Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Kukhulupirika Kumatanthauzanji?

Kodi Kukhulupirika Kumatanthauzanji?

 Kodi Kukhulupirika Kumatanthauzanji?

AHASIDI a Chiyuda a m’zaka za zana lachiŵiri B.C.E. anali kudziona ngati anali okhulupirikadi. Dzina lawoli likuchokera ku liwu la Chihebri lakuti cha·sidhʹ, lomwe limatanthauza “kukhulupirika.” Liwuli likuchokera ku dzina lakuti cheʹsedh limene nthaŵi zambiri amalimasulira kuti “kukoma mtima,” “chikondi chokhulupirika,” “ubwino,” ndi “chifundo.” Malinga ndi buku lakuti Theological Dictionary of the Old Testament, liwu lakuti cheʹsedh “limatanthauza kukonda kuchitapo kanthu, kupanga ubale wodalirana, ndiponso kupirira [ndipo] silimangosonyeza zimene munthu akuganiza zokha ayi, koma zimene angachite chifukwa cha zimene akuganizazo. Ndi khalidwe limene limasunga moyo kapena kuupulumutsa. Ndiko kuthandiza munthu amene waona tsoka kapena mavuto. Ndi umboni wakuti pali ubwenzi.”

N’zachionekere kuti m’zinenero zambiri, palibe liwu limodzi limene lingapereke tanthauzo lonse la liwu lachihebri limeneli malinga ndi mmene analigwiritsira ntchito m’Baibulo. Mulimonse mmene zingakhalire, malinga ndi Baibulo, kukhulupirika kumatanthauza zambiri osati chabe kungokwanitsa malonjezo. Kumaphatikizapo chikondi ndi kuchita zinthu zothandiza zimene zingapindulitse ena. Kuti timvetse tanthauzo la kukhulupirika kwenikweni, tiyeni tipende mmene Yehova anasonyezera kukhulupirika kwa Abrahamu, Mose, Davide, mtundu wa Israyeli, ndi kwa anthu onse.

Yehova Anakhulupirika

Yehova anamuuza mnzake Abrahamu kuti: “Ine ndine chikopa chako.” (Genesis 15:1; Yesaya 41:8) Iye sanangonena mawuŵa koma anachitadi zimenezo. Yehova anamuteteza ndi kum’pulumutsa Abrahamu ndi banja lake kwa Farao ndi kwa Abimeleki. Anamuthandiza Abrahamu kupulumutsa Loti m’manja mwa mafumu anayi amene anamugwira. Yehova anabwezeretsa mphamvu zobereka za Abrahamu amene anali ndi zaka 100 ndi za Sara amene anali ndi zaka 90 kuti Mbewu imene anailonjeza idzabadwe kudzera mwa iwo. Yehova anali kulankhula ndi Abrahamu nthaŵi zonse kudzera m’masomphenya, maloto, ndi angelo amithenga. Inde, Yehova anakhulupirika kwa Abrahamu panthaŵi imene anali moyo ndiponso patapita nthaŵi yaitali iye atamwalira. Kwa zaka mazana ambiri, Yehova anasungabe malonjezo ake kwa mbadwa za Abrahamu, mtundu wa Israyeli, ngakhale kuti mtunduwu unali wopulupudza. Ubale wa Yehova ndi Abrahamu unasonyeza tanthauzo la kukhulupirika kwenikweni lomwe ndi kuchitapo kanthu chifukwa cha chikondi.​—Genesis, machaputala 12 mpaka 25.

Timamva kuti ‘Yehova ananena ndi Mose mopenyana maso, monga munthu alankhula ndi bwenzi lake.’ (Eksodo 33:11) Inde, Mose anali ndi ubale wapafupi kwambiri ndi Yehova kuposa mneneri wina aliyense amene anakhalako Yesu Kristu asanafike. Kodi Yehova anakhulupirika motani kwa Mose?

Mose, monga mwamuna wa zaka 40 wamphamvu  ndi wanzeru zake, anafuna kuti amasule anthu a fuko lake mwa iye yekha. Koma nthaŵi inali isanafike ndipo anafunika kuthaŵa kuti apulumutse moyo wake. Anakaŵeta nkhosa ku Midyani kwa zaka 40. (Machitidwe 7:23-30) Komabe, Yehova sanamusiye Mose. Nthaŵi itakwana, anam’bwezeranso ku Igupto kuti akatsogolere Aisrayeli kuwatulutsa m’dzikolo.

Mofananamo, Yehova anakhulupirika kwa Davide, mfumu yachiŵiri yotchuka kwambiri ya Israyeli. Davide akali mnyamata, Yehova anauza mneneri Samueli kuti: “Nyamuka um’dzoze, pakuti ndi ameneyu.” Kuyambira pamenepo, Yehova anam’teteza ndi kum’tsogolera Davide mokhulupirika pamene anali kukula monga mfumu ya Israyeli ya m’tsogolo. Anam’pulumutsa “pa mphamvu ya mkango, ndi mphamvu ya chimbalangondo” ndiponso ku dzanja la chimphona chija, Goliati Mfilisti. Anamuthandiza kugonjetsa adani ambirimbiri a Israyeli, ndiponso anam’pulumutsa ku mkondo umene Sauli mdani wake wanjiru anam’ponyera.​—1 Samueli 16:12; 17:37; 18:11; 19:10.

Inde, Davide anali munthu wopanda ungwiro. Ndipotu anachita machimo aakulu. Komabe, m’malo mwa kungom’siya, Yehova anasonyeza chikondi chokhulupirika kwa Davide pamene analapa zedi. Nthaŵi yonse imene Davide anali moyo, Yehova mobwerezabwereza anasunga moyo wake ndi kuupulumutsa. Anachitapo kanthu kuthandiza munthu amene anali akuvutika. Kunalidi kukoma mtima kumeneko!​—2 Samueli 11:1–12:25; 24:1-17.

Mtundu wa Israyeli wonse unakhala pa ubale wopatulika ndi Yehova pamene unavomereza mfundo za m’pangano la Chilamulo cha Mose paphiri la Sinai. (Eksodo 19:3-8) N’chifukwa chake Aisrayeli amawasonyeza kuti anali paukwati ndi Yehova. Iwo anauzidwa kuti: “Yehova wakuitana iwe monga mkazi.” Ndipo Yehova anawauza Aisrayeliwo kuti: “Ndi kukoma mtima kwa chikhalire ndidzakuchitira chifundo.” (Yesaya 54:6, 8) Kodi Yehova anakhulupirika motani paubale wapadera umenewu?

Yehova anatsogolera kuchitapo kanthu mwa kuwapatsa Aisrayeli zosoŵa zawo ndi kulimbikitsa ubale wawo ndi iye. Anawatulutsa ku Igupto, anawalinganiza kukhala mtundu, ndipo anawafikitsa “m’dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi.” (Eksodo 3:8) Anali kuwalangiza mwauzimu nthaŵi ndi nthaŵi kudzera mwa ansembe, Alevi, ndi aneneri ndi amithenga otsatizanatsatizana. (2 Mbiri 17:7-9; Nehemiya 8:7-9; Yeremiya 7:25) Yehova anali kulanga mtunduwo ukayamba kulambira milungu ina. Anthuwo akalapa, anali kuwakhululukira. N’zoona kuti mtundu wa Israyeli unali “mkazi” wovuta kwambiri. Komabe, Yehova sanawasiye mwamsanga. Anakhala nawobe mokhulupirika chifukwa cha zimene analonjeza Abrahamu, mpaka pamene zolinga Zake kwa iwo zinakwaniritsidwa. (Deuteronomo 7:7-9) Okwatirana lerolino atengeretu chitsanzo chabwino kwambiri chimenechi.

Yehova akukhulupirikanso kwa anthu onse m’njira yakuti amapereka zofunika zazikulu pamoyo kwa onse, olungama ndi osalungama. (Mateyu 5:45; Machitidwe 17:25) Ndiponso kuposa pamenepo, wapereka Mwana wake monga nsembe ya dipo kuti anthu akhale ndi mwayi womasuka ku uchimo ndi imfa ndi kukhala ndi chiyembekezo  chaulemerero chokhala ndi moyo wangwiro ndiponso wosatha m’Paradaiso. (Mateyu 20:28; Yohane 3:16) Kupereka mphatso ya dipo inali njira yoposatu yochitapo kanthu posunga moyo ndi kuupulumutsa. Kunalidi “kuthandiza munthu amene waona tsoka kapena mavuto.”

Chitani Zothandiza Pofuna Kuonetsa Kukhulupirika Kwanu

Popeza kuti tanthauzo lake n’lofanana ndi kukoma mtima, liwuli kukhulupirika lilinso ndi ganizo lamphamvu la kuthandizana. Ngati munthu wakukomerani mtima, inunso mudzafunika kum’chitira mofananamo. N’chimodzimodzinso ndi kukhulupirika. Umboni wakuti Davide anamvetsa tanthauzo la liwu lakuti cheʹsedh ukuoneka m’zimene iye ananena. Anati: “Ndidzagwadira kuloza ku Kachisi wanu woyera, ndi kuyamika dzina lanu.” Chifukwa chiyani? “Chifukwa cha chifundo chanu [“kukoma mtima kwanu,” NW] ndi choonadi chanu.” (Salmo 138:2) Davide, monga munthu amene Yehova anamukomera mtima, mwachionekere anakhudzidwa mtima kum’lambira ndi kum’tamanda iye. Motero, tikamasinkhasinkha mmene Yehova amatikomera mtima, kodi timakhudzidwa mtima ndi kuchitanso chimodzimodzi? Mwachitsanzo, ngati anthu akunyoza dzina la Yehova, kodi mumakakamizika kulankhula pom’khalira kumbuyo chifukwa chakuti simukufuna kuti mbiri yake iipe?

Ndi zimenetu zinachitikira Mkristu wina watsopano pamodzi ndi mkazi wake atapita kumaliro a wachibale wawo amene anamwalira pangozi ya njinga yamoto. Maliro akewo sanali achipembedzo, ndipo amene analipo analoledwa kulankhula kenakake kokhudza amene anamwalirayo. Munthu wina amene analankhula anaimba mlandu Mulungu poganiza kuti mnyamatayo anamwalira nthaŵi isanakwane. Iye ananena kuti, ‘Mulungu anafuna kuti mnyamatayo apite kumwamba n’chifukwa chake anamutenga.’ Mbale wathu wachikristuyo anaona kuti sizingatheke kuti angokhala osalankhulapo. Anapita pamalo olankhulira ngakhale kuti analibe Baibulo kapena notsi. Anafunsa kuti: “Kodi mukuganiza kuti Mulungu wamphamvuyonse yemwe ndi wachifundo angafune kuti zimenezi zichitike?” Ndiyeno anayamba kukamba nkhani yosakonzekera kwa mphindi khumi. Anagwira mawu Malemba kufotokoza chifukwa chake timamwalira, zimene Mulungu wachita kuti apulumutse anthu ku imfa, ndi chiyembekezo chabwino kwambiri cha kuuka kwa akufa ndi kukhala ndi moyo kosatha m’dziko lapansi la paradaiso. Anthu oposa 100 amene analipowo anaombera m’manja kwanthaŵi yaitali. Nthaŵi ina mbaleyo pokumbukira zimene zinachitikazo anati: “Mtima wanga unadzala chimwemwe kuposa kale lonse. Ndinathokoza Yehova chifukwa chondiphunzitsa nzeru zake ndiponso pondipatsa mwayi woti nditeteze dzina lake loyera.”

Kukhulupirika kwathu kwa Yehova kumaphatikizaponso kukhulupirika pa Mawu ake, Baibulo. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti kudzera m’Baibulo, Yehova akutiphunzitsa mmene tingakhalire ndi moyo. Malamulo ndi mfundo zake zachikhalidwe zimene zili mmenemo n’zabwino kwambiri ndiponso n’zothandiza koposa pa moyo wa munthu. (Yesaya 48:17) Musalole kuti zonena za ena kapena kufooka kwanu kukusiyitseni kutsatira malamulo a Yehova. Pitirizani kukhulupirika pa Mawu a Mulungu.

Kukhulupirika kwathu kwa Mulungu kumaphatikizaponso kukhulupirika ku gulu lake. Kwa zaka zambiri, pakhala kuwongolera ndi kusintha koyenera pakamvedwe kathu ka malemba ena. Nkhani ndi yakuti palibe amene amadya bwino mwauzimu monga mmene ife timachitira. (Mateyu 24:45-47) Mosakayika konse, Yehova wathandiza mokhulupirika gulu lake lamakono. Kodi ifenso sitingachite chimodzimodzi? A. H. Macmillan anachita zimenezo. Atatsala pang’ono kumwalira, iye anati: “Ndaona gulu la Yehova likukula. Nthaŵi imene ndinadzipatulira kwa Mulungu ndili ndi zaka 23 mu September 1900, gululi linali laling’ono koma tsopano ndi gulu la padziko lonse la anthu achimwemwe amene akulengeza choonadi mwachangu. . . . Ndikutsimikiza kuposa kale, pamene ndikuona kuti utumiki wanga kwa Mulungu padziko lapansi lino watsala pang’ono kutha, kuti Yehova watsogolera anthu ake ndi kuwapatsa zimene anafunikiradi panthaŵi yake.” Mbale Macmillan  anatumikira mokhulupirika kwa zaka 66, mpaka pamene anamwalira pa August 26, 1966. Anali chitsanzo chabwino cha kukhulupirika ku gulu looneka la Mulungu.

Kuphatikiza pa kukhulupirika ku gulu, kodi tidzakhulupirika kwa wina ndi mnzake? Ikafika nthaŵi ya chizunzo, kodi tidzakhulupirikabe kwa abale ndi alongo athu? Nthaŵi ya nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse, abale athu ku Netherlands anapereka chitsanzo chabwino cha kukhulupirika. Mkulu wina wa mpingo wa Groningen, dzina lake Klaas de Vries, a Gestapo a chipani cha Nazi anam’panikiza kumufunsa mafunso mopanda chifundo. Kenako anam’bindikiritsa kwayekha kwa masiku 12 ndipo anali kungom’patsa buledi ndi madzi basi. Ndiyeno anayambanso kumufunsa. Atamuloza mfuti ndi kumuopseza kuti amupha nthaŵi ina iliyonse, anamupatsa mphindi ziŵiri kuti aulule kumene kunali abale ena audindo, ndiponso kuulula zofunika zina ndi zina. Klaas anangoti: “Palibe zina zimene ndikuuzeni. . . . Sindingapereke abale anga.” Anamuopseza ndi mfuti katatu. Pomaliza, a Gestapo aja analeka kum’funsa, ndipo anam’tumiza ku ndende ina. Sanapereke abale ake.

Kodi tidzakhulupirika kwa wachibale wathu amene timakhala naye nthaŵi zonse​—mkazi kapena mwamuna wathu? Kodi tikukhulupirika pa lumbiro lathu laukwati mofanana ndi mmene Yehova analemekezera pangano la ubale wake ndi mtundu wa Israyeli? Khulupirikani mu ukwati nthaŵi zonse ndiponso kulitsani ubale weniweni ndi mnzanuyo. Khalani patsogolo kusamala ukwati wanu. Chezani limodzi, lankhulanani nthaŵi iliyonse ndiponso momasuka, thandizanani ndi kulimbikitsana, mvetseranani, sekani pamodzi, lirani pamodzi, seŵerani pamodzi, yesetsani pamodzi kuti mukwaniritse zolinga zanu, sangalatsanani, khalani mabwenzi. Samalani kwambiri kuti mupeŵe kuwasonyeza anthu ena chikondi cha mu ukwati. Ngakhale kuti ndi bwino kudziŵana ndiponso kukhala mabwenzi ndi anthu ena omwe simuli nawo pabanja, chikondi cha mu ukwati muyenera kuchisonyeza kwa mnzanu yekhayo amene muli naye pabanja basi. Musalole kuti wina asokoneze banja lanu.​—Miyambo 5:15-20.

Khulupirikanibe kwa Mboni zinzanu ndi ku banja lanu. Musawaiwale pamene zaka zikupita. Pitirizani kulankhulana, lemberanani makalata, imbiranani mafoni, chezeranani. Zilibe kanthu kuti zinthu zili motani kwa inu, yesetsani kuti musawakhumudwitse. Chitani zotheka kuti iwo azisangalala kunena kuti akukudziŵani kapena kuti ndinu mbale wawo. Kukhulupirika kwanu kwa iwo kudzakuthandizani kuti mupitirizebe kuchita zabwino ndipo zidzakulimbikitsani.​—Estere 4:6-16.

Inde, kukhulupirika kwenikweni kumaphatikizapo kuchita zinthu zothandiza kuti tisunge ubale wathu wamtengo wapatali. Chitani zonse zimene mungathe kuti mubwezere kukoma mtima kwa Yehova. Tsanzirani kukhulupirika kwa Yehova pochita ndi mpingo wachikristu, mnzanu m’banja, banja lanu, ndi mabwenzi anu. Lengezani makhalidwe abwino a Yehova mokhulupirika kwa anansi anu. Wamasalmo analankhula moyenerera kuti: “Ndidzaimbira zachifundo za Yehova nthaŵi yonse: pakamwa panga ndidzadziŵitsira chikhulupiriko chanu ku mibadwomibadwo.” (Salmo 89:1) Kodi sitikukopeka mtima ndi Mulungu woteroyo? Ndithudi, “chifundo chake chimamka muyaya.”​—Salmo 100:5.

[Chithunzi patsamba 23]

A. H. Macmillan