Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

‘Mawu a Yehova Anapitirizabe Kukula’

‘Mawu a Yehova Anapitirizabe Kukula’

 ‘Mawu a Yehova Anapitirizabe Kukula’

“Atumiza lamulo lake ku dziko lapansi; mawu ake athamanga liŵiro.”​—SALMO 147:15.

1, 2. Kodi ndi ntchito yotani imene Yesu anapatsa ophunzira ake, ndipo kodi inaphatikizapo kutani?

UMODZI mwa maulosi ochititsa chidwi kwambiri m’Baibulo uli pa Machitidwe 1:8. Atangotsala pang’ono kukwera kumwamba, Yesu anauza otsatira ake okhulupirika kuti: “Mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera atadza pa inu: ndipo mudzakhala mboni zanga . . . kufikira malekezero ake a dziko.” Anawapatsatu ntchito yaikulu kwabasi!

2 Kufalitsa Mawu a Mulungu padziko lonse kuyenera kuti kunaoneka ngati ntchito yovuta zedi kwa ophunzira ochepa amene anapatsidwa ntchito imeneyi. Taonani zomwe anafunika kuchita. Anafunika kuthandiza anthu kumvetsa uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. (Mateyu 24:14) Kuchitira umboni za Yesu kunatanthauzanso kuuza ena za ziphunzitso zake zamphamvu ndi kufotokoza zomwe iye adzachite m’chifuno cha Yehova. Komanso, ntchito imeneyi inaphatikizapo kuphunzitsa anthu a mitundu yonse ndipo kenako n’kuwabatiza. Ndipotu zimenezi zinayenera kuchitika padziko lonse lapansi!​—Mateyu 28:19, 20.

3. Kodi Yesu anatsimikizira otsatira ake za chiyani, nanga kodi anachita motani ndi ntchito imene anawapatsa?

3 Komabe, Yesu anatsimikizira otsatira akewo kuti adzakhala ndi mzimu woyera pogwira ntchito imene anawapatsayo. Chotero, ngakhale kuti ntchitoyo inali yaikulu ndi kuti otsutsa anayesetsa mwakhama komanso mwachipongwe kuti awafooketse, ophunzira oyambirira a Yesu ameneŵa anakwaniritsa zimene anawalamulira. Zimenezi zinalembedwa m’mabuku ndipo n’zosatsutsika.

4. Kodi ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa inasonyeza motani chikondi cha Mulungu?

4 Ntchito yapadziko lonse yolalikira ndi kuphunzitsa inasonyeza chikondi chimene Mulungu anali nacho pa anthu amene anali asanam’dziŵe. Inawapatsa mwayi woyandikira kwa Yehova ndi kukhululukidwa machimo awo. (Machitidwe 26:18) Ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa inasonyezanso chikondi chimene Mulungu ali nacho pa olengeza uthengawo, chifukwa chakuti inawapatsa mwayi wosonyeza kudzipereka kwawo kwa Yehova ndi kusonyezanso chikondi chawo pa anthu anzawo. (Mateyu 22:37-39) Mtumwi Paulo anauona utumiki wachikristu monga chinthu chamtengo wapatali mwakuti anauyerekezera ndi “chuma.”​—2 Akorinto 4:7.

5. (a) Kodi mbiri yodalirika ya Akristu oyambirira timaipeza kuti, nanga mbiri imeneyi ikusimba za kusefukira kwa chiyani? (b) N’chifukwa chiyani buku la Machitidwe lili lofunika kwa atumiki a Mulungu lerolino?

5 Mbiri yodalirika ya ntchito yolalikira imene Akristu oyambirira amagwira ikupezeka m’buku louziridwa la Machitidwe, lomwe wophunzira Luka analemba. Imeneyi ndi mbiri yonena za kusefukira kwa chidziŵitso mochititsa chidwi ndiponso mofulumira kwambiri. Kufalikira kwa chidziŵitso cha Mawu a Mulungu kumeneku kumatikumbutsa Salmo 147:15, limene limati: “[Yehova] atumiza lamulo lake ku dziko lapansi; mawu ake athamanga liŵiro.” Mbiri ya Akristu oyambirirawo, omwe analandira mphamvu ya mzimu woyera, n’njosangalatsa ndiponso yofunika kwambiri kwa ife lerolino. Mboni za Yehova zikugwira ntchito yomweyo yolalikira ndi kupanga ophunzira, koma tsopano pamlingo waukulu kwambiri. Timakumananso ndi mavuto ofanana ndi amene Akristu anakumana nawo m’zaka za zana loyamba.  Tikamalingalira mmene Yehova anadalitsira ndi kulimbikitsira Akristu oyambirirawo, chikhulupiriro chathu chakuti akutichirikiza chimalimba.

Kuwonjezeka kwa Ophunzira

6. Ndi mawu ati onena za kukula amene akupezeka katatu m’buku la Machitidwe, ndipo kodi amatanthauzanji?

6 Njira imodzi yopendera kukwaniritsidwa kwa Machitidwe 1:8 ndiyo kulingalira mawu akuti “Mawu a Mulungu anakula.” Mawu ameneŵa, ngakhale kuti penapake n’ngosiyana pang’ono, akupezeka katatu kokha m’Baibulo ndipo katatu konseko akupezeka m’buku la Machitidwe. (Machitidwe 6:7; 12:24; 19:20) “Mawu a Ambuye” kapena kuti “Mawu a Mulungu” otchulidwa m’ndime zimenezi, akutanthauza uthenga wabwino​—uthenga wogwira mtima wa choonadi cha Mulungu, uthenga wamoyo komanso wamphamvu umene umasintha miyoyo ya anthu olandira uthengawu.​—Ahebri 4:12.

7. Kodi kukula kwa Mawu a Mulungu kukugwirizana ndi chiyani pa Machitidwe 6:7, ndipo chinachitika n’chiyani pa tsiku la Pentekoste mu 33 C.E.?

7 Kukula kwa Mawu a Mulungu kwatchulidwa kwanthaŵi yoyamba pa Machitidwe 6:7. Pamenepo timaŵerenga kuti: “Ndipo mawu a Mulungu anakula; ndipo chiŵerengero cha akuphunzira chidachulukatu ku Yerusalemu; ndipo khamu lalikulu la ansembe linamvera chikhulupirirocho.” Pano, kukula kwa mawu kukugwirizana ndi kuwonjezeka kwa chiŵerengero cha ophunzira. Mmbuyomo, pa tsiku la Pentekoste mu 33 C.E., Mulungu anatsanulira mzimu wake woyera pa ophunzira pafupifupi 120 omwe anasonkhana m’chipinda chapamwamba. Kenako mtumwi Petro anakamba nkhani yogwira mtima, ndipo mwa onse amene anamvetsera, anthu 3,000 anakhala okhulupirira tsiku lomwelo. Kunalitu balalabalala pamene anthu masauzande anali piringupiringu kuloŵera kumaiŵe a mu Yerusalemu ndi m’madera ena apafupi kuti akabatizidwe m’dzina la Yesu, munthu amene anapachikidwa ngati wachifwamba masiku 50 mmbuyomo!​—Machitidwe 2:41.

8. Kodi chiŵerengero cha ophunzira chinawonjezeka motani m’zaka zotsatira pambuyo pa Pentekoste mu 33 C.E.?

 8 Komatu chimenecho chinali chiyambi chabe. Khama losatha la atsogoleri achipembedzo achiyuda lofuna kuimitsa ntchito yolalikira linagwa m’dera. Chomwe chinakhumudwitsa atsogoleri amenewo chinali chakuti, “Ambuye anawaonjezera [ophunzirawo] tsiku ndi tsiku amene akuti apulumutsidwe.” (Machitidwe 2:47) Posakhalitsa, “chiŵerengero cha amuna chinali ngati zikwi zisanu.” Pambuyo pake, “anawonjezedwa kwa Ambuye okhulupirira ambiri, ndiwo amuna ndi akazi.” (Machitidwe 4:4; 5:14) Timaŵerenga zomwe zinachitika kachiŵirika kuti: “Ndipo Mpingo wa m’Yudeya lonse ndi Galileya ndi Samariya unali nawo mtendere, nukhazikika; ndipo unayenda m’kuopa kwa Ambuye ndi m’chitonthozo cha Mzimu Woyera, nuchuluka.” (Machitidwe 9:31) Patapita zaka zingapo, mwinamwake cha m’ma 58 C.E., anatchulapo kuti ‘ambirimbiri mwa Ayuda anakhulupirira.’ (Machitidwe 21:20) Panthaŵiyo, Akunja okhulupirira analiponso ambirimbiri.

9. Kodi Akristu oyambirira mungawafotokoze motani?

9 Mokulira, chiŵerengerochi chinawonjezeka makamaka chifukwa cha atsopano amene analapa ndi kutembenuka mtima. Chipembedzocho chinali chatsopano​—koma chinali kupita patsogolo mofulumira. M’malo momangopita kutchalitchi mwamwambo, ophunzirawo, omwe nthaŵi inayake anaphunzitsidwa choonadi ndi ena amene ankazunzidwa mwakhanza, anali odzipereka ndi mtima wonse kwa Yehova ndi kuchita Mawu ake mofunitsitsa. (Machitidwe 16:23, 26-33) Amene anatembenukira ku Chikristu anasankha kuchita zimenezo atalingalira mosamalitsa, komanso mwachikumbumtima. (Aroma 12:1) Anawaphunzitsa njira za Mulungu; ndipo choonadi chinali m’malingaliro ndi m’mitima yawo. (Ahebri 8:10, 11) Iwo anali okonzeka kufera chikhulupiriro chawo.​—Machitidwe 7:51-60.

10. Kodi Akristu oyambirira anadziŵa kuti anali ndi udindo wotani, nanga ndani akufanana nawo lerolino?

10 Amene analandira ziphunzitso zachikristu anazindikira udindo wawo wouza ena choonadi. Zimenezi zinathandizira kwambiri kuti chiŵerengero cha ophunzira chipitirire kuwonjezeka. Katswiri wina wa Baibulo anati: “Kuuza ena za chikhulupiriro sunali udindo wa alaliki achangu okha kapena wa okhawo ochita kuikidwa mwapadera kuti akhale alaliki. Kulalikira unali mwayi wapadera ndi udindo wa membala aliyense wa Tchalitchi. . . . Kudzipereka kwa Akristu onse kunasonkhezera kwambiri Chikristu kuchokera pachiyambi penipeni.” Katswiriyu analembanso kuti: “Kwa Akristu oyambirirawo, kulalikira inali ntchito yopatsa moyo.” Akristu enieni lerolino amaonanso choncho.

Choonadi Chinafalikira M’mayiko Ambiri

11. Kodi kukula kwa mawu a Mulungu kotchulidwa pa Machitidwe 12:24 kumatanthauzanji, ndipo zimenezi zinachitika motani?

11 Mawu onena za kukula kwa mawu a Mulungu akupezeka kachiŵiri pa Machitidwe 12:24 pomwe pamati: “Mawu a Mulungu anakula, nachulukitsa.” Pano mawuŵa akutanthauza kuti choonadi chinafalikira m’mayiko ambiri. Ngakhale kuti maboma ankatsutsa, koma ntchito inapitabe patsogolo. Choyamba mzimu woyera unatsanulidwa mu Yerusalemu, ndipo kuchokera kumeneko, mawu anafalikira mofulumira kwambiri. Chizunzo chomwe chinabuka mu Yerusalemu, chinabalalitsira ophunzirawo mu Yudeya ndi mu Samaliya monse. Kodi zotsatira zake zinali zotani? “Iwo akubalalitsidwa anapitapita nalalikira mawuwo.” (Machitidwe 8:1, 4) Filipo anauzidwa kukachitira umboni kwa munthu winawake, ndipo munthuyo atabatizidwa, anatenga uthengawo n’kukaulengeza ku Aitiopiya. (Machitidwe 8:26-28, 38, 39) Mwamsanga, choonadi chinafalikira ku Luda, ku chigwa cha Sarona, ndi ku Yopa. (Machitidwe 9:35, 42) Pambuyo pake, mtumwi Paulo anayenda ulendo wamakilomita masauzande ambiri panyanja ndi pamtunda pomwe, kukakhazikitsa mipingo m’mayiko ambiri a m’mphepete mwa Nyanja ya Mediterranean. Mtumwi Petro anapita ku Babulo. (1 Petro 5:13) M’zaka 30 zokha kuchokera pamene mzimu woyera unatsanulidwa pa Pentekoste, Paulo analemba kuti uthenga wabwino unali ‘utalalikidwa m’cholengedwa chonse cha pansi pa thambo,’ mwinamwake kutanthauza dera linalake ladziko lapansi limene linali lotchuka m’nthaŵiyo.​—Akolose 1:23.

12. Kodi otsutsa Chikristu anavomereza motani kuti mawu a Mulungu anafalikira m’mayiko ambiri?

 12 Ngakhale otsutsa Chikristu nawonso anavomereza kuti Mawu a Mulungu anazika mizu mu Ufumu wonse wa Roma. Mwachitsanzo, Machitidwe 17:6 amati mu Tesalonika, kumpoto kwa Girisi, otsutsa anafuula nati: “Omwe aja asanduliza dziko lokhalamo anthu, afika kunonso.” Komanso, kuchiyambi kwa zaka za zana lachiŵiri, Pliny Wamng’ono ku Bituniya, analemba kalata yokhudza Chikristu yopita kwa Talajani, Mfumu ya Roma. Iye anadandaula kuti: “Sichikupezeka m’mizinda mokha, koma chafalitsanso chinyengo chake m’midzi ndi m’mayiko oyandikana nawo.”

13. Kodi kufalikira kwa mawu a Mulungu m’mayiko ochuluka kwasonyeza motani chikondi cha Mulungu pa mtundu wa anthu?

13 Kufalikira kumeneku kwa mawu a Mulungu m’mayiko ochuluka kunasonyeza chikondi chakuya chomwe Yehova alinacho pa anthu ofunika kuwomboledwa. Petro ataona mzimu woyera ukugwira ntchito pa Korneliyo Wakunjayo, anati: “Zoona ndizindikira kuti Mulungu alibe tsankhu; koma m’mitundu yonse, wakumuopa iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye.” (Machitidwe 10:34, 35) Inde, uthenga wabwino unali ndipo uli wa anthu onse, ndipo kufalikira kwa mawu a Mulungu m’mayiko ochuluka kunapatsa anthu mwayi kwina kulikonse wolabadira chikondi cha Mulungu. M’zaka zino za m’ma 2000, mawu a Mulungu afalikiradi padziko lonse lapansi.

Kukula kwa Mawu a Mulungu Kumene Kunapambana

14. Kodi ndi kukula kotani kwa Mawu a Mulungu komwe Machitidwe 19:20 akufotokoza, nanga kodi Mawu a Mulungu anapambana chiyani?

14 Mawu onena za kukula kwa mawu a Mulungu akupezeka kachitatu pa Machitidwe 19:20: “Mawu a Ambuye anachuluka mwamphamvu nalakika.” Mawu achigiriki choyambirira omwe atembenuzidwa kuti “nalakika” amatanthauza “kuchita mwachamuna.” Mavesi oyambirira amati ambiri mu Efeso anakhulupirira, ndipo amatsenga ambiri anatentha mabuku awo pamaso pa anthu onse. Choncho, mawu a Mulungu anapambana zikhulupiriro za zipembedzo zonyenga. Mphamvu za uthenga wabwino zinapambananso zopinga zina, monga chizunzo. Panalibe chimene chikanaimitsa kufalikira kwa uthenga wabwino. Izinso zikufanana kwabasi ndi kufalikira kwa Chikristu choona m’nthaŵi yathu ino.

15. (a) Kodi wolemba mbiri ya Baibulo wina analemba kuti chiyani za Akristu oyambirira? (b) Kodi ophunzira ankati ndani amachititsa kuti zinthu ziziwayendera bwino?

15 Atumwi ndi Akristu ena oyambirira analalikira mawu a Mulungu mwachangu. Ponena za iwowa, wolemba mbiri ya Baibulo wina anati: “Anthu ameneŵa akafuna kulankhula za Ambuye wawo, sanali kusoŵa nkomwe njira zochitira zimenezo. Ndithudi, chomwe chimatichititsa chidwi kwambiri mwa amuna ndi akazi ameneŵa ndi changu chawo osati njira zawozo.” Komabe, Akristu oyambirirawo ankadziŵa kuti utumiki wawo sunali kuyenda bwino chifukwa cha khama lawo lokha ayi. Mulungu anawalamula kupitirizabe ntchito yawoyo, ndipo anawachirikiza kuti aikwaniritse. Mulungu ndi amene amakulitsa mwauzimu. Mtumwi Paulo anachitira umboni zimenezi m’kalata yomwe analembera mpingo wa ku Korinto. Iye anati: “Ndinawoka ine, anathirira Apolo; koma Mulungu anakulitsa. Pakuti ife ndife antchito anzake a Mulungu.”​—1 Akorinto 3:6, 9.

 Mzimu Woyera Pantchito Yake

16. N’chiyani chomwe chikusonyeza kuti mzimu woyera unapatsa mphamvu ophunzira kuti alankhule molimba mtima?

16 Kumbukirani kuti Yesu amauza ophunzira ake motsimikiza kuti mzimu woyera udzachita mbali yofunika pa kufalikira kwa mawu a Mulungu ndi kuti mzimu woyera udzapatsa mphamvu ophunzirawo m’ntchito yawo yolalikira. (Machitidwe 1:8) Kodi zimenezi zinachitika motani? Mosakhalitsa kuchokera pamene mzimu woyera unatsanulidwa pa ophunzirawo pa Pentekoste, Petro ndi Yohane anawaitana kukalankhula m’bwalo lalikulu lamilandu m’dzikomo la Sanihedirini. Oweruza m’bwalo lachiyuda limeneli ndi amene analamula kuti Yesu Kristu aphedwe. Kodi atumwiwo ananjenjemera ndi mantha pamaso pa akuluakulu ankhanzawo? Sanatero m’pang’ono pomwe! Mzimu woyera unalimbitsa Petro ndi Yohane kuti athe kulankhula molimba mtima mwakuti adani awo anazizwa kwambiri, ndipo “anawazindikira, kuti anakhala pamodzi ndi Yesu.” (Machitidwe 4:8, 13) Mzimu woyera unam’chititsanso Stefano kuchitira umboni molimba mtima m’bwalo lomweli la Sanihedirini. (Machitidwe 6:12; 7:55, 56) Mmbuyomo, mzimu woyera unali utatsogolera ophunzira kulalikira molimba mtima. Luka anati: “Mmene adapemphera iwo, panagwedezeka pamalo pamene adasonkhanirapo; ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nalankhula mawu a Mulungu molimbika mtima.”​—Machitidwe 4:31.

17. Kodi ndi m’njira zina ziti mmene mzimu woyera unathandizira ophunzira muutumiki wawo?

17 Kupyolera mwa mzimu wake woyera wamphamvuwo, Yehova, limodzi ndi Yesu woukitsidwayo, anatsogolera ntchito yolalikira. (Yohane 14:28; 15:26) Mzimu utatsanulidwa pa Korneliyo, achibale ake, ndi mabwenzi ake apamtima, mtumwi Petro anazindikira kuti zinali zotheka kuti Akunja osadulidwa abatizidwe m’dzina la Yesu Kristu. (Machitidwe 10:24, 44-48) Pambuyo pake, mzimu unachita mbali yofunika poika Barnaba ndi Saulo (mtumwi Paulo) kuti agwire ntchito yaumishonale komanso kuwasonyeza komwe ayenera kupita ndi kumene sayenera kupita. (Machitidwe 13:2, 4; 16:6, 7) Unatsogolera atumwi komanso amuna achikulire m’Yerusalemu posankha zochita. (Machitidwe 15:23, 28, 29) Mzimu woyera unatsogoleranso poika oyang’anira mumpingo wachikristu.​—Machitidwe 20:28.

18. Kodi Akristu oyambirira anasonyeza motani chikondi?

18 Komanso, mzimu woyera unaonekera mwa Akristu enieniwo, mwakuti anasonyeza mikhalidwe yaumulungu, monga chikondi. (Agalatiya 5:22, 23) Chikondi chinasonkhezera ophunzirawo kuti azithandizana. Mwachitsanzo, pambuyo pa Pentekoste mu 33 C.E., kunakhazikitsidwa thumba la ndalama mu Yerusalemu lothandizira zofunika pa moyo wa ophunzirawo. Nkhaniyi m’Baibulo imati: “Mwa iwo munalibe wosoŵa; pakuti onse amene anali nayo minda, kapena nyumba, anazigulitsa nabwera nawo malonda ake a izo adazigulitsa, nawaika pa mapazi a atumwi; ndipo anagaŵira yense monga kusoŵa kwake.” (Machitidwe 4:34, 35) Chikondi choterechi sanali kuchisonyeza kwa okhulupirira anzawo okha komanso kwa ena, mwa kuwauza uthenga wabwino komanso mwa ntchito zina zachifundo. (Machitidwe 28:8, 9) Yesu anati otsatira ake adzadziŵika ndi chikondi chodzimana.  (Yohane 13:34, 35) Ndithudi mkhalidwe wofunika wa chikondi unakokera anthu kwa Mulungu ndiponso unathandizira kuti chiŵerengero cha ophunzira chiwonjezeke m’zaka za zana loyamba monga momwe chikuchitiranso lerolino.​—Mateyu 5:14, 16.

19. (a) Kodi Mawu a Yehova anakula m’njira zitatu ziti m’zaka za zana loyamba? (b) Kodi m’nkhani yotsatira tidzaphunzira chiyani?

19 Mawu akuti “mzimu woyera” akupezeka nthaŵi 41 m’buku la Machitidwe. Mwachionekere, kuwonjezeka kwa Akristu oona m’zaka za zana loyamba kunagwirizana kwambiri ndi mphamvu ndi chitsogozo cha mzimu woyera. Chiŵerengero cha ophunzira chinawonjezeka, mawu a Mulungu anafalikira dera lalikulu, ndipo mphamvu zake zinachuluka kuposa zipembedzo ndi filosofi ya m’nthaŵiyo. Kukula kofanana ndi kwa m’zaka za zana loyamba kukuchitikanso m’ntchito ya Mboni za Yehova lerolino. M’nkhani yotsatira, tidzaphunzira za kukula kochititsanso chidwi kwa Mawu a Mulungu m’nthaŵi zamakono zino.

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi chiŵerengero cha ophunzira oyambirira chinawonjezeka motani?

• Kodi mawu a Mulungu anafalikira m’mayiko ambiri m’njira yotani?

• Kodi mawu a Mulungu anapambana motani m’zaka za zana loyamba?

• Kodi mzimu woyera unachita mbali yofunika yotani pa kukula kwa Mawu a Mulungu?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 12]

Filipo analalikira kwa Mwaitiopiya, kufalitsa uthenga wabwino m’mayiko ena

[Chithunzi patsamba 13]

Mzimu woyera unatsogolera atumwi ndi amuna achikulire mu Yerusalemu

[Mawu a Chithunzi patsamba 10]

Pamwamba kona ya kumanja: Mmene Mzinda wa Yerusalemu unkaonekera m’nthaŵi ya Kachisi Wachiŵiri - maloŵa ali pa Holyland Hotel, mu Yerusalemu