Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Tinkachitira Zinthu Limodzi

Tinkachitira Zinthu Limodzi

 Mbiri ya Moyo Wanga

Tinkachitira Zinthu Limodzi

YOSIMBIDWA NDI MELBA BARRY

Pa July 2, 1999, ine ndi mwamuna wanga tinali pamsonkhano waukulu wa Mboni za Yehova, monga tinali kuchitira kwa zaka 57 zomwe tinali m’banja. Lachisanu, Lloyd anali kukamba nkhani yomaliza pamsonkhano wachigawo umenewo ku Hawaii. Mwadzidzidzi, anagwa. Ngakhale kuti anthu anayesetsa kuti am’tsitsimule, iye anamwalira. *

NDIKUTHOKOZA kwambiri abale ndi alongo achikristu a ku Hawaii amene anandithandiza kupirira panthaŵi yovutayi. Lloyd anali atakhudza miyoyo ya ambiri mwa iwo ndiponso ya anthu ena ambiri padziko lonse.

Kwa zaka pafupifupi ziŵiri kuchokera pamene anamwalira, ndakhala ndikuganizira za moyo wa mtengo wapatali womwe tinali nawo tili amishonale m’mayiko achilendo, ndiponso palikulu la padziko lonse la Mboni za Yehova ku Brooklyn, New York. Ndimakumbukiranso pamene ndinali wamng’ono ku Sydney m’dziko la Australia ndiponso mavuto omwe ine ndi Lloyd tinakumana nawo pofuna kukwatirana kumayambiriro kwa nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse. Komabe, bwanji ndikuuzeni kaye za mmene ndinakhalira Mboni, ndiponso kukumana ndi Lloyd mu 1939.

Mmene Ndinakhalira Mboni

Makolo anga a James ndi a Henrietta Jones anali achikondi ndi osamalira ana. Ndinamaliza sukulu mu 1932 ndili ndi zaka 14 zokha. Panthaŵiyo, dziko linali pa Umphawi Wadzaoneni. Ndinayamba ntchito kuti ndithandize banja lathu ndi ang’ono anga aŵiri. Pazaka zochepa, ndinali pantchito yamalipiro abwino ndipo ndinali kuyang’anira atsikana ena.

Panthaŵiyo, amayi analandira mabuku ofotokoza Baibulo kwa munthu wina wa Mboni za  Yehova ndipo mwamsanga anakhulupirira kuti apeza choonadi. Izi zinachitika mu 1935. Ena tonse m’banjamo tinaganiza kuti azungulira mutu. Koma tsiku lina, ndinaona kabuku kamutu wakuti Where Are the Dead? (Kodi Akufa Ali Kuti?) ndipo ndinachita chidwi kwambiri ndi mutuwo. Choncho, ndinaŵerenga kabukuko mobisa. Kusintha kwa zinthu kunali komweko! Nthaŵi yomweyo ndinayamba kupita kumsonkhano wapakati pa mlungu wotchedwa Chitsanzo cha Phunziro limodzi ndi amayi. Kabuku kakuti Model Study, (Chitsanzo cha Phunziro) kanali ndi mafunso, mayankho ake, ndiponso malemba ochirikiza mayankhowo. M’kupita kwanthaŵi, timabukuti tinalipo mitundu itatu.

Nthaŵi imeneyo, mu April 1938, Joseph F. Rutherford, woimira likulu la padziko lonse la Mboni za Yehova, anadzacheza ku Sydney. Aka kanali koyamba kwa ine kumvetsera nkhani yapoyera. Dongosolo linali lakuti nkhaniyo aikambire mu Sydney Town Hall, koma anthu otsutsa anapangitsa kuti izi zilephereke. Mmalo mwake nkhaniyo anaikambira pamalo azamaseŵero okulirapo otchedwa Sydney Sports Ground. Chifukwa chakuti otsutsa anafalitsa nkhani zokhudza msonkhanowo, anthu okwana 10,000 anasonkhana. Izi zinali zodabwitsa pakuti panthaŵiyo mu Australia munali Mboni 1,300 zokha basi.

Posapita nthaŵi, ndinalalikira nawo koyamba, popanda kuphunzitsidwa. Gulu lathu litafika ku gawo lolalikira, yemwe ankatsogolera anati, “Iwe ukalalikira ku nyumba iyo.” Ndinali ndi mantha kwambiri moti mayi wa m’nyumbayo atatsegula chitseko, ndinam’funsa kuti, “Kodi nthaŵi ili bwanji?” Analowa m’nyumba kukaona nthaŵi, n’kutulukanso kudzandiuza. Sindinathe kunena kalikonse, ndinangobwerera kupita ku galimoto.

Komabe sindinalekere pomwepo ndipo posapita nthaŵi ndinali kuuza ena uthenga wa Ufumu nthaŵi zonse. (Mateyu 24:14) M’March 1939, ndinasonyeza kudzipatulira kwa Yehova mwa kubatizidwa m’chibafa chosambiramo cha omwe tinayandikana nawo nyumba a Dorothy Hutchings. Chifukwa chakuti kunalibe abale, nditangobatizidwa kumene, ndinapatsidwa maudindo apampingo omwe amapatsidwa kwa amuna achikristu.

Kaŵirikaŵiri tinali kusonkhana m’nyumba za anthu, koma nthaŵi zina pakakhala nkhani zapoyera, tinkabwereka holo. Mbale wooneka bwino wachinyamata wochokera ku Beteli, ofesi yathu yanthambi, anabwera kudzakamba nkhani ku mpingo wathu waung’onowo. Analinso ndi chifukwa china chomwe sindinachidziŵe. Iye anabwera kudzafufuza za ine. Inde, ndi mmene ndinakumanirana ndi Lloyd.

Kukumana Ndi Banja la Lloyd

Tsopano ndinali kulakalaka kutumikira Yehova nthaŵi zonse. Koma pamene ndinafunsira upainiya (kugwira ntchito yolalikira nthaŵi zonse), ndinapemphedwa ngati ndingakonde kutumikira pa Beteli. Choncho mu September 1939, mwezi umene nkhondo yachiŵiri yapadziko lonse inayamba, ndinakhala membala wa banja la Beteli m’dera loyandikana ndi mzinda wa Sydney la Strathfield.

Mu December 1939, ndinapita kumsonkhano ku New Zealand. Pakuti Lloyd anali wa ku New Zealand, nayenso anapita. Tinayenda limodzi pasitima ndipo tinadziŵanako bwino. Lloyd anakonza kuti ndionane ndi amayi ake, abambo ake, ndi achemwali ake pamsonkhano ku Wellington ndiponso kunyumba kwawo ku Christchurch.

Kutsekedwa kwa Ntchito Yathu

Loŵeruka pa January 18, 1941, akuluakulu a boma anabwera pagalimoto zakuda pafupifupi zisanu ndi imodzi kudzalanda malowo. Pakuti ndinali kugwira ntchito m’kanyumba ka pageti lalikulu loloŵera ku Beteli, ndinali woyamba kuwaona. Tinali titauzidwa kale za kutsekedwako maola 18 anthuwo asanabwere, ndiye pafupifupi mabuku onse ndi mafaelo anali  atasamutsidwa kale panthambipo. Mlungu wotsatira, Lloyd ndi anthu ena anayi a m’banja la Beteli anamangidwa.

Ndinadziŵa kuti chimene abale kundende anali kuchisoŵa kwambiri ndi chakudya chauzimu. Kuti ndim’limbikitse Lloyd, ndinaganiza zom’lembera “makalata achikondi.” Ndinkayamba kulemba kalatayo monga mmene kalata yachikondi imakhalira, koma kenako ndimakoperamo nkhani zathunthu za mu Nsanja ya Olonda n’kumaliza monga wokondedwa wake. Patapita miyezi inayi ndi theka, Lloyd anamasulidwa.

Ukwati ndi Kupitiriza Utumiki

Mu 1940, amayi ake a Lloyd anadzacheza ku Australia, ndipo Lloyd anawauza kuti tikuganizira kuti tikwatirane. Amayi akewo anamulangiza kuti tisakwatirane chifukwa mapeto a dongosolo la zinthu ali pafupi kwambiri. (Mateyu 24:3-14) Anauzanso anzake za cholinga chakecho, koma nthaŵi zonse ankamuuza kuti asakwatire. Mapeto ake, mu February 1942, Lloyd anatenga ine pamodzi ndi Mboni zinayi zomwe zinalonjeza kusunga chinsinsi n’kupita nafe ku ofesi ya boma kukalembetsa, ndipo tinakwatirana. Panthaŵiyo, Mboni za Yehova ku Australia zinalibe mwayi womangitsa maukwati.

Ngakhale kuti ine ndi Lloyd sitinaloledwe kutumikirabe pa Beteli titakwatirana, tinapemphedwa kukhala apainiya apadera. Tinali okondwa kukatumikira ku tauni yaing’ono ya Wagga Wagga. Ntchito yathu yolalikira inali yoletsedwabe, ndiponso tinalibe njira yopezera ndalama, choncho tinam’senzetsadi Yehova nkhaŵa zathu.​—Salmo 55:22.

Tinkapita kumidzi panjinga yokwerapo anthu aŵiri. Tinkapeza anthu abwino, ndipo pankapita nthaŵi yaitali tikukambirana nawo. Ambiri mwa iwo sanavomere kuphunzira Baibulo. Komabe, munthu wina yemwe anali ndi golosale, anali kuyamikira kwambiri ntchito yathu ndipo amatipatsa ndiwo zamasamba ndi zipatso mlungu uliwonse. Titakhala ku Wagga Wagga, kwa miyezi isanu ndi umodzi, tinaitanidwanso ku Beteli.

 Banja la Beteli linali litasamuka ku ofesi ya ku Strathfield mu May 1942 ndipo linali kukhala m’nyumba za lendi. Poopa kuti angawatulukire, anali kusamukira kunyumba zina pambuyo pa masabata angapo. Titabwerera ku Beteli m’mwezi wa August, tinakakhala nawo m’nyumba ina yoteroyo. Ntchito yathu inali yosindikiza mabuku m’chipinda china chapansi. Mapeto ake, mu June 1943, ntchito yathu inatsegulidwa.

Kukonzekera Umishonale

Mu April 1947 tinapatsidwa mafomu oyambirira ofunsira maphunziro pa Sukulu ya Gileadi yophunzitsa Baibulo ya Watchtower yomwe inali ku South Lansing, ku New York, U.S.A. Panthaŵiyo tinapatsidwa ntchito yochezera mipingo ndi kuilimbikitsa mwauzimu mu Australia. Patapita miyezi yochepa, tinaitanidwa kukakhala nawo mu kalasi la nambala 11 ku Gileadi. Tinali ndi masabata atatu oti tikonzekere ndi kulongedza katundu wathu. Tinasiya banja ndi anzathu mu December 1947 kupita ku New York limodzi ndi anzathu ena 15 ochokera ku Australia omwenso anaitanidwa kukakhala nawo m’kalasi lomwelo.

Miyezi yochepa ya maphunziro pa Sukulu ya Gileadi inatha mofulumira, ndipo tinapemphedwa kuti tikatumikire ku Japan monga amishonale. Chifukwa chakuti panapita nthaŵi kuti tipeze mapepala a chilolezo chopitira ku Japan, Lloyd anaikidwa kukhala woyang’anira woyendayenda wa Mboni za Yehova. Mipingo yomwe timaiyendera inali ya mumzinda wa Los Angeles mpaka kumalire ndi dziko la Mexico. Tinalibe galimoto, koma mwachikondi, mlungu uliwonse Mbonizo zinali kutitengera ku mpingo wina. Dera limodzi lalikululo, tsopano ndi zigawo zitatu za Chingelezi ndi zitatunso za Chisipaniya. Chigawo chilichonse chili ndi madera pafupifupi khumi.

Kenako, mu October 1949, tinali paulendo wapasitima yomwe kale inali ya asilikali kupita ku Japan. Mbali ina ya sitimayo inali ya amuna ndipo inayo inali ya akazi ndi ana. Kutatsala tsiku limodzi kuti tifike ku Yokohama, tinakumana ndi chimphepo cha mkuntho. Mwachionekere, mphepoyo inakankha mitambo ndipo pamene dzuŵa linkatuluka tsiku lotsatira pa October 31, tinatha kuona phiri lonse la Fuji. Tinalandiridwadi bwino kwambiri ku gawo lathu latsopanolo!

Kugwira Ntchito ndi Anthu a ku Japan

Pamene tinali kuyandikira ku doko, tinaona anthu mazanamazana atsitsi lakuda. ‘Koma ndiye ndi anthu a phokoso bwanji!’ Tinatero m’maganizo mwathu pakumva phokoso la nsapato zawo. Aliyense anavala nsapato za thabwa zomwe zinali kugogoda pamalo otsitsira katundu opangidwanso ndi matabwa. Tinagona ku Yokohama ndipo tsiku lotsatira tinakwera sitima yapamtunda kupita ku gawo lathu la umishonale ku Kobe. Kumeneko, Don Haslett yemwe tinali naye limodzi ku Gileadi, anali atafika kale miyezi ingapo, ndipo anachita lendi nyumba ina kukhala nyumba ya amishonale. Inali nyumba yaikulu yokongola yomangidwa ngati ya ku America, yosanjika kamodzi koma m’katimo munalibe chilichonse.

Posoŵa matiresi ogonapo, tinamweta udzu utaliutali womwe unali panja pa nyumbayo, n’kuuyala pansi. Ndi mmene tinayambira moyo wa umishonale. Tinalibe chilichonse kupatulapo zomwe tinabwera nazo. Tinapeza mbaula zing’onozing’ono zotchedwa hibachi, kuti tiziotha ndi kuphikapo. Tsiku lina usiku, Lloyd anapeza amishonale anzathu aŵiri Percy ndi Ilma Iszlaub atakomoka. Anatha kuwatsitsimula mwa kutsegula mawindo kuti mpweya wabwino ndi wozizira uloŵe. Inenso ndinakomoka tsiku lina pamene ndinali kuphika pa mbaulazi. Komabe zinthu zina sizinatenge nthaŵi kuzizoloŵera!

Kuphunzira chilankhulo kunali kofunika kwambiri. Tinali kuphunzira Chijapani kwa maola 11 tsiku lililonse kwa mwezi wathunthu. Kenako tinayamba kupita kukalalikira titalemba chiganizo chimodzi kapena ziŵiri kuti tikapeze poyambira. Tsiku loyambirira lenileni, ndinakumana ndi mayi wabwino dzina lake Miyo Takagi, yemwe anandilandira mokoma mtima. Pa maulendo obwereza, ine ndi Miyo tinali kulimbana ndi dikishonale yachingelezi yomasulira Chijapani mpaka pamene phunziro la Baibulolo  linayamba kupita patsogolo. Mu 1999, pamwambo wopatulira nyumba zowonjezera za ofesi yanthambi ku Japan, ndinakumananso ndi Miyo ndi anthu enanso okondedwa omwe ndinaphunzira nawo. Papita zaka 50, koma iwo akadali ofalitsa a Ufumu achangu. Akuchita zomwe angathe potumikira Yehova.

Tili ku Kobe, pa April 1, 1950, anthu pafupifupi 180 anasonkhana nawo pa mwambo wa Chikumbutso cha imfa ya Kristu. Tsiku lotsatira m’maŵa, tinadabwa kuona anthu 35 atabwera kuti akalalikire nawo. Mmishonale aliyense anatenga atatu kapena anayi mwa anthu atsopanoŵa kupita nawo kolalikira. Eni nyumba sanalankhule ndi ine mlendo amene ndinkamva pang’ono Chijapani, koma ndi Ajapani atsopano omwe anabwera ku Chikumbutsowo. Kukambirana kwawoko kunkangopitirira, ine osamva zomwe amakambirana. Ndine wosangalala kuti ena mwa atsopano ameneŵa, anapita patsogolo m’chidziŵitso ndipo apitirizabe ntchito yolalikira mpaka lero.

Mwayi wa Maudindo Ambiri Osangalatsa

Ine ndi Lloyd tinapitirizabe ntchito yathu ya umishonale ku Kobe mpaka mu 1952, pamene tinasamukira ku Tokyo, komwe Lloyd anapatsidwa ntchito yoyang’anira ofesi yanthambi. Ntchito yake inamuyendetsa mu Japan ndi ku mayiko ena. Paulendo wina womwe Nathan H. Knorr anadzacheza ku Tokyo kuchokera ku likulu la padziko lonse, anandifunsa kuti: “Kodi ukudziŵa kumene mwamuna wako adzapita paulendo wotsatira woyendera maofesi anthambi? Adzapitatu ku Australia ndi ku New Zealand. Ukhoza kupita nawo ngati uli ndi ndalama zoyendera.” Ndinasangalala kwambiri! Panali patapita zaka zisanu ndi zinayi chichokere kumudzi.

Mwamsanga, tinadziŵitsa mabanja athu powalembera makalata. Amayi anandithandiza ndalama zoyendera. Ine ndi Lloyd tinali otanganidwa ndi ntchito yathu ndipo tinalibe ndalama zoyendera kukaona anthu kumudzi. Choncho ili linali yankho la mapemphero anga. Tangoganizirani chisangalalo cha amayi pondiona. Iwo anati: “Ndiyamba kusunga ndalama kuti mudzabwerenso pakatha zaka zitatu.” Tinasiyana tili ndi maganizo amenewo. Koma n’zomvetsa chisoni kuti anamwalira m’July chaka chotsatira. Ndikukhulupirira kuti zidzakhala zosangalatsa kwambiri kukumana nawo m’dziko latsopano.

Mpaka mu 1960, ntchito yanga inali ya umishonale basi. Kenako ndinalandira kalata yofotokoza kuti: “Kuyambira lero, uzichapa ndi kusita zovala za anthu onse a m’banja la Beteli.” Panthaŵiyo banja la Beteli, linali ndi anthu pafupifupi 12, ndiye ndinakwanitsa kugwira ntchitoyo ndi ntchito yanga ya umishonale.

Mu 1962, nyumba yathu ya Beteli yachijapani inagumulidwa ndipo nyumba ina yatsopano yosanjikiza kasanu, anaimaliza kumanga m’chaka chotsatira. Ndinapatsidwa ntchito yothandiza abale achinyamata atsopano pa Beteli kusamalira zipinda zawo ndi kuika zinthu m’malo ake. Malinga ndi mwambo wa ku Japan, anyamata sankaphunzitsidwa ntchito iliyonse ya pakhomo. Ankalimbikitsidwa kulimbikira sukulu basi, ndipo amayi awo anali kuwachitira chilichonse. Posapita nthaŵi anadziŵa kuti sindingawachitire chilichonse monga ankachitira amayi awo. M’kupita kwanthaŵi ambiri anapita patsogolo, n’kumagwira ntchito zina zofunika m’gululi.

Tsiku lina m’nthaŵi yachilimwe kunatentha kwambiri. Munthu wina wophunzira Baibulo anabwera kudzaona malo athu ndipo anandipeza ndikutsuka m’bafa. Iye anati “Muuze bwana wanu kuti ndikhoza kupereka ndalama zoti mulembere  mtsikana wantchito azikugwirirani ntchitoyi.” Ndinam’thokoza chifukwa cha kukoma mtima kwake, koma ndinam’fotokozera kuti ndinali wofunitsitsa kwambiri kugwira ntchito iliyonse yomwe ndapatsidwa m’gulu la Yehova.

Panthaŵi imeneyi, ine ndi Lloyd tinaitanidwa kukakhala nawo m’kalasi la nambala 39 ku Gileadi. Unalitu mwayi waukulu kwabasi kupitanso kusukulu mu 1964, tili ndi zaka 46! Kwenikweni maphunzirowo anakonzedwera omwe anali kutumikira m’maofesi anthambi kuti athe kugwira bwino ntchito zawo. Maphunziro a miyezi khumi ameneŵa atatha, tinatumizidwanso ku Japan. Panthaŵiyi, ku Japan kunali ofalitsa Ufumu oposa 3,000.

Ofalitsa anawonjezeka mofulumira kwambiri mwakuti pofika mu 1972, Mboni zinaposa pa 14,000, ndipo ofesi yatsopano yosanjikiza kanayi inamangidwa ku Numazu kumwera kwa mzinda wa Tokyo. Kuchokera pa nyumba yathuyo, phiri la Fuji linkaoneka bwino kwambiri. Magazini a Chijapani oposa miliyoni imodzi anali kusindikizidwa mwezi uliwonse pogwiritsa ntchito makina aakulu kwambiri osindikizira. Koma zinthu zinkaoneka kuti zatsala pang’ono kusintha kwa ife.

Kumapeto kwa 1974, Lloyd analandira kalata yochokera ku likulu la Mboni za Yehova ku Brooklyn yomuitana kuti akatumikire m’Bungwe Lolamulira. Poyamba ndinaganiza kuti: ‘Tsopano tisiyana basi. Pakuti Lloyd ali ndi chiyembekezo chokakhala ndi moyo kumwamba ndipo ine padziko lapansi, nthaŵi ina tidzasiyana ndithu. Mwina Lloyd apite yekha ku Brooklyn ine nditsale.’ Koma ndinasintha maganizowo mwamsanga ndipo ndi mtima wonse m’March 1975 ndinapita limodzi ndi Lloyd.

Madalitso pa Likulu

Ngakhale ku Brooklyn, mtima wa Lloyd unali ku Japan. Nthaŵi zonse ankanena zomwe tinakumana nazo kumeneko. Koma tsopano, tinali ndi mwayi wodziŵananso ndi anthu ena. Zaka 24 zomalizira za moyo wake, ntchito yake yaikulu inali kuyendera maofesi anthambi padziko lonse. Ndinayenda naye maulendo ambiri.

Kuchezera abale athu achikristu m’mayiko ena, kunandithandiza kuzindikira mavuto a m’moyo wawo. Sindidzaiwala zomwe msungwana wina wazaka khumi, dzina lake Entellia anali kukumana nazo. Mtsikanayu ndinakumana naye kumpoto kwa Africa. Anali kukonda dzina la Mulungu ndipo ankapita ku misonkhano yachikristu mwa kuyenda pansi kwa ola limodzi ndi theka kupita ndi kubwera. Ngakhale kuti anali kuzunzidwa ndi abale ake, Entellia anali atadzipatulira kwa Yehova. Titapita kumpingo kwawo tinapeza kuti ku pulatifomu kunali getsi limodzi lokha losaŵala kwambiri, koma anthu ena onse anali mumdima. Komabe zinali zochititsa chidwi kumva abale ndi alongo akuimba bwino kwambiri mumdimawo.

Nthaŵi yosangalatsa kwambiri m’moyo wathu inali mu December 1998 pamene ine ndi Lloyd tinali nawo m’gulu la alendo pa Msonkhano Wachigawo wa mutu wakuti “Njira ya Moyo ya Mulungu” ku Cuba. Tinachita chidwi kwambiri kuona abale ndi alongo akuyamikira ndiponso kusangalala poona abale ochokera ku likulu ku Brooklyn akudzacheza nawo. Ndimakumbukira okondedwa ambiri omwe ndinakumana nawo amene akutamanda Yehova mwamphamvu.

Kukhala ndi Anthu a Mulungu

Ngakhale kuti kwathu ndi ku Australia, ndimakonda anthu kulikonse kumene gulu la Yehova landitumiza. Ndi mmene zinalili ku Japan. Tsopano ndakhala ku United States kwa zaka zopitirira 25, ndipo ndikuona chimodzimodzi. Pamene mwamuna wanga anamwalira, sindinaganize zobwerera ku Australia, koma kukhalabe pa Beteli ku Brooklyn komwe Yehova wandipatsa ntchito.

Tsopano ndili ndi zaka zoposa 80. Ndakhala mu utumiki wanthaŵi zonse zaka 61, komabe ndine wofunitsitsa kutumikira Yehova kulikonse komwe angafune. Iye wandisamaliradi. Ndimanyadira zaka zoposa 57 zomwe ndinakhala ndi mnzanga wokondedwa wokonda Yehova. Ndikutsimikiza kuti Yehova apitirizabe kutidalitsa, ndipo ndikudziŵa kuti sadzaiwala ntchito yathu ndi chikondicho tidachionetsera ku dzina lake.​—Ahebri 6:10.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Onani Nsanja ya Olonda ya October 1, 1999, masamba 16 ndi 17.

[Chithunzi patsamba 25]

Ndi amayi mu 1956

[Chithunzi patsamba 26]

Ndi Lloyd ndiponso ofalitsa achijapani kumayambiriro kwa m’ma 1950

[Zithunzi patsamba 26]

Ndi wophunzira Baibulo wanga woyamba, ku Japan, Miyo Takagi, kumayambiriro kwa m’ma 1950 ndi mu 1999

[Chithunzi patsamba 28]

Ndili ndi Lloyd kufalitsa magazini ku Japan