Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kulalikira Anthu Ovuta Kuwapeza

Kulalikira Anthu Ovuta Kuwapeza

 Olengeza Ufumu Akusimba

Kulalikira Anthu Ovuta Kuwapeza

MBONI ZA YEHOVA zimayesetsa kulalikira uthenga wa Ufumu kwa aliyense amene zingakumane naye. Nthaŵi zina, kulalikira anthu amene kaŵirikaŵiri sapezeka pa nyumba kumafunika khama lapadera. (Marko 13:10) Mpainiya wina wapadera m’dziko lina ku South America akusimba zomwe anachita pankhaniyi.

“Tsiku lina ndinamva kuti wolamulira wa dzikolo adzabwera kudzayendera dera lomwe ine ndi mkazi wanga tinali kulalikira. Popeza kuti iye mwachionekere anali m’gulu la anthu amene kaŵirikaŵiri sapezeka pa nyumba, ndinamulembera kalata ndipo m’kalatayo ndinaikamo mabuku ofotokoza Baibulo angapo, kuphatikizapo bulosha lakuti Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? komanso buku lakuti Mankind’s Search for God ndi Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. M’kalatayo ndinafotokoza cholinga cha mabuku ameneŵa lililonse palokha.

“Popeza kuti ndinkafuna kudziŵa maganizo ake pa mabuku ameneŵa, ndinapempha kuti ndikaonane naye. Patapita milungu ingapo, anandilola ndipo popita ndinatenga vidiyo yakuti Jehovah’s Witnesses​—The Organization Behind the Name. Ndinacheza naye kwa maola aŵiri. Titaonerera limodzi vidiyoyo, ndinam’funsa maganizo ake pa vidiyoyo. Anayankha amvekere: ‘Palibenso gulu ngati lanuli padziko lapansi. Ndikulakalaka ndikanakhala ndi anthu ngati inu amene akanandithandiza kukwaniritsa zolinga za boma langa!’ Kenako anandifunsa ngati ndinapitako kulikulu la dziko lonse la gulu lathu. Ndinamuuza kuti ngakhale kuti kuyambira ndili ndi zaka 14 ndicho chakhala cholinga changa, sindinapezebe mwayi wokaona likulu lathu la dziko lonse ku Brooklyn, New York. Chinalitu chimodzi mwa zolinga zovuta kuzikwaniritsa. Anandiyang’anitsitsa mwachidwi kwakanthaŵi ndithu. Kenako ananena kuti akufuna kuti ndipeze mwayi umenewo. Anatikonzera makalata otilola mwalamulo ndipo anatipatsa mphatso ya tikiti ya ndege!

“Wolamulirayo tsopano amalandira magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! nthaŵi zonse. Tikukhulupirira kuti mwina posachedwapa tiyamba kuphunzira naye Baibulo.”