Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Anapeza Zosoŵa Zake Zauzimu

Anapeza Zosoŵa Zake Zauzimu

 Olengeza Ufumu Akusimba

Anapeza Zosoŵa Zake Zauzimu

CHILUMBA cha Cyprus chili kumpoto cha kum’maŵa kwenikweni m’nyanja ya Mediterranean. M’nthaŵi za m’Baibulo, chilumba cha Cyprus chinali chotchuka ndi miyala ya mkuwa ndi matabwa abwino kwambiri. Paulo ndi Barnaba analalikirako uthenga wabwino wa Ufumu pa ulendo wawo woyamba waumishonale. (Machitidwe 13:4-12) Lerolino, uthenga wabwino ukupindulitsabe anthu ambiri ku Cyprus. Ndi mmene zilili ndi Lucas, wazaka zoposa 40. Iye anati:

“M’banja lathu tinalimo ana asanu ndi aŵiri, ndipo tinkakhala pafamu ya ng’ombe. Kuyambira ndili wamng’ono, ndinkakonda kuŵerenga. Buku lomwe ndinkalikonda linali Baibulo laling’ono la Malemba Achigiriki Achikristu. Pamene ndinali ndi zaka khumi, ine ndi anzanga ena tinapanga kagulu kophunzira Baibulo. Koma gululo silinakhalitse chifukwa akuluakulu ena m’mudzimo ankati ndife opanduka.

“Pambuyo pake, ndikuphunzira sukulu ku United States, ndinakumana ndi anthu azipembedzo zosiyanasiyana. Zimenezo, zinandipatsanso chidwi cha zinthu zauzimu. Kwa masiku ambiri, ndinkaŵerenga za zipembedzo zosiyanasiyana mu laibulale ya pa yunivesite. Ndinapitanso kumapemphero a matchalitchi osiyanasiyana, koma ngakhale ndinayesetsa, sindinakhutirebe mwauzimu.

“Nditamaliza maphunziro, ndinabwerera ku Cyprus komwe ndinakhala woyang’anira ntchito yofufuza zamankhwala. Munthu wachikulire wa Mboni za Yehova, dzina lake Antonis, ankakonda kubwera kuntchito kwanga kudzacheza nane. Koma atsogoleri a tchalitchi cha Greek Orthodox anadziŵa za kucheza kwathu.

“Posapita nthaŵi, mbusa wina anabwera kudzandiona. Anandiuza kuti ndisamacheze ndi Mboni za Yehova. Pakuti kuyambira ndili mwana ndinaphunzitsidwa kuti tchalitchi cha Greek Orthodox chimaphunzitsa choonadi, ndinavomereza ndipo ndinasiya kucheza ndi Antonis n’kuyamba kuphunzitsidwa Baibulo ndi mbusayo. Komanso ndinayendera nyumba zambiri za agulupa ku Cyprus. Ndinapitanso kumpoto kwa dziko la Greece kukaona phiri la Athos, phiri lomwe tchalitchi cha Orthodox chimati n’lopatulika kwambiri. Komabe sindinapeze mayankho a mafunso anga a m’Baibulo.

“Ndiyeno ndinapemphera kwa Mulungu kuti andithandize kupeza choonadi. Patapita kanthaŵi pang’ono, Antonis anabweranso kuntchito kwanga, ndipo ndinaona kuti linali yankho la pemphero langa. Kenako ndinaleka kupita kwa mbusa uja n’kuyamba kuphunzira Baibulo ndi Antonis. Ndinapitiriza kuphunzira zambiri ndipo mu October 1997, ndinasonyeza kudzipatulira kwa Yehova mwa kubatizidwa m’madzi.

“Panthaŵiyo, mkazi wanga ndi ana anga aakazi aŵiri, woyamba wazaka 14 ndi wachiŵiri wazaka 10, sanakondwere nazo. Koma chifukwa cha khalidwe langa labwino, mkazi wanga anabwera ku msonkhano pa Nyumba ya Ufumu. Kukoma mtima ndi chidwi chomwe Mboni zinamusonyeza, zinamukhudza mtima kwambiri. Kugwiritsa ntchito Baibulo kwa Mboni, kunam’chititsa chidwi koposa. Mapeto ake, mkazi wanga ndi ana anga akazi aŵiri aja, anavomera kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Zinalitu zosangalatsa kwambiri pamene atatuwa anabatizidwa pa Msonkhano Wachigawo wakuti “Mawu a Ulosi a Mulungu” mu 1999!

“Inde, chilakolako changa cha choonadi chinakwaniritsidwa. Tsopano banja lathu lonse, ine, mkazi wanga, ndi ana athu anayi, ndife ogwirizana kulambira Yehova koyera.”