Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Phindu la Uthenga Wabwino

Phindu la Uthenga Wabwino

 Phindu la Uthenga Wabwino

“Yehova wandidzoza ine ndilalikire mawu abwino kwa ofatsa; Iye wanditumiza ndikamange osweka mtima; . . . ndikatonthoze mtima wa onse amene akulira maliro.”​—YESAYA 61:​1, 2.

1, 2. (a) Kodi Yesu anadziulula kuti anali yani, ndipo anachita motani zimenezo? (b) Kodi uthenga wabwino umene Yesu analengeza unali ndi phindu lotani?

YESU anali mu Sunagoge ku Nazarete tsiku lina la Sabata kuchiyambi kwa utumiki wake. Malinga ndi nkhaniyo, “anapereka kwa Iye buku la Yesaya mneneri. Ndipo mmene Iye adafunyulula bukulo, anapeza pomwe panalembedwa, Mzimu wa Ambuye uli pa Ine, chifukwa chake Iye anandidzoza Ine ndiuze anthu . . . Uthenga Wabwino.” Yesu anapitiriza kuŵerenga ndime ya ulosiyo. Kenako anakhala pansi n’kunena kuti: “Lero lembo ili lakwanitsidwa m’makutu anu.”​—Luka 4:​16-21.

2 Yesu mwa kuchita zimenezi, anadziulula kuti anali mlaliki woloseredwayo, wolengeza uthenga wabwino ndiponso wotonthoza. (Mateyu 4:23) Ndipotu uthenga umene Yesu analengeza unalidi uthenga wabwino. Iye anawauza omvera ake kuti: “Ine ndine kuunika kwa dziko lapansi; iye wonditsata Ine sadzayenda mumdima, koma adzakhala nako kuunika kwa moyo.” (Yohane 8:12) Iye ananenanso kuti: “Ngati mukhala inu m’mawu anga, muli akuphunzira anga ndithu; ndipo mudzazindikira choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani.” (Yohane 8:​31, 32) Inde, Yesu anali ndi “mawu a moyo wosatha.” (Yohane 6:​68, 69) Mosakayika, kuwala, moyo, ndiponso ufulu ndi zinthu zabwino kwambiri zofunika kuziyamikira.

3. Kodi ophunzira a Yesu analalikira uthenga wabwino wotani?

3 Pentekoste wa 33 C.E. atatha, ophunzira anapitiriza ntchito ya Yesu yolalikira. Analalikira ‘uthenga wabwino wa Ufumu’ kwa Aisrayeli  ndiponso kwa anthu a mitundu ina. (Mateyu 24:14; Machitidwe 15:7; Aroma 1:16) Amene anamvera uthengawo anam’dziŵa Yehova Mulungu. Anamasuka ku ukapolo wa chipembedzo ndipo anakhala mbali ya m’mtundu watsopano wauzimu, “Israyeli wa Mulungu,” anthu amene akuyembekeza kukalamulira kosatha kumwamba pamodzi ndi Mbuye wawo, Yesu Kristu. (Agalatiya 5:1; 6:16; Aefeso 3:​5-7; Akolose 1:​4, 5; Chivumbulutso 22:5) Linali phindu lalikulutu limenelo!

Kulalikira Lerolino

4. Kodi ntchito yolalikira uthenga wabwino ikukwaniritsidwa motani lerolino?

4 Lerolino, Akristu odzozedwa mothandizidwa ndi “khamu lalikulu” la “nkhosa zina,” akupitiriza kukwaniritsa ntchito yoloseredwayo imene inapatsidwa kwa Yesu poyambirira. (Chivumbulutso 7:9; Yohane 10:16) Zotsatira zake n’zakuti uthenga wabwino ukulalikidwa pa mlingo waukulu kuposa kale lonse. Mboni za Yehova m’mayiko ndi m’madera okwana 235 ‘zalalikira mawu abwino kwa ofatsa; kumanga osweka mtima; kulalikira kwa am’nsinga mamasulidwe, ndi kwa omangidwa kutsegulidwa kwa m’ndende; kulalikira chaka chokomera Yehova, ndi tsiku lakubwezera la Mulungu wathu; kutonthoza mtima wa onse amene akulira maliro.’ (Yesaya 61:​1, 2) Motero, ntchito yachikristu yolalikira ikupitiriza kupindulitsa anthu ambiri ndi kupereka chitonthozo chenicheni kwa “iwo okhala m’nsautso iliyonse.”​—2 Akorinto 1:​3, 4.

5. Kodi Mboni za Yehova n’zosiyana motani ndi Matchalitchi Achikristu pankhani ya kulalikira uthenga wabwino?

5 N’zoona kuti Matchalitchi Achikristu amalimbikitsa njira zina zolalikira. Ena amatumiza amishonale kukatembenuza anthu m’mayiko ena. Mwachitsanzo, magazini ya The Orthodox Christian Mission Center Magazine inasimba zimene amishonale a tchalitchi cha Orthodox anachita ku Madagascar, kumwera kwa Africa, ku Tanzania, ndi ku Zimbabwe. Komabe, m’tchalitchi cha Orthodox, monganso mmene zilili m’matchalitchi ena Achikristu, anthu ena onse salalikira nawo. Mosiyana ndi amenewo, Mboni za Yehova zonse zodzipatulira zimayesetsa kulalikira. Zimadziŵa kuti kulengeza uthenga wabwino kumasonyeza kuti chikhulupiriro chawo ndi chenicheni. Paulo anati: “Ndi mtima munthu akhulupira kutengapo chilungamo; ndi mkamwa avomereza kutengapo chipulumutso.” Ndipotu, chikhulupiriro chimene sichilimbikitsa munthu kuchitapo kanthu, n’chakufa.​—Aroma 10:10; Yakobo 2:17.

Uthenga Wabwino Umene Umabweretsa Phindu Losatha

6. Kodi ndi uthenga wabwino wotani umene ukulalikidwa lerolino?

6 Mboni za Yehova zimalalikira uthenga wabwino kuposa wina uliwonse. Zimatsegula mabaibulo awo ndi kusonyeza anthu omvera kuti Yesu anapereka nsembe moyo wake kuti apatse anthu njira yom’fikira Mulungu, kuwakhululukira machimo awo ndi kuyembekeza kudzakhala ndi moyo wosatha. (Yohane 3:16; 2 Akorinto 5:​18, 19) Zimalengeza kuti Ufumu wa Mulungu unakhazikitsidwa kumwamba m’manja mwa Mfumu yodzozedwa, Yesu Kristu, ndipo kuti posachedwapa udzachotsa kuipa pa dziko lapansi ndi kuyang’anira kubwezeretsedwa kwa Paradaiso. (Chivumbulutso 11:15; 21:​3, 4) Izo pokwaniritsa ulosi wa Yesaya, zimauza anansi awo kuti tsopano ndi “chaka chokomera Yehova” pamene mwayi udakalipo woti anthu alabadire uthenga wabwino. Izo zimachenjezanso kuti posachedwapa lifika “tsiku lakubwezera la Mulungu wathu” pamene Yehova adzawononga ochita zoipa onse amene sakulapa.​—Salmo 37:​9-11.

7. Kodi ndi chochitika chiti chimene chikusonyeza kugwirizana kwa Mboni za Yehova, ndipo n’chifukwa chiyani izo n’zogwirizana motero?

7 Umenewu ndi uthenga wabwino wokhawo umene uli ndi phindu losatha makamaka m’dziko lino limene ladzala ndi mavuto ndi matsoka. Amene amavomera uthengawu amakhala nawo m’gulu la abale achikristu ogwirizana a padziko lonse amene salola kuti kusiyana kwa dziko limene akuchokera, fuko lawo ndi chuma chawo ziwagawanitse. Iwo ‘ali nacho chikondi, popeza kuti ndicho chomangira cha mtima wamphumphu.’ (Akolose 3:14; Yohane 15:12) Zimenezi n’zimene zinachitika chaka chatha m’dziko lina la mu Africa. Tsiku lina m’maŵa, kuomba mfuti kosalekeza kunadzidzimutsa anthu mu mzinda waukulu wa m’dzikolo. Gulu lina linkafuna kulanda boma. Pamene zinthu zinasintha n’kuyamba kumenyana kwa mafuko osiyana, banja lina la Mboni analidzudzula  chifukwa chosunga Mboni zinzawo zimene zinali za fuko lina. Banjalo linayankha kuti: “Mboni za Yehova zokha ndizotu zimene zikukhala m’nyumba yathu.” Kusiyana mafuko kunali kosafunika kwa iwo. Chomwe chinali chofunika kwa iwo chinali chikondi​—kutonthoza amene anafunikira chitonthozo. Wachibale wina wa banjalo yemwe si Mboni anati: “Anthu a m’zipembedzo zina zonse anali kupereka olambira anzawo kwa adani. Mboni za Yehova zokha ndi zimene sizinachite zimenezi.” Nkhani zambiri zosimba zochitika zofanana ndi zimenezi zochokera m’mayiko amene asakazika ndi nkhondo zachiweniweni zikusonyeza kuti Mboni za Yehova ‘zimakondadi abale.’​—1 Petro 2:17.

Uthenga Wabwino Umasintha Anthu

8, 9. (a) Kodi ndi kusintha kotani kumene anthu amene amalandira uthenga wabwino amapanga? (b) Kodi ndi zochitika ziti zimene zikusonyeza mphamvu ya uthenga wabwino?

8 Uthenga wabwino umapindulitsa ‘m’moyo uno ndi m’moyo ulinkudza’ monga mmene Paulo ananenera. (1 Timoteo 4:8) Umapereka chiyembekezo chabwino ndi chotsimikizika cha m’tsogolo ndiponso umathandiza kuti “moyo uno” ukhale wabwinopo. Munthu aliyense payekha yemwe ndi Mboni ya Yehova, amatsogozedwa ndi Mawu a Mulungu, Baibulo, kuti atsatire zimene Mulungu amafuna. (Salmo 119:101) Mtima wake umakhala watsopano pamene akukulitsa makhalidwe monga chilungamo ndi kukhulupirika.​—Aefeso 4:24.

9 Taganizirani chitsanzo cha Franco. Iye anali ndi vuto la kupsa mtima. Chinachake chikalakwika, iye ankapsa mtima mwachiwawa ndipo akatero ankaphwanya zinthu. Mkazi wake anaphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, ndipo pang’ono n’pang’ono chitsanzo chawo chachikristu chinathandiza Franco kuona kuti anafunika kusintha. Anaphunzira Baibulo ndi Mbonizo ndipo kenako anatha kuonetsa zipatso za mzimu woyera zomwe ndi mtendere ndiponso chiletso. (Agalatiya 5:​22, 23) Iye anali mmodzi mwa anthu okwana 492 amene anabatizidwa ku Belgium m’chaka chautumiki cha 2001. Taganizaninso za Alejandro. Mnyamata ameneyu anali wokonda mankhwala osokoneza bongo moti khalidwe lake linaipiratu mpaka kufika poti ankadalira kutoleza zinthu zabwinopo zimene zinatayidwa kudzala n’kumagulitsa kuti agulire mankhwala osokoneza bongo. Pamene Alejandro anali ndi zaka 22, Mboni za Yehova zinam’pempha kuphunzira naye Baibulo ndipo anavomera. Ankaŵerenga Baibulo tsiku ndi tsiku ndipo anali kupita ku misonkhano yachikristu. Anasiya khalidwe lake loipalo mwamsanga moti anayamba kulalikira nawo isanathe miyezi isanu ndi umodzi. Iye anali mmodzi mwa anthu 10,115 amene anachita ntchito imeneyi ku Panama chaka chatha.

Uthenga Wabwino Umapindulitsa Anthu Ofatsa

10. Kodi ndani amene amamvera uthenga wabwino, ndipo maganizo awo amasintha bwanji?

10 Yesaya analosera kuti uthenga wabwino  udzalalikidwa kwa anthu ofatsa. Kodi anthu ofatsa ameneŵa ndani? Ndi anthu amene buku la Machitidwe limawafotokoza kuti ndi amene “anaikidwiratu ku moyo wosatha.” (Machitidwe 13:48) Ameneŵa ndi anthu odzichepetsa amene amapezeka m’magulu onse a anthu amene amamvera uthenga wa choonadi. Anthu oterowo amaphunzira kuti kuchita zimene Mulungu amafuna kumapindulitsa kwambiri kuposa china chilichonse chimene anthu m’dziko angapereke. (1 Yohane 2:​15-17) Koma kodi Mboni za Yehova zimawafika anthu pamtima motani zikamalalikira?

11. Malinga ndi zimene Paulo ananena, kodi uthenga wabwino uyenera kulalikidwa motani?

11 Eya, talingalirani chitsanzo cha mtumwi Paulo amene analembera Akorinto kuti: “Ine, abale, mmene ndinadza kwa inu, sindinadza ndi kuposa kwa mawu, kapena kwa nzeru, polalikira kwa inu chinsinsi cha Mulungu. Pakuti ndinatsimikiza mtima kuti ndisadziŵe kanthu mwa inu, koma Yesu Kristu, ndi Iye wopachikidwa.” (1 Akorinto 2:​1, 2) Paulo sanafune kuwachititsa chidwi anthu amene anali kumumvera ndi maphunziro ake. Anaphunzitsa mfundo zotsimikizika za Mulungu zokha basi, mfundo zimene lerolino zili m’Baibulo. Onaninso zimene Paulo anamulimbikitsa mlaliki mnzake, Timoteo. Anati: “Lalikira mawu; chita nawo pa nthaŵi yake.” (2 Timoteo 4:2) Timoteo anafunika kulalikira “mawu,” uthenga wa Mulungu. Paulo analemberanso Timoteo kuti: “Uchite changu kudzionetsera kwa Mulungu wovomerezeka, wantchito wopanda chifukwa cha kuchita manyazi, wolunjika nawo bwino mawu a choonadi.”​—2 Timoteo 2:15.

12. Kodi Mboni za Yehova lerolino zimamvera motani zimene Paulo ananena ndi kutsatira chitsanzo chake?

12 Mboni za Yehova zimatsatira chitsanzo cha Paulo ndiponso kumvera zimene iye anauza Timoteo. Zimazindikira mphamvu ya Mawu a Mulungu ndipo zimaigwiritsa bwino ntchito pamene zikufuna kuuza anansi awo mawu oyenerera opatsa chiyembekezo ndiponso otonthoza. (Salmo 119:52; 2 Timoteo 3:​16, 17; Ahebri 4:12) N’zoona kuti zimagwiritsa ntchito mabuku ophunzirira Baibulo kuti anthu a chidwi adziŵe zambiri za m’Baibulo panthaŵi imene ali ndi mpata wokwanira. Komabe izo nthaŵi zonse zimayesetsa kuwasonyeza anthu mawu a m’Malemba. Zimadziŵa kuti Mawu amene Mulungu anawauzira adzakhudza mitima ya anthu odzichepetsa. Ndipo kugwiritsa ntchito Mawu a Mulungu mwa njira imeneyi kumalimbitsanso chikhulupiriro chawo.

‘Kutonthoza Mtima wa Onse Amene Akulira Maliro’

13. Kodi ndi zinthu zotani zimene zinachitika mu 2001 zimene zinachititsa kuti kutonthoza mtima wa onse akulira maliro kufunike kwambiri?

13 M’chaka cha 2001 munachitikanso masoka, ndipo motero anthu ambiri anafuna kutonthozedwa. Mu September chaka chimenechi, ku United States kunachitika chitsanzo chachikulu cha masoka pamene zigaŵenga zinaphulitsa likulu la zamalonda padziko lonse la World Trade Center ku New York ndiponso likulu la asilikali a dzikolo la Pentagon kufupi ndi ku Washington, D.C. Kuphulitsa kumenekutu kunathetsa nzeru anthu m’dziko lonselo. Poona zimenezi, Mboni za Yehova zikuyesetsa kukwaniritsa ntchito yawo ‘yotonthoza mtima wa onse amene akulira maliro.’ Zochitika zochepa chabe zotsatirazi zisonyeza mmene Mboni za Yehova zikuchitira zimenezi.

14, 15. Kodi Mboni zinatha bwanji kugwiritsa ntchito malemba mogwira mtima potonthoza anthu olira maliro pa zochitika zosiyana ziŵiri?

14 Mboni ina yomwe ndi mlaliki wa nthaŵi zonse inalankhula ndi mkazi wina m’mbali mwa msewu n’kum’funsa mmene ankaganizira za kuukira kwa zigaŵenga kumene kunali kutangochitika kumene. Mkaziyo anayamba kulira. Iye anati anali ndi chisoni chachikulu ndipo akanakonda akanathandizapo mwa njira inayake. Mboniyo inamuuza mkaziyo kuti Mulungu amatiganizira tonsefe, ndipo inaŵerenga Yesaya 61:​1, 2. Mawu a Mulungu ouziridwa ameneŵa anamugwira mtima mkaziyo, amene ananena kuti aliyense anali kulira. Analandira trakiti ndipo anapempha Mboniyo kuti idzamuchezere kunyumba kwake.

15 Mboni ziŵiri zimene zinali kulalikira zinakumana ndi mwamuna wina amene anali kugwira ntchito kuseri kwa nyumba yake. Zinam’pempha kuti zimuonetse mawu otonthoza a m’Malemba poganizira tsoka limene linangochitika kumene pa likulu la zamalonda la padziko lonse la World Trade Center. Atavomera, Mbonizo zinaŵerenga 2 Akorinto 1:​3-7, pamene mawu ake ena amati: “Chitonthozo . . . chichuluka mwa Kristu.”  Mwamunayo anathokoza kwambiri kuti anansi ake a Mboni anali kuuza anthu ena mawu otonthoza ndipo anati: “Mulungu adalitse ntchito yabwino kwambiri imene mukuchita.”

16, 17. Kodi ndi zochitika ziŵiri ziti zimene zinasonyeza kuti Baibulo lili ndi mphamvu yothandiza anthu amene akumva chisoni kapena kuvutika maganizo chifukwa cha masoka?

16 Mboni ina pobwerera kwa anthu amene anasonyeza chidwi inakumana ndi mwamuna yemwe anali mwana wa mayi wina amene anasonyeza chidwi m’mbuyomo. Mboniyo inafotokoza kuti inafuna kudziŵa kuti anansi awo ali bwanji pambuyo pa tsoka limene linali litangochitika kumenelo. Mwamunayo anadabwa kuti Mboniyo inapatula nthaŵi yake kuchezera anthu ndi kuwaona kuti ali bwanji. Iye ananena kuti anali kugwira ntchito pafupi ndi likulu la zamalonda padziko lonse pamene zigaŵengazi zinkaukira ndipo anaona zonse zimene zinachitika. Atafunsa chifukwa chake Mulungu amalola anthu kuvutika, Mboniyo inaŵerenga mavesi a m’Baibulo, kuphatikizapo Salmo 37:39 limene limati: “Chipulumutso cha olungama chidzera kwa Yehova, Iye ndiye mphamvu yawo m’nyengo ya nsautso.” Mwamunayo anafunsa mokoma mtima mmene Mboniyo ndi banja lake analili ndipo anaipempha kuti idzabwerenso. Anayamikiranso ndi mtima wonse kubwera kwa Mboniyo.

17 Wina mwa anthu zikwizikwi olira maliro amene Mboni za Yehova zinawatonthoza pambuyo pa kuukira kwa zigaŵenga anali mkazi wina amene Mbonizo zinakumana naye pamene zinali kuchezera anansi awo. Mkaziyo anasokonezeka maganizo kwambiri ndi zimene zinachitikazo ndipo anamvetsera pamene Mboni zinali kuŵerenga Salmo 72:​12-14. Mavesi ameneŵa amati: “Adzapulumutsa waumphawi wopfuulayo; ndi wozunzika amene alibe mthandizi. Adzachitira nsoni wosauka ndi waumphawi, nadzapulumutsa moyo wa aumphawi. Adzawombola moyo wawo ku chinyengo ndi chiwawa; ndipo mwazi wawo udzakhala wa mtengo pamaso pake.” Mawu ameneŵa analitu ogwira mtima. Mkaziyo anapempha Mbonizo kuti ziŵerengenso mavesiwo ndipo anaziitanira m’nyumba yake kuti apitirize kukambirana. Pamapeto pa kukambiranako, phunziro la Baibulo linayambika.

18. Kodi Mboni ina inathandiza motani anansi ake pamene anaipempha kupemphera m’malo mwawo?

18 Mboni ina imagwira ntchito mu lesitilanti imene ili m’dera lomwe kumakhala anthu olemera kwambiri komwe ambiri sankasonyeza chidwi  chenicheni ndi uthenga wabwino wa Ufumu tsokali lisanachitike. Zigaŵenga zitaukira, anthu m’derali anasokonezeka maganizo. Lachisanu madzulo kuukiraku kutachitika, wamkulu wa lesitilantiyo anapempha kuti aliyense apite panja ndi kunyamula makandulo, kuchita mwambo wokhala chete kwakanthaŵi pokumbukira anthu amene anamwalira pa tsokali. Polemekeza malingaliro awo, Mboniyo inatuluka ndi kukaima m’mbali mwa kamsewu, osalankhula chilichonse. Wamkulu wa lesitilantiyo ankadziŵa kuti iye anali mtumiki wa Mboni za Yehova, motero anam’pempha kupemphera m’malo mwa anthuwo atamaliza mwambo wokhala chetewo. Mboniyo inavomera. M’pemphero lakelo, iye anatchula za kulira kumene kunali ponseponse m’dzikolo koma anati olirawo asalire mopanda chiyembekezo. Anatchula za nthaŵi pamene zochitika zomvetsa chisoni zoterozo sizidzachitikanso ndipo anati onse angayandikire kwa Mulungu wa chitonthozo mwa kudziŵa zolondola kuchokera m’Baibulo. Atanena kuti “Amen,” wamkulu wa lesitilantiyo ndiponso anthu oposa 60 amene anali panja pa lesitilantiyo, anam’yandikira wa Mboniyo, kum’thokoza, kum’kumbatira, ndi kumuuza kuti pemphero lakelo linali labwino kuposa lina lililonse limene iwo anamvapo.

Phindu kwa Anthu

19. Kodi n’chochitika chiti chimene chikusonyeza kuti ena amaona miyezo yapamwamba yomwe Mboni za Yehova zimatsatira?

19 M’madera mmene muli Mboni za Yehova anthu amapindula kwambiri ndi kukhalapo kwawo makamaka masiku ano, monga mmene anthu ambiri avomerezera zimenezi. Inde, anthu amene amalimbikitsa mtendere, kuona mtima, ndiponso makhalidwe oyera angakhaledi opindulitsa. M’dziko lina la m’kati mwa Asia, Mboni zinakumana ndi ofesala wakale wa bungwe la chitetezo la boma amene anapuma pantchito. Iye anati nthaŵi ina anapatsidwa ntchito yofufuza magulu osiyanasiyana a zipembedzo. Atafufuza Mboni za Yehova, anachita chidwi ndi kuona mtima kwawo ndiponso makhalidwe awo abwino. Anasirira kwambiri chikhulupiriro chawo cholimba ndi kutinso zimene amaphunzitsa n’zochokera m’Malemba. Ofesala wopuma pantchitoyu anavomera kuphunzira Baibulo.

20. (a) Kodi nkhani zosimba zimene Mboni za Yehova zinachita chaka chatha zikusonyeza chiyani? (b) Kodi n’chiyani chikusonyeza kuti pali ntchito yambiri yoti ichitike, ndipo timauona motani mwayi wathu wolalikira?

20 Zochitika zochepa chabe zimene tazisimba m’nkhani ino, mwa zochitika zikwizikwi zimene tikanatha kuzisimba, n’zoonekeratu kuti Mboni za Yehova zinatanganidwa m’chaka cha utumiki cha 2001. * Zinalankhula ndi anthu miyandamiyanda, zinatonthoza anthu ambiri amene anali kulira maliro, ndipo ntchito yawo yolalikira inapindula. Panali anthu okwana 263,431 amene anasonyeza kudzipatulira kwawo kwa Mulungu mwa kubatizidwa. Chiŵerengero cha olalikira padziko lonse chinawonjezeka ndi 1.7 peresenti. Ndipo kupezeka kwa anthu okwana 15,374,986 pa Chikumbutso cha imfa ya Yesu chimene chimachitika chaka ndi chaka kukusonyeza kuti padakali ntchito yambiri yoti ichitike. (1 Akorinto 11:​23-26) Tiyenitu tipitirize kufunafuna odzichepetsa amene amalabadira uthenga wabwino. Ndiponso tiyeni tipitirize kutonthoza “osweka mtima” kwa nthaŵi imene chaka chokomera Yehova chidakalipobe. Tilitu ndi ntchito yokhutiritsa! Inde, tonsefe tikugwirizana ndi zimene Yesaya ananena kuti: “Ndidzakondwa kwambiri mwa Yehova, moyo wanga udzakondwerera mwa Mulungu wanga.” (Yesaya 61:10) Mulungu apitirizetu kutigwiritsira ntchito pamene akukwaniritsa mawu a ulosi aŵa: “Ambuye Yehova adzaphukitsa chilungamo ndi matamando pamaso pa amitundu onse.”​—Yesaya 61:11.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 20 Tchati chimene chili pa masamba 19 mpaka 22 chikusimba zimene Mboni za Yehova zinachita m’chaka chautumiki cha 2001.

 Kodi Mukukumbukira?

• Kodi anthu odzichepetsa anapindula motani ndi uthenga wabwino umene Yesu analalikira?

• Kodi anthu amene analabadira kulalikira kwa ophunzira a Yesu a m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino anapeza phindu lotani?

• Kodi anthu amene amvera uthengawu lerolino apindula nawo motani?

• Kodi timauona motani mwayi wathu wamtengo wapatali wolalikira?

[Mafunso]

 [Tchati pamasamba 19-22]

LIPOTI LA CHAKA CHAUTUMIKI CHA 2001 LA MBONI ZA YEHOVA PADZIKO LONSE

 (Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

[Zithunzi patsamba 15]

Mboni za Yehova nthaŵi zonse zimakumbukira ntchito yawo yolalikira

[Zithunzi patsamba 17]

Anthu amene amalabadira uthenga wabwino amakhala nawo m’gulu la abale ogwirizana a padziko lonse