Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Lamulo la Chikhalidwe Ndilo Chiphunzitso cha Anthu Onse

Lamulo la Chikhalidwe Ndilo Chiphunzitso cha Anthu Onse

 Lamulo la Chikhalidwe Ndilo Chiphunzitso cha Anthu Onse

“Chifukwa chake zinthu zilizonse mukafuna kuti anthu achitire inu, inunso muwachitire iwo zotero.”​—Mateyu 7:12.

YESU Kristu ndi amene analankhula mawu ameneŵa pafupifupi zaka zikwi ziŵiri zapitazo pa Ulaliki wake wotchuka wa pa Phiri. Zaka mazana ambiri chiyambireni nthaŵi imeneyo, anthu anenapo ndi kulemba zambiri pa mawu osavuta ameneŵa. Mwachitsanzo, awathokoza kuti ndiyo “mfundo imene yamanga Malemba,” kuti ndiwo “mawu achidule ofotokoza udindo umene Mkristu ali nawo kwa mnansi wake,” ndiponso kuti ndiyo “mfundo yaikulu ya chikhalidwe.” Mawu ameneŵa ndi odziŵika kwambiri moti ambiri amati ndi Lamulo la Chikhalidwe.

Koma sikuti mfundo imeneyi ya Lamulo la Chikhalidwe imangopezeka kumayiko omwe amati ndi achikristu okha ayi. Ayuda, Abuda ndi Agiriki anzeru ankalimbikitsa mwambi wa chikhalidwe umenewu m’njira zosiyanasiyana. Mawu amene Confucius analankhula ndiwo odziŵika kwambiri makamaka kwa anthu a kum’maŵa ku Far East. Kumayiko amenewo anthu amam’tama kwambiri Confucius kuti anali munthu wanzeru koposa komanso mphunzitsi. Lamuloli limapezeka katatu mu The Analects, buku lachitatu mwa mabuku anayi a Confucius otchedwa Four Books. Confucius poyankha mafunso a ophunzira, ananena kaŵiri konse kuti: “Zimene simufuna kuti ena akuchitireni, musawachitire zomwezo.” Nthaŵi ina wophunzira wake dzina lake Zigong ananena modzitama kuti “Zimene sindifuna kuti ena andichitire, inenso sindifuna kuwachitira zomwezo.” Atatero, mphunzitsiyo anapereka yankho lofuna kuganizapo kwambiri lakuti, “Inde, koma sukuthabe kuchita zimenezo.”

Munthu akaŵerenga mawuŵa a Confucius, atha kuona kuti iwo salimbikitsa munthu kuchitapo kanthu kusiyana ndi mawu amene Yesu ananena pambuyo pake. Kusiyana kwake koonekeratu n’kwakuti Lamulo la Chikhalidwe limene Yesu ananena limafuna munthu kutsimikiza mtima kuchitira ena zabwino. Anthu akanakhala kuti akutsata mawu olimbikitsa a Yesu mwa kusamala za ena, kuchita zotheka kuti athandize anzawo ndi kutsata lamulo limeneli masiku onse, kodi muganiza kuti dzikoli lero likanakhala labwino? Inde.

Kaya lamulolo lanenedwa m’njira yolimbikitsa kapena yosalimbikitsa, kapenanso m’njira ina iliyonse, chofunika n’chakuti anthu amene akhalako nthaŵi zosiyanasiyana, kumalo osiyanasiyana komanso osiyana zikhalidwe akhulupirira kwambiri mfundo imeneyi ya Lamulo la Chikhalidwe. Zimenezi zikungosonyeza kuti zimene Yesu ananena mu Ulaliki wa pa Phiri ndi chiphunzitso cha anthu onse ndipo chimakhudza moyo wa anthu amene akhala ndi moyo nthaŵi zosiyanasiyana kulikonse.

Ndiye tadzifunsani kuti: ‘Kodi ndingakonde kuti ena azindilemekeza, kundichitira  chilungamo ndi kundiuza zoona zokhazokha? Kodi ndingakonde kukhala m’dziko lopanda kusankhana mitundu, upandu ndi nkhondo? Kodi ndingakonde kukhala m’banja limene aliyense amalemekeza maganizo a mnzake ndiponso kuwafunira zabwino?’ Kodi pali amene sangafune zimenezi? Tsoka lake ndi loti ndi ochepa chabe amene ali ndi zinthu zimenezi. Ambiri safuna n’komwe kuganiza zoti angapeze zinthu zimenezi.

Lamulo la Chikhalidwe Lisweka

M’mbiri yonse ya munthu, akhalapo anthu ena amene achitira nkhanza anthu anzawo ndi kupondereza ufulu wawo. Nkhanza zimenezi zikuphatikizapo malonda a ukapolo mu Africa, makampu a boma la Nazi opherako anthu, kulemba ana ntchito mowakakamiza, ndiponso kupululutsa anthu a mtundu wina m’madera ambiri. Palinso nkhanza zina zambirimbiri zoopsa.

M’dziko limene tikukhalali masiku ano, anthu akugwiritsa ntchito njira ndi makina otsogola kwambiri ndipo anthuwo ndi odzikonda. Ndi anthu ochepa chabe amene amaganiza za ena pakabuka nkhani imene ingasokoneze mtendere wawo kapena ufulu wawo wachibadwidwe umene amaganiza kuti ali nawo. (2 Timoteo 3:1-5) N’chifukwa chiyani anthu ambiri akhala adyera, ankhanza, opanda chifundo ndi odzikonda? Kodi si chifukwa chakuti akukankhira padera Lamulo la Chikhalidwe poganiza kuti ndi losatheka kulitsatira komanso ndi lachikale ngakhale kuti ambiri amalidziŵa? Anthu ambiri amene amati amakhulupirira Mulungu alinso otere ndipo zimenezi ndi zachisoni. Ndiye malinga ndi mmene zinthu zikuyendera, anthu azipitiriza kukhalabe odzikonda kwambiri.

Koma nawa mafunso ofunika kwambiri oti tiwapende: Kodi kutsata Lamulo la Chikhalidwe kumafuna chiyani? Kodi alipo amene akulitsata? Ndipo kodi idzafika nthaŵi yoti anthu onse adzatsata lamulolo? Kuti mupeze mayankho olondola a mafunsoŵa, ŵerengani nkhani yotsatira.

[Chithunzi patsamba 3]

Confucius ndi anthu ena anaphunzitsa za Lamulo la Chikhalidwe m’njira zosiyanasiyana