Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mulidi Ololera?

Kodi Mulidi Ololera?

 Kodi Mulidi Ololera?

KODI munakwiyapo chifukwa cha khalidwe losayenera la winawake? Kodi mumachitapo kanthu msangamsanga pamene mabwenzi anu a pamtima ayamba kutengeka ndi makhalidwe oipa?

Nthaŵi zina pamafunika kuchitapo kanthu mofulumira ndi molimba mtima kuti tiletse tchimo lalikulu kufalikira. Mwachitsanzo, pamene kuchita zolakwa moonetsera kunatsala pang’ono kuipitsa Aisrayeli m’zaka za m’ma 1400 B.C.E., Pinehasi mdzukulu wa Aroni anachita chinthu chofunika kwambiri pochotsa choipacho. Yehova Mulungu anavomereza zimene anachita, nati: “Pinehasi . . . wabweza kuzaza kwanga pa ana a Israyeli, popeza anachita nsanje ndi nsanje yanga pakati pawo.”​—Numeri 25:1-11.

Zimene anachita Pinehasi zinali zoyenerera poletsa khalidwe loipa kufalikira. Koma bwanji za kuipidwa kosaletseka chifukwa cha zophophonya chabe za anthu ena? Ngati titati tichite zinthu mwaphuma kapena popanda chifukwa chomveka bwino, tingasonyeze kuti sitikonda chilungamo koma kuti ndife osalolera​—munthu amene savomereza n’komwe kuti ena amaphophonya. Kodi n’chiyani chingatithandize kupeŵa mbuna imeneyi?

‘Yehova Amakhululukira Mphulupulu Zako Zonse’

Yehova ndi “Mulungu wansanje (wachangu); Mulungu wosalola aliyense kupikisana naye.” (Eksodo 20:5, NW, mawu am’munsi) Pokhala Mlengi, iye ali ndi ufulu wotilamula kuti tizimulambira mosagaŵanika. (Chivumbulutso 4:11) Komatu, Yehova amalolera zofooka za anthu. Motero wamasalmo Davide anaimba za iye kuti: “Yehova ndiye wa nsoni zokoma ndi wachisomo, wosakwiya msanga, ndi wa chifundo chochuluka. Sadzatsutsana nawo nthawi zonse . . . Sanatichitira monga mwa zolakwa zathu, kapena kutibwezera monga mwa mphulupulu zathu.” Inde, ngati talapa Mulungu ‘amatikhululukira mphulupulu zathu zonse.’​—Salmo 103:3, 8-10.

Chifukwa chakuti Yehova amamvetsa kuti anthu amabadwa ochimwa, iye ‘satsutsa’ ochimwa olapa. (Salmo 51:5; Aroma 5:12) Ndipotu n’cholinga chake kuti achotse uchimo ndi kupanda ungwiro. Kufikira zimenezo zitachitika zonse bwinobwino, m’malo motichitira zinthu monga mwa zochita zathu, mwachifundo Mulungu amatikhululukira pamaziko a nsembe ya dipo ya Yesu Kristu. Palibe aliyense akanakhala woyenera kupulumuka chikhala kuti Yehova sanatichitire chifundo pamene kuli koyenera kutero. (Salmo 130:3) Tikuyamikiratu kwambiri kuti Atate wathu wakumwamba, yemwe moyenerera amafuna kuti tizimulambira iye yekha, ali Mulungu wachifundo.

M’pofunika Kusamala

Popeza kuti Ambuye Mfumu ya chilengedwe chonse ali wololera pochita zinthu ndi anthu opanda ungwiro, kodi ife sitiyenera kuchitanso chimodzimodzi? Kulolera kumatanthauza kuleza mtima pa malingaliro kapena makhalidwe a anthu ena. Kodi ifeyo patokha tili ndi mtima umenewo, kukhala woleza mtima ndi wodziletsa pamene ena alankhula kapena achita zinthu zomwe si zolakwika kwenikweni koma mwinamwake mawuwo kapena kachitidweko n’kosayenera?

N’zoona kuti sitifunika kukhala wololera monyanyira. Mwachitsanzo, pamakhala mavuto oopsa pamene akuluakulu achipembedzo alekerera ansembe amene amagona anyamata ndi atsikana mobwerezabwereza. Mtolankhani wina ku Ireland anati: “Akuluakulu a tchalitchi anangosamutsira [ku malo ena] wansembe wolakwayo polingalira kuti zimene  zinachitikira anazo kunali kungochita tchimo chabe.”

Kodi kungosamutsa munthu woteroyo ndicho chitsanzo cha kulolera koyenera? Ayi ndithu. Tiyerekeze kuti bungwe loyendetsa ntchito zachipatala linalola dokotala wa opaleshoni yemwe sagwira bwino ntchito yake kupitiriza kuchita anthu opaleshoni. Ngakhale kuti amapha kapena kulemaza odwala amene amawachita opaleshoniwo, bungwelo limangomusamutsa kuchoka pa chipatala china n’kumupititsa pa china. Lingaliro lolakwika la kufuna kugwirizanitsa anthu ogwira ntchitoyi lingachititse “kulolera” koteroko. Koma bwanji za anthu amene anamwalira kapena amene analumala kwambiri chifukwa cha khalidwe lonyalanyaza ndiponso laupandulo?

Pamakhalanso ngozi ngati munthu salolera kwenikweni. Pamene Yesu anali padziko lapansi, Ayuda ena otchedwa Azelote molakwa anali kugwiritsa ntchito chitsanzo cha Pinehasi poyesa kulungamitsa zochita zawo. Zochita zina zonkitsa kwambiri za Azelote ena zinali “kusakanikirana ndi khamu la anthu mu Yerusalemu panthaŵi ya mapwando ndi panthaŵi zinanso pamene anthu ambiri amasonkhana ndiyeno amabaya adani awo ndi mipeni pamene adaniwo sanali kuyembekezera kuti pangachitike zoterozo.”

Monga Akristu, sitingachite kuthana nawo zenizeni amene satisangalatsa monga ankachitira Azelote. Komano, kodi pamlingo winawake kusalolera kumatichititsa kuwavutitsa mwa njira inayake anthu omwe sitigwirizana nawo, mwinamwake mwa kuwanyoza? Ngati tilidi ololera, sitidzalankhula mawu oŵaŵa oterowo.

M’zaka zoyambira pa 100 B.C.E. kufika pa 1 B.C.E., Afarisi anali gulu lina la anthu osalolera. Nthaŵi zonse anali kutsutsa anzawo ndipo sanali kuvomereza kuti munthu amalakwa. Afarisi onyadawo anali kunyoza anthu wamba; ankawanena kuti anali ‘otembereredwa.” (Yohane 7:49) Panali pomveka kuti Yesu anatsutsa anthu odzilungamitsa otero kuti: “Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! chifukwa mupereka limodzi la magawo khumi la timbewu tonunkhira, ndi katsabola, ndi la chitowe, nimusiya zolemera za chilamulo, ndizo kuweruza kolungama, ndi kuchitira chifundo, ndi chikhulupiriro; koma zijazo munayenera kuzichita, osasiya izi zomwe.”​—Mateyu 23:23.

Mwa kunena zimenezi Yesu sanatanthauze kuti Chilamulo cha Mose n’chosafunika kwenikweni. Iye anali kungosonyeza kuti mbali “zolemera,” kapena kuti zofunika kwambiri, za Chilamulo zinafuna kugwiritsa ntchito Chilamulocho molingalira bwino ndi mwachifundo. Komatu Yesu ndi ophunzira ake anaoneka osiyana kwabasi ndi Afarisi ndi Azelote osalolerawo!

Yehova Mulungu ngakhalenso Yesu Kristu savomereza choipa. Posachedwapa ‘adzabwezera chilango kwa iwo osamudziŵa Mulungu, ndi iwo osamvera Uthenga Wabwino wa Ambuye wathu Yesu.’ (2 Atesalonika 1:6-10) Komabe, ngakhale ndi wachangu pochita chilungamo, Yesu salephera kusonyeza kuleza mtima, chifundo, ndi nkhaŵa yachikondi ya Atate wake wakumwamba kwa onse ofuna kuchita zolungama. (Yesaya 42:1-3; Mateyu 11:28-30; 12:18-21) Yesu anatipatsatu chitsanzo chabwino zedi!

Loleranani Moleza Mtima

Ngakhale kuti tingakhale achangu kwambiri pochita cholungama, n’kofunika kugwiritsa ntchito uphungu wa mtumwi Paulo wakuti: “Kulolerana wina ndi mnzake, ndi kukhululukirana eni okha, ngati wina ali nacho chifukwa pa mnzake; monganso Ambuye anakhululukira inu, teroni inunso.” (Akolose 3:13; Mateyu 6:14, 15) Kulolera kumafuna kupirira zophophonya ndi zolakwa za ena m’dziko lopanda ungwiroli. Tifunika kulingalira mofatsa pa zimene timayembekezera kwa ena.​—Afilipi 4:5.

Kukhala ololera sikutanthauza m’pang’ono pomwe kuti mukuvomereza cholakwa kapena kuti simukuona zophophonya. Mbali zina za mmene wokhulupirira mnzathu amaganizira kapena amachitira zinthu zingakhale zosemphana  ndi miyezo ya Yehova. Munthuyo angakhale kuti sanapatuke kwambiri koti Mulungu n’kumukana, koma zimenezo zingachenjeze kuti pakufunika kusintha. (Genesis 4:6, 7) Kumakhalatu kumukonda kwambiri wolakwayo pamene awo oyeneretsedwa mwauzimu ayesa kumubweza mu mzimu wa chifatso. (Agalatiya 6:1) Komabe kuti muthe kuchita zimenezi bwino lomwe, m’pofunika kukhala wodera nkhaŵa m’malo mokhala ndi mzimu wosuliza.

“Ndi Chifatso ndi Mantha”

Nanga bwanji zoleza mtima ndi anthu amene tikusiyana nawo malingaliro pa chipembedzo? Ku Ireland mu Masukulu a Anthu Onse omwe anayambika mu 1831 anaikamo “Phunziro la Aliyense” lomwe limati: “Yesu Kristu sanakonze zoti anthu azikakamizidwa mwachiwawa kuloŵa chipembedzo chake. . . . Kukangana ndi anansi athu ndiponso kuwavutitsa sindiyo njira yowatsimikizira kuti ifeyo tikulondola ndipo iwo akulakwitsa. Zidzangowatsimikizira kuti tilibe mzimu wachikristu.”

Yesu anaphunzitsa ndi kuchita zinthu mwa njira yomwe inakopera anthu ku Mawu a Mulungu, ifenso tiyenera kutero. (Marko 6:34; Luka 4:22, 31, 32; 1 Petro 2:21) Pokhala munthu wangwiro yemwe Mulungu anamupatsanso kuzindikira kwapadera, Yesu ankadziŵa zam’mtima mwa munthu. Motero pamene kunali koyenera, Yesu ankatha kunena mawu oŵaŵa kwa adani a Yehova. (Mateyu 23:13-33) Pochita zimenezi sikuti anali wosalolera.

Ife mosiyana ndi Yesu sitidziŵa zam’mtima mwa munthu. Choncho tifunika kutsatira uphungu wa mtumwi Petro wakuti: “Mumupatulikitse Ambuye Kristu m’mitima yanu; okonzeka nthaŵi zonse kuchita chodzikanira pa yense wakukufunsani chifukwa cha chiyembekezo chili mwa inu, komatu ndi chifatso ndi mantha.” (1 Petro 3:15) Monga atumiki a Yehova, tiyenera kuteteza zimene timakhulupirira chifukwa n’zozikidwa kwambiri pa Mawu a Mulungu. Koma tifunika kutero m’njira imene imalemekeza ena limodzinso ndi zikhulupiriro zawo. Paulo analemba kuti:“Mawu anu akhale m’chisomo, okoleretsa, kuti mukadziŵe inu mayankhidwe anu a kwa yense akatani.”​—Akolose 4:6.

Mu ulaliki wake wotchuka wa pa phiri Yesu anati: “Zinthu zilizonse mukafuna kuti anthu achitire inu, inunso muwachitire iwo zotero.” (Mateyu 7:12) Motero tiyeni tizipirirana ndi kusonyeza ulemu kwa anthu omwe timawalalikira uthenga wabwino. Mwa kugwirizanitsa changu chathu pochita chilungamo ndi kulolera kofotokozedwa m’Baibulo, tidzasangalatsa Yehova ndipo tidzakhaladi ololera.

[Chithunzi patsamba 23]

Pewani mtima wosalolera wa Afarisi

[Chithunzi patsamba 23]

Yesu anasonyeza mzimu wololera wa Atate ake. Kodi inunso m’mausonyeza?