Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mungapange Dziko Lapansi Kukhala Malo Abwinopo?

Kodi Mungapange Dziko Lapansi Kukhala Malo Abwinopo?

 Kodi Mungapange Dziko Lapansi Kukhala Malo Abwinopo?

“Ndale zikulephera kugwirizanitsa anthu. Zilibe mfundo zokwanira zoti zingakonzenso miyambo ya makhalidwe abwino yomwe anthu ankakhulupirira kale. Mfundo zabwino zandale sizingabwezeretse makhalidwe akale a kufunsira mbeta kapena a ukwati. Komanso, sizingachititse abambo kukhala ndi udindo wosamalira ana awo kapena kuchititsa anthu kudana ndi zinthu zoipa ndi kuchita nazo manyazi monga ankachitira kale . . . Malamulo sangathetse mavuto ambiri achikhalidwe amene amatisautsaŵa.”

KODI mukuvomereza mawuŵa omwe ananena yemwe kale anali wachiŵiri kwa mkulu wa bungwe lina la boma ku United States? Ngati mukuvomereza, kodi mavutoŵa omwe ambiri amachitika chifukwa cha dyera, kusoŵa chikondi m’mabanja, kusadzisunga, umbuli, ndi zifukwa zina zomwe zikuwononga khalidwe la anthu, angathetsedwe bwanji? Ena amaganiza kuti palibe njira yowathetsera moti amangodzikhalira akumagwira ntchito zawo za masiku onse momwe angathere. Anthu ena amaganiza kuti tsiku lina mtsogoleri wina wachikoka ndiponso wabwino kwambiri, mwinanso wachipembedzo, adzatulukira ndi kuwatsogolera ku njira yolondola.

Ndiponsotu, zaka masauzande aŵiri zapitazo, anthu anafuna kugwira Yesu Kristu kuti amulonge ufumu chifukwa anadziŵa kuti anatumidwa ndi Mulungu ndipo ndiye akanakhala mfumu yoyenera. Komabe, Yesu atadziŵa zolinga zawo, anachoka mofulumira. (Yohane 6:14, 15) Kenako Yesu anauza kazembe wachiroma kuti: “Ufumu wanga suli wa dziko lino lapansi.” (Yohane 18:31-36) Komabe, masiku ano ndi anthu ochepa amene amakana ufumu monga anachitira Yesu. Ndipo ngakhale atsogoleri a matchalitchi amene amadzinenera kuti amam’tsatira zimawavuta kukana ufumu. Ena mwa anthu ameneŵa ayesa kupanga dziko lapansi kukhala malo abwinopo mwa kulimbikitsa olamulira a boma kuti achite zimenezo kapena iwo eni kukhala pa maudindo a ndale. Timatsimikiza zimenezi mwa kuona zomwe zachitika m’zaka za m’ma 1960 ndi 1970.

Zomwe Achipembedzo Achita Poyesa Kuwongolera Zinthu pa Dziko Lapansi

Kumapeto kwa m’ma 1960, anthu ena a maphunziro apamwamba a zaumulungu a m’dziko lina la ku Latin America anayamba kumenyera ufulu anthu osauka ndi oponderezedwa. Kuti akwaniritse zimenezi, anapeka mfundo yopezera ufulu yomwe inanena kuti Kristu si mpulumutsi m’lingaliro la Baibulo chabe komanso kuti ndi mpulumutsi pa ndale ndi pa mavuto a zachuma. Ku United States, atsogoleri ambiri a matchalitchi amene anali kuda nkhaŵa ndi kuloŵa pansi kwa makhalidwe abwino anapanga bungwe lotchedwa Moral Majority. Cholinga cha bungwe limeneli chinali kuika pa maudindo a ndale anthu amene angapange malamulo a makhalidwe abwino a m’banja. M’mayiko ambiri a chisilamu, magulu otereŵa nawonso ayesa kuthetsa katangale ndi kusakaza ndalama mwa kulimbikitsa anthu kutsatira Koran.

Kodi mukukhulupirira kuti dziko lapansi ndi malo abwinopo chifukwa cha zomwe anthuŵa achita? Kunena zoona, makhalidwe abwino akupitiriza kuloŵa pansi ndipo kusiyana pakati pa olemera ndi osauka kukukulirakulira ngakhale m’mayiko amene mfundo yopeka yopezera ufulu inali yamphamvu kwambiri.

Bungwe la Moral Majority litalephera kukwaniritsa zolinga zake zazikulu ku United States, Jerry Falwell yemwe anayambitsa bungweli analithetsa  mu 1989. Mabungwe ena analoŵa m’malo mwake. Komabe, Paul Weyrich yemwe anali munthu woyamba kugwiritsa ntchito mawu akuti “gulu la makhalidwe abwino,” analemba m’magazini a Christianity Today kuti: “Ngakhale anthu atakonda mfundo zathu ndi kusankha atsogoleri athu, vuto ndi lakuti timalephera kukwaniritsa mfundo zomwe timaganiza kuti ndizo zofunika kwambiri.” Iye analembanso kuti: “Chikhalidwe chikuloŵabe pansi. Tazingidwa ndi vuto la kutha kwa chikhalidwe ndipo vuto limeneli ndi lalikulu kwambiri moti a ndale lawathetsa nzeru.”

Cal Thomas yemwe amalemba mabuku ndiponso m’nyuzipepala ananena mosabisa zomwe akuganiza kuti ndilo vuto lalikulu lomwe likulepheretsa kukweza miyoyo ya anthu pogwiritsa ntchito ndale. Iye anati: “Kusintha kwenikweni kungatheke ngati munthu aliyense atasintha mtima wake, osati kupambana chisankho. Izi zili choncho chifukwa chakuti mavuto athu aakulu si a ndale kapena a chuma koma a chikhalidwe ndi chipembedzo.”

Koma kodi mavuto okhudza chikhalidwe ndi chipembedzo angathe bwanji m’dziko lomwe mulibe miyezo yoyenera ndipo anthu amangodzisankhira okha chabwino ndi choipa? Ngati anthu odziŵa kukopa ena ndiponso a zolinga zabwino​—kaya akhale achipembedzo kapena ayi​—akulephera kupanga dziko lapansi kukhala malo abwinopo, kodi ndani angathe kuchita zimenezo? Yankho la funso limeneli tilipeza m’nkhani yotsatira. Ndipotu yankholo ndilo chifukwa chachikulu chomwe Yesu ananenera kuti Ufumu wake suli wa dziko lino lapansi.

 [Mawu a Chithunzi patsamba 2]

CHIKUTO: Madzi akuda: WHO/​UNICEF photo; dziko: Mountain High Maps® Copyright © 1997 Digital Wisdom, Inc.

[Mawu a Chithunzi patsamba 3]

Ana: Chithunzi cha UN; dziko: Mountain High Maps® Copyright © 1997 Digital Wisdom, Inc.