Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Yehova Anatiphunzitsa Kupirira ndi Kulimbikira

Yehova Anatiphunzitsa Kupirira ndi Kulimbikira

 Mbiri ya Moyo Wanga

Yehova Anatiphunzitsa Kupirira ndi Kulimbikira

YOSIMBIDWA NDI ARISTOTELIS APOSTOLIDIS

Mzinda wa ku Russia wotchedwa Pyatigorsk womwe ndi wotchuka chifukwa cha migodi imene ili kumeneko ndiponso nyengo yabwino, uli ku mapiri aang’onoang’ono a kumpoto kwa mapiri a Caucasus. Ndinabadwira kumeneko mu 1929 ku banja la Agiriki othaŵa kwawo. Patapita zaka khumi kuyambira pamene kupulula anthu, kuopseza, ndi kuyeretsa fuko kwa ulamuliro wankhanza wa Stalin zinatha, tinakhalanso anthu othaŵa kwawo pamene anatithamangitsa kupita ku Greece.

TITASAMUKIRA ku Piraiévs, ku Greece, mawu oti “othaŵa kwawo” anali ndi tanthauzo latsopano kwa ife. Tinkaona ngati ndife alendo enieni. Ngakhale kuti mkulu wanga ndi ine mayina athu anali a afilosofi aŵiri achigiriki otchuka kwambiri, Socrates ndi Aristotle, sitinali kumva mayinaŵa akutchulidwatchulidwa. Anthu onse ankangotitcha ana a ku Russia.

Nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse itangoyamba kumene, mayi anga okondedwa anamwalira. Iwo anali munthu wofunika kwambiri panyumba pathu ndipo kumwalira kwawo kunandipweteka kwambiri. Popeza anadwala kwa nthaŵi yaitalipo, anandiphunzitsa kugwira ntchito zambiri zapanyumba. Kuphunzira ntchito zimenezi kunandithandiza kwambiri m’zaka zam’tsogolo.

Nkhondo Ndiponso Kumasuka

Tsiku lililonse linkaoneka ngati ndi lomaliza kukhala ndi moyo chifukwa cha nkhondo, Anazi amene analanda dzikoli, ndi kuwombera kosalekeza kwa mayiko amene anali kulimbana ndi Germany. Panali umphaŵi wadzaoneni, njala, ndi imfa zosaneneka. Kuyambira ndili ndi zaka 11, ndinali kugwira ntchito zolimba  pamodzi ndi bambo anga kuti tipeze zosoŵa za anthu atatufe. Maphunziro anga a kusukulu anabwerera m’mbuyo chifukwa chosadziŵa bwino Chigiriki, ndiponso chifukwa cha nkhondo ndi zotsatira zake.

Dziko la Greece linamasuka m’manja mwa Germany mu October 1944. Patangopita nthaŵi yochepa, ndinakumana ndi Mboni za Yehova. Chiyembekezo cha m’Baibulo cha tsogolo labwino mu ulamuliro wa Ufumu wa Mulungu chinandikhudza mtima kwambiri poona kutaya mtima ndi chisoni zimene zinalipo panthaŵiyo. (Salmo 37:29) Lonjezo la Mulungu lakuti anthu adzakhala ndi moyo wosatha komanso kukhala mwamtendere padziko lapansi lino, linali mankhwala othetsa nkhaŵa zanga. (Yesaya 9:7) Ine ndi bambo tinabatizidwa mu 1946, posonyeza kudzipatulira kwathu kwa Yehova.

M’chaka chotsatira, ndinasangalala kulandira utumiki wanga woyamba monga mtumiki wolengeza (panopa timati mtumiki wa magazini) mu mpingo wachiŵiri umene unakhazikitsidwa mu Piraiévs. Gawo lathu linayambira ku Piraiévs mpaka ku Eleusis, mtunda wa makilomita 50. Panthaŵi imeneyo, mumpingomu munali Akristu ambiri odzozedwa ndi mzimu. Ndinali ndi mwayi wogwira nawo ntchito limodzi ndi kumaphunzira kwa iwo. Ndinkasangalala kucheza nawo chifukwa anali ndi nkhani zambiri zosimba zimene anakumana nazo zosonyeza kulimbikira kumene kumafunika kuti tigwire ntchito yolalikira. Zimene anakumana nazo zinandithandiza kuona kuti kuleza mtima ndi kulimbikira kwambiri n’zofunika kuti titumikire Yehova mokhulupirika. (Machitidwe 14:22) Ndikusangalalatu kwambiri kuti lerolino m’dera limeneli muli mipingo ya Mboni za Yehova yoposa 50.

Mavuto Osayembekezeka

Patapita nthaŵi, ndinadziŵana ndi Eleni yemwe anali mtsikana wachikristu wabwino ndiponso wachangu mumzinda wa Patras. Tinapalana ubwenzi kumapeto kwa chaka cha 1952. Komabe, patangopita miyezi yochepa, Eleni anadwala kwambiri. Madokotala anapeza kuti iye anali ndi kansa ya mu ubongo, ndipo vuto lakelo linali lalikulu kwambiri. Anafunika kum’chita opaleshoni mwamsanga. Titayesetsa zolimba, tinapeza dokotala wina mu mzinda wa Athens amene anavomera kutsatira zikhulupiriro zathu zachipembedzo ndi kuchita opaleshoni yopanda magazi. Anatero ngakhale kuti panthaŵiyo panalibe njira zokwanira zochitira opaleshoni yotere. (Levitiko 17:10-14; Machitidwe 15:28, 29) Atachita opaleshoni, madokotalawo anali ndi chiyembekezo choti tsogolo la bwenzi langa likhala labwino koma sananene kuti matendawo sadzayambiranso.

Kodi mmene zinalilimu ndikanatani? Popeza kuti zinthu zinasintha, kodi ndikanathetsa ubwenzi wathu n’kusakhala ndi udindo uliwonse pa iye? Ayi! Pamene ndinangotomera ndiye kuti ndinalonjeza, ndipo ndinafuna kuti inde wanga akhale inde. (Mateyu 5:37) Sindinalole kuganiza zomusiya. Mkulu wa Eleni anasamalira m’ng’ono wakeyu ndipo anapezako bwino. Zitatero tinakwatirana mu December 1954.

Patapita zaka zitatu, matenda a Eleni anayambiranso ndipo anafika poipa kwambiri. Dokotala yemwe uja anachitanso opaleshoni ina. Panthaŵiyi, analoŵa kwambiri m’kati mwa ubongo kuti achotseretu kansayo. Zimenezi zinachititsa kuti mkazi wanga azerezeke pang’ono, ndipo mphamvu yolankhula inasokonezeka. Zitatero, tonsefe tsopano tinali ndi mavuto  atsopano ambirimbiri. Ngakhale ntchito yaing’onong’ono inali ngati chimtolo kwa mkazi wanga wokondedwa. Kuipiraipira kwa matenda ake kunachititsa kuti tisinthe kotheratu zochita zathu za tsiku ndi tsiku. Ndipo kuposa zonsezi, tinafunika kupirira ndi kulimbikira kwambiri.

Panthaŵi ino tsopano, zimene mayi anandiphunzitsa zinathandiza kwambiri. M’maŵa uliwonse ndinali kukonza zinthu zogwiritsa ntchito pokonza chakudya, ndipo Eleni ankaphika. Nthaŵi zambiri tinali kuitana alendo, kuphatikizapo atumiki a nthaŵi zonse, anthu amene tinali kuphunzira nawo Baibulo, ndi Akristu anzathu osoŵa a mumpingo wathu. Onseŵa anali kuyamikira kuti zakudyazo zinali zokoma kwambiri. Ine ndi Eleni tinalinso kugwirira limodzi ntchito zapanyumba, motero kuti nyumba yathu inali yaukhondo ndiponso yaudongo. Mavuto ameneŵa anapitiriza kwa zaka 30.

Changu Ngakhale Anali Kudwala

Zinkandilimbikitsa kwambiri ndiponso kulimbikitsa anthu ena kuona kuti zonsezi sizinabwezere m’mbuyo chikondi cha mkazi wanga kwa Yehova ndiponso changu chake muutumiki. Patapita nthaŵi, ndiponso atayesetsa kwambiri, Eleni ankatha kulankhula mawu ochepa chabe. Ankakonda kuwauza anthu mumsewu uthenga wabwino wa m’Baibulo. Popita kukachita bizinesi, ndinali kumutenga ndipo ndinkaimika galimoto m’mbali mwa msewu mmene munali kudutsa anthu ambiri. Iye ankatsegula zenera la galimoto n’kumauza anthu odutsa mumsewumo kuti alandire Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Tsiku lina anagaŵira magazini okwana 80 m’maola aŵiri. Nthaŵi zambiri, iye anali kugaŵira magazini onse akale amene anali kumpingo. Eleni analinso kuchita mitundu ina ya ulaliki nthaŵi zonse.

Kwa zaka zonse zimene mkazi wanga anali kudwala, anali kutsagana nane kumisonkhano nthaŵi zonse. Sanaphonyepo msonkhano wachigawo kapena wadera wina uliwonse, ngakhale panthaŵi imene tinkachitira misonkhanoyo ku mayiko ena chifukwa cha kuzunzidwa kwa Mboni za Yehova ku Greece. Ngakhale kuti sankatha kuchita zambiri, iye anakondwa kupezeka pamisonkhano yachigawo ku Austria, Germany, Cyprus, ndi mayiko ena. Eleni sankadandaula kapena kufuna kuti ndizimuchitira zambiri, ngakhale pamene kuwonjezeka kwa maudindo anga muutumiki wa Yehova nthaŵi zina kunkachititsa kuti zinthu zikhale zovuta kwa iye.

Mavuto ameneŵa anandiphunzitsa kukhala wopirira ndiponso wolimbikira kwa nthaŵi yaitali. Ndinaona Yehova akundithandiza nthaŵi zambiri. Abale ndi alongo anadzipereka zedi kutithandiza m’njira zosiyanasiyana, ndipo madokotala anatithandiza mwachifundo. M’zaka zonse za mavutozi, sitinasoŵepo zofunika kwambiri pa moyo ngakhale kuti sizikanatheka kuti ndigwire ntchito yokhazikika malinga ndi mavuto athuŵa. Nthaŵi zonse, kuchita zimene Yehova amafuna ndi kum’tumikira zinkakhala patsogolo.​—Mateyu 6:33.

Anthu ambiri akhala akutifunsa chimene chinatilimbitsa m’nthaŵi zonse zovutazi. Ndikamayang’ana m’mbuyo ndimaona kuti phunziro la Baibulo laumwini, kupemphera kwa  Mulungu kuchokera pansi pa mtima, kupezeka pa misonkhano yachikristu nthaŵi zonse, ndi kulalikira nawo mwachangu zinatithandiza kupirira ndi kulimbikira. Tinkakumbutsidwa nthaŵi zonse mawu olimbikitsa amene ali pa Salmo 37:3-5 akuti: “Khulupirira Yehova, ndipo chita chokoma; . . . Udzikondweretsenso mwa Yehova; . . . Pereka njira yako kwa Yehova; khulupiriranso Iye, adzachichita.” Vesi ina imene inatithandiza kwambiri ndi Salmo 55:22 imene imati: “Umsenze Yehova nkhawa zako, ndipo Iye adzakugwiriziza.” Monga mwana amene amadalira kotheratu bambo ake, tinali kutula nkhaŵa zathu kwa Yehova ndi kumusiyira.​—Yakobo 1:6.

Pa April 12, 1987, pamene mkazi wanga anali kulalikira kumaso kwa nyumba yathu, chitseko cholemera chachitsulo chimene chinali kutsekeka kumbuyo kwake chinam’menya ndi kum’gwetsera m’mbali mwa msewu n’kumuvulaza koopsa. Zitatero, anakhala ali chikomokere kwa zaka zitatu zotsatira. Anamwalira kumayambiriro a chaka cha 1990.

Kutumikira Yehova ndi Nzeru Zanga Zonse

Kale mu 1960, ndinasankhidwa kutumikira monga mtumiki wa mpingo ku Nikaia, Piraiévs. Kuyambira pamenepo, ndinakhala ndi mwayi wotumikira m’mipingo ina yambiri ku Piraiévs. Ngakhale kuti ndinalibe ana angaanga, ndinasangalala kuthandiza ana ambiri auzimu kukhala olimba m’choonadi. Ena mwa ameneŵa tsopano akutumikira monga akulu mumpingo, atumiki otumikira, apainiya, ndi a m’banja la Beteli.

Atabwezeretsa ulamuliro wa demokalase ku Greece mu 1975, Mboni za Yehova zinayamba kuchita misonkhano yachigawo momasuka, osabisalanso m’nkhalango. Luso limene ena a ife tinapeza pokonza misonkhano yachigawo ku mayiko ena linatithandiza kwambiri. Motero, ndinapeza chimwemwe ndiponso mwayi wotumikira m’makomiti osiyanasiyana a msonkhano wachigawo kwa zaka zambiri.

Kenaka, mu 1979, panali makonzedwe omanga Nyumba ya Msonkhano yoyamba ku Greece, kunja kwa mzinda wa Athens. Ndinauzidwa kuti ndithandize kulinganiza ndi kugwira ntchito yomanga yaikuluyi. Ntchitoyi inafunanso kupirira ndi kulimbikira kwambiri. Kugwira ntchito ndi abale ndi alongo mazanamazana odzipereka kwa zaka zitatu kunalimbikitsa chikondi chathu ndi kutigwirizanitsa kwambiri. Sindidzaiŵala zonse zimene zinandichitikira pantchito yomanga imeneyi.

Kukwaniritsa Zosoŵa Zauzimu za Akaidi

Patapita zaka zingapo, mwayi wina unanditsegukira. Pafupi ndi gawo la mpingo wathu, ku Korydallos, pali imodzi mwa ndende zazikulu kwambiri m’Greece. Anandisankha kuyendera ndendeyi mlungu uliwonse monga mtumiki wa Mboni za Yehova kuyambira mu April 1991. Kumeneko amandilola kuchititsa maphunziro a Baibulo ndi misonkhano yachikristu kwa akaidi amene ali ndi chidwi. Ambiri mwa akaidiwo asintha kwambiri, zimene zasonyeza kuti Mawu a Mulungu alidi ndi mphamvu yaikulu. (Ahebri 4:12) Zimenezi zachititsa chidwi oyang’anira ndendeyo pamodzi ndi akaidi ena. Ena mwa akaidi amene ndinali kuphunzira nawo Baibulo anawamasula ndipo panopa akufalitsa uthenga wabwino.

Nthaŵi ina ndinali kuphunzira ndi akaidi atatu odziŵika kwambiri chifukwa chozembetsa mankhwala osokoneza bongo. Pamene anali kupita patsogolo mwauzimu, ankafika ku phunziro lawo la Baibulo atameta bwino, atapesa bwino tsitsi lawo, ndiponso atavala shati ndi tayi m’kati mwa mwezi wa August womwe ndi umodzi mwa miyezi yotentha kwambiri ku Greece. Akuluakulu a ndendeyo pamodzi ndi ogwira ntchito ena anatuluka m’maofesi awo kudzaona zodabwitsazi. Sanathe kukhulupirira kuti akaidiwo anasinthadi motero.

Ku nyumba ya ndende ya azimayi kunachitikanso nkhani ina yolimbikitsa ngati imeneyi. Mkazi wina amene anapatsidwa chilango chokhala m’ndende kwa moyo wake wonse chifukwa cha kupha munthu, anayamba kuphunzira Baibulo. Mkaziyu anali woukira kwambiri. Komabe, pasanapite nthaŵi yaitali, choonadi cha Baibulo chimene anali kuphunzira chinam’sintha zedi moti anthu ambiri ananena  kuti mkaziyu anali ngati mkango umene unali kusintha kukhala nkhosa. (Yesaya 11:6, 7) Posakhalitsa, wamkulu wa ndendeyo anayamba kum’lemekeza ndi kum’khulupirira mkaziyu. Ndinasangalala kumuona akupita patsogolo kwambiri mpaka kufika podzipatulira kwa Yehova.

Kuthandiza Odwala ndi Okalamba

Kuona mmene mkazi wanga anavutikira ndi matenda kwa nthaŵi yaitali kwandichititsa kudera nkhaŵa kwambiri zosoŵa za anthu odwala ndi okalamba amene tili nawo. Nkhani iliyonse imene inatuluka m’zofalitsa zathu yotilimbikitsa kuthandiza mwachikondi anthu oterowo, inali kudzutsa chidwi changa. Ndinali kuyamikira kwambiri nkhani zimenezo ndipo ndinali kuzisonkhanitsa pamodzi. Patapita zaka zingapo, ndinasonkhanitsa faelo ya nkhani zimenezi ya masamba oposa 100, kuyamba ndi nkhani yakuti “Kuwaganizira Anthu Okalamba ndi Ovutika,” ya mu Nsanja ya Olonda yachingelezi ya July 15, 1962. Zambiri mwa nkhani zimenezi zinasonyeza kuti zingakhale bwino kuti mpingo uliwonse ukhale ndi makonzedwe othandiza anthu odwala ndi okalamba.​—1 Yohane 3:17, 18.

Akulu anakonza gulu la abale ndi alongo amene anadzipereka kusamalira odwala ndi okalamba mumpingo mwathu. Anthu odziperekawo tinawagaŵa m’timagulu tosiyanasiyana. Panali kagulu kothandiza masana, kena kothandiza usiku wonse, kena kothandiza pa za thiransipoti, ndiponso kena kothandiza usana ndi usiku. Kagulu komalizaka kanali kokonzeka kuthandiza nthaŵi ina iliyonse.

Zotsatira za ntchito imeneyi zakhala zolimbikitsa kwambiri. Mwachitsanzo, mlongo wina amene anali kudwala ndipo anali kukhala yekha, tinam’peza atakomoka paulendo wina wa tsiku ndi tsiku wom’chezera kunyumba kwake. Tinadziŵitsa mlongo wina amene anali kukhala pafupi yemwenso anali ndi galimoto. Anam’tengera mlongo wodwalayo kuchipatala m’nthaŵi yochepa zedi​—mphindi khumi zokha! Madokotala anati changu chimenecho chinapulumutsa moyo wa mlongoyo.

Kuyamikira kumene odwala ndi okalamba akusonyeza ku gululi n’kokhutiritsa kwambiri. N’kosangalatsa kwambiri kuyembekezera kudzakhala ndi abale ndi alongo ameneŵa m’dziko latsopano la Mulungu mmene matenda ndi ukalamba sizidzakhalako. Mphoto inanso ndiyo kudziŵa kuti anathandizidwa kupirira chifukwa cha thandizo limene analandira pamene anali kuvutika.

Kulimbikira Kwabweretsa Mphoto

Tsopano ndikutumikira monga mkulu mumpingo wina wa mu Piraiévs. Ngakhale kuti ndakalamba ndiponso ndikumadwaladwala, ndikusangalala kuti ndikuthabe kugwira nawo ntchito za mpingo.

Kwa zaka zonsezi, mavuto ndi zochitika zadzidzidzi zinafuna kupirira ndi kulimbikira kwambiri. Komabe, nthaŵi zonse Yehova wakhala akundipatsa mphamvu zimene ndinafunikira kuti ndithane ndi mavuto ameneŵa. Ndaona nthaŵi ndi nthaŵi kuti zimene wamasalmo ananena n’zoona. Iye anati: “Pamene ndinati, Litereka phazi langa, chifundo chanu, Mulungu, chinandichirikiza. Pondichulukira zolingalira zanga m’kati mwanga, zotonthoza zanu zikondweretsa moyo wanga.”​—Salmo 94:18, 19.

[Chithunzi patsamba 25]

Ndili ndi mkazi wanga, Eleni, atamuchita opaleshoni yachiŵiri mu 1957

[Chithunzi patsamba 26]

Pa msonkhano wachigawo ku Nuremberg, Germany, mu 1969

[Chithunzi patsamba 28]

Gulu la abale ndi alongo amene anali kuthandiza odwala ndi okalamba