Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Muli ndi Mzimu Wosafa?

Kodi Muli ndi Mzimu Wosafa?

 Kodi Muli ndi Mzimu Wosafa?

“LEMBA lililonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m’chilungamo,” analemba motero mtumwi Paulo. (2 Timoteo 3:16) Inde, Baibulo ndi buku la choonadi lochokera kwa Mulungu woona, Yehova.​—Salmo 83:18.

Popeza kuti Yehova ndiye Mlengi wa zonse, kuphatikizapo anthu, amadziŵa zimene zimachitika tikamwalira. (Ahebri 3:4; Chivumbulutso 4:11) Ndipo m’Baibulo, Mawu amene iye anauzira, amapereka mayankho olondola ndiponso okhutiritsa a mafunso okhudza moyo munthu akamwalira.

Kodi Mzimu N’chiyani?

M’Baibulo, mawu amene anawatembenuza kuti “mzimu” kwenikweni amatanthauza “mpweya.” Koma amatanthauzanso zambiri osati kupuma chabe. Mwachitsanzo, wolemba Baibulo Yakobo anati: “Thupi lopanda mzimu lili lakufa.” (Yakobo 2:26) Choncho, mzimu ndi umene umachititsa thupi kukhala lamoyo.

Mphamvu yopatsa moyo imeneyi si mpweya umene timapuma umene umaloŵa m’mapapu ayi. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti munthu akaleka kupuma, maselo a thupi amakhalabe ali moyo kwa kanthaŵi​—“kwa mphindi zingapo,” malinga ndi buku la maumboni la The World Book Encyclopedia. N’chifukwa chake zimatheka kum’tsitsimutsa munthu. Koma mphamvu ya moyo ikachoka m’maselo a thupi, n’kosatheka kubwezeretsa moyo. Zikatere, mpweya uliwonse sungabwezere moyo ngakhale selo limodzi la thupi. Choncho mzimu ndi mphamvu ya moyo yosaoneka imene imachititsa maselo ndiponso munthu kukhala ndi moyo. Ndipo kupuma kumachirikiza mphamvu ya moyo imeneyi.​—Yobu 34:​14, 15.

Kodi mzimu umenewu umagwira ntchito mwa anthu okha? Baibulo limatipatsanso yankho lolondola pa funso limeneli. Mfumu yanzeru Solomo inavomereza kuti anthu ndi nyama “onsewo ali ndi mpweya [“mzimu,” NW] umodzi.” Ndiyeno anafunsa kuti: “Ndani adziŵa mzimu wa ana a anthu wokwera kumwamba, ndi mzimu wa nyama wotsikira kunsi ku dziko?” (Mlaliki 3:​19-21) Motero, onse, anthu ndi nyama ali ndi mzimu. Kodi zimenezi zingatheke bwanji?

 Mzimu, kapena mphamvu ya moyo, tingauyerekeze ndi mphamvu ya magetsi imene imaloŵa m’makina kapena chiwiya chilichonse chamagetsi. Mphamvu ya magetsi yosaonekayo ingagwire ntchito zosiyanasiyana, zikumadalira mtundu wa chiwiya chimene ikupatsa mphamvu. Mwachitsanzo, mphamvu ya magetsi ingatenthetse chitofu, ingachititse kompyuta kutsegula mapulogalamu ake, ndiponso ingachititse wailesi yakanema kuonetsa zithunzi ndi kutulutsa mawu. Ngakhale zili choncho, mphamvu ya magetsiyo sikhala ndi maonekedwe a chiwiya chimene ikupatsa mphamvu. Imangokhala mphamvu chabe basi. Mofananamo, mphamvu ya moyo ilibe mikhalidwe ya cholengedwa chimene imachirikiza moyo wake. Ilibe mikhalidwe yaumunthu ndipo singaganize chilichonse. Anthu ndi nyama “ali ndi mpweya [“mzimu”] umodzi.” (Mlaliki 3:19) Choncho, munthu akamwalira, mzimu wake supitiriza kukhala ndi moyo kumalo ena monga cholengedwa chauzimu.

Nangano, kodi mkhalidwe wa akufa ndi wotani? Ndipo n’chiyani chimachitikira mzimu munthu akamwalira?

“Kufumbiko Udzabwerera”

Pamene munthu woyamba, Adamu, mwadala sanamvere lamulo la Mulungu, anauzidwa kuti: “M’thukuta la nkhope yako udzadya chakudya, kufikira kuti udzabwerera kunthaka: chifukwa kuti mmenemo unatengedwa: chifukwa kuti ndiwe fumbi, ndi kufumbiko udzabwerera.” (Genesis 3:19) Kodi Adamu anali kuti Yehova asanamulenge kuchokera kufumbi? Sanali kwina kulikonse! Iye kunalibeko. Chotero pamene Yehova Mulungu ananena kuti Adamu ‘adzabwerera kufumbi,’ iye anatanthauza kuti Adamu adzafa n’kukhala dothi. Adamu sakanasamukira kumalo a mizimu. Pomwalira iye akakhalanso wopanda moyo. Chilango chake chinali imfa​—kusakhala wamoyo​—osati kusamukira kumalo ena.​—Aroma 6:23.

Bwanji za anthu ena amene anamwalira? Mlaliki 9:​5, 10 amamveketsa bwino mkhalidwe wa akufa. Pamenepo timaŵerenga kuti: “Akufa sadziŵa kanthu bi. . . . Mulibe ntchito ngakhale kulingirira ngakhale kudziŵa, ngakhale nzeru, kumanda.” Choncho, imfa ndiyo kusakhalako. Wamasalmo analemba kuti munthu akamwalira, “mpweya [“mzimu”] wake uchoka, abwerera kumka ku nthaka yake; tsiku lomwelo zotsimikiza mtima zake zitayika.”​—Salmo 146:4.

Inde, akufa sali ndi moyo kwinakwake. Sangadziŵe kanthu. Sangakuoneni, sangakumveni, ndiponso sangalankhule nanu. Sangakuthandizeni kapena kukuvulazani. Ndithudi, simufunika kuopa akufa. Koma kodi ndi  motani mmene mzimu ‘umachokera’ mwa munthu pomwalira iye?

Mzimu ‘Ubwerera kwa Mulungu’

Baibulo limanena kuti munthu akamwalira, ‘mzimu ubwerera kwa Mulungu amene anaupereka.’ (Mlaliki 12:7) Kodi amatanthauza kuti mzukwa umakwera ndi kudutsa mlengalenga mpaka kukafika kwa Mulungu? Kutalitali! Baibulo likamati ‘kubwerera’ silitanthauza kuchoka kwenikweni pamalo ena kupita kwina. Mwachitsanzo, Aisrayeli osakhulupirika anawauza kuti: “Bwererani kudza kwa Ine, ndipo Ine ndidzabwerera kwa inu, ati Yehova wa makamu.” (Malaki 3:7) ‘Kubwerera’ kwa Aisrayeli kwa Mulungu kunatanthauza kusiya njira zawo zoipa ndi kuyambanso kutsatira njira zolungama za Mulungu. Ndipo ‘kubwerera’ kwa Yehova kwa Aisrayeli kunatanthauza kuwakomeranso mtima anthu ake. Mbali zonse ziŵirizi, ‘kubwerera’ kunali kusintha maganizo, osati kuchoka kwenikweni pamalo ena kupita kwina.

Mofananamo, pamene mzimu ‘ubwerera’ kwa Mulungu sikuti umachokadi padziko lapansi kupita kumwamba ayi. Mphamvu ya moyo ikachoka mwa munthu, Mulungu yekha ndi amene angathe kuibwezeretsa mwa iye. Motero, mzimu ‘ubwerera kwa Mulungu’ m’lingaliro lakuti ngati munthuyo ati adzakhale ndi moyo m’tsogolo, zikudalira Mulungu basi.

Mwachitsanzo, talingalirani zimene Malemba amanena za imfa ya Yesu Kristu. Wolemba Uthenga Wabwino Luka anati: “Yesu anafuula ndi mawu aakulu, anati, Atate, m’manja mwanu ndipereka mzimu wanga. Ndipo pakutero anapereka mzimu wake.” (Luka 23:46) Pamene mzimu wa Yesu unachoka, iye sananyamuke ulendo kupita kumwamba. Yesu sanauke kwa akufa mpaka tsiku lachitatu. Ndipo panapita masiku ena 40 asanakwere kumwamba. (Machitidwe 1:​3, 9) Komabe pomwalira, Yesu mwachidaliro anaika mzimu wake m’manja mwa Atate ake, ali ndi chikhulupiriro chonse kuti Yehova adzabwezeretsa moyo wake.

Inde, Mulungu ndi amene angabwezeretse moyo wa munthu. (Salmo 104:30) Zimenezitu zimatipatsa chiyembekezo chachikulu!

Chiyembekezo Chodalirika

Baibulo limati: “Ikudza nthaŵi, imene onse ali m’manda [“achikumbukiro,” NW] adzamva mawu ake [a Yesu ], nadzatulukira.” (Yohane 5:​28, 29) Inde, Yesu Kristu analonjeza kuti onse amene ali m’chikumbumtima cha Yehova adzauka, kapena kuti adzakhalanso ndi moyo. Ndithudi, ena mwa iwo adzakhala anthu amene atsatira njira yolungama monga atumiki a Yehova. Koma anthu ena miyandamiyanda anamwalira asanapeze mwayi wosankha kutsatira miyezo yolungama ya Mulungu. Mwina sanadziŵe zimene Yehova amafuna kapena analibe nthaŵi yokwanira kuti asinthe. Mulungu akuwakumbukiranso anthu otere ndipo adzawaukitsa. Tikutero chifukwa Baibulo limati: “Kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama.”​—Machitidwe 24:15.

Lerolino, dziko ladzala ndi udani ndi nkhondo, chiwawa ndi kukhetsa mwazi, kuipitsa dziko ndi matenda. Ngati akufa atawaukitsira padziko ngati limeneli, ndiye kuti chimwemwe chawo chingakhale chakanthaŵi. Koma Mlengi walonjeza kuti posachedwapa achotsa dziko lilipoli limene Satana Mdyerekezi akulilamulira. (Miyambo 2:​21, 22; Danieli 2:44; 1 Yohane 5:19) Ndiyeno, “dziko latsopano” la anthu olungama lidzafikadi.​—2 Petro 3:13.

Nthaŵi imeneyo “wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.” (Yesaya 33:24) Imfa adzaichotsa, chifukwa Mulungu “adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa; zoyambazo zapita.” (Chivumbulutso 21:4) N’chiyembekezo chosangalatsatu chimenechi kwa amene “ali m’manda achikumbukiro”!

Pochotsa kuipa padziko lapansi, Yehova adzawononga oipa osati olungama. (Salmo 37:​10, 11; 145:20) Ndithudi, “khamu lalikulu” la anthu “ochokera mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe” adzapulumuka “chisautso chachikulu” chimene chidzawononga  dziko loipa lilipoli. (Chivumbulutso 7:​9-14) Choncho, padzakhala anthu ambiri olandira anthu amene adzauka kwa akufa.

Kodi mukulakalaka kudzaonanso anthu amene munali kuwakonda amene anamwalira? Kodi mukufuna kudzakhala ndi moyo kosatha m’Paradaiso padziko lapansi? Ndiyetu mufunika kuzidziŵa molondola zimene Mulungu akufuna ndi zolinga zake. (Yohane 17:3) Yehova akufuna kuti “anthu onse apulumuke, nafike pozindikira choonadi.”​—1 Timoteo 2:​3, 4.

[Chithunzi patsamba 4]

“Chifukwa kuti ndiwe fumbi, ndi kufumbiko udzabwerera”

[Chithunzi patsamba 5]

Mzimu tingauyerekeze ndi mphamvu ya magetsi

[Chithunzi patsamba 7]

Kuuka kwa akufa kudzadzetsa chimwemwe chosatha