anaikhoza ntchito imene Mulungu anam’patsa. (Yoswa 1:8) Mtsogoleri wathu, Yesu Kristu, anati: “Kwalembedwa, Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha, koma ndi mawu onse akutuluka m’kamwa mwa Mulungu.” (Mateyu 4:4) Ngati timafunikira chakudya tsiku ndi tsiku, kuli bwanji nanga chakudya chauzimu chimene timafunikira nthaŵi zonse!

7 Nicole, mtsikana wa zaka 13, anayamba kuŵerenga Baibulo tsiku ndi tsiku atazindikira zosoŵa zake zauzimu. * Tsopano ali ndi zaka 16 ndipo waŵerenga Baibulo lonselo kumaliza. Ndiyeno wayambanso kuliŵerenga kachiŵiri ndipo watsala pang’ono kufika pakati. Njira imene akugwiritsa ntchito ndi yosavuta. Iye akuti: “Ndimaonetsetsa kuti tsiku lisangodutsa popanda kuŵerengako chaputala chimodzi.” Kodi kuŵerenga kwake Baibulo tsiku ndi tsiku kwamuthandiza bwanji? Akuyankha kuti: “Masiku  ano kuli zinthu zambiri zimene zingasonkhezere munthu kuchita zoipa. Tsiku ndi tsiku ndimakumana ndi zinthu zimenezi kusukulu ndi kwina kulikonse zimene zimayesa chikhulupiriro changa. Kuŵerenga Baibulo tsiku lililonse kumandithandiza kukumbukira mwamsanga malamulo a m’Baibulo ndi mfundo zake za makhalidwe abwino zimene zimandithandiza kulimbana ndi mavuto ameneŵa. Choncho ndimaona kuti Yehova ndi Yesu ali nane.”

8. Kodi Yesu anali ndi chizoloŵezi chotani ku sunagoge, ndipo achinyamata angamutsanzire bwanji?

8 Yesu anali ndi chizoloŵezi chomvetsera ndi kuŵerenga nawo Malemba mu sunagoge. (Luka 4:16; Machitidwe 15:21) Ngati achinyamata atsatira chitsanzo chake mwa kupezeka nthaŵi zonse pa misonkhano yachikristu kumene amaŵerenga Baibulo ndi kuliphunzira, amapindula kwambiri. Richard wa zaka 14 amayamikira misonkhano yotereyi. Iye akuti: “Kwa ine, misonkhano imeneyi ndi yofunika kwambiri. Nthaŵi zonse imandikumbutsa zabwino ndi zoipa, zoyenera ndi zosayenera, khalidwe lofunika longa la Kristu ndi khalidwe losafunika losemphana ndi Kristu. Sindifunika kuchita kukumana ndi mavuto kuti ndidziŵe phindu la zimenezi ayi.” Inde, “Mboni [“Zikumbutso,” NW] za Yehova zili zokhazikika, zakuwapatsa opusa nzeru.” (Salmo 19:7) Nayenso Nicole amaonetsetsa kuti akupezeka pa misokhano ya mpingo yonse isanu mlungu uliwonse. Amakonzekeranso misonkhanoyo maola aŵiri kapena atatu.​—Aefeso 5:15, 16.

9. Kodi achinyamata angatani kuti ‘akule m’nzeru’?

9 Nthaŵi ya unyamata ndi nthaŵi yabwino ‘yodziŵa Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene anam’tuma.’ (Yohane 17:3) Mwina mukudziŵa achinyamata ena amene nthaŵi zambiri amakhala akuŵerenga magazini a zithunzithunzi ndi nkhani zoseketsa, kuonera wailesi yakanema, kuchita maseŵero a pa vidiyo, kapena kufufuza nkhani zosiyanasiyana pa makompyuta. N’kutsatiriranji achinyamata oterowo pomwe mungatsatire chitsanzo changwiro cha Mtsogoleri wathu? Pamene iye anali mnyamata, ankakonda kuphunzira za Yehova. Chinachitika n’chiyani? Chifukwa cha kukonda kwake zinthu zauzimu, “Yesu anakulabe m’nzeru.” (Luka 2:52) Inunso mungatero.

‘Muzimverana Wina ndi Mnzake’

10. N’chiyani chingathandize kuti banja likhale la mtendere ndi chimwemwe?

10 Panyumba pangakhale malo a mtendere ndi chisangalalo kapena bwalo la ndewu ndi mikangano. (Miyambo 21:19; 26:21) Ngati titsatira utsogoleri wa Kristu, mtendere ndi chimwemwe m’banja zimawonjezeka. Ndipotu, Yesu ndi chitsanzo chabwino pa moyo wa banja. Malemba amati: ‘Muzimverana wina ndi mnzake m’kuopa Kristu. Akazi inu, mverani amuna anu a inu eni, monga kumvera Ambuye. Pakuti mwamuna ndiye mutu wa mkazi, monganso Kristu ndiye mutu wa Eklesia, ali yekha Mpulumutsi wa thupilo. . . . Amuna inu, kondani akazi anu, monganso Kristu anakonda Eklesia, nadzipereka yekha m’malo mwake.’ (Aefeso 5:21-25) Mtumwi Paulo analembera mpingo wa ku Kolose kuti: “Ana inu, mverani akubala inu m’zonse, pakuti ichi Ambuye akondwera nacho.”​—Akolose 3:18-20.

11. Kodi mwamuna angasonyeze bwanji kuti amaonadi utsogoleri wa Kristu kukhala weniweni?

11 Ngati onse atsatira uphungu umenewu ndiye kuti mwamuna adzatsogolera banja, mkazi wake adzamuthandiza mokhulupirika, ndipo ana awo adzamvera iwo monga makolo awo. Komabe kuti umutu wa mwamuna ukhale wosangalatsa, chofunika si china ayi koma kuti auchite moyenera. Mwamuna wanzeru ayenera kuphunzira mmene angakhalire mutu mwa kutsanzira  Mutu ndi Mtsogoleri wake, Kristu Yesu. (1 Akorinto 11:3) Yesu, ngakhale kuti anadzakhala “mutu pamtu pa zonse,” anabwera ku dziko lapansi, osati kuti ‘atumikiridwe koma kutumikira.’ (Aefeso 1:22; Mateyu 20:28) N’chimodzimodzinso ndi mwamuna wachikristu. Pokhala mutu, amasamala udindo wake m’njira yoti athandize mkazi wake ndi ana, inde, banja lake lonse pa zofuna zawo, osati chifukwa cha dyera. (1 Akorinto 13:4, 5) Amayesetsa kutsanzira makhalidwe abwino amene mutu wake, Yesu Kristu, ali nawo. Iye, mofanana ndi Yesu Kristu, amakhala wofatsa ndi wodzichepetsa mtima. (Mateyu 11:28-30) Mawu monga akuti “pepani” kapena “inuyo mwalondola” samuvuta kuwanena akalakwitsa. Chitsanzo chake chabwino chimapeputsira zinthu mkazi wake kuti akhale “womthangatira” ndi ‘mnzake,’ kuti aphunzire kwa iye ndi kugwira naye ntchito.​—Genesis 2:20; Malaki 2:14.

12. Kodi n’chiyani chingathandize mkazi kutsatira mfundo ya umutu?

12 Nayenso mkazi afunika kugonjera mwamuna wake. Koma ngati atengera mzimu wa dziko, angayambe kupeputsa mfundo ya umutu, ndipo zoti afunika kugonjera mwamuna wake sizidzam’sangalatsa. Malemba sanena kuti mwamuna azichita kupondereza mkazi wake ayi, koma amafuna kuti akazi azigonjera amuna awo basi. (Aefeso 5:24) Baibulo limanenanso kuti mwamuna kapena tate ali ndi udindo m’banja, ndipo ngati atsatira uphungu umenewu, banja limakhala la mtendere ndiponso lolongosoka.​—Afilipi 2:5.

13. Kodi Yesu anapereka chitsanzo chotani kwa ana pankhani ya kugonjera?

13 Ana afunika kumvera makolo awo. Pankhani imeneyi, Yesu anali chitsanzo chabwino kwambiri. Zitatha zimene zinachitika kukachisi nthaŵi imene Yesu anatsala masiku atatu ali ndi zaka 12, “anatsika nawo [makolo ake] pamodzi nadza ku Nazarete; nawamvera iwo.” (Luka 2:51) Ana akamagonjera makolo awo, mtendere ndi kugwirizana zimalimba m’banja. Ngati anthu onse m’banja agonjera utsogoleri wa Kristu, banjalo limakhala lachimwemwe.

14, 15. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti zinthu zitiyendere bwino tikakhala ndi mavuto panyumba? Perekani chitsanzo.

14 Ngakhale mavuto atabuka panyumba, chinsinsi choti zinthu ziyende bwino ndicho kutsanzira Yesu ndi kugonjera utsogoleri wake. Mwachitsanzo, pamene a Jerry a zaka 35 anakwatira a Lana, amene anali ndi mwana wamkazi, panabuka vuto limene onsewo sankaliganizira. A Jerry anafotokoza kuti: “Ndinadziŵa kuti ngati ndikufuna kukhala mutu wabwino, ndiyenera kutsata mfundo za makhalidwe abwino za m’Baibulo zimene zimachititsa kuti mabanja ena azikhala bwino. Koma posakhalitsa ndinapeza kuti ndinafunika nzeru zakuya ndi kuzindikira kokulirapo kuti nditsate mfundozo.” Mwana wawo wopezayo anali kuwaona ngati munthu wosokoneza amene anadanitsa iye ndi mayi ake ndipo anadana nawo bambo akewo kwadzaoneni. A Jerry anafunika kuzindikira kuti aone kuti maganizo ameneŵa anakhudza zimene mtsikanayo anali kulankhula ndi kuchita. Kodi anathetsa bwanji vutoli? Iwo akuyankha kuti: “Ine ndi mkazi wanga Lana tinagwirizana kuti pakali pano, iyeyo azilanga mwanayo posamalira mbali imeneyi ya ukholo pamene ineyo ndinaika mtima pa kukonza ubale wanga ndi mwana wanga wom’pezayo kuti ukhale wabwino. Patapita nthaŵi, njira imeneyi inathandiza kwambiri.”

15 Tikakhala ndi mavuto panyumba, tifunika kuzindikira kuti tidziŵe chifukwa chake ena m’banjamo akulankhula ndi kuchita zinthu mmene akuchitiramo. Tifunikanso nzeru kuti tigwiritse ntchito mfundo za makhalidwe abwino za Mulungu moyenera. Mwachitsanzo, Yesu anazindikira chifukwa chake mkazi amene anali kudwala nthenda ya kukha magazi anamukhudza, ndipo anachita naye mwanzeru ndiponso mwachifundo. (Levitiko 15:25-27; Marko 5:30-34) Nzeru ndi kuzindikira ndi makhalidwe a Mtsogoleri wathu. (Miyambo 8:12) Tidzakhala okondwa ngati tichita monga mmene iye angachitire.

“Muthange Mwafuna Ufumu”

16. Kodi n’chiyani chiyenera kukhala patsogolo m’moyo wathu, ndipo Yesu anasonyeza motani zimenezi mwa chitsanzo chake?

16 Yesu anafotokoza momveka bwino chimene anthu otsatira utsogoleri wake ayenera kuika patsogolo m’moyo wawo. Anati: “Koma muthange mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake  [cha Mulungu].” (Mateyu 6:33) Ndipo anatisonyeza mmene tingachitire zimenezi mwa chitsanzo chake. Yesu atasala kudya masiku 40, komanso kusinkhasinkha ndi kupemphera zimene anachita atabatizidwa, anakumana ndi mayesero. Satana Mdyerekezi anamuuza kuti am’patsa ulamuliro wa “mayiko onse a dziko lapansi.” Tangoganizani moyo umene Yesu akanakhala nawo akanavomera ulamuliro umene Mdyerekezi anali kum’patsawo! Koma Kristu anaika mtima pa kuchita chifuniro cha Atate ake. Anazindikiranso kuti moyo wotero m’dziko la Satana ukanakhala waufupi. Iye nthaŵi yomweyo anakana ulamuliro umene Satana anali kum’patsa, ndipo anati: “Kwalembedwa, Ambuye Mulungu wako udzam’gwadira, ndipo iye yekhayekha udzam’lambira.” Zitangochitika kumene zimenezi, Yesu “anayamba kulalikira, ndi kunena, Tembenukani mitima, pakuti Ufumu wa Kumwamba wayandikira.” (Mateyu 4:2, 8-10, 17) Kristu, moyo wake wonse padziko lapansi, anali mlengezi wa nthaŵi zonse wa Ufumu wa Mulungu.

17. Kodi tingasonyeze motani kuti zinthu za Ufumu timaziika patsogolo?

17 Tiyenera kutsanzira Mtsogoleri wathu ndi kusalola dziko la Satana kutikopa kuti cholinga chathu chachikulu chikhale kufunafuna ntchito ya ndalama zambiri. (Marko 1:17-21) Kungakhaletu kupusa ngati tikoledwa m’msampha wofunafuna choyamba zinthu za m’dziko motero kuti zinthu za Ufumu n’kutsatira pambuyo pake. Yesu watipatsa ntchito yolalikira Ufumu ndi kupanga ophunzira. (Mateyu 24:14; 28:19, 20) N’zoona kuti tili ndi udindo m’banja kapena maudindo ena oti tiwasamalire, koma kodi sitisangalala kugwiritsa ntchito nthaŵi yathu madzulo komanso Loŵeruka ndi Lamlungu kuchita ntchito yathu yachikristu yolalikira ndi kuphunzitsa? Ndipo n’zolimbikitsatu kuti chaka chautumiki cha 2001, anthu pafupifupi 780,000 anatumikira monga atumiki a nthaŵi zonse, kapena apainiya.

18. Kodi n’chiyani chimatithandiza kusangalala ndi utumiki?

18 Nkhani za m’Mauthenga Abwino zimasonyeza kuti Yesu anali wachangu ndiponso wachifundo. Ataona zosoŵa zauzimu za anthu amene anali naye pafupi, anawamvera chifundo ndipo anakondwera kuwathandiza. (Marko 6:31-34) Utumiki wathu umakhala wosangalatsa ngati tiuchita chifukwa chokonda anthu ena ndi kufunitsitsa kuwathandiza. Koma kodi tingathe bwanji kukhala ofunitsitsa kuthandiza anthu ena? Mwamuna wina dzina lake Jayson anati: “Pamene ndinali mnyamata, sindinkakonda kwambiri utumiki.” N’chiyani chinam’thandiza kuyamba kukonda ntchito imeneyi? Iye akuyankha  kuti: “M’banja mwathu, Loŵeruka lililonse tinali kupita muutumiki wa kumunda m’maŵa. Zimenezi zinandithandiza chifukwa kupitapita mu utumiki kunandichititsa kuona phindu lake ndiponso kukonda kwambiri utumikiwu.” Ifenso tizichita nawo utumiki nthaŵi zonse ndiponso mwakhama.

19. Kodi tifunika kutsimikiza mtima kuchita chiyani pankhani ya utsogoleri wa Kristu?

19 Inde, kutsatira utsogoleri wa Kristu n’kotsitsimula ndiponso kopindulitsa. Tikatero, nthaŵi ya unyamata imakhala yokula m’chidziŵitso ndi nzeru. Banja limakhala lamtendere ndi lachimwemwe, ndipo utumiki umakhala ntchito yosangalatsa ndiponso yokhutiritsa. Ndiyetu, mmene timakhalira tsiku ndi tsiku ndiponso posankha zochita, tiyeni titsimikize mtima kusonyeza kuti utsogoleri wa Kristu timauonadi kukhala weniweni. (Akolose 3:23, 24) Komabe, Yesu Kristu akutitsogoleranso mwa njira ina. Njira imeneyo ndi mpingo wachikristu. Nkhani yotsatirayi ifotokoza mmene tingapindulire ndi makonzedwe ameneŵa.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 7 Tasintha mayina ena.

Kodi Mukukumbukira?

• Tikamatsatira Mtsogoleri wathu woikidwa ndi Mulungu, timapindula motani?

• Kodi achinyamata angasonyeze bwanji kuti akufuna kutsatira utsogoleri wa Kristu?

• Kodi amene amagonjera utsogoleri wa Kristu mabanja awo amakhala otani?

• Kodi utumiki wathu ungasonyeze bwanji kuti timaonadi utsogoleri wa Kristu kukhala weniweni?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 9]

Unyamata ndi nthaŵi yabwino yodziŵa za Mulungu ndi Mtsogoleri wathu amene anamuika

[Chithunzi patsamba 10]

Kugonjera utsogoleri wa Kristu kumabweretsa chimwemwe m’banja

[Zithunzi patsamba 12]

Yesu anafunafuna Ufumu choyamba. Kodi inunso mumatero?