Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Khalani ndi Chikhulupiriro Monga cha Abrahamu!

Khalani ndi Chikhulupiriro Monga cha Abrahamu!

 Khalani ndi Chikhulupiriro Monga cha Abrahamu!

“Iwo a chikhulupiriro ndiwo ana a Abrahamu.”​—AGALATIYA 3:7.

1. Kodi Abramu anathana nacho motani chiyeso chatsopano ku Kanani?

ABRAMU anasiya moyo wosangalatsa mumzinda wa Uri pomvera lamulo la Yehova. Mavuto amene anakumana nawo zaka zotsatira anali chiyambi chabe cha chiyeso cha kukhulupirika chomwe anakumana nacho ku Igupto. Nkhani ya m’Baibulo imati: “Ndipo munali njala m’dzikomo.” Kunalitu kosavuta kuti Abramu akhumudwe ndi zimenezi. Komabe, anayesetsa kupezera banja lake zofunika pa moyo. ‘Abramu anatsikira ku Aigupto kukakhala kumeneko, chifukwa kuti njala inali yaikulu m’dziko mmenemo.’ Kunali kovuta kuti banja la Abramu lalikululo liloŵe mu Igupto osalidziŵa. Kodi Yehova anali kudzakwaniritsa malonjezo ake ndi kuteteza Abramu ku ngozi?​—Genesis 12:10; Eksodo 16:2, 3.

2, 3. (a) N’chifukwa chiyani Abramu anabisa kuti Sarai si mkazi wake? (b) Kodi Abramu anachita motani ndi mkazi wake pankhaniyi”?

2 Pa Genesis 12:11-13 timaŵerenga kuti: “Panali pamene anayandikira kuloŵa m’Aigupto, anati kwa Sarai mkazi wake, ‘Taonani, ndidziŵa kuti ndiwe mkazi wokongola maonekedwe ako; ndipo padzakhala pamene adzakuona iwe Aigupto, adzati, uyu ndi mkazi wake: ndipo adzandipha ine, koma iwe adzakuleka ndi moyo. Uzikanenatu, kuti iwe ndiwe mlongo wanga: kuti chidzakhala chabwino ndi ine, chifukwa cha iwe, ndi kuti moyo wanga usungike ndi iwe.’” Ngakhale kuti Sarai anali ndi zaka zopitirira 65 anali wokongolabe mochititsa kaso. Zimenezi zinaika moyo wa Abramu pa ngozi. * (Genesis 12:4, 5; 17:17) Koposa zonse, nkhani yaikulu inali yokhudza chifuno cha Yehova, chifukwa chakuti iye ananena kuti kupyolera m’mbewu ya Abramu mitundu yonse ya padziko lapansi idzadalitsidwa. (Genesis 12:2, 3, 7) Popeza kuti Abramu anali wopanda mwana, kunalidi kofunika kwambiri kuti akhalebe ndi moyo.

3 Abramu anauza mkazi wake za kugwiritsa ntchito njira yomwe anagwirizana poyamba, kuti azinena kuti ndi mlongo wake. Onani kuti ngakhale anali ndi udindo wa umutu, iye sanagwiritse ntchito udindo wakewo mosaganizira ena. M’malo mwake anapempha mkazi wake kuti agwirizane naye ndi kumuthandiza. (Genesis 12:11-13; 20:13) Pamenepa, Abramu anapereka chitsanzo chabwino kwambiri kwa amuna kuti azichita udindo wawo wa umutu mwachikondi. Ndipo Sarai mwa kusonyeza kugonjera kwake ali chitsanzo chabwino kwa akazi lerolino.​—Aefeso 5:23-28; Akolose 4:6.

4. Kodi atumiki okhulupirika a Mulungu lerolino angachite motani ngati miyoyo ya abale awo ili pangozi?

4 Sarai anatha kunena kuti Abramu anali mlongo wake chifukwa chakuti analidi mlongo wake ndithu. (Genesis 20:12) Komabe, Abramu sanali wokakamizika kuuza anthu zinthu zosayenera kuwauza. (Mateyu 7:6) Atumiki okhulupirika a Mulungu lerolino amatsatira lamulo la m’Baibulo lakuti azikhala oona mtima. (Ahebri 13:18) Mwachitsanzo, sangayerekeze kunena umboni wabodza m’khoti. Komabe, ngati abale awo ali pa ngozi yauzimu kapena yakuthupi, panthaŵi ya chizunzo kapena nkhondo yapachiŵeniŵeni, iwo amatsatira uphungu wa Yesu wakuti “khalani ochenjera monga njoka, ndi oona mtima monga nkhunda.”​—Mateyu 10:16; onani Nsanja ya Olonda, ya November 1, 1996, tsamba 18, ndime 19.

5. N’chifukwa chiyani Sarai anali wofunitsitsa kumvera pempho la Abramu?

 5 Kodi Sarai anatani ndi pempho la Abramu? Mtumwi Petro anafotokoza za akazi monga Sarai kuti ali “akuyembekezera Mulungu.” Choncho, Sarai anadziŵa kugwirizana kwa zochitika zimenezo ndi nkhani zauzimu. Kowonjezera pamenepo, anali kukonda ndi kulemekeza mwamuna wake. Chotero Sarai anasankha ‘kumvera mwamuna wake’ndi kubisa zoti anali mkazi wokwatiwa. (1 Petro 3:5) N’zoona kuti kuchita zimenezo kunamuika pangozi. “Pamene Abramu analoŵa m’Aigupto, Aigupto anaona kuti mkazi anali wokongola kwambiri. Ndipo akalonga ake a Farao anamuona iye, nam’yamikira iye kwa Farao; ndipo anamuka ndi mkazi kunyumba kwake kwa Farao.”​—Genesis 12:14, 15.

Yehova Anam’landitsa

6, 7. Kodi Abramu ndi Sarai zinawachitikira n’zotani ndipo kodi Yehova anam’landitsa motani Sarai?

6 Zinalitu zovutitsa maganizo kwambiri kwa Abramu ndi Sarai! Zikuoneka kuti Sarai anatsala pang’ono kum’gwirira. Komanso, kusadziŵa kwa Farao kuti Sarai anali wokwatiwa, kunachititsa Abramu kulandira mphatso zambiri kotero kuti “anali nazo nkhosa, ndi ng’ombe, ndi abulu, ndi akapolo, ndi adzakazi, ndi abulu aakazi, ndi ngamila.” * (Genesis 12:16) Mphatso zimenezi ziyenera kuti zinam’nyansa Abramu kwambiri. Ngakhale kuti zinthu zinkaoneka ngati zafika poipa kwambiri, Yehova sanamusiye Abramu.

7 “Koma Yehova anavutitsa Farao ndi banja lake ndi nthenda zazikulu chifukwa cha Sarai mkazi wake wa Abramu.” (Genesis 12:17) Mwanjira yomwe sanaitchule, Farao anadziŵa chomwe chinkachititsa “nthenda” zazikuluzo. Mwamsanga “Farao anaitana Abramu, nati, ‘Nanga n’chiyani ichi wandichitira ine? chifukwa chanji sunandiuza ine kuti ndiye mkazi wako? Chifukwa chanji unati, Ndiye mlongo wanga? Kotero ndinamtenga iye akhale mkazi wanga; tsopano suyu mkazi wako; mtenge nuchoke. Ndipo Farao analamulira anthu ake za iye; ndipo anamperekeza iye m’njira ndi mkazi wake ndi zonse anali nazo.”​—Genesis 12:18-20; Salmo 105:14, 15.

8. Kodi Yehova amalonjeza chitetezo chotani kwa Akristu lerolino?

8 Lerolino, Yehova sateteza atumiki ake ku imfa, chiwawa, chilala, kapena masoka achilengedwe. Yehova amatilonjeza kuti adzatiteteza ku zinthu zomwe zingawononge unansi wathu ndi iye. (Salmo 91:1-4) Amachita zimenezi makamaka mwa kutichenjeza panthaŵi yake pogwiritsa ntchito Mawu ake ndiponso “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mateyu 24:45) Bwanji nanga za kuopa kuphedwa pachizunzo? Ngakhale kuti Mulungu angalole anthu ake kufa, komabe sadzalola mpang’ono pomwe kuti onse atheretu psiti. (Salmo 116:15) Ndipo ngati okhulupirika ena amwalira, timatsimikiza kuti adzawaukitsa.​—Yohane 5:28, 29.

Kudzimana N’cholinga Chosungabe Mtendere

9. Kodi n’chiyani chikusonyeza kuti Abramu anapitirizabe kusamukasamuka ku Kanani?

9 Chilala chitatha ku Kanani, ‘Abramu anachoka ku Aigupto, iye ndi mkazi wake, ndi zonse anali nazo, ndi Loti pamodzi naye, kumka ku dziko la kumwera. Ndipo Abramu anali wolemera ndithu ndi ng’ombe ndi siliva ndi golidi.’ (Genesis 13:1, 2) Chotero anthu okhala kumeneko ankaona kuti anali munthu wamphamvu ndi wachikoka, kalonga wamkulu. (Genesis 23:6) Abramu analibe chikhumbo chokhazikika ndi kuchita nawo ndale za Akanani. M’malo mwake, “anankabe ulendo wake kuchokera ku dziko la kumwera kumka ku Beteli, kufikira kumalo kumene kunali hema wake poyamba paja, pakati pa Beteli ndi Ai.” Monga mwanthaŵi zonse, kulikonse komwe Abramu anapita anaika kulambira Yehova patsogolo.​—Genesis 13:3, 4.

10. Kodi ndi vuto lotani lomwe linabuka pakati pa abusa a Abramu ndi a Loti, ndipo n’chifukwa chiyani kunali kofunika kulithetsa msanga?

10 ‘Ndiponso Loti yemwe ankayenda ndi Abramu anali ndi nkhosa ndi ng’ombe ndi  mahema. Ndipo dziko silinathe kuwakwanira iwo, kuti akhale pamodzi: chifukwa kuti chuma chawo chinali chambiri, ndipo sanathe kukhala pamodzi. Ndipo panali ndewu, abusa a Abramu kudana ndi abusa a Loti: Akanani ndi Aperezi ndipo analinkukhala nthaŵi yomweyo m’dzikomo.” (Genesis 13:5-7) Malowo analibe msipu ndi madzi okwanira oti zoŵeta za Abramu ndi Loti zizidya. Choncho mkangano ndi chidani zinayamba pakati pa abusa. Mkangano woterowo unali wosaloledwa kwa olambira Mulungu woona. Ngati mkanganowo ukanapitirira zotsatira zake zikanakhala udani waukulu. Choncho kodi Abramu anathetsa bwanji vutoli? Abramu anayamba kulera Loti atate ake a Lotiyo atamwalira. Mwinamwake anali kum’lera monga mwana wa m’banja lake. Monga wamkulu pa aŵiriwo, kodi Abramu sindiye anali woyenera kutenga zinthu zabwino koposa?

11, 12. Kodi Abramu anapatsa Loti mwayi wotani, ndipo n’chifukwa chiyani Loti sanasankhe mwa nzeru?

11 Koma “Abramu anati kwa Loti, Tisachite ndewu, ine ndi iwe, abusa anga ndi abusa ako: chifukwa kuti ife ndife abale. Dziko lonse silili pamaso pako kodi? Ulekanetu ndi ine: ukanka iwe ku dzanja lamanzere, ine ndinka ku dzanja lamanja: ukanka iwe ku dzanja lamanja, ine ndinka ku dzanja lamanzere.’” Pafupi ndi Beteli pali malo omwe amatchedwa kuti “malo okwera ooneka bwino a ku Palestina.” Mwinamwake kuchokera pamalo ameneŵa “Loti anatukula maso ake nayang’ana chigwa chonse cha Yordano kuti chonsecho chinali ndi madzi ambiri, asanawononge Yehova Sodomu ndi Gomora, monga munda wa Yehova, monga dziko la Aigupto pakumka ku Zoari.”​—Genesis 13:8-10.

12 Ngakhale kuti Baibulo limatchula Loti monga munthu “wolungama,” pazifukwa zina iye sanapereke mwayi kwa Abramu pa nkhaniyi ndipo zikuoneka kuti sanafunsire n’komwe uphungu kwa Abrahamu. (2 Petro 2:7) “Loti anasankha chigwa chonse cha Yordano; ndipo Loti anachoka ulendo wake kumka kum’maŵa: ndipo analekana wina ndi mnzake. Ndipo Abramu anakhala m’dziko la Kanani, ndipo Loti anakhala m’midzi ya m’chigwa, nasendeza hema wake kufikira ku Sodomu.” (Genesis 13:11, 12) Sodomu unali mzinda wolemera ndipo wa zinthu zambiri zopindulitsa mwakuthupi. (Ezekieli 16:49, 50) Ngakhale kuti zomwe Loti anasankha zingaoneke ngati zanzeru polingalira zinthu zakuthupi, kwenikweni zinali zopanda nzeru m’lingaliro lauzimu. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti “anthu a ku Sodomu anali oipa ndi ochimwa kwambiri pamaso pa Yehova,” amatero Genesis 13:13. Zomwe Loti anasankha zosamukira kumeneko zinali kudzadzetsera banja lake mavuto aakulu.

13. Kodi chitsanzo cha Abramu n’chothandiza motani kwa Akristu omwe angasiyane maganizo pankhani yandalama?

13 Abramu ankakhulupirira lonjezo la Yehova lakuti m’kupita kwanthaŵi mbewu yake idzatenga dziko lonselo; choncho, iye sanafune kukanganirana kachigawo kochepa chabe ka dzikolo. Mofunitsitsa, anachita mogwirizana ndi mfundo yachikhalidwe yomwe patapita nthaŵi inalembedwa pa 1 Akorinto 10:24 kuti: “Munthu asafune zake za iye yekha, koma za mnzake.” Choncho ndi bwino kuti abale amene angasiyane maganizo pankhani yandalama azikumbukira chochitika chimenechi. Ena m’malo motsatira uphungu wopezeka pa Mateyu 18:15-17, atengera abale awo kukhoti. (1 Akorinto 6:1, 7) Chitsanzo cha Abramu chikusonyeza kuti ndi bwino kutaya ndalama kusiyana ndi kunyozetsa dzina la Yehova kapena kuwononga  mtendere wampingo wachikristu.​—Yakobo 3:18.

14. Kodi Abramu anayembekezera madalitso otani chifukwa cha kukoma mtima kwake?

14 Abramu anayembekezera madalitso chifukwa cha kukoma mtima kwake. Mulungu anati: “Ndipo ndidzayesa mbewu yako monga fumbi lapansi: chotere kuti ngati munthu angathe kuŵerenga fumbi lapansi, chomwechonso mbewu yako idzaŵerengedwa.” Mawu ameneŵa ayenera kuti analimbikitsa kwambiri Abramu wopanda mwanayo! Kenako, Mulungu analamula kuti: “Tauka, nuyendeyende m’dzikoli m’litali mwake ndi m’mimba mwake; chifukwa kuti ndidzakupatsa iwe limenelo.” (Genesis 13:16, 17) Zoonadi, Abramu sanaloledwe kukhazikika m’malo abwino a mumzinda. Anakhalabe wolekana ndi Akanani. Akristunso lerolino ayenera kukhala olekana ndi dzikoli. Sikuti amadziona kukhala opambana ena, koma kuti sayanjana kwambiri ndi wina aliyense amene angawakope kuchita zosemphana ndi Malemba.​—1 Petro 4:3, 4.

15. (a) Kodi kuyendayenda kwa Abramu kuyenera kuti kunatanthauzanji? (b) Kodi Abramu anapereka chitsanzo chotani kumabanja achikristu lerolino?

15 M’nthaŵi za m’Baibulo, munthu asanalandire dziko, amayenera kuyendera dzikolo. Choncho kuyendayenda m’dzikolo mwina kunakumbutsa Abramu nthaŵi zonse kuti tsiku lina dzikolo lidzakhala la ana ake. Momvera, “Abramu [“anapitiriza kukhala m’mahema,” NW], nasuntha hema wake nafika nakhala pa mitengo yathundu ya pa Mamre, imene ili m’Hebroni, namumangira Yehova kumeneko guwa la nsembe.” (Genesis 13:18) Pamenepanso Abramu anasonyeza kuti anali kuika kulambira patsogolo. Kodi phunziro labanja, pemphero labanja, ndiponso kupezeka pamisonkhano m’maziika patsogolo m’banja lanu?

Mdani Aukira

16. (a) N’chifukwa chiyani mawu oyambirira pa Genesis 14:1 amamveka oopsa? (b) Kodi cholinga cha nkhondo ya mafumu anayi akum’maŵa chinali chiyani?

16 “Ndipo panali masiku a Amarafele mfumu ya Sinara, ndi Arioki mfumu ya Elasara, ndi Kedorelaomere mfumu ya Elamu, * ndi Tidala mfumu ya Goimu, iwo anathira nkhondo.” M’chihebri chenicheni, mawu oyambawo akuti (“Ndipo panali masiku a . . . ”) amamveka oopsa, kusonyeza “nthaŵi ya chiyeso chomwe kumapeto kwake kuli madalitso.” (Genesis 14:1, 2, NW, mawu am’munsi) Chiyesocho chinayamba pamene mafumu akum’maŵa anayiwo ndi ankhondo awo anasakaza dziko la Kanani. Kodi cholinga chawo chinali chiyani? Chinalitu kupondereza mizinda isanu yopandukayo: Sodomu, Gomora, Adima, Zeboimu, ndi Bela. Pogonjetsa mizinda isanuyi, mafumu anayiwo “anaguba monga gulu limodzi kupita kuchigwa cha Sidimu, kapena kuti, nyanja yam’chere.” Loti ndi banja lake ankakhala kufupi ndi kumeneko.​—Genesis 14:3-7.

17. N’chifukwa chiyani kugwidwa kwa Loti kunali chiyeso chachikhulupiriro kwa Abramu?

17 Mafumu achikanani analimbana koopsa ndi ankhondowo, koma anagonja mochititsa manyazi. “Ndipo [opambanawo] anatenga chuma chonse cha Sodomu ndi Gomora ndi zakudya zawo zonse, namuka. Ndipo anagwira Loti mwana wa Abramu amene anakhala m’Sodomu, ndi chuma chake, namuka.” Abramu  anamva nkhani yomvetsa chisoniyi: ‘Ndipo anadza wina amene anapulumuka namuuza Abramu Mhebri; ndipo iye analinkukhala pa mitengo yathundu ya pa Mamre M-amori, mkulu wake wa Esakolo, ndi mkulu wake wa Aneri; amenewo ndiwo opangana naye Abramu. Pamenepo anamva Abramu kuti mphwake anagwidwa.’ (Genesis 14:8-14) Chinalitu chiyeso chachikulu chachikhulupiriro! Kodi Abramu akanamuumira mtima mphwake chifukwa chakuti anasankha malo abwino koposa? Kumbukiraninso kuti ankhondowo anachokera m’dziko lakwawo ku Sinara. Kumenyana nawo kukanatanthauza kudzitsekera njira yobwerera kwawo. Komanso, kodi Abramu akanatha bwanji kulimbana ndi asilikali amene magulu ankhondo ophatikizana a Akanani awalephera kuwagonjetsa?

18, 19. (a) Kodi Abramu anam’pulumutsa bwanji Loti? (b) Kodi ndani anatamandidwa chifukwa cha kupambana kumeneku?

18 Apanso Abramu anakhulupirira Yehova kwambiri. “Anatuluka natsogolera anyamata ake opangika, obadwa kunyumba kwake, mazana atatu kudza khumi ndi asanu ndi atatu, nawalondola kufikira ku Dani. Ndipo anadzigawanizira iwo usiku, iye ndi anyamata ake, nawakantha, nawapitikitsa kufikira ku Hoba, ndiko ku dzanja lamanzere la ku Damasiko. Ndipo anabwera nacho chuma chonse, nabwera naye Loti yemwe ndi chuma chake, ndi akazi ndi anthu omwe.” (Genesis 14:14-16) Mosonyeza kukhulupirira kwambiri Yehova, Abramu anatsogolera gulu lake lankhondo laling’onolo mpaka anapulumutsa Loti ndi banja lake. Abramu tsopano anakumana ndi Melikizedeke yemwe anali mfumu komanso mkulu wansembe ku Salemu. “Melikizedeke mfumu ya ku Salemu, anatuluka nawo mkate ndi vinyo: iye ndiye wansembe wa Mulungu Wamkulukulu. Ndipo anam’dalitsa iye, nati, Abramu adalitsike ndi Mulungu Wamkulukulu, mwini kumwamba ndi dziko lapansi; ayamikike Mulungu Wamkulukulu amene wapereka adani ako m’dzanja lako. Ndipo anampatsa iye limodzi la magawo khumi la zonse.”​—Genesis 14:18-20.

19 Inde, kupambana mwini wake ndi Yehova. Kachiŵirinso Yehova anamulanditsa Abramu chifukwa cha chikhulupiriro chake. Anthu a Mulungu lerolino samachita nawo nkhondo yeniyeni, koma amakumana ndi ziyeso ndi mavuto ambiri. Nkhani yathu yotsatira isonyeza mmene chitsanzo cha Abramu chingatithandizire kupirira bwinobwino ziyesozo.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Buku la Insight on the Scriptures (lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova) limanena kuti, “mipukutu yamakedzana imasimba za Farao amene analamula amuna okhala ndi zida kukagwira mkazi wokongola ndi kupha mwamuna wake.” Choncho sikuti Abramu ankachita mantha pachabe.

^ ndime 6 Hagara, amene m’kupita kwanthaŵi anadzakhala mkazi wamng’ono wa Abramu ayenera kuti anali mmodzi mwa antchito amene Abramu analandira panthaŵiyo.​—Genesis 16:1.

^ ndime 16 Otsutsa ena anena kuti Elamu sanakhalepo ndi mphamvu zoterozo ku Sinara ndipo kuti nkhani yokhudza kuukira kwa Kedorelaomere ndi yonama. Kuti mumve umboni wa zofukula m’mabwinja wovomereza nkhani ya m’Baibuloyi, onani Nsanja ya Olonda ya July 1, 1989, masamba 4-7.

Kodi Mwazindikira?

• Kodi ndi motani mmene chilala m’dziko la Kanani chinalili chiyeso cha chikhulupiriro kwa Abramu?

• Kodi ndi motani mmene Abramu ndi Sarai anaperekera chitsanzo chabwino kwa amuna ndi akazi apabanja lerolino?

• Kodi tingatengepo phunziro lotani pa mmene Abramu anathetsera mkangano wa antchito ake ndi antchito a Loti?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 22]

Abramu sanaumirire ufulu wake koma anaika zofuna za Loti patsogolo pa zake

[Chithunzi patsamba 24]

Abramu anadalira Yehova populumutsa mphwake Loti