Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Tenganipo Phunziro pa Zomwe Nikodemo Anachita

Tenganipo Phunziro pa Zomwe Nikodemo Anachita

 Tenganipo Phunziro pa Zomwe Nikodemo Anachita

“NGATI munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikanize yekha, nanyamule mtengo wozunzirapo wake tsiku ndi tsiku, nanditsate Ine.” (Luka 9:23, NW) Asodzi a nsomba odzichepetsa ndi wokhometsa msonkho wonyozedwa analabadira mosanyinyirika pempho limenelo. Anasiya zonse, n’kutsata Yesu.​—Mateyu 4:18-22; Luka 5:27, 28.

Pempho la Yesu likugwirabe ntchito lerolino ndipo ambiri alabadira. Komabe, anthu ena amene amasangalala kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova amazengereza ‘kudzikana okha, ndi kunyamula mtengo wawo wozunzirapo.’ Amachita mphwayi kusenza udindo ndiponso mwayi wamtengo wapatali wokhala ophunzira a Yesu.

N’chifukwa chiyani ena amazengereza kulabadira pempho la Yesu ndi kudzipatulira okha kwa Yehova Mulungu? Kunena zoona, amene sanakulire m’chiphunzitso chozikidwa pa chikhulupiriro cha  Chiyuda ndiponso cha Chikristu chakuti kuli Mulungu mmodzi yekha, angafunike nthaŵi yaitali ndithu kuti afike pozindikira kuti Mlengi weniweni Wamphamvuyonse alikodi. Komabe, ngakhale atatsimikiza kuti Mulungu ndi weniweni, ena safunabe kutsatira mapazi a Yesu. Iwo angachite mantha kuti achibale awo ndiponso anzawo adzayamba kuwaseka ngati atakhala a Mboni za Yehova. Ena amene sazindikira kufulumira kwa nthaŵi yomwe tikukhalayi, amayamba kufunafuna kutchuka ndi chuma. (Mateyu 24:36-42; 1 Timoteo 6:9, 10) Mulimonse mmene zingakhalire, anthu amene akuzengerezabe kusankha kukhala otsatira a Yesu, angatengepo phunziro pa nkhani ya Nikodemo, yemwe anali wolamulira wachiyuda wolemera kwambiri m’nthaŵi ya Yesu.

Kupatsidwa Mwayi Wabwino Kwambiri

Patangotha miyezi isanu ndi umodzi Yesu atayamba utumiki wake wapadziko lapansi, Nikodemo akuzindikira kuti Yesu ‘ndi mphunzitsi wochokera kwa Mulungu.’ Atachita chidwi ndi zozizwitsa zomwe Yesu wangochita kumene mu Yerusalemu pa Paskha wa mu 30 C.E., Nikodemo akudza kwa Yesu usiku kukamuuza kuti akumukhulupirira ndiponso kukaphunzira zambiri zokhudza ziphunzitso zake. Atatero, Yesu akuuza Nikodemo choonadi chozama chokhudza kufunika koti ‘abadwenso’ kuti akaloŵe mu Ufumu wa Mulungu. Panthaŵiyi, Yesu akunenanso mawu awa: “Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.”​—Yohane 3:1-16.

Nikodemo alitu ndi mwayi woyembekezera zinthu zabwino kwambiri m’tsogolo. Ali ndi mwayi wokhala mnzake wapamtima wa Yesu, akumachitira umboni woona ndi maso mbali zosiyanasiyana za moyo wa Yesu padziko lapansi. Nikodemo monga wolamulira wa Ayuda  ndiponso mphunzitsi mu Israyeli, akudziŵa zambiri zokhudza Mawu a Mulungu. Alinso ndi luntha monga momwe taonera kuti wazindikira Yesu kuti ali mphunzitsi wotumidwa ndi Mulungu. Nikodemo ali ndi chidwi kwambiri ndi nkhani zauzimu, ndipo wadzichepetsa kwambiri kusiyana ndi masiku onse. N’zovutadi kwambiri kuti membala wa bwalo lalikulu lamilandu la Ayuda avomereze mwana wa kalipentala wamba kuti ali wotumidwa ndi Mulungu. Makhalidwe onseŵa ali ofunika kwambiri kwa munthu kuti akhale wophunzira wa Yesu.

Chidwi cha Nikodemo mwamuna wa ku Nazarete ameneyu, chikuoneka kuti sichikuchepa. Patapita zaka ziŵiri ndi theka, pa Madyerero a Misasa, Nikodemo akuchita nawo msonkhano wa bwalo lalikulu la Ayuda la Sanihedirini. Panthaŵiyi, Nikodemo akadali “m’modzi wa iwo.” Akulu ansembe ndi Afarisi akutumiza anyamata kuti akam’gwire Yesu. Anyamatawo akubwerako ndi kunena kuti: “Nthaŵi yonse palibe munthu analankhula chotero.” Afarisi akuyamba kuwanyodola anyamatawo nati: “Kodi mwasokeretsedwa inunso? Kodi wina wa akulu anakhulupirira Iye, kapena wa Afarisi? Koma khamu ili losadziŵa chilamulo, likhala lotembereredwa.” Nikodemo akulephera kuugwira mtima ndipo akulankhula kuti: “Kodi chilamulo chathu chiweruza munthu, osayamba kumva iye, ndi kuzindikira chimene achita?” Atanena zimenezi, Afarisi ena akum’tsutsa amvekere: “Kodi iwenso uli wotuluka m’Galileya? Santhula, nuone kuti m’Galileya sanauka mneneri.”​—Yohane 7:1, 10, 32, 45-52.

Kenako patapita miyezi isanu ndi umodzi, pa Tsiku la Paskha wa 33 C.E., Nikodemo akuona mtembo wa Yesu akuutsitsa pa mtengo wozunzirapo. Iye akuthandiza Yosefe wa ku Arimateya yemwenso ali mmodzi wa mamembala a Sanihedirini, pokonza thupi la Yesu kuti akaliike m’manda. Kuti athe kukonza thupilo, Nikodemo akubweretsa “chisanganizo cha mure ndi aloe” chandalama pafupifupi mapaundi 100 a ku Roma, zomwe ndi ndalama zofanana ndi mapaundi 72 a ku England. Ndalama zambiri zedi. Iye anafunikanso kulimba mtima kukumana ndi zomwe Afarisi anzake angam’chitire akamudziŵa kuti akuyanjana ndi “wonyenga” monga momwe Afarisiwo amam’tchulira Yesu. Atakonza thupi la Yesu mofulumira, aŵiriwo akuika Yesu m’manda atsopano chapafupi pomwepo. Komabe, ngakhale panthaŵi imeneyi,  Nikodemo sakudziŵikabe monga wophunzira wa Yesu.​—Yohane 19:38-42; Mateyu 27:63; Marko 15:43.

Chifukwa Chomwe Sanachitirepo Kanthu

Yohane m’nkhani yake sanaulule chifukwa chomwe Nikodemo anazengerezera ‘kunyamula mtengo wake wozunzirapo’ ndi kumutsata Yesu. Komabe, anatchula mbali zina zomwe zingavumbule zomwe zinachititsa kuti Mfarisi ameneyu zimuvute kusankha zochita.

Choyamba, Yohane ananena kuti wolamulira wa Ayuda ameneyu “anadza kwa Yesu usiku.” (Yohane 3:2) Katswiri wina wamaphunziro a Baibulo ananena kuti, “Nikodemo anadza kwa Yesu usiku osati chifukwa cha mantha koma ankafuna kupeŵa khamu la anthu lomwe likanasokoneza zokambirana zake ndi Yesu.” Komabe, Yohane anali kunena za Nikodemo pamene anatchula za mwamuna “amene anadza kwa [Yesu] usiku poyamba paja,” komanso m’nkhani yomweyo anatchula za Yosefe wa ku Arimateya monga “wophunzira wa Yesu, koma mobisika, chifukwa cha kuopa Ayuda.” (Yohane 19:38, 39) Choncho, zikuoneka kuti Nikodemo anapita kwa Yesu usiku chifukwa ‘choopa Ayuda,’ monga momwe anthu enanso a m’nthaŵi yake ankaopera kuchita chilichonse chokhudzana ndi Yesu.​—Yohane 7:13.

Kodi mwazengereza kusankha kukhala wophunzira wa Yesu chifukwa choganizira zomwe achibale, mabwenzi, kapena anzanu anganene? Mwambi wina umati: “Kuopa anthu kutchera msampha.” Kodi mungathane nawo bwanji mantha amenewo? Mwambiwo umapitiriza kuti: “Koma wokhulupirira Yehova adzapulumuka.” (Miyambo 29:25) Kuti mukulitse chikhulupiriro chimenechi mwa Yehova mufunika kuona nokha kuti Mulungu adzakuthandizani pamene muli m’mavuto. Pempherani kwa Yehova ndipo m’pempheni kuti akulimbitseni mtima kusankha zochita pankhani ya kulambira kwanu ngakhale zitakhala zazing’ono. Pang’ono ndi pang’ono, chikhulupiriro chanu mwa Yehova chidzakula mpaka poti muzidzatha kusankha zinthu zikuluzikulu mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu.

Udindo wa Nikodemo ndiponso kutchuka kwake monga wolamulira mwina n’kumenenso kunam’lepheretsa kudzikana yekha, chinthu chomwe chinali chofunika kwambiri. Panthaŵiyo, ayenera kuti anali kukondabe kwambiri udindo wake monga membala wa Sanihedirini. Kodi mumazengereza kuchitapo kanthu kuti mukhale wotsatira wa Kristu chifukwa choopa kutaya udindo wanu wapamwamba kapena kutaya mwayi winawake woti mukanatukuka? Palibe n’chimodzi chomwe mwa zimenezi chimene tingachiyerekezere ndi ulemu wapadera wotumikira Wam’mwambamwamba wa chilengedwe chonse, amene ali wofunitsitsa kukwaniritsa zomwe mungam’pemphe mogwirizana ndi chifuniro chake.​—Salmo 10:17; 83:18; 145:18.

Chifukwa china chomwe Nikodemo anazengerezera chiyenera kuti chinali chuma chomwe anali nacho. Monga Mfarisi, iye ayenera kuti ankasonkhezeredwa ndi ena amene anali “okonda ndalama.” (Luka 16:14) Chokhacho choti anakwanitsa kugula msanganizo wa mure ndi aloe wokwera mtengo ndi umboni wakuti analidi wachuma. Ena masiku ano akuzengerezabe kusenza maudindo a Mkristu chifukwa chodera nkhaŵa chuma chomwe ali nacho. Komabe, Yesu analangiza otsatira ake kuti: “Musadere nkhaŵa moyo wanu, chimene mudzadya ndi chimene mudzamwa; kapena thupi lanu, chimene mudzavala. . . . Pakuti Atate wanu wa Kumwamba adziŵa kuti musoŵa zonse zimenezo. Koma muthange mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzawonjezedwa kwa inu.”​—Mateyu 6:25-33.

Anataya Mwayi Waukulu

N’zochititsa chidwi kuti nkhani ya Nikodemo yomwe imapezeka mu Uthenga Wabwino wa Yohane wokha, siitchula ngati iye anakhala wotsatira wa Yesu kapena ayi. Malinga ndi nthano ina, Nikodemo akuti anakhala wotsatira wa Yesu, anabatizidwa, anazunzidwa ndi Ayuda, anachotsedwa pa udindo wake, ndipo pomaliza anathamangitsidwa ku Yerusalemu. Mulimonse mmene zinalili, chodziŵika n’chakuti: Mwa  kuzengereza kutsatira Yesu akadali padziko lapansi, iye anataya mwayi waukulu.

Nikodemo akanayamba kutsatira Yesu panthaŵi yoyamba yomwe anakumana naye, ndiye kuti akanakhala wophunzira wapamtima wa Yesu. Akanakhala wophunzira wapadera kwambiri chifukwa anali kudziŵa zambiri, anali ndi luntha, anali wodzichepetsa, ndiponso anali kuzindikira zosoŵa zake zauzimu. Inde, akanamva zinthu zochititsa chidwi zomwe Mphunzitsi Wamkulu ankalankhula, akanaphunzira zinthu zofunika kwambiri m’mafanizo a Yesu, akanaona ndi maso ake zozizwitsa zomwe Yesu anachita, ndiponso akanapeza mphamvu kuchokera ku malangizo otsazikirana omwe Yesu anapatsa atumwi ake. Koma ayi ndithu, anataya mwayi wa zonsezi.

Kuzengereza kwa Nikodemo kunamutayitsa zambiri. Mwayi winanso womwe anataya unali pempho la Yesu lakuti: “Idzani kuno kwa Ine nonsenu akulema ndi akuthodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu. Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa Ine; chifukwa ndili wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. Pakuti goli langa lili lofewa, ndi katundu wanga ali wopepuka.” (Mateyu 11:28-30) Nikodemo anataya mwayi wopeza mpumulo umenewu kuchokera kwa Yesu m’lingaliro lenileni.

Nanga Bwanji Inuyo?

Kuyambira mu 1914, Yesu Kristu wakhala ali kumwamba monga Mfumu ya Ufumu wakumwamba wa Mulungu. Polosera zomwe zidzachitike m’nthaŵi ya kukhalapo kwake, mwa zina, iye anati: “Uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.” (Mateyu 24:14) Chimaliziro chisanafike, ntchito yolalikira padziko lonse iyenera kukwaniritsidwa. Yesu Kristu amakondwera kuti anthu opanda ungwiro akugwira nawo ntchito imeneyi. Inunso mutha kugwira nawo ntchitoyi.

Nikodemo anazindikira kuti Yesu anachokera kwa Mulungu. (Yohane 3:2) Chifukwa cha kuphunzira kwanu Baibulo mwina inunso mwazindikira zimenezi. Mwina mwasintha zina ndi zina pa moyo wanu kuti mugwirizane ndi mfundo za chikhalidwe za m’Baibulo. Mwina mumafika pamisonkhano ya Mboni za Yehova kuti muphunzire zambiri kuchokera m’Baibulo. Mukuchita bwino kwambiri. Komabe, Nikodemo anafunika kuchita zambiri osati kungozindikira kokha kuti Yesu anatumidwa ndi Mulungu. Anafunika ‘kudzikana yekha, ndi kunyamula mtengo wozunzirapo wake tsiku ndi tsiku, ndi kumutsata Yesu.’​—Luka 9:23, NW.

Mverani zomwe mtumwi Paulo akutiuza. Iye analemba kuti: “Ndipo ochita naye pamodzi tidandauliranso kuti musalandire chisomo cha Mulungu kwachabe inu, (pakuti anena, M’nyengo yolandiridwa ndinamva iwe, Ndipo m’tsiku la chipulumutso ndinakuthandiza; taonani, tsopano ndiyo nyengo yabwino yolandiridwa, taonani, tsopano ndilo tsiku la chipulumutso).”​—2 Akorinto 6:1, 2.

Tsopano ndiyo nthaŵi yokulitsa chikhulupiriro chomwe chingakulimbikitseni kuchitapo kanthu. Kuti muchite zimenezi, sinkhasinkhani zomwe mukuphunzira m’Baibulo. Pempherani kwa Yehova, ndipo m’pempheni kuti akuthandizeni kusonyeza chikhulupiriro choterocho. Pamene mukulandira chithandizo chake, kuyamikira kwanu ndiponso chikondi chanu kwa iye, zidzakulimbikitsani kufunitsitsa ‘kudzikana nokha, ndi kunyamula mtengo wanu wozunzirapo tsiku ndi tsiku, ndi kumutsata Yesu Kristu nthaŵi zonse.’ Kodi muchitapo kanthu tsopano?

[Chithunzi patsamba 9]

Poyamba, Nikodemo anaikira kumbuyo Yesu molimba mtima

[Chithunzi patsamba 9]

Ngakhale Nikodemo ankatsutsidwa, iye anathandiza kukonza mtembo wa Yesu kuti akauike m’manda

[Chithunzi patsamba 10]

Phunziro laumwini ndiponso pemphero zingakulimbikitseni kuchitapo kanthu

[Chithunzi patsamba 10]

Kodi mudzavomereza mwayi wogwira ntchito motsogozedwa ndi Yesu Kristu?