Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Ufulu Wanu wa Kukhulupirira

Ufulu Wanu wa Kukhulupirira

 Ufulu Wanu wa Kukhulupirira

Mosakayika mumanyadira ufulu wanu wa kukhulupirira zimene mukufuna. Ndi mmenenso pafupifupi aliyense akuchitira. Pogwiritsa ntchito ufulu umenewu, anthu mabiliyoni asanu ndi limodzi padziko lapansi ali ndi zikhulupiriro zambiri zosiyanasiyana. Kusiyanasiyana kwa zimene anthu amakhulupirira kumawonjezera chidwi, chimwemwe, ndi chisangalalo pa moyo monga kumachitira kusiyanasiyana kwa mitundu, maonekedwe, kukoma, fungo, ndi kuimba kwa zinthu zachilengedwe. Inde, kusiyanasiyana kumeneku kumapangitsa moyo kukhala wochititsa chidwi ndiponso wosangalatsa.​—Salmo 104:24.

KOMABE mpofunika kusamala. Zikhulupiriro zina n’zoopsa. Mwachitsanzo, kuchiyambi kwa zaka za m’ma 1900, anthu ena ankakhulupirira kuti Ayuda komanso gulu la a Freemason anakonza zoti “asokoneze Akristu onse ndi kukhazikitsa boma la padziko lonse limene adzalamulira mogwirizana.” Gwero la chikhulupiriro chimenechi linali thirakiti lina limene anthu otsutsana ndi Ayuda anakonza lakuti Protocols of the Learned Elders of Zion. Thirakitilo linati zina zimene anakonza ndizo kuvomereza msonkho wokwera kwambiri, kulimbikitsa kupanga zida zankhondo, ndi kuphangira ntchito zonse za bizinesi n’cholinga chakuti ‘awononge mofulumira chuma cha Akunja.’ Linatinso anakonza zoti aphangire maphunziro kuti ‘achititse Akunja kukhala ngati zilombo zosaganiza,’ komanso kukonza njanji ya pansi panthaka kuti agwirizanitse mizinda yaikulu ndi cholinga chakuti akulu a Ayuda athe ‘kugonjetsa otsutsa onse mwa kuwapheratu.’

Ndithudi, onseŵa anali mabodza omwe anawakonza ndi cholinga chakuti asonkhezere anthu kudana ndi Ayuda. Mark Jones wa ku British Museum anati: ‘Bodza lamkunkhuniza limeneli linafalikira m’mayiko ena kuyambira ku Russia,’ kumene linaoneka koyamba m’nyuzipepala mu 1903. Linafika ku London ndipo linaoneka m’nyuzipepala ya The Times pa May 8, 1920. Patapita chaka, nyuzipepala ya The Times inavumbula kuti thirakitilo linali lachinyengo. Komabe panthaŵiyo zinthu zinali zitaipa kale. Jones anati: ‘Mabodza ngati ameneŵa ndi ovuta kuwagonjetsa.’ Anthu akavomereza, mabodzaŵa amabala zikhulupiriro zaudani ndiponso zoopsa kwambiri. Kaŵirikaŵiri zotsatira zake zimakhala zovulaza kwambiri monga momwe mbiri ya m’zaka za m’ma 1900 yasonyezera.​—Miyambo 6:16-19.

Kusiyana Pakati pa Chikhulupiriro ndi Choonadi

Inde, zikhulupiriro zina zolakwika zingayambe popanda mabodza opeka mwadala. Nthaŵi zina, timaona zinthu molakwika. Ndi anthu angati amene amwalira mwamsanga chifukwa chochita zinthu zimene anali kukhulupirira kuti n’zolondola? Nthaŵi zina timakhulupirira chinthu chifukwa chakuti tangofuna kuchikhulupirira. Pulofesa wina ananena kuti ngakhale a sayansi “amatamanda kwambiri ziphunzitso  zawo ndi zimene apeza.” Zimene amakhulupirirazo zimawalepheretsa kufufuza mozama kuti apeze zoona zake zenizeni. Ndiyeno amathera moyo wawo wonse kuyesayesa mosaphula kanthu kuchirikiza zikhulupiriro zolakwikazo.​—Yeremiya 17:9.

Zachitikanso chimodzimodzi pa zikhulupiriro za chipembedzo. Zikhulupiriro za chipembedzo, zimatsutsana kwambiri. (1 Timoteo 4:1; 2 Timoteo 4:3, 4) Pamene munthu ali ndi chikhulupiro cholimba mwa Mulungu, wina amati munthu ameneyu alibe umboni uliwonse wochirikiza kukhulupirira Mulungu kwakeko. Ena amati tili ndi mzimu wosafa umene umapulumuka munthu akamwalira, pamene ena amakhulupirira kuti munthu akamwalira sakhalanso ndi moyo mpang’ono pomwe. Mwachionekere, n’zosatheka kuti zikhulupiriro zonse zotsutsanazi zikhale zoona. Motero, kodi si kwanzeru kuonetsetsa kuti zimene mumakhulupirira n’zoonadi osati zimene mwangofuna kuti mukhulupirire? (Miyambo 1:5) Kodi mungachite bwanji zimenezo? Nkhani yotsatira ipenda funso limeneli.

[Chithunzi patsamba 3]

Nkhani ya mu 1921 imene inavumbula thirakiti lakuti “Protocols of the Learned Elders of Zion”