Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mulungu Wapukuta Misozi Yake

Mulungu Wapukuta Misozi Yake

 Olengeza Ufumu Akusimba

Mulungu Wapukuta Misozi Yake

ANTHU amene amasintha miyoyo yawo kuti agwirizane ndi malamulo ndi mfundo zachikhalidwe za Yehova, amadalitsidwa kwambiri. Ngakhale kuti kusintha n’kovuta nthaŵi zambiri, chithandizo ndi chilimbikitso zilipo. (Salmo 84:11) Nkhani yotsatirayi yochokera Kumwera cha Kum’maŵa kwa Asia ikufotokoza zimenezi.

Pamene Mboni ina ya ku France inali pa tchuti, inalankhula ndi mwini sitolo wina dzina lake Kim * za cholinga cha Yehova padziko lapansi. Mboniyo inaperekanso buku lakuti Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi. Pamene anali kuona bukulo ndi kuŵerenga mwa apo ndi apo, anapeza mawu akuti “adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo.” (Chivumbulutso 21:4) Kim akukumbukira kuti: “Vesi imeneyi inandikhudza kwambiri. Poona mmene ndimaonekera wachimwemwe pogwira ntchito m’sitolo, ndani akanadziŵa kuti ndikafika kunyumba madzulo ndinali kulira kufikira nditagona?” Poulula chifukwa chake anali wachisoni, iye akuti: “Ndinakhala pachibwenzi ndi mwamuna wina kwa zaka 18 ndipo ndinali wosasangalala chifukwa anakana kundikwatira. Ndinafuna kuthetsa ubwenzi wathu, koma popeza ndinakhala naye kwanthaŵi yaitali, ndinali kulephera kuti ndithetse.”

Patapita nthaŵi yochepa, Kim anavomera kuphunzira Baibulo ndi wa Mboni za Yehova wina dzina lake Linh. Kim akuti: “Ndinafunitsitsa kuchita zimene Baibulo limaphunzitsa. Mwachitsanzo, ndinaleka kulambira makolo anga, ngakhale kuti zimenezi zinachititsa kuti achibale anga anditsutse. Ndiponso, ndinayesetsa kuti tilembetse ukwati wathu mwalamulo, koma mwamunayo anakana kutero. M’nthaŵi yovuta imeneyi, Mboni ya ku France ija inali kunditumizirabe zofalitsa zofotokoza Baibulo, ndipo Linh anali kundilimbikitsa kwambiri. Alongo ameneŵa analeza mtima ndipo anandithandiza mwachikondi. Zimenezi zinandithandiza kupirira mpaka pamene ndinatulukira makhalidwe a mwamunayo. Ndinapeza kuti anali ndi ‘akazi’ ena 5 ndi ana 25! Zimenezi zinandilimbikitsa kuti ndilekane naye.

“Kunali kovuta kusiya nyumba yaikulu yabwino kwambiri n’kukakhala m’kanyumba kakang’ono. Ndiponso, mwamunayo anandiumiriza kuti ndibwerere ndikakhale nayenso. Anandiopsezanso kuti ndikakana andilemaza ndi asidi. Mwachithandizo cha Yehova, ndinachita zabwino.” Kim anapitabe patsogolo ndipo kenako anabatizidwa mu April 1998. Ndiponso mkulu wake ndi mng’ono wake pamodzi ndi mwana wake wamwamuna anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova.

Kim akuti: “Ndinali kuganiza kuti moyo wanga udzakhala wopanda chiyembekezo mpaka kalekale. Koma lerolino, ndine wachimwemwe ndipo sindiliranso usiku. Yehova wapukuta kale misozi m’maso mwanga.”

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Tasintha mayina.