Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Dziko Lonse Linawonongedwa!

Dziko Lonse Linawonongedwa!

 Dziko Lonse Linawonongedwa!

Tangomwazani maso ndi kuona mmene dziko lilili mizinda yake, chikhalidwe chake, kupita kwake patsogolo pa za sayansi ndiponso anthu ake miyandamiyanda Mmene dzikoli likuonekera, n’zosavuta kuganiza kuti lidzakhalako mpaka kalekale si choncho kodi? Kodi mukuganiza kuti tsiku lina dzikoli lingadzawonongedwe kotheratu? Zimenezo zingakhale zovuta kwambiri kuziganizira. Komabe, kodi mukudziŵa kuti, malinga ndi umboni wodalirika, panali dziko lomwe linawonongedwa kotheratu lathuli lisanafike?

SITIKUNENATU za dziko la anthu osatukuka ayi. Dziko lomwe linawonongedwalo linali lotukuka, lokhala ndi mizinda, zinthu zaluso zosiyanasiyana, ndiponso lodziŵa sayansi. Komabe, Baibulo limatiuza kuti mwadzidzidzi, pa tsiku la 17 la mwezi wachiŵiri, zaka 352 kholo lakale Abrahamu asanabadwe, chigumula chinayamba ndipo chinasesa dziko lonse. *

Kodi nkhani imeneyo n’njolondola? Kodi zimenezo zinachitikadi? Kodi kale kunalidi dziko, lisanafike lamakonoli, lomwe linatukuka kwambiri kenako n’kuwonongedwa? Ngati linalikodi, n’chifukwa chiyani linatha? Kodi chinalakwika n’chiyani? Ndipo kodi pali phunziro lililonse lomwe tingatengepo pa kuwonongedwa kwake?

 Kodi Dziko Lakale Linawonongedwadi?

Ngati chiwonongeko chochititsa mantha chimenecho chinachitikadi ndiye kuti sichikanatha kuiŵalika m’pang’ono pomwe. Motero, m’mayiko ambiri muli zinthu zomwe zimakumbutsa anthu chiwonongekocho. Mwachitsanzo, taganizirani za deti lenileni lopezeka m’Malemba. Mwezi wachiŵiri wa kalendala yakale unali kuyambira pakati pa mwezi womwe tsopano timati October mpaka pakati pa November. Choncho, tsiku la 17 n’lofanana pafupifupi ndi tsiku loyamba la November. Motero, sikuti zinangochitika mwamwayi kuti m’mayiko ambiri amachita madyerero okondwerera anthu akufa pa nthaŵi imeneyi ya chaka.

Chikhalidwe cha anthu chimapereka umboni wina wotsimikiza kuti Chigumula chinachitikadi. Pafupifupi mitundu yonse ya anthu akale ili ndi nthano yosimba zoti makolo awo anapulumuka chigumula cha dziko lonse. Anthu otchedwa Apigime a ku Africa, Aselote a ku Ulaya, Ainka a ku South America, onseŵa ali ndi nthano zofananako monganso momwe zilili ndi anthu a ku Alaska, Australia, China, India, Lithuania, Mexico, Micronesia, New Zealand, ndi mbali zina za ku North America, kungotchulapo ochepa chabe.

N’zoona kuti m’kupita kwa nthaŵi, nthano zimenezi azikometsera ndi mawu ena koma zonse zili ndi mfundo zambiri zosonyeza kuti zikusimba za chinthu chimodzi. Mfundo zake ndi izi: Mulungu anakwiya ndi kuipa kwa anthu. Anabweretsa chigumula chachikulu. Anthu onse anawonongedwa. Komabe, anthu oŵerengeka olungama anapulumutsidwa. Anthu ameneŵa anakhoma chingalawa chomwe iwo ndi nyama anapulumukiramo. Patapita nthaŵi, mbalame zinatumidwa kukaona ngati madzi anaphwa. Kenako, chingalawacho chinatera pa phiri. Atatuluka, anthu opulumukawo anapereka nsembe.

Kodi kufanana kumeneku kukutsimikiza chiyani? Sizingatheke kuti mfundozi zinafanana mwamwayi. Umboni wonse wa nthano zimenezi ukugwirizana ndi umboni wakale wa m’Baibulo wakuti anthu onse anachokera kwa anthu amene anapulumuka chigumula chomwe chinawononga anthu ena onse. Chotero, sitiyenera kuchita kudalira nthano kuti tidziŵe zomwe zinachitika. Tili ndi nkhani yosungidwa bwino m’Malemba Achihebri a m’Baibulo.​—Genesis machaputala 6-8.

Baibulo lili ndi nkhani zakale zouziridwa kuyambira  pachiyambi cha moyo wa munthu. Komabe, umboni umasonyeza kuti limeneli si buku wamba la mbiri yakale. Ulosi wake wosalephera ndiponso kuya kwa nzeru zake kumasonyeza kuti lilidi monga mmene ilo limanenera kuti ndi Mawu a Mulungu kwa anthu. Mosiyana ndi nthano, Baibulo m’nkhani zake zamakedzana, limatchula mayina ndi madeti komanso mfundo zatsatanetsatane zokhudza mibadwo ndi malo. Limatipatsa chithunzi cha mmene moyo unalili Chigumula chisanachitike ndiponso limavumbula chifukwa chomwe dziko lonse linathera mwadzidzidzi.

Kodi chinalakwika n’chiyani ndi dziko lakale limenelo? Nkhani yotsatirayi iyankha funso limeneli. Funsoli n’lofunika kwambiri kwa anthu amene angamadzifunse kuti kodi tsogolo la dziko lotukuka lamakonoli n’lotani?

[Mawu a M’munsi]

[Tchati patsamba 4]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Nthano za Chigumula pa Dziko Lonse

Dziko Nthano Zogwirizana ndi Mfundo

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10

Greece 7 ◆ ◆ ◆ ◆ ◆ ◆

Rome 6 ◆ ◆ ◆ ◆ ◆ ◆

Lithuania 6 ◆ ◆ ◆ ◆ ◆ ◆

Assyria 9 ◆ ◆ ◆ ◆ ◆ ◆ ◆ ◆ ◆

Tanzania 7 ◆ ◆ ◆ ◆ ◆ ◆ ◆

India - m’Chihindu 6 ◆ ◆ ◆ ◆ ◆ ◆

New Zealand - m’Chimaori 5 ◆ ◆ ◆ ◆ ◆

Micronesia 7 ◆ ◆ ◆ ◆ ◆ ◆ ◆

Washington U.S.A.

- m’Chiyakima 7 ◆ ◆ ◆ ◆ ◆ ◆ ◆

Mississippi U.S.A.

- m’Chichoctaw 7 ◆ ◆ ◆ ◆ ◆ ◆ ◆

Mexico - m’Chimichoacan 5 ◆ ◆ ◆ ◆ ◆

South America - m’Chiquechua 4 ◆ ◆ ◆ ◆

Bolivia - m’Chiriguano 5 ◆ ◆ ◆ ◆ ◆

Guyana - m’Chiarawak 6 ◆ ◆ ◆ ◆ ◆ ◆

1: Mulungu anakwiya ndi kuipa

2: Anawononga ndi Chigumula

3: Analamulidwa ndi Mulungu

4: Mulungu anapereka chenjezo

5: Anthu oŵerengeka anapulumuka

6: Anapulumukira m’chingalawa

7: Nyama zinapulumutsidwa

8: Mbalame kapena nyama zina zinatumidwa

9: Kenako chingalawa chinatera pa phiri

10: Atatuluka anapereka nsembe