Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zoyenera Kuchita Ngati Mukuvutika Maganizo

Zoyenera Kuchita Ngati Mukuvutika Maganizo

 Zoyenera Kuchita Ngati Mukuvutika Maganizo

● Asafu anadandaula kuti: “Indedi, ndinayeretsa mtima wanga kwachabe, ndipo ndinasamba m’manja mosalakwa; popeza andisautsa tsiku lonse, nandilanga m’mamawa monse.”​—Salmo 73:13, 14.

● Baruki anadandaula nati: “Kalanga ine tsopano! pakuti Yehova wawonjezera chisoni pa zowawa zanga; ndalema ndi kubuula kwanga, sindipeza kupuma.”​—Yeremiya 45:3.

● Naomi analira kuti: “Wamphamvuyonse anandichitira zowawa ndithu. Ndinachoka pano wolemera, nandibwezanso kwathu Yehova wopanda kanthu; munditcheranji Naomi, popeza Yehova wandichitira umboni wakunditsutsa, ndi Wamphamvuyonse wandichitira chowawa?”​—Rute 1:20, 21.

BAIBULO lili ndi zitsanzo zambiri za olambira Yehova okhulupirika omwe panthaŵi ina anali ndi maganizo ofoola kwambiri. N’zoonadi kuti monga anthu opanda ungwiro, tonsefe timakhala ndi maganizo oterowo nthaŵi ndi nthaŵi. Ena a ife sitichedwa kugwa mphwayi mwinanso kuphatikizapo kudzimvera chisoni kuposa ena chifukwa cha mavuto omwe tinakumana nawo.

Koma ngati osachitapo kanthu, maganizo ameneŵa angawononge ubwenzi wathu ndi anzathu ndiponso ndi Yehova Mulungu. Mayi wina wachikristu yemwe sachedwa kudzimvera chisoni anati: “Kwanthaŵi yaitali, anzanga a mu mpingo akandiitana kuti ndikacheze nawo, ndimakana chifukwa chodzimva kuti ndine wosayenera kuyanja nawo.” Maganizo ameneŵa angadzetse mavuto aakulu m’moyo wa munthu. Kodi mungawathetse motani?

Muyandikireni Yehova

Mu Salmo 73, Asafu anafotokoza nkhaŵa yake moona mtima. Poyerekezera moyo wake ndi wa anthu oipa omwe anali kutukuka, iye anachita nsanje. Anaona kuti anthu osapembedza Mulungu anali odzikuza ndi achiwawa, koma sanali kulangidwa. Ndiyeno Asafu anakayikira kufunika kokhala ndi moyo wachilungamo.​—Salmo 73:3-9, 13, 14.

Kodi inuyo, mofanana ndi Asafu, mwaona anthu ochita zoipa moonetsera akutukuka? Kodi Asafu anathetsa motani maganizo ake ogwetsa mphwayiwo? Iye akupitiriza kunena kuti: “Ndinayesa kudziŵitsa ichi, ndinavutika nacho; mpaka ndinaloŵa m’zoyera za Mulungu, ndi kulingalira chitsiriziro chawo.” (Salmo 73:16, 17) Asafu anatsata njira zoyenera mwa kupemphera kwa Yehova. Tikagwiritsa ntchito mawu amene mtumwi Paulo ananena pambuyo pake, Asafu anapondereza ‘chibadwidwe cha umunthu’ mwa kudzutsa ‘munthu wauzimu’ mu mtima mwake. Ndi maganizo auzimu atsopano, anamvetsetsa kuti Yehova amada kuipa ndiponso kuti panthaŵi yake, oipa adzalangidwa.​—1 Akorinto 2:14, 15.

 N’kofunikatu kwambiri kulola Baibulo kuti likuthandizeni kudziŵa zoona zenizeni za moyo! Yehova akutikumbutsa kuti amaona zomwe oipa amachita. Baibulo limaphunzitsa kuti: “Musanyengedwe; Mulungu sanyozeka; pakuti chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta. . . . Koma tisaleme pakuchita zabwino.” (Agalatiya 6:7-9) Yehova adzaika oipa “poterera”; ‘adzawagwetsa ndi kuwawononga.’ (Salmo 73:18) Chilungamo cha Mulungu chidzapambana pomalizira pake.

Kudya pagome lauzimu la Yehova mosalekeza ndi kuyanjana ndi anthu a Mulungu, kudzakuthandizani kulimbitsa chikhulupiriro chanu ndi kugonjetsa kufooketsedwa kapena maganizo ena odziona ngati wosafunika. (Ahebri 10:25) Mwa kum’yandikira Mulungu monga anachitira Asafu, mwachikondi angakuthandizeni. Asafu akupitiriza kuti: “Ndikhala ndi Inu chikhalire: Mwandigwira dzanja langa la manja. Mudzanditsogolera ndi uphungu wanu, ndipo mutatero, mudzandilandira mu ulemerero.” (Salmo 73:23, 24) Mkristu wina yemwe anazunzidwa kwambiri ali mwana anaona kuti mawu awa ali anzeru. Iye anati: “Moyo wanga unasintha chifukwa choyanjana kwambiri ndi mpingo. Ndinaona bwino lomwe kuti akulu achikristu ndi achikondi, osati apolisi, koma abusa.” Inde, akulu achikristu achifundo amagwira ntchito yaikulu pothetsa maganizo owononga.​—Yesaya 32:1, 2; 1 Atesalonika 2:7, 8.

Mverani Malangizo a Yehova

Baruki, yemwe anali mlembi wa mneneri Yeremiya, anadandaula chifukwa cha kutopetsa kwa ntchito yake. Koma mokoma mtima, Yehova anauza Baruki zoona zake. “Kodi udzifunira wekha zinthu zazikulu? Usazifune; pakuti, taona, ndidzatengera zoipa pa anthu onse, ati Yehova: koma moyo wako ndidzakupatsa iwe ngati chofunkha m’malo monse mmene mupitamo.”​—Yeremiya 45:2-5.

Mosapita m’mbali, Yehova anafotokoza kuti kudzifunira zinthu zazikulu ndiko kunapangitsa Baruki kutaya mtima. Baruki sakanapeza chimwemwe m’ntchito yomwe Mulungu anam’patsa ngati panthaŵiyo, anali kudzifunira zinthu zazikulu. Inunso mudzaona kuti njira yothandiza kwambiri kuti tisagwe ulesi, ndiyo kupeŵa zojejemetsa ndi kuyamikira mtendere wa mumtima pokhutira ndi kutumikira Mulungu.​—Afilipi 4:6, 7.

Mayi wamasiye Naomi, sanalole madandaulo kum’fooketsa mwamuna wake ndi ana ake aamuna aŵiri atamwalira ku dziko la Amoabu. Komabe zikusonyeza kuti kwa kanthaŵi, anada nkhaŵa za iye mwini ndi apongozi ake aakazi aŵiri. Powapempha kuti apite, Naomi anati: “Chandiwawa koposa chifukwa cha inu popeza dzanja la Yehova landitulukira.”  Komanso pamene anafika ku Betelehemu anaumirira kuti: “Musanditcha Naomi [Wosangalatsa], munditche Mara [Wokhumudwa]; pakuti Wamphamvuyonse anandichitira zowawa ndithu.”​—Rute 1:13, 20.

Komabe Naomi sanadzipatule n’kumangokhala yekha m’madandaulo. Sanadzipatule kwa Yehova ndi anthu ake. Ali ku Moabu, anamva kuti “Yehova adasamalira anthu ake ndi kuwapatsa chakudya.” (Rute 1:6) Anadziŵa kuti komwe kunali anthu a Yehova ndiwo malo abwino kwambiri oyenera kukhalako. Pambuyo pake, Naomi ndi mpongozi wake Rute anabwerera ku Yuda ndipo mwaluntha, analangiza Rute zoyenera kuchita kwa mbale wa mwamuna wake, Boazi, yemwe anali womuombolera choloŵa.

Masiku anonso, okhulupirika omwe amuna kapena akazi awo anamwalira, akuthetsa madandaulo mwa kukhala otanganidwa mu mpingo wachikristu. Monga Naomi, ndi mtima wonse akusamala nkhani zauzimu, kuŵerenga Mawu a Mulungu tsiku ndi tsiku.

Phindu Lotsatira Nzeru ya Mulungu

Nkhani za m’Baibulo zimenezi zikutipatsa nzeru pa zimene munthu angachite ndi zotsatira za kuvutika maganizo. Asafu anafuna chithandizo pa chihema cha Yehova ndi kuyembekezera chitsogozo chake modekha. Baruki anagwiritsa ntchito uphungu ndi kupewa zododometsa. Naomi anali wotanganidwa pakati pa anthu a Yehova, kum’konzekeretsa mtsikanayo Rute kulandira choloŵa chake polambira Mulungu woona.​—1 Akorinto 4:7; Agalatiya 5:26; 6:4.

Mungathetse malingaliro ofoola ndi ena osayenera mwa kulingalira kupambana kumene Yehova wapatsa anthu ake, payekhapayekha ndiponso monga gulu. Kuti zimenezi zitheke, lingalirani chikondi chopambana cha Yehova pokupatsani dipo. Yamikirani chikondi chenicheni cha abale achikristu. Ganizirani kwambiri za mmene moyo wanu udzakhalira m’dziko latsopano la Mulungu lomwe lili pafupi kudzali. Ndipo vomerezanani ndi Asafu kuti: “Kundikomera kuyandikiza kwa Mulungu: ndimuyesa Ambuye Yehova pothawirapo ine, kuti ndifotokozere ntchito zanu zonse.”​—Salmo 73:28.