Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Onetsani Kuti Mukupita Patsogolo

Onetsani Kuti Mukupita Patsogolo

 Onetsani Kuti Mukupita Patsogolo

“Izi uzisamalitse; mu izi ukhale; kuti kukula mtima kwako [“kupita kwako patsogolo,” NW] kuonekere kwa onse.”​—1 TIMOTEO 4:15.

1. Kodi mungadziŵe bwanji kuti chipatso chapsa ndipo chifunika kudya?

TAGANIZANI za chipatso chimene mumakonda kwambiri. Mwina pichesi, peyala, mango, kapena china chilichonse. Kodi mutha kudziŵa kuti chapsa tsopano ndipo chifunika kudya? Inde. Fungo lake, maonekedwe ake ndiponso kutiwisika kwake kumapatsa njala. Mukangoti mwalumako, m’kamwa monse mumangoti tseketseke, kukomatu kumeneko! Mtima wanu umasangalala zedi.

2. Kodi timaona bwanji kuti munthu ndi wachikulire, ndipo zimenezi zimakhudza motani ubale wa anthu?

2 Zinthu zosangalatsa ngati zimenezi zimachitikanso mbali zina za moyo. Mwachitsanzo, monga momwe zimakhalira ndi chipatso chikapsa, uchikulire wauzimu umaonekera mwa munthu mwa njira zambiri. Timazindikira kuti munthu ndi wachikulire tikaona kuzindikira kwake, luntha, nzeru zake ndi zina zotero. (Yobu 32:7-9) Zimasangalatsa kwambiri kucheza ndi kugwira ntchito ndi anthu amene amaonetsa makhalidwe ameneŵa pa kaganizidwe kawo ndi zochita zawo.​—Miyambo 13:20.

3. Kodi kafotokozedwe ka Yesu ka anthu a panthaŵiyo kamasonyeza chiyani za uchikulire?

3 Komanso munthu atha kukhala wamkulu kuthupi, koma ndi mmene amalankhulira kapena zimene amachita, angaonetse kuti ndi mwana m’maganizo ndiponso mwauzimu. Mwachitsanzo, pamene Yesu Kristu analankhula za mbadwo wopulupudza umene unalipo panthaŵi imene iye anali ndi moyo, anati: “Yohane anadza wosadya, wosamwa, ndipo iwo amati, Ali ndi chiŵanda. Mwana wa munthu anadza wakudya, ndi wakumwa, ndipo iwo amati, Onani munthu wakudyaidya ndi wakumwaimwa vinyo.” Ngakhale kuti anthu amenewo anali achikulire kuthupi, Yesu  anati iwo anachita ngati “ana”​—anali osakhwima maganizo. Ndiye chifukwa chake iye anawonjeza kuti: “Nzeru iyesedwa yolungama ndi ntchito zake.”​—Mateyu 11:16-19.

4. Kodi kupita patsogolo komanso uchikulire zimaonekera m’njira ziti?

4 Malinga ndi mawu a Yesu, titha kuona kuti munthu ali ndi nzeru yeniyeni​—chizindikiro cha uchikulire​—mwa ntchito zake ndi zotsatira za ntchitozo. Mogwirizana ndi mfundo imeneyi, taonani zimene mtumwi Paulo analangiza Timoteo. Paulo atafotokoza zimene Timoteo anafunika kusamalira, anati: “Izi uzisamalitse; mu izi ukhale; kuti kukula mtima kwako [“kupita kwako patsogolo”] kuonekere kwa onse.” (1 Timoteo 4:15) Inde, Mkristu akamapita patsogolo kuti afike pa uchikulire ‘zimaonekera’ bwinobwino. Uchikulire wachikristu, mofanana ndi nyale yowala, si khalidwe lobisika. (Mateyu 5:14-16) Chotero, tipenda njira zazikulu ziŵiri zimene kupita patsogolo komanso uchikulire zimaonekera: (1) kukula m’chidziŵitso, kuzindikira ndi nzeru; (2) kuonetsa chipatso cha mzimu.

Umodzi wa Chikhulupiriro ndi wa Chidziŵitso

5. Kodi uchikulire tingaufotokoze bwanji?

5 Madikishonale ambiri amati uchikulire ndiwo kukula, kukhwima kapenanso kufika pa muyeso wofunikira. Chipatso, chimene tatchula poyamba chija, chimakhwima kapena kupsa, chikamaliza kukula ndipo maonekedwe ake, fungo lake ngakhale kukoma kwake zikafika pofunikira. Choncho uchikulire n’chimodzimodzi ndi ubwino wopambana zedi, kukwanira, ngakhale ungwiro.​—Yesaya 18:5; Mateyu 5:45-48; Yakobo 1:4.

6, 7. (a) N’chiyani chikusonyeza kuti Yehova akufunitsitsa kuti olambira ake onse afike pa uchikulire wauzimu? (b) Kodi uchikulire wauzimu umagwirizana ndi chiyani?

6 Yehova Mulungu amafunitsitsa kuti olambira ake onse afike pa uchikulire wauzimu. Pofuna kuti zimenezo zitheke, wapereka zinthu zabwino kwambiri mumpingo wachikristu. Mtumwi Paulo polembera Akristu a ku Efeso anati: “Anapatsa ena akhale atumwi; ndi ena aneneri; ndi ena alaliki; ndi ena abusa, ndi ena aphunzitsi; kuti akonzere oyera mtima ku ntchito ya utumiki, kumangirira thupi la Kristu; kufikira ife tonse tikafikira ku umodzi wa chikhulupiriro, ndi wa chizindikiritso [“chidziŵitso cholondola,” NW] cha Mwana wa Mulungu, kwa munthu wangwiro [“wamkulu msinkhu,” NW] ku muyeso wa msinkhu wa chidzalo cha Kristu. Kuti tisakhalenso makanda, ogwedezekagwedezeka, natengekatengeka ndi mphepo yonse ya chiphunzitso, ndi tsenga la anthu, ndi kuchenjerera kukatsata chinyengo cha kusokeretsa.”​—Aefeso 4:11-14.

7 M’mavesi ameneŵa, Paulo anafotokoza kuti zina mwa zifukwa zimene Mulungu waperekera mphatso zauzimu zambiri ngati zimenezi mumpingo ndi zakuti onse ‘afikire umodzi wa chikhulupiriro ndi wa chidziŵitso cholondola,’ akhale ‘munthu wamkulu msinkhu,’ nakhale ndi ‘muyeso wa msinkhu wa Kristu.’ Tikatero m’pamene tingapewe kukhala ngati makanda auzimu ogwedezekagwedezeka ndi zikhulupiriro ndi ziphunzitso zonyenga. Chotero tikuona kugwirizana kumene kulipo pakati pa kufika pa uchikulire wachikristu ndi kupeza ‘umodzi wa chikhulupiriro ndi wa chidziŵitso cholondola cha Mwana wa Mulungu.’ Uphungu wa Paulo  uli ndi mfundo zingapo zimene tifunikira kulabadira.

8. Kodi kufikira “umodzi” wa chikhulupiriro ndi wa chidziŵitso cholondola kumafuna chiyani?

8 Choyamba, popeza tifunika kusunga “umodzi,” Mkristu wachikulire ayenera kukhala wogwirizana kotheratu ndi okhulupirira anzake pa chikhulupiriro ndi chidziŵitso. Salimbikitsa ndipo saumirira maganizo akeake kapena kukhala ndi zikhulupiriro zakezake pa kamvetsedwe kake ka Baibulo. Koma amakhulupirira mfundo zonse za choonadi chimene Yehova Mulungu amavumbula kudzera mwa Mwana wake, Yesu Kristu, ndi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” Mwa kudya nthaŵi zonse chakudya chauzimu chimene timalandira “panthaŵi yake”​—m’mabuku achikristu, misonkhano ya mpingo, yadera ndi yachigawo​—ndiye kuti tikusunga “umodzi” ndi Akristu anzathu pa chikhulupiriro ndi chidziŵitso.​—Mateyu 24:45.

9. Fotokozani zimene mawu akuti “chikhulupiriro” amatanthauza malinga ndi mmene Paulo anawagwiritsira ntchito m’kalata yake kwa Aefeso?

9 Chachiŵiri, mawu akuti “chikhulupiriro” sakunena maganizo osakayika amene Mkristu amakhala nawo, koma zonse zimene timakhulupirira, “kupingasa, ndi utali, ndi kukwera” kwake. (Aefeso 3:18; 4:5; Akolose 1:23; 2:7) Ndipotu umodzi ungatheke bwanji pakati pa Mkristu ndi okhulupirira anzake ngati iye amangokhulupirira kapena kuvomereza mbali zina za “chikhulupiriro”? Zimenezi zikutanthauza kuti sitifunikira chabe kukhutira ndi kungodziŵa ziphunzitso zoyamba za Baibulo kapena kungodziŵa choonadi pang’ono kapena mwa apo ndi apo ayi. Zikutanthauza kuti tikhale ofunitsitsa kutengerapo mwayi pa makonzedwe onse amene Yehova wapereka m’gulu lake kuti tizifufuza m’Mawu ake mwakuya. Tiyesetsenso kupeza chidziŵitso cholondola, chakuya komanso chokwana bwino cha chifuniro cha Mulungu ndi zolinga zake. Zimenezi zikuphatikizapo kupatula nthaŵi yoŵerenga ndi kuphunzira Baibulo ndi mabuku olifotokoza, kupemphera kwa Mulungu kuti atithandize ndi kutitsogolera, kufika pamisonkhano yachikristu mokhazikika ndiponso kuchita nawo mokwanira ntchito yolalikira Ufumu ndi yopanga ophunzira.​—Miyambo 2:1-5.

10. Kodi mawu akuti “kufikira ife tonse tikafikira” akutanthauza chiyani malinga ndi mmene awagwiritsira ntchito pa Aefeso 4:13?

10 Chachitatu, Paulo asanafotokoze cholinga cha mbali zitatu chimenecho anayamba ndi mawu akuti “kufikira ife tonse tikafikira.” Za mawu akuti “ife tonse,” buku lina lofotokoza Baibulo limati satanthauza “osati ife tonse, mmodzi ndi mmodzi, payekhapayekha, koma onse pamodzi.” Mwa mawu ena, ifeyo aliyense payekha pamodzi ndi abale athu onse, tifunikira kuyesetsa umo tingathere kuti tipeze cholinga chathu chokhala Mkristu wachikulire. The Interpreter’s Bible limati: “Munthu sangakule mwa iye yekha kufika pa msinkhu wonse wauzimu, monganso mbali ina ya thupi singakule mwa iyo yokha mpaka kukhwima koma imakulira limodzi ndi thupi lonse bwinobwino.” Paulo anakumbutsa Akristu a ku Efeso kuti anafunikira, “pamodzi ndi oyera mtima onse,” kuzindikira ukulu wonse wa chikhulupiriro chimenecho.​—Aefeso 3:18a.

11. (a) Kodi kupita patsogolo mwauzimu sikutanthauza chiyani? (b) Kodi tifunika kuchita chiyani kuti tipite patsogolo?

11 Malinga ndi mawu a Paulo, titha kuona kuti kupita patsogolo mwauzimu sikutanthauza kungodzaza maganizo athu ndi chidziŵitso kapena kukhala ophunzira kwambiri. Mkristu wachikulire si munthu amene amafuna kukopa chidwi cha anzake ndi nzeru zake ayi. Kusiyana ndi zimenezo, Baibulo limati: “Mayendedwe a olungama akunga kuunika kwa mbanda kucha, kunkabe kuwala kufikira usana woti mbe.” (Miyambo 4:18) Inde, “mayendedwe” ndiwo ‘amankabe nawala’ osati munthu ayi. Tikamachita khama kuti tiyendere limodzi ndi chidziŵitso chowalirawalirabe cha Mawu a Mulungu chimene Yehova akupatsa anthu ake, tizipita patsogolo mwauzimu. Choncho kuyendera limodzi ndiko kupita patsogolo, ndipo  tonsefe titha kuchita zimenezi.​—Salmo 97:11; 119:105.

Onetsani “Chipatso cha Mzimu”

12. N’chifukwa chiyani kuonetsa chipatso cha mzimu kuli kofunika pamene tikuyesetsa kupita patsogolo mwauzimu?

12 Pamene kusunga ‘umodzi wa chikhulupiriro ndi wa chidziŵitso cholondola’ kuli kofunika, tifunikanso kuonetsa chipatso cha mzimu wa Mulungu m’mbali iliyonse ya moyo wathu. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti malinga ndi mmene taonera, uchikulire si wobisika koma umaonekera bwino mwa makhalidwe amene angathandize ndi kulimbikitsa ena. Ndithudi, pamene tikuyesetsa kupita patsogolo mwauzimu si cholinga chathu kuti tioneke otsogola kapena apamwamba ayi. Koma pamene tikukula mwauzimu ndi kutsata utsogoleri wa mzimu wa Mulungu, maganizo athu ndi zochita zathu zimasintha kwambiri. Mtumwi Paulo anati: “Muyendeyende ndi Mzimu, ndipo musafitse chilakolako cha thupi.”​—Agalatiya 5:16.

13. Kodi ndi kusintha kotani kumene kuli umboni wosatsutsika wakuti munthu akupita patsogolo?

13 Ndiyeno Paulo anatchula “ntchito za thupi,” zimene zili zambiri komanso “zionekera.” Munthu asanadziŵe zimene Mulungu amafuna, amatsata njira za dziko pa moyo wake ndipo moyo wakewo ungakhale ndi zina mwa zinthu zimene Paulo anatchula: “Dama, chodetsa, kukhumba zonyansa, kupembedza mafano, nyanga, madano, ndewu, kaduka, zopsa mtima, zotetana, magaŵano, mipatuko, njiru, kuledzera, mchezo, ndi zina zotere.” (Agalatiya 5:19-21) Koma pamene apita patsogolo mwauzimu, amayamba kugonjetsa “ntchito za thupi” zoipazi ndi kulola “chipatso cha Mzimu” kutenga malo. Kusintha kumeneku kooneka kwa onse ndi umboni wosatsutsika wakuti munthuyo akupita patsogolo kukhala Mkristu wachikulire.​—Agalatiya 5:22.

14. Fotokozani ziganizo ziŵirizo, “ntchito za thupi” ndi “chipatso cha Mzimu.”

14 Tione ziganizo ziŵirizo, “ntchito za thupi” ndi “chipatso cha Mzimu.” “Ntchito” ndi zochita za munthu. Mwa mawu ena, zimene Paulo analemba kukhala ntchito za thupi ndi zinthu zimene munthu amachita dala kapena posonkhezeredwa ndi thupi lochimwa. (Aroma 1:24, 28; 7:21-25) Koma mawu akuti “chipatso cha Mzimu” akutanthauza kuti munthu amakhala ndi makhalidwe otchulidwawo chifukwa cha mphamvu ya mzimu wa Mulungu osati chifukwa choyesetsa kusintha khalidwe lake kapena kuwongola umunthu wake. Monga momwe mtengo umabalira zipatso pousamalira bwinobwino, munthunso amaonetsa chipatso cha mzimu pamene mzimu woyera  ugwira ntchito mwaufulu pamoyo wake.​—Salmo 1:1-3.

15. N’chifukwa chiyani tifunika kusamalira mbali zonse za “chipatso cha Mzimu”?

15 Mfundo ina yofunika kuiona ndi mmene Paulo anagwiritsira ntchito liwulo, “chipatso” pofotokoza makhalidwe onse abwino amene anatchula. Mzimuwo subala zipatso zosiyanasiyana kuti ife tisankhepo chimene tikufuna ayi. Makhalidwe onsewo omwe Paulo anatchula​—chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso ndi chiletso​—ndi ofunika ndipo onse pamodzi amatheketsa umunthu watsopano wachikristu. (Aefeso 4:24; Akolose 3:10) Chotero, pamene zingatheke kuti ena mwa makhalidwe ameneŵa angaonekere kwambiri pamoyo wathu chifukwa cha umunthu wathu ndi mtima wathu, tifunika kuonetsetsa kuti tikusamalira mbali zonse zimene Paulo anatchula. Tikatero, tidzaonetsa kwambiri umunthu ngati wa Kristu pamoyo wathu.​—1 Petro 2:12, 21.

16. Kodi cholinga chathu n’chiyani tikamayesetsa kukhala Akristu achikulire, ndipo zimenezo zingatheke bwanji?

16 Phunziro lalikulu limene tikutengapo pa zimene Paulo anafotokoza ndi lakuti pamene tikuyesetsa kukhala Akristu achikulire, si cholinga chathu kukhala ndi chidziŵitso choposa kapena kukhala ophunzira kwambiri. Ndiponso sikuti tikhale ndi umunthu wonyaditsa ayi. Koma kuti mzimu wa Mulungu uzigwira ntchito mwaufulu pamoyo wathu. Timakhala achikulire mwauzimu malinga ndi mmene timalabadirira utsogoleri wa mzimu wa Mulungu m’maganizo athu ndi pa zochita zathu. Kodi zimenezi zingatheke bwanji? Tiyenera kutsegula mtima ndi maganizo athu kuti mzimu wa Mulungu uzitilamulira. Zimenezi zimaphatikizapo kufika pamisonkhano yachikristu mokhazikika ndi kutenga nawo mbali. Tifunikanso nthaŵi zonse kuphunzira Mawu a Mulungu ndi kuwasinkhasinkha, kulola mfundo zake zachikhalidwe kutitsogolera pochita zinthu ndi anthu ena ndiponso pa zosankha zathu. Pamenepo, kupita kwathu patsogolo kudzaonekera kwambiri.

Mulungu Alemekezeke ndi Kupita Kwanu Patsogolo

17. Kodi kupita patsogolo kukugwirizana bwanji ndi kulemekeza Atate wathu wakumwamba?

17 Amene amalemekezeka ndi kutamandika ifeyo tikamaonetsa kupita kwathu patsogolo ndi Yehova, Atate wathu wakumwamba amene amatheketsa kuti tikhale achikulire mwauzimu, si ifeyo ayi. Usiku, Yesu asanaphedwe, anauza ophunzira ake kuti: “Mwa ichi alemekezedwa Atate wanga, kuti mubale chipatso chambiri; ndipo mudzakhala akuphunzira anga.” (Yohane 15:8) Ophunzirawo analemekeza Yehova mwa zonse ziŵiri​—chipatso cha mzimu ndi chipatso cha Ufumu chimene utumiki wawo unabala.​—Machitidwe 11:4, 18; 13:48.

18. (a) Kodi ntchito yotuta komanso yosangalatsa imene ikuchitika lero ndi yotani? (b) Kodi kututa kumeneku kumatipatsa ntchito yotani?

18 Lerolino, Yehova wadalitsa anthu ake pamene akuchita ntchito yotuta yauzimu padziko lonse. Kwa zaka zambiri tsopano, chaka ndi chaka anthu pafupifupi 300,000 atsopano amadzipatulira kwa Yehova ndipo amaonetsa kudzipatulira kwawoko mwa kubatizidwa m’madzi. Zimenezi zimatisangalatsa ndipotu zimakondweretsanso mtima wa Yehova.  (Miyambo 27:11) Komabe, kuti atsopano onseŵa apitirize kukondweretsa Yehova ndi kum’tamanda, afunika ‘ayende mwa [Kristu], ozika mizu ndi omangirika mwa Iye, ndi okhazikika m’chikhulupiriro.” (Akolose 2:6, 7) Zimenezi zimapatsa anthu a Mulungu ntchito ya mbali ziŵiri. Mbali inayo ndi yakuti ngati munabatizidwa posachedwa pomwepa, kodi ndinu wokonzeka kuyesetsa kuti ‘kupita kwanu patsogolo kuonekere kwa onse’? Inayo ndi yakuti ngati mwakhala m’choonadi nthaŵi yaitali, kodi ndinu wokonzeka kusenza udindo wosamalira atsopano mwauzimu? Pambali zonse ziŵirizi, n’zachionekere kuti m’pofunika kulimbikira kuti mukhale aakulu msinkhu.​—Afilipi 3:16; Ahebri 6:1.

19. Kodi mungakhale ndi mwayi komanso madalitso otani ngati mukuonetsa kupita patsogolo?

19 Onse amene akulimbikira kuonetsa kuti akupita patsogolo adzapeza madalitso odabwitsa kwambiri. Kumbukirani mawu olimbikitsa amene Paulo ananena atauza Timoteo kuti azipita patsogolo. Anati: “Udzipenyerere wekha, ndi chiphunzitsocho. Uzikhala mu izi; pakuti pochita ichi udzadzipulumutsa iwe wekha ndi iwo akumva iwe.” (1 Timoteo 4:16) Mwa kuchita khama poonetsa kuti mukupita patsogolo, inunso mungakhale ndi mwayi wolemekeza dzina la Mulungu ndi kulandira madalitso ake.

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi uchikulire wauzimu umaonekera motani?

• Kodi ndi chidziŵitso komanso kuzindikira kotani kumene kumasonyeza uchikulire?

• Kodi kuonetsa “chipatso cha Mzimu” kumasonyeza motani kuti munthu akupita patsogolo mwauzimu?

• Kodi tiyenera kukonzekera kuchita chiyani pamene tikuyesetsa kukhala achikulire?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 13]

Kupsa, kapena kukhwima, kumaonekera

[Chithunzi patsamba 15]

Timapita patsogolo mwauzimu mwa kuyendera limodzi ndi choonadi chovumbulidwa

[Chithunzi patsamba 17]

Pemphero limatithandiza kuonetsa “chipatso cha Mzimu”