Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Enoke Anayenda ndi Mulungu M’dziko la Anthu Osapembedza

Enoke Anayenda ndi Mulungu M’dziko la Anthu Osapembedza

 Enoke Anayenda ndi Mulungu M’dziko la Anthu Osapembedza

MDYEREKEZI amaganiza kuti angapatutse anthu onse m’njira ya Mulungu, ndipo nthaŵi inayake zinkaoneka ngati zikumuyendera. Kwa zaka pafupifupi mazana asanu pambuyo pa imfa ya Abele, kunalibe mtumiki wokhulupirika wa Yehova. Choncho, uchimo ndi mikhalidwe yosasangalatsa Mulungu zinali ponseponse.

Enoke anakhala ndi moyo padziko lapansi m’nthaŵi ya anthu osapembedza imeneyo. Mbiri ya m’Baibulo imasonyeza kuti anabadwa m’chaka cha 3404 B.C.E. Ngakhale kuti ena m’nthaŵi yake sanaope Mulungu, Enoke anali mwamuna wovomerezeka kwa Mulungu. Pamene mtumwi Paulo anali kutchula atumiki a Yehova omwe ndi zitsanzo za chikhulupiriro kwa Akristu, anatchulanso Enoke. Kodi Enoke anali yani? Kodi anakumana ndi mavuto otani? Nanga anathana nawo motani? Ndipo kodi kukhulupirika kwakeko kuli ndi phindu lanji kwa ife?

M’masiku a Enosi, pafupifupi zaka mazana anayi Enoke asanabadwe, “anthu anayamba kutchula dzina la Yehova.” (Genesis 4:26) Anthu anayamba kugwiritsa ntchito dzina la Mulungu kuchokera pa chiyambi m’mbiri ya anthu. Chotero, zikuoneka kuti kutchula dzina la Yehova kumene kunayamba m’nthaŵi ya Enosi sikunali kuitanira pa Yehova m’chikhulupiriro ndi kulambira koyera. Akatswiri ena a Chihebri amati Genesis 4:26 ayenera kukhala ndi mawu akuti “anayamba kutchula . . . mwachipongwe,” kapena kuti “pomwepo anayamba kuchitira chipongwe.” Anthu ayenera kuti ankadzitcha kuti Yehova, kapena ankapatsa anthu ena dzinali, ndipo mwa kulambira anthu amenewo ankati akulambira Mulungu. Mwinanso anapatsa dzina la Mulunguli kwa mafano.

‘Enoke Anayenda ndi Mulungu Woona’

Ngakhale kuti Enoke anali pakati pa anthu osaopa Mulungu, iye ‘anayendabe ndi Mulungu woona,’ Yehova. Sitinamvepo kuti makolo ake​—Seti, Enosi, Kenani, Mahalalele, ndi Yaredi​—anayenda ndi Mulungu. Iwo sanayende ndi Mulungu monga momwe Enoke anachitira, ndipo n’zoonekeratu kuti moyo wake unam’siyanitsa ndi makolo akewo.​—Genesis 5:3-27.

Kuyenda ndi Yehova kunatanthauza kumudziŵa bwino ndi kupanga ubwenzi ndi Mulungu. Izi zinatheka chifukwa chakuti m’moyo wake wonse, Enoke anachita mogwirizana ndi chifuno cha Mulungu. Yehova anachita chidwi ndi kudzipereka kwa Enoke. Ndiponso, Septuagint yachigiriki imati “Enoke anakondweretsa kwambiri” Mulungu, mfundo yomwenso mtumwi Paulo anatchula.​—Genesis 5:22; Ahebri 11:5.

Chomwe chinam’thandiza kwambiri Enoke kukhala ndi ubwenzi wabwino ndi Yehova, chinali chikhulupiriro chake. Ayenera kuti anasonyeza chikhulupiriro mwa “mbewu” yolonjezedwa ya “mkazi” wophiphiritsa wa Mulungu. Ngati Enoke ankam’dziŵa bwino Adamu, ayenera kuti ankadziŵanso zambiri za momwe Mulungu anachitira ndi mwamuna ndi mkazi oyambawo m’munda wa Edene. Popeza kuti Enoke ankam’dziŵa bwino Mulungu, n’chifukwa chake ‘ankamufunafuna Iye.’​—Genesis 3:15; Ahebri 11:6, 13.

Kuti Enoke akhale paubwenzi wabwino ndi Yehova, panafunika zoposa kungodziŵa chabe Mulungu. Zilinso chimodzimodzi kwa ife lerolino. Ngati ifeyo tili paubwenzi wabwino ndi munthu winawake, kodi si zoona kuti maganizo ndi zochita  zathu zimakhudzidwa ndi mmene iye amaonera zinthu? Timapewa kunena mawu kapena kuchita zinthu zomwe zingawononge ubwenzi umenewo. Ndipo ngati tikulingalira zosintha zinthu zina zomwe ife timachita, kodi sitimalingaliranso mmene zimenezi zidzakhudzire ubwenzi umenewu?

Mofananamo, kufunitsitsa kwathu kukhalabe paubwenzi wabwino ndi Mulungu, kumakhudzanso zimene timachita. Chofunika koposa, ndicho kudziŵa bwino lomwe zimene iye amakonda ndi zimene amadana nazo. Tikatero tidzafunika kutsogoleredwa ndi zimene tadziŵazo, kuyesetsa kumukondweretsa ndi zomwe timaganiza ndiponso zochita zathu.

Inde, ngati tikufuna kuyenda ndi Mulungu, tiyenera kumukondweretsa. N’zimene Enoke anachita kwa zaka zambiri. Kwenikweni, verebu lachihebri losonyeza kuti Enoke ‘anayenda’ ndi Mulungu, limasonyeza kuti anachita mobwerezabwereza, kapena kuti ankachita zimenezo nthaŵi zonse. Munthu winanso wokhulupirika amene ‘anayenda ndi Mulungu’ anali Nowa.​—Genesis 6:9.

Enoke anali ndi banja, ndipo anabereka “ana aamuna ndi aakazi.” Mmodzi mwa ana ake aamuna anali Metusela. (Genesis 5:21, 22) Mosakayikira, Enoke anachita zonse zotheka kutsogolera banja lake moyenera. Komabe, chifukwa chakuti anali pakati pa anthu osaopa Mulungu, sichinali chapafupi kuti iye atumikire Mulungu. Munthu mmodzi yekha wa m’nthaŵi yake, amene anasonyeza chikhulupiriro mwa Yehova, ayenera kuti anali Lameke, atate ake a Nowa. (Genesis 5:28, 29) Komabe, Enoke anatsata kulambira koona molimba mtima.

Kodi chinam’thandiza Enoke kukhalabe wokhulupirika kwa Mulungu n’chiyani? Mosakayikira, sanapange ubwenzi ndi anthu onyoza dzina la Yehova kapena ena osayenera kukhala mabwenzi a munthu wolambira Mulungu. Kufunafuna thandizo la Yehova m’pemphero kuyenera kuti kunalimbikitsa Enoke kuti atsimikize mtima kupeŵa chilichonse chosasangalatsa Mlengi wake.

Ulosi wa Kuwonongedwa kwa Osapembedza

Tikakhala pakati pa anthu osapembedza, kusungabe miyezo yapamwamba yamakhalidwe abwino  kumavuta kwabasi. Koma Enoke analengezanso uthenga wotsimikizika wa kuŵeruzidwa kwa oipa. Motsogoleredwa ndi mzimu wa Mulungu, Enoke analosera kuti: “Taona, wadza Ambuye ndi oyera ake zikwi makumi, kudzachitira onse chiweruziro, ndi kutsutsa osapembedza onse, pantchito zawo zonse zosapembedza, zimene anazichita kosapembedza, ndi pa zolimba zimene ochimwa osapembedza adalankhula pa Iye.”​—Yuda 14, 15.

Kodi uthenga umenewo unakhudza motani anthu osakhulupirira okakamira zoipawo? Si kulakwitsa kuganiza kuti anthu anadana naye Enoke chifukwa cha mawu ochititsa nthumanzi amenewo. Mwinamwake ankamulalatira, kumunyodola ndi kumuopseza. Mwina ena ankafuna kungomupheratu. Komabe, Enoke sanachite mantha. Ankadziŵa zomwe zinachitikira Abele wolungama uja, ndipo mofanana naye, Enoke nayenso anatsimikiza mtima kutumikira Mulungu zivute zitani.

“Mulungu Anamtenga”

Zikuoneka kuti pamene ‘Mulungu amatenga’ Enoke n’kuti moyo wake uli pangozi yaikulu. (Genesis 5:24) Yehova sanalole kuti mneneri wake wokhulupirika azunzidwe ndi adani ankhanza. Malinga n’kunena kwa mtumwi Paulo, “Enoke anatengedwa kuti angaone imfa.” (Ahebri 11:5) Ambiri amati Enoke sanafe​—amati Mulungu anamtenga kupita naye kumwamba ndipo adakali ndi moyo. Komatu Yesu ananena mosapita mbali kuti: “Kulibe munthu anakwera kumwamba, koma iye wotsikayo kuchokera kumwamba, ndiye Mwana wa munthu.” Yesu anali “mtsogoleri” wa onse okwera kumwamba.​—Yohane 3:13; Ahebri 6:19, 20.

Nanga n’chiyani chomwe chinachitikira Enoke? ‘Kutengedwa kwakeko kuti asaone imfa’ kungatanthauze kuti Mulungu anamuika m’masomphenya aulosi. Ndiyeno ali m’kati moona masomphenyawo, moyo wake unachotsedwa. Mwa njira imeneyi, Enoke sanamve ululu wa imfa. Chotero iye “sanapezeka,” mwachionekere chifukwa chakuti Yehova anaika m’manda thupi lake monga momwe anaikira thupi la Mose.​—Deuteronomo 34:5, 6.

Enoke anakhala ndi moyo zaka 365. Sanakhalitse poyerekeza ndi ena ambiri omwe anakhalako m’nthaŵi yake. Koma chofunika kwambiri kwa okonda Yehova n’chakuti am’tumikire mokhulupirika mpaka pamapeto a moyo wawo. Tikudziŵa kuti Enoke anachita zimenezo chifukwa chakuti “asanam’tenge, anachitidwa umboni kuti anakondweretsa Mulungu.” Malemba sanena mmene Yehova anauzira Enoke zimenezi. Komabe, Enoke asanamwalire, Mulungu anamutsimikizira kuti anakondwera naye, ndipo tingatsimikize kuti Yehova adzam’kumbukira poukitsa akufa.

Tsanzirani Chikhulupiriro cha Enoke

Moyenerera tingatsanzire chikhulupiriro cha anthu odzipereka kwa Mulungu. (Ahebri 13:7) Chifukwa cha chikhulupiriro chake, Enoke anali woyamba kukhala mneneri wokhulupirika wa Mulungu. M’masiku a Enoke, dziko linali monga momwe lilili panopa​—linadzaza ndi anthu achiwawa, achipongwe, ndiponso osapembedza. Komabe, Enoke anali wosiyana ndi anthu amenewo. Anali ndi chikhulupiriro chenicheni, ndipo anali chitsanzo cha kudzipereka kwaumulungu. Inde, Yehova anam’patsa uthenga wofunika kwambiri wa chiŵeruzo kuti alengeze, komanso anamulimbikitsa kuti athe kulengeza uthengawo. Molimba mtima Enoke anagwira ntchito imene anamupatsa, ndipo Mulungu anamusamalira pamene adani anali kumutsutsa.

Tikasonyeza chikhulupiriro monga momwe Enoke anachitira, Yehova adzatilimbikitsa kuti tithe kulengeza uthenga wake m’masiku otsiriza ano. Adzatithandiza kukhala olimba mtima potsutsidwa, ndipo kudzipereka kwathu kwa Mulungu kudzatisiyanitsa kwambiri ndi anthu osapembedza. Chikhulupiriro chidzatithandiza kuyenda ndi Mulungu ndi kutithandiza kuchita zinthu mokondweretsa mtima wake. (Miyambo 27:11) Ndi chikhulupiriro, Enoke wolungamayo anapambana poyenda ndi Yehova m’dziko la anthu osapembedza, nafenso tingapambane.

[Bokosi patsamba 30]

Kodi Baibulo Linagwira Mawu Buku la Enoke?

Buku la Enoke ndi buku lomwe silipezeka pa mndandanda wa mabuku ovomerezeka a m’Baibulo ndipo wolemba wake sadziŵika. Amanena kuti analemba ndi Enoke koma si zoona. Buku limeneli, limene mwina analilemba nthaŵi ina yake m’zaka za zana lachiŵiri ndi loyamba B.C.E., lili ndi nthano za Ayuda zokokomeza, zosamveka ndiponso zosagwirizana ndi mbiri. Mwachionekere, anali kuyesa kufotokoza mwatsatanetsatane nkhani yaifupi ya m’buku la Genesis yonena za Enoke. Umenewu ndi umboni wokwanira wakuti anthu okonda Mawu amene Mulungu anauzira ayenera kupeŵa bukuli.

M’Baibulo, buku la Yuda lokha ndi limene lili ndi mawu aulosi a Enoke. Mawuwo amati: “Taona, wadza Ambuye ndi oyera ake zikwi makumi, kudzachitira onse chiweruziro, ndi kutsutsa osapembedza onse, pantchito zawo zonse zosapembedza, zimene anazichita kosapembedza, ndi pa zolimba zimene ochimwa osapembedza analankhula pa Iye.” (Yuda 14, 15) Akatswiri ambiri amanena kuti ulosi wa Enoke wotsutsa anthu osapembedza a m’nthaŵi yake, anaugwira mawu mwachindunji m’Buku la Enoke. Kodi n’zotheka kuti Yuda anagwiritsa ntchito buku losadalirika lopanda umboni monga gwero lake?

Malemba sakunena mmene Yuda anadziŵira za ulosi wa Enoke. Mwina anangogwira mawu nkhani yodziwika, mbiri yodalirika yakale. Paulo ayenera kuti anachitanso chimodzimodzi pamene anatchula Yane ndi Yambre monga a matsenga a m’nyumba ya Farao omwe sanali kudziŵika mayina awo amene anatsutsana ndi Mose. Ngati wolemba Buku la Enoke anapeza magwero akale a mtundu umenewu, tingakanirenji kuti nayenso Yuda anapeza magwero oterowo? *​—Eksodo 7:11, 22; 2 Timoteo 3:8.

Nkhani yakuti Yuda anadziŵa motani za uthenga wa Enoke kwa anthu osapembedza ndi yaing’ono. Kudalirika kwake kwagona pa mfundo yakuti Yuda analemba mouziridwa ndi Mulungu. (2 Timoteo 3:16) Mzimu woyera wa Mulungu unam’teteza kuti asalembe zabodza.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 28 Wophunzira Stefano anafotokozanso mfundo zina zimene sizikupezeka paliponse m’Malemba Achihebri. Anafotokoza za kuphunzira kwa Mose nzeru zonse za Aigupto, zoti anali ndi zaka 40 pothaŵa ku Igupto, zoti anakhala ku Midyani kwa zaka 40, ndiponso zoti angelo anatenga nawo mbali popereka Chilamulo cha Mose.​—Machitidwe 7:22, 23, 30, 38.

[Chithunzi patsamba 31]

Enoke analengeza uthenga wa Yehova Molimba mtima