Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuunika kwa Mulungu Kumachotsa Mdima!

Kuunika kwa Mulungu Kumachotsa Mdima!

 Kuunika kwa Mulungu Kumachotsa Mdima!

“Yehova adzaunika mumdima mwanga.”​—2 SAMUELI 22:29.

1. Kodi kuunika kumagwirizana bwanji ndi moyo?

“ANATI Mulungu, Kuyere; ndipo kunayera.” (Genesis 1:3) Nkhani yosimba za kulengedwa kwa zinthu imene ili m’buku la Genesis, ikugwiritsa ntchito mawu ofunika kwambiri ameneŵa pom’sonyeza Yehova kukhala gwero la kuunika. Popanda kuunika, padziko lapansi sipakanakhala chinthu chilichonse chamoyo. Yehova alinso gwero la kuunika kwauzimu komwe n’kofunika kwambiri kuti kutitsogolere pa moyo wathu. (Salmo 43:3) Mfumu Davide anasonyeza kuti kuunika kwauzimu n’kogwirizana kwambiri ndi moyo, pamene analemba kuti: “Pakuti chitsime cha moyo chili ndi Inu: m’kuunika kwanu tidzaona kuunika.”​—Salmo 36:9.

2. Kodi Paulo anasonyeza kuti kuunika n’kogwirizana kwambiri ndi chiyani?

2 Patapita zaka pafupifupi 1,000 Davide atamwalira, mtumwi Paulo anatchula za nkhani yosimba za kulengedwa kwa zinthu. Polembera mpingo wachikristu wa ku Korinto, iye anati: “Mulungu amene anati, Kuunika kudzawala kutuluka mumdima.” Kenako Paulo anasonyeza kuti kuunika kwauzimu n’kogwirizana kwambiri ndi chidziŵitso chochokera kwa Mulungu pamene anawonjezera kuti: “Anawala m’mitima yathu kutipatsa chiwalitsiro cha chidziŵitso cha ulemerero wa Mulungu pankhope pa Yesu Kristu.” (2 Akorinto 4:6) Kodi timalandira motani kuunika kumeneku?

Baibulo Limabweretsa Kuunika

3. Kodi Yehova amapereka kuunika kotani kudzera m’Baibulo?

3 Njira yaikulu imene Yehova amatiunikira mwauzimu ndiyo kudzera m’Mawu ake amene anawauzira, Baibulo. Motero, pamene tiphunzira Baibulo ndi kudziŵa zambiri kuchokera kwa Mulungu, timalola kuti kuunika kwake kutiwalire. Yehova kudzera m’Baibulo, amatidziŵitsa zolinga zake ndiponso amatiuza mmene tingachitire zimene amafuna. Zimenezi zimatithandiza kuti moyo wathu ukhale ndi cholinga ndiponso zimatithandiza kukwaniritsa zosoŵa zathu zauzimu. (Mlaliki 12:1; Mateyu 5:3) Yesu pogwira mawu Chilamulo cha Mose, anatsindika kuti tiyenera kusamalira zosoŵa zathu zauzimu pamene anati: “Kwalembedwa, Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha, koma ndi mawu onse akutuluka mkamwa mwa Mulungu.”​—Mateyu 4:4; Deuteronomo 8:3.

4. Kodi ndi motani mmene Yesu alili “kuunika kwa dziko lapansi”?

4 Yesu akugwirizanitsidwa kwambiri ndi kuunika kwauzimu. Ndipotu, iye anadzinena yekha kuti ndiye “kuunika kwa dziko lapansi” ndipo anati: “Iye wonditsata  Ine sadzayenda mumdima, koma adzakhala nako kuunika kwa moyo.” (Yohane 8:12) Mawu ameneŵa akutithandiza kudziŵa udindo waukulu umene Yesu ali nawo wouza anthu choonadi cha Yehova. Kuti tipeŵe mdima ndi kuyenda m’kuunika kwa Mulungu, tiyenera kumvera zonse zimene Yesu ananena ndi kutsatira kwambiri chitsanzo chake ndi ziphunzitso zake zimene zili m’Baibulo.

5. Kodi Yesu atamwalira ophunzira ake anali ndi udindo wotani?

5 Patatsala masiku ochepa kuti aphedwe, Yesu, anabwerezanso kudzitchula kuti iye ndiye kuunika ndipo anauza ophunzira ake kuti: “Katsala kanthaŵi kakang’ono ndipo kuunika kuli mwa inu. Yendani pokhala muli nako kuunika, kuti mdima sungakupezeni; ndipo woyenda mumdima sadziŵa kumene amukako. Pokhala muli nako kuunika, khulupirirani kuunikako, kuti mukakhale ana a kuunikako.” (Yohane 12:35, 36) Amene anakhala ana a kuunika, anaphunzira “mawu a moyo” a m’Baibulo. (2 Timoteo 1:13, 14) Ndiyeno iwo anagwiritsa ntchito mawu a moyo ameneŵa kutulutsa mumdima anthu ena oona mtima ndi kuwaloŵetsa m’kuunika kwa Mulungu.

6. Kodi pa 1 Yohane 1:5 timapezapo choonadi chotani chonena za kuunika ndi mdima?

6 Mtumwi Yohane analemba kuti: “Mulungu ndiye kuunika, ndipo mwa Iye monse mulibe mdima.” (1 Yohane 1:5) Onani kusiyana kwa kuunika ndi mdima m’mawu ameneŵa. Kuunika kwauzimu kumachokera kwa Yehova ndipo sangagwirizane ndi mdima wauzimu. Nangano, kodi ndani amene ali gwero la mdima?

Gwero la Mdima Wauzimu

7. Kodi mdima wauzimu umene uli m’dzikoli ukuchokera kwa yani, ndipo amasonkhezera motani anthu?

7 Mtumwi Paulo ananenapo za “mulungu wa nthaŵi ya pansi pano.” Pogwiritsa ntchito mawu ameneŵa, iye anatanthauza Satana Mdyerekezi. Paulo anapitiriza kunena kuti mulungu ameneyu “[a]nachititsa khungu maganizo awo a osakhulupirira, kuti chiwalitsiro cha Uthenga Wabwino wa ulemerero wa Kristu, amene ali chithunzithunzi cha Mulungu, chisawawalire.” (2 Akorinto 4:4) Anthu ambiri amati amakhulupirira kuti Mulungu aliko. Komabe ambiri mwa iwo sakhulupirira kuti kuli Mdyerekezi. Chifukwa chiyani? Safuna kuvomereza kuti winawake woipa, wamphamvu kuposa anthu angakhaleko ndi kulamulira mmene anthuwo amaganizira. Komabe, monga mmene Paulo anasonyezera, Mdyerekezi alikodi, ndipo amasonkhezera anthu kuti asaone kuunika kwa choonadi. Mphamvu za Satana zosonkhezera mmene anthu amaganizira tikuziona m’mawu aulosi ofotokoza kuti iye ndiye “wonyenga wa dziko lonse.” (Chivumbulutso 12:9) Chifukwa cha zochita za Satana, zimene mneneri Yesaya analosera zikukhudza anthu onse kupatulapo amene akutumikira Yehova. Iye anati: “Taona, mdima udzaphimba dziko lapansi, ndi mdima wa bii mitundu ya anthu.”​—Yesaya 60:2.

8. Kodi anthu amene ali mumdima wauzimu amasonyeza motani kuti asokonezeka?

8 Mumdima wa ndiwe yani, munthu sungathe kuona chilichonse. Utha kusochera kapena kusokonezeka mosavuta. N’chimodzimodzi ndi anthu amene ali mumdima wauzimu. Satha kuzindikira ndipo posakhalitsa amasokonezeka mwauzimu. Sangathe kusiyanitsa zoona ndi zonama, zabwino ndi zoipa. Mneneri Yesaya anali kunena za anthu amene ali mumdima ngati umenewo pamene analemba kuti: “Tsoka kwa iwo amene ayesa zoipa zabwino, ndi zabwino zoipa; amene aika mdima m’malo mwa kuyera, ndi kuyera m’malo mwa mdima; amene aika zowawa m’malo mwa zotsekemera, ndi zotsekemera m’malo mwa zowawa!” (Yesaya 5:20) Amene ali mumdima wauzimu amasonkhezeredwa ndi mulungu wa mdima, Satana Mdyerekezi, ndipo motero amatalikirana ndi gwero la kuunika ndi moyo.​—Aefeso 4:17-19.

Mavuto Oti Munthu Awagonjetse Pochoka Mumdima Kuloŵa M’kuunika

9. Fotokozani mmene anthu ochita zoipa amakondera mdima weniweni ndiponso mdima wauzimu.

9 Yobu, munthu wokhulupirika, anafotokoza mmene anthu ochita zoipa amakondera mdima weniweni, pamene ananena kuti: “Ndipo diso la wachigololo liyembekezera chisisira, ndi kuti, Palibe diso lidzandiona; navala chophimba pankhope pake.” (Yobu 24:15) Anthu ochita zoipa  alinso mumdima wauzimu, ndipo mdima umenewo ungakhale waukulu kwambiri. Mtumwi Paulo ananena kuti chiwerewere, kuba, umbombo, kuledzera, kulalata ndi kulanda n’zofala kwa anthu amene ali mumdima umenewu. Koma aliyense amene amaloŵa m’kuunika kwa Mawu a Mulungu angathe kusintha. Paulo m’kalata yake kwa Akorinto anamveketsa bwino kuti n’zotheka kusintha motero. Akristu ambiri a ku Korinto ankakonda kuchita ntchito za mdima, koma Paulo anawauza kuti: “Koma munasambitsidwa, koma munayeretsedwa, koma munayesedwa olungama, m’dzina la Ambuye Yesu Kristu, ndi mwa Mzimu wa Mulungu wathu.”​—1 Akorinto 6:9-11.

10, 11. Kodi Yesu anasonyeza motani kum’ganizira munthu amene anam’chiritsa khungu lake? (b) N’chifukwa chiyani ambiri sasankha kuunika?

10 Mosakayika, munthu akatuluka mumdima wa ndiwe yani ndi kulowa m’kuunika, pangatenge nthaŵi kuti maso ake azoloŵere kuunikako. Ku Betsaida, Yesu anachiritsa munthu wakhungu koma iye mwachifundo anachita zimenezo pang’onopang’ono. “Anam’gwira dzanja munthu wakhunguyo, natulukira naye kunja kwa mudzi; ndipo atam’thira malovu m’maso mwake, naika manja pa iye, anamfunsa, Uona kanthu kodi? Ndipo anakweza maso, nanena, Ndiona anthu; pakuti ndiwapenya ayendayenda ngati mitengo. Pamenepo anaikanso manja m’maso mwake; ndipo anapenyetsa, nachiritsidwa, naona zonse mbee.” (Marko 8:23-25) Mwachionekere, Yesu anachiritsa munthu wakhunguyo pang’onopang’ono kuti azoloŵere bwino kuwala kwa dzuŵa. Titha kuyerekeza chimwemwe chimene munthuyo anali nacho pamene anatha kuona.

11 Komabe, chimwemwe chimene munthu ameneyo anali nacho n’chochepa poyerekezera ndi chimwemwe cha anthu amene amathandizidwa kutuluka pang’onopang’ono mumdima wauzimu kuloŵa m’kuunika kwa choonadi. Tikamaona chimwemwe chawo, tingadabwe kuti n’chifukwa chiyani anthu ena sakopeka ndi kuunikako. Yesu anafotokoza chifukwa chake kuti: “Chiweruziro ndi ichi, kuti kuunika kunadza ku dziko lapansi, ndipo anthu anakonda mdima koposa kuunika; pakuti ntchito zawo zinali zoipa. Pakuti yense wakuchita zoipa adana nako kuunika, ndipo sakudza kwa kuunika, kuti zingatsutsidwe ntchito zake.” (Yohane 3:19, 20) Inde, ambiri amakonda kuchita “zoipa,” monga chiwerewere, kupondereza anzawo, kunama, chinyengo, ndi kuba, ndipo mumdima wauzimu wa Satana ndi malo awo abwino kwambiri ochitiramo zimenezi mmene akufunira.

Kupita Patsogolo M’kuunika

12. Kodi tapindula motani mwa kuloŵa m’kuunika?

12 Kuyambira pamene tinadziŵa za kuunika, kodi tikuona kuti tasintha motani pa moyo wathu? Nthaŵi zina ndi bwino kuyang’ana m’mbuyo ndi kuona mmene tapitira patsogolo mwauzimu. Kodi ndi makhalidwe oipa ati amene tasiya? Kodi ndi mavuto ati m’moyo amene tawawongolera? Kodi zolinga zathu zam’tsogolo tazisintha motani? Mwa mphamvu za Yehova ndiponso mothandizidwa ndi mzimu wake woyera, tingapitirize kusintha mtima wathu ndi mmene timaganizira zimene zingasonyeze kuti tikuyenda m’kuunika. (Aefeso 4:23, 24) Paulo anafotokoza zimenezi motere: “Kale munali mdima, koma tsopano muli kuunika mwa Ambuye; yendani monga ana a kuunika, pakuti chipatso cha kuunika tichipeza m’ubwino wonse, ndi chilungamo, ndi choonadi.”  (Aefeso 5:8, 9) Kulola kuti kuunika kwa Yehova kutitsogolere kumatipatsa chiyembekezo ndiponso kukhala ndi cholinga pa moyo komanso kumawonjezera chimwemwe cha anthu amene timakhala nawo. Ndipotu, kusintha koteroko kumasangalatsa Yehova kwambiri.​—Miyambo 27:11.

13. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira kuunika kwa Yehova, ndipo n’chiyani chimafunika kuti tichite zimenezo?

13 Timasonyeza kuyamikira moyo wachimwemwe umene tili nawo mwa kuonetsa kuunika kwa Yehova​—kuuza anthu a m’banja mwathu, anzathu, ndi anansi athu zimene taphunzira m’Baibulo. (Mateyu 5:12-16; 24:14) Kwa anthu amene amakana kumvera zimene tikuwauza, kulalikira kwathu pamodzi ndi khalidwe lathu labwino lachikristu zimawatsutsa. Paulo anafotokoza kuti: “Kuyesera chokondweretsa Ambuye n’chiyani; ndipo musayanjane nazo ntchito za mdima zosabala kanthu, koma makamakanso muzitsutse.” (Aefeso 5:10, 11) Tifunika kulimba mtima kuti tithandize anthu ena kuchoka mumdima ndi kuloŵa m’kuunika. Chofunika kwambiri n’chakuti tiyenera kukhala achifundo ndi oganizira anthu ena komanso kufunitsitsa ndi mtima wonse kugaŵira ena kuunika kwa choonadi kuti apindule mpaka kalekale.​—Mateyu 28:19, 20.

Chenjerani ndi Kuunika Konyenga

14. Kodi tifunika kumvera chenjezo lotani pankhani ya kuunika?

14 Anthu amene ali panyanja usiku, angasangalale ndi kuunika kulikonse kumene angaone. Kale ku England, anthu ankayatsa moto m’zigwembe za miyala kusonyeza malo amene anthu oyenda panyanja angabisale ngati kunali namondwe. Oyendetsa sitima za m’madzi anali kuyamikira kwambiri kulondoleredwa ndi kuunika kumeneku kuti afike pokocheza sitima potetezeka. Komabe, moto wina unali wonyenga. Sitima zambiri, m’malo mopeza pokocheza pabwino, zinali kusocheretsedwa ndipo zinali kugunda miyala ya m’mbali mwa nyanja n’kusweka, ndipo katundu amene anali m’sitimayo anali kubedwa. M’dziko lachinyengo lino, tifunika kusamala kuti tisatengeke ndi kuunika konyenga kumene kungatikope kuti tisweke mwauzimu. Timauzidwa kuti: “Satana yemwe adzionetsa ngati mngelo wa kuunika.” Mofanana ndi iyeyo, atumiki ake, kuphatikizapo ampatuko, ali “ochita ochenjerera” amene “adzionetsa monga atumiki a chilungamo.” Ngati timvera mfundo zabodza za anthu ngati ameneŵa, chidaliro chathu m’Mawu a Yehova a choonadi, Baibulo, chingafooke ndipo chikhulupiriro chathu chingafe.​—2 Akorinto 11:13-15; 1 Timoteo 1:19.

15. Kodi n’chiyani chingatithandize kukhalabe m’njira yakumuka nayo kumoyo?

 15 Wamasalmo analemba kuti: “Mawu anu ndiwo nyali ya ku mapazi anga, ndi kuunika kwa panjira panga.” (Salmo 119:105) Inde, ‘njira yochepetsa yomuka nayo ku moyo’ ikuunikiridwa bwinobwino ndi Mulungu wathu wachikondi, Yehova, “amene afuna anthu onse apulumuke, nafike pozindikira choonadi.” (Mateyu 7:14; 1 Timoteo 2:4) Kugwiritsa ntchito malamulo a Baibulo kudzatiteteza kuti tisapatuke panjira yochepetsayo kuloŵa m’njira za mdima. Paulo analemba kuti: “Lemba lililonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m’chilungamo.” (2 Timoteo 3:16) Pamene tikukula mwauzimu ndiye kuti tikuphunzitsidwa ndi Mawu a Mulungu. Tingadzidzudzule tokha ndi kuunika kwa Mawu a Mulungu kapena, ngati n’kofunika, abusa achikondi mumpingo wachikristu angatidzudzule. Mofananamo, tingakonze zinthu ndi kulandira modzichepetsa chilango cha m’chilungamo kuti tipitirize kuyenda m’njira yopita ku moyo.

Yendani M’kuunika Moyamikira

16. Kodi tingayamikire motani mphatso yabwino kwambiri ya Yehova ya kuunika?

16 Kodi tingayamikire bwanji mphatso yabwino kwambiri ya Yehova ya kuunika? Yohane chaputala 9 chimatiuza kuti Yesu atachiritsa munthu amene anali wogontha chibadwire, munthuyo anasonkhezereka kuyamikira. Motani? Anakhulupirira Yesu monga Mwana wa Mulungu ndipo anam’dziŵitsa kwa anthu onse kuti iye anali “mneneri.” Ndiponso iye anawatsutsa molimba mtima anthu amene ankayesetsa kunyoza zozizwitsa za Yesu. (Yohane 9:17, 30-34) Mtumwi Paulo amatcha anthu odzozedwa a mumpingo wachikristu kuti ndi “anthu a mwini wake.” Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti nawonso ali ndi mtima woyamikira monga wa munthu amene anali wakhungu chibadwire uja amene anachiritsidwa. Amayamikira Yehova, Mpatsi wawo, mwa ‘kulalikira zoposazo za Iye amene anawaitana kutuluka mumdima, kuloŵa kuunika kwake kodabwitsa.’ (1 Petro 2:9; Akolose 1:13) Amene akuyembekezera kudzakhala padziko lapansi alinso ndi mtima woyamikira ngati umenewo, ndipo amathandiza abale awo odzozedwa polengeza “zoposazo” za Yehova. Ndi mwayi wosayerekezekatu umenewu umene Mulungu wapereka kwa anthu opanda ungwiro.

17, 18. (a) Kodi munthu aliyense payekha ali ndi udindo wotani? (b) Kodi Mkristu aliyense akulimbikitsidwa kupeŵa chiyani, potsanzira Timoteo?

17 Kuyamikira kuunika kwa choonadi kochokera pansi pa mtima n’kofunika kwambiri. Kumbukirani kuti palibe amene amabadwa akudziŵa choonadi. Ena amaphunzira choonadi atakula kale, ndipo sachedwa kuona phindu la kuunika poyerekezera ndi mdima. Ena ali ndi mwayi wapadera woleredwa ndi makolo oopa Mulungu. Kwa anthu otere, n’kosavuta kukuona kuunika mopepuka. Wa Mboni wina amene makolo ake anali kutumikira Yehova iye asanabadwe, anavomereza kuti zinam’tengera nthaŵi ndiponso kuyesetsa kuti azindikire phindu lenileni ndi kufunika kwa choonadi chimene anaphunzira kuyambira ali wamng’ono. Tonsefe, kaya ana kapena achikulire tifunika kuyamikira choonadi chimene Yehova wavumbula.

18 Timoteo wachinyamata anaphunzitsidwa “malembo opatulika” kuyambira ali wamng’ono, koma kuti akhwime mwauzimu monga Mkristu, anadzipereka mwakhama muutumiki wake. (2 Timoteo 3:15) Motero, iye anakwanitsa kuthandiza mtumwi Paulo, amene anamulimbikitsa kuti: “Uchite changu kudzionetsera kwa Mulungu wovomerezeka, wantchito wopanda chifukwa cha kuchita manyazi, wolunjika nawo  bwino mawu a choonadi.” Tiyenitu tonsefe, monga Timoteo, tipeŵe kuchita zinthu zimene zingatichititse manyazi​—kapena zimene zingapangitse Yehova kuchita nafe manyazi.​—2 Timoteo 2:15.

19. (a) Monga Davide, kodi tonsefe tiyenera kunena kuti chiyani? (b) Kodi tikambirana chiyani m’nkhani yotsatirayi?

19 Tili ndi zifukwa zambiri zoyamikirira Yehova amene anatipatsa kuunika kwa choonadi chake. Ife, monganso Mfumu Davide, tikuti: “Inu ndinu nyali yanga, Yehova; ndipo Yehova adzaunika mumdima mwanga.” (2 Samueli 22:29) Komabe, sitifuna kukhala osasamala, popeza kuchita zimenezi kungatichititse kubwerera mumdima mmene tinatulutsidwamo. Motero, nkhani yotsatirayi itithandiza kupenda mmene choonadi cha Mulungu timachionera kukhala chofunika m’moyo wathu.

Kodi Mwaphunzira Chiyani?

• Kodi Yehova amatiunikira motani mwauzimu?

• Kodi mdima wauzimu umene watikuta umabweretsa mavuto otani?

• Kodi tifunika kupeŵa ngozi zotani?

• Kodi tingasonyeze bwanji kuyamikira kuunika kwa choonadi?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 8]

Yehova ndiye gwero la kuunika kwenikweni ndiponso kuunika kwauzimu

[Chithunzi patsamba 10]

Monga mmene Yesu anachiritsira pang’onopang’ono munthu wakhungu chibadwire, amatithandizanso chimodzimodzi kutuluka mumdima wauzimu?

[Chithunzi patsamba 11]

Kusocheretsedwa ndi kuunika konyenga kwa Satana kungatichititse kusweka mwauzimu