Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Opani Yehova ndi Kusunga Malamulo Ake

Opani Yehova ndi Kusunga Malamulo Ake

 Opani Yehova ndi Kusunga Malamulo Ake

“Opa[ni] Mulungu, musunge malamulo ake; pakuti choyenera anthu onse ndi ichi.”​—MLALIKI 12:13.

1, 2. (a) Kodi mantha angatiteteze bwanji mwakuthupi? (b) N’chifukwa chiyani makolo anzeru amayesetsa kuphunzitsa ana awo kuti azikhala ndi mantha oyenera?

“MANTHA amateteza moyo pamene kulimba mtima kumaika moyo pachiswe,” anatero Leonardo da Vinci. Kulimba mtima kwachibwana koika moyo pachiswe kumachititsa munthu kusaona ngozi zimene zingatsatire, pamene mantha amamuthandiza kukhala wosamala. Mwachitsanzo, ngati tafika m’mphepete mwa chiphompho chimene tingathe kugweramo, ambirife mwachibadwa timabwerera m’mbuyo. N’chimodzimodzinso ndi mantha oyenera, amatiteteza ku ngozi. Ndiponso, mantha oterowo amalimbikitsa ubale wathu ndi Mulungu monga mmene taphunzirira m’nkhani yathayi.

2 Komabe, n’kofunika kuphunzira kuopa zinthu zambiri za masiku ano zimene zingativulaze. Popeza ana aang’ono sakudziŵa kuopsa kwa magetsi kapena magalimoto a m’mizinda, angachite ngozi yaikulu mosavuta. * Makolo anzeru amaphunzitsa ana awo kuti azikhala ndi mantha, kuwachenjeza mobwerezabwereza za zinthu zimene zingawavulaze. Makolo amadziŵa kuti mantha amenewo angapulumutse moyo wa ana awo.

3. N’chifukwa chiyani Yehova amatichenjeza za ngozi zauzimu ndipo amachita zimenezo motani?

3 Yehova amatideranso nkhaŵa chimodzimodzi. Monga Atate wachikondi, amatiphunzitsa kudzera m’Mawu ake ndi gulu lake kuti tipindule. (Yesaya 48:17) Ena mwa maphunziro a Mulungu ameneŵa amatichenjeza “mobwerezabwereza” za misampha yauzimu ndi cholinga choti tiope ngozi zoterozo. (2 Mbiri 36:15, NW; 2 Petro 3:1) M’mbiri yonse, anthu akanapeŵa masoka auzimu ambiri ndi kuvutika kwakukulu ‘ngati akadakhala nawo mtima wotere wakumuopa Mulungu ndi kusunga malamulo ake.’ (Deuteronomo 5:29) Kodi tingatani kuti tikhale ndi mtima woopa Mulungu ndi kupeŵa ngozi zauzimu mu “nthaŵi zoŵaŵitsa” zino?​—2 Timoteo 3:1.

Patukani pa Zoipa

4. (a) Kodi Akristu ayenera kudana ndi chiyani? (b) Kodi Yehova amaliona bwanji khalidwe la uchimo? (Onani mawu a m’munsi)

4 Baibulo limafotokoza kuti “kuopa Yehova ndiko kuda zoipa.” (Miyambo 8:13) Buku lina lotanthauzira  mawu a m’Baibulo limanena kuti kuda kumeneku ndiko “kunyansidwa ndi anthu kapena zinthu zimene amazikana, kuzida ndiponso zimene munthu sufuna kuzikhudza m’pang’ono pomwe kapena kukhala nazo pafupi.” Motero, kuopa Mulungu kumaphatikizapo kuipidwa kapena kunyansidwa ndi zinthu zimene Yehova amaziona kuti n’zoipa. * (Salmo 97:10) Kumatichititsa kupatuka pa zoipa monga mmene tingabwerere mmbuyo titagwidwa ndi mantha achibadwa ngati tafika m’mphepete mwa chiphompho. Baibulo limati: “Apatuka pa zoipa poopa Yehova.”​—Miyambo 16:6.

5. (a) Kodi tingakulitse bwanji kuopa Mulungu ndi kudana ndi zoipa? (b) Kodi zimene zinachitikira mtundu wa Israyeli zikutiphunzitsa chiyani pankhaniyi?

5 Tingakulitse mantha ameneŵa ndi kudana ndi zoipa mwa kulingalira zotsatira zopweteka zimene uchimo umabweretsa. Baibulo limatitsimikizira kuti tidzatuta zimene tifesa, kaya tikufesera kwa thupi kapena kwa mzimu. (Agalatiya 6:7, 8) N’chifukwa chake, Yehova akufotokoza momveka bwino zotsatira za kusamvera malamulo ake ndi kusiya kulambira koona. Akanakhala kuti Mulungu sanali kuteteza mtundu waung’ono wa Israyeli, mitundu yaikulu ndiponso yamphamvu imene inazungulira mtunduwu ikanauwononga. (Deuteronomo 28:15, 45-48) Zotsatira zomvetsa chisoni za kusamvera kwa Israyeli anazilemba m’Baibulo “kutichenjeza” kuti tiphunzirepo kanthu ndi kukulitsa kuopa Mulungu.​—1 Akorinto 10:11.

6. Kodi ndi zitsanzo zina ziti za m’Malemba zimene tingazipende kuti tiphunzire kuopa Mulungu? (Onani mawu a m’munsi.)

6 Kuphatikiza pa zimene zinachitikira mtundu wa Israyeli wonse, Baibulo limasimba za anthu amene anali a nsanje, achiwerewere, adyera, kapena onyada. * Ena mwa anthu ameneŵa anali atatumikira Yehova kwa zaka zambiri, koma nthaŵi ina kuopa kwawo Mulungu kunakhala kosakwanira, ndipo anatuta zotsatirapo zopweteka. Kusinkhasinkha zitsanzo za m’Malemba zimenezi kungalimbitse kutsimikiza mtima kwathu koti tisachite monga mmene iwo anachitira. Zingakhaletu zomvetsa chisoni kudikira mpaka titakumana ndi tsoka lalikulu kenako n’kuyamba kumvera langizo la Mulungu. Njira yabwino yophunzirira si imene anthu ambiri amakhulupirira yoti tiziyamba kaye takumana nazo ndi kuona kupweteka kwake.​—Salmo 19:7.

7. Kodi ndi munthu wotani amene Yehova amamuitanira m’hema wake wophiphiritsa?

7 Chifukwa china chachikulu chimene chingatichititse  kuopa Mulungu ndicho kufuna kuteteza ubale wathu ndi iye. Timaopa kukhumudwitsa Yehova chifukwa timaona ubale wathu ndi iye kukhala wamtengo wapatali. Kodi ndi munthu wotani amene Mulungu amamuona kukhala bwenzi lake, amene angamuitanire m’hema wake wophiphiritsa? Ndi yekhayo “wakuyendayo mokwanira [“mosachimwa,” NW], nachita chilungamo.” (Salmo 15:1, 2) Ngati mwayi umenewu wokhala paubale ndi Mlengi timauona kuti ndi wamtengo wapatali, tidzasamala kuti tiyende osachimwa pamaso pake.

8. Kodi Aisrayeli a m’nthaŵi ya Malaki anapeputsa motani ubale wawo ndi Mulungu?

8 Mwachisoni, Aisrayeli ena a m’nthaŵi ya Malaki anapeputsa ubale wawo ndi Mulungu. M’malo moopa ndi kulemekeza Yehova, iwo anali kupereka nyama zodwala ndi zopunduka pa guwa la nsembe. Kusaopa kwawo Mulungu kunaonekeranso pa mmene anali kuonera ukwati. Pofuna kukwatira atsikana, amuna anali kusudzula akazi a ubwana wawo pa zifukwa zosakwanira. Malaki anawauza kuti Yehova anali kudana ndi “kuleka [“kusudzula,” NW]” ndipo kuti chinyengo chawo chinawasiyanitsa ndi Mulungu wawo. Kodi Mulungu akanayanja bwanji nsembe zawo pamene guwa la nsembe mophiphiritsa linadzaza ndi misozi ya akazi amene anawasiya amene anali kuwawidwa mumtima? Kusonyeza poyera kusalemekeza miyezo yake kumeneko kunachititsa Yehova kufunsa kuti: “Kundiopa kuli kuti?”​—Malaki 1:6-8; 2:13-16.

9, 10. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timaona ubale wathu ndi Yehova kukhala wamtengo wapatali?

9 Lerolino, Yehova akuonanso kusweka mtima kwa akazi ndi ana ambiri osalakwa amene amuna ndi atate odzikonda ndiponso a makhalidwe oipa awasiya komanso akuona akazi ndi amayi amene asiya amuna ndi ana awo. Ndithudi, zimamumvetsa chisoni. Amene ali bwenzi la Mulungu adzaona nkhanizi monga mmene Mulungu amaonera ndipo adzayesetsa kulimbitsa ukwati wake. Sadzatsatira mmene anthu kunjaku amaganizira amene amapeputsa kufunika koti ukwati ukhale wokhalitsa, ndiponso ‘adzathaŵa dama.’​—1 Akorinto 6:18.

10 Muukwati komanso m’mbali zina za moyo wathu, kudana ndi zinthu zimene Yehova amaziona kuti n’zoipa, ndiponso kuyamikira ubale wathu ndi iye kochokera pansi pa mtima kudzachititsa kuti atiyanje. Mtumwi Petro ananena motsindika kuti: “Zoona ndizindikira kuti Mulungu alibe tsankhu; koma m’mitundu yonse, wakumuwopa iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye.” (Machitidwe 10:34, 35) Tili ndi zitsanzo zambiri m’Malemba zimene zimasonyeza mmene kuopa Mulungu kunachititsira anthu ena kuchita zolungama pamene anali m’mayesero osiyanasiyana.

Anthu Atatu Amene Anaopa Mulungu

11. Kodi ndi nthaŵi iti pamene ananena kuti Abrahamu anali ‘woopa Mulungu’?

11 Muli munthu mmodzi m’Baibulo amene Yehova ananena kuti anali bwenzi lake. Ameneyu ndi Abrahamu, kholo lakale. (Yesaya 41:8) Kuopa Mulungu kwa Abrahamu kunayesedwa pamene Mulungu anamuuza kuti apereke nsembe mwana wake mmodzi yekha, Isake, amene Mulungu kudzera mwa iye akanakwaniritsa lonjezo lake lakuti mbadwa za Abrahamu zidzakhala mtundu waukulu. (Genesis 12:2, 3; 17:19) Kodi “bwenzi la Yehova” likanakhoza mayeso opweteka ameneŵo? (Yakobo 2:23) Panthaŵi imene Abrahamu anatenga mpeni kuti aphe Isake, mngelo wa Yehova anati: “Usaike dzanja lako pa mwana, usam’chitire iye kanthu; chifukwa tsopano ndidziŵa kuti iwe umuopa Mulungu, pakuti sunandikanize ine mwana wako, mwana wako wayekha.”​—Genesis 22:10-12.

12. Kodi n’chiyani chinachititsa Abrahamu kuopa Mulungu, ndipo tingatani kuti nafenso tiope Mulungu monga mmene iye anachitira?

12 Ngakhale kuti Abrahamu anali kuopa Yehova zisanachitike zimenezi, panthaŵi iyi ndi pamene anasonyeza mwapadera kuopa Mulungu. Kufunitsitsa kwake kupereka nsembe Isake kunaposa kumvera chabe kosonyeza ulemu. Abrahamu anachita zimenezi chifukwa cha kukhulupirira kotheratu kuti Atate wake akumwamba adzakwaniritsa zimene analonjeza mwa kuukitsa Isake ngati n’koyenera. Monga mmene Paulo analembera, Abrahamu “[a]nakhazikikanso mumtima kuti, chimene [Mulungu] analonjeza, anali nayonso mphamvu ya kuchichita.” (Aroma 4:16-21) Kodi ndife okonzeka kuchita zimene Mulungu akufuna ngakhale kuti tingafunikire kudzimana  kwambiri? Kodi timakhulupirira ndi mtima wonse kuti kumvera kumeneko tidzapindula nako kosatha, tikumadziŵa kuti Yehova “ali wobwezera mphoto iwo akum’funa Iye”? (Ahebri 11:6) Kumeneko ndiye kuopa Mulungu kwenikweni.​—Salmo 115:11.

13. N’chifukwa chiyani Yosefe anayeneradi kunena kuti iye anali munthu ‘woopa Mulungu’?

13 Tiyeni tipende chitsanzo china cha kuopa Mulungu​—chitsanzo cha Yosefe. Iye tsiku ndi tsiku anali kumukakamiza kuti achite chigololo pamene anali kapolo m’nyumba ya Potifara. Mwachionekere, panalibe njira yopeŵera kuti asamaonane ndi mkazi wa mbuye wake, yemwe sanaleke kumunyengerera kuti agone naye. Kenako, pamene mkaziyo ‘anamugwira’ Yosefe, iye “[a]nathaŵa natulukira kubwalo.” Kodi n’chiyani chinam’chititsa kupatuka pa choipa mwamsanga? Mosakayika, chifukwa chachikulu chinali kuopa Mulungu. Sanafune kuchita ‘choipa chachikulu ichi ndi kuchimwira Mulungu.’ (Genesis 39:7-12) Yosefe anayeneradi kunena kuti iye anali munthu ‘woopa Mulungu.’​—Genesis 42:18.

14. Kodi chifundo cha Yosefe chinasonyeza motani kuopa Mulungu kwenikweni?

14 Patapita zaka, Yosefe anakumana pamaso n’pamaso ndi abale ake amene anamugulitsa kuukapolo mopanda chifundo. Akanatha kugwiritsa ntchito mosavuta kusoŵa kwawo chakudya kukhala mpata woti awabwezere zoipa zimene anamuchitira. Koma kuchitira anthu nkhanza sikusonyeza kuopa Mulungu. (Levitiko 25:43) Motero, Yosefe atapeza umboni wokwanira wakuti abale akewo anasintha mitima yawo, anawachitira chifundo ndi kuwakhululukira. Monga mmene anachitira Yosefe, kuopa kwathu Mulungu kudzatichititsa kugonjetsa choipa mwakuchita chabwino, ndipo kudzatiteteza kuti tisagwere m’chiyeso.​—Genesis 45:1-11; Salmo 130:3, 4; Aroma 12:17-21.

15. N’chifukwa chiyani khalidwe la Yobu linasangalatsa mtima wa Yehova?

15 Yobu analinso chitsanzo china chabwino cha munthu woopa Mulungu. Yehova anauza Mdyerekezi kuti: “Kodi waonerera mtumiki wanga Yobu? pakuti palibe wina wonga iye m’dzikomo, munthu wangwiro ndi woongoka, wakuopa Mulungu ndi kupeŵa zoipa.” (Yobu 1:8) Kwa zaka zambiri, khalidwe lopanda banga la Yobu linasangalatsa mtima wa Atate ake a kumwamba. Iye anaopa Mulungu chifukwa chakuti anadziŵa kuti kunali koyenera kutero ndipo kuti ndicho chinthu chabwino kwambiri kuposa china chilichonse pa moyo wa munthu. Yobu anati: “Tawonani, kuopa Ambuye ndiko nzeru; ndi kupatukana nacho choipa ndiko luntha.” (Yobu 28:28) Yobu monga munthu wokwatira sanachite chidwi ndi atsikana mosayenera kapena kusunga malingaliro a chiwerewere mumtima mwake. Ngakhale anali munthu wolemera, sanaike chidaliro chake chonse pa chumacho, ndipo sanayerekeze n’komwe kulambira mafano alionse. (Yobu 31:1, 9-11, 24-28)

16. (a) Kodi Yobu anasonyeza chifundo m’njira zotani? (b) Kodi Yobu anaonetsa motani kuti anakhululuka?

16 Komabe, kuopa Mulungu kumatanthauza kuchita zabwino ndiponso kupeŵa zoipa. Motero, Yobu anachita chifundo ndi anthu osaona, opunduka, ndi osauka. (Levitiko 19:14; Yobu 29:15, 16) Yobu anadziŵa kuti “munthu amene sachitira chifundo mnzake, adzasiyanso kuopa Wamphamvuyonse.” (Yobu 6:14, NW) Kupanda chifundo kungaphatikizepo kusakhululuka kapena kusunga chakukhosi. Yobu atalangizidwa ndi Mulungu, anapempherera anzake atatu aja amene anaonjezera kwambiri chisoni chake. (Yobu 42:7-10) Kodi sitingachite chimodzimodzi, kukhululukira wokhulupirira mnzathu amene watikhumudwitsa mwa njira ina yake? Kupempherera munthu amene watilakwilayo kuchokera pansi  pa mtima kungatithandize kwambiri kuti tisasunge mkwiyo. Madalitso amene Yobu analandira chifukwa cha kuopa Mulungu akutipatsa chithunzi cha ‘kukoma mtima kwakukulu kumene Yehova wasungira iwo akumuopa iye.’​—Salmo 31:19; Yakobo 5:11.

Kusiyana kwa Kuopa Mulungu ndi Kuopa Munthu

17. Kodi kuopa anthu kungatichitire chiyani, koma n’chifukwa chiyani kuopa anthu ndi kusaona za m’tsogolo?

17 Kuopa Mulungu kungatilimbikitse kuti tichite zabwino pamene kuopa munthu kungafooketse chikhulupiriro chathu. N’chifukwa chake Yesu polimbikitsa ophunzira ake kuti alalikire uthenga wabwino mwachangu anawauza kuti: “Musamaopa amene akupha thupi, koma moyo sangathe kuupha; koma makamaka muope iye, wokhoza kuwononga moyo ndi thupi lomwe m’gehena.” (Mateyu 10:28) Yesu anafotokoza kuti kuopa anthu ndiko kusaona za m’tsogolo, chifukwa anthu sangawononge moyo wam’tsogolo umene tikuyembekezera. Ndiponso, timaopa Mulungu chifukwa tikudziŵa kuti ali ndi mphamvu zochititsa mantha poyerekeza ndi mphamvu za amitundu onse zomwe n’zosanunkha kanthu. (Yesaya 40:15) Ife, monga Abrahamu tili ndi chidaliro chonse m’mphamvu za Yehova zoukitsa atumiki Ake okhulupirika. (Chivumbulutso 2:10) Motero, timanena ndi chikhulupiriro chonse kuti: “Ngati Mulungu ali ndi ife, adzatikaniza ndani?”​—Aroma 8:31.

18. Kodi Yehova amafupa motani anthu amene akumuopa?

18 Kaya amene akutitsutsa ndi munthu wa m’banja mwathu kapena munthu wokonda kumenya anzake kusukulu, tidzapeza kuti “wakuopa Yehova akhulupirira kolimba.” (Miyambo 14:26) Tingam’pemphe Mulungu kuti atipatse mphamvu tikumadziŵa kuti atimva. (Salmo 145:19) Yehova samaiwala amene akumuopa. Akutitsimikizira kudzera mwa mneneri wake Malaki kuti: “Pamenepo iwo akuopa Yehova analankhulana wina ndi mnzake; ndipo Yehova anawatchera khutu namva, ndi buku la chikumbutso linalembedwa pamaso pake, la kwa iwo akuopa Yehova, nakumbukira dzina lake.”​—Malaki 3:16.

19. Kodi ndi mantha ati amene adzatha, koma ndi ati amene adzapitirira mpaka muyaya?

19 Tatsala pang’ono kufika m’nthaŵi imene aliyense padziko lapansi adzalambira Yehova ndipo kuopa munthu kudzatheratu. (Yesaya 11:9) Anthu sadzaopanso njala, matenda, upandu ndi nkhondo. Koma kuopa Mulungu kudzapitirizabe mpaka muyaya pamene atumiki ake okhulupirika a kumwamba ndi padziko lapansi adzapitiriza kumulemekeza ndi kumumvera. (Chivumbulutso 15:4) Padakali pano, tiyeni tonsefe timvere langizo la Solomo louziridwa lakuti: “Mtima wako usachitire nsanje akuchimwawo; koma opabe Yehova tsiku lonse; pakutitu padzakhala mphotho; ndipo chiyembekezo chako sichidzalephereka.”​—Miyambo 23:17, 18.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Makolo ena amatha mantha ndi zinthu zimene zingawavulaze ngati ntchito imene amagwira imawachititsa kukumana ndi zinthu za ngozi nthaŵi zonse. Pamene mmisiri wina yemwe anagwira ntchito yake kwa nthaŵi yaitali anamufunsa chifukwa chimene akalipentala ambiri amakhalira oduka chala, iye anati: “N’chifukwa chakuti amatha mantha ndi masowo a magetsi amphamvu kwambiri.”

^ ndime 4 Yehova amanyansidwa ndi zinthu zoipa. Mwachitsanzo, Aefeso 4:29 amafotokoza kuti kalankhulidwe konyansa ndiyo ‘nkhani yovunda.’ Liwu la Chigiriki limene analimasulira kuti “yovunda” kwenikweni limanena za chipatso, nsomba, kapena nyama yoti yawola ndipo ikununkha. Liwu limeneli likusonyeza bwino mmene tiyenera kunyansidwira ndi kalankhulidwe kotukwana kapena kolaula. Mofananamo, Malemba nthaŵi zambiri amanena kuti mafano ali ngati “manyi.” (Deuteronomo 29:17, NW; Ezekieli 6:9, NW) Kuipidwa kwathu ndi manyi kwachibadwa, kukutithandiza kumvetsa mmene Mulungu amaipidwira ndi mafano alionse.

^ ndime 6 Mwachitsanzo, talingalirani nkhani za m’Malemba zonena za Kaini (Genesis 4:3-12); Davide (2 Samueli 11:2–12:14); Gehazi (2 Mafumu 5:20-27); ndi Uziya (2 Mbiri 26:16-21).

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi timaphunzira bwanji kudana ndi choipa?

• Kodi Aisrayeli a m’nthaŵi ya Malaki anapeputsa motani ubale wawo ndi Yehova?

• Kodi tingaphunzire chiyani kwa Abrahamu, Yosefe, ndi Yobu pankhani ya kuopa Mulungu?

• Kodi ndi mantha ati amene adzapitirizabe, ndipo n’chifukwa chiyani?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 19]

Makolo anzeru amaphunzitsa ana awo mantha oyenera

[Chithunzi patsamba 20]

Monga mmene mantha amatithandizira kupeŵa ngozi, kuopa Mulungu kumatithandizanso kupeŵa zoipa

[Chithunzi patsamba 23]

Yobu anaopabe Mulungu ngakhale pamene anzake onyenga atatu anaonjezera chisoni chake

[Mawu a Chithunzi]

Kuchokera m’Baibulo la Vulgata Latina, 1795