Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Uthenga Wabwino wa Ufumu N’chiyani?

Kodi Uthenga Wabwino wa Ufumu N’chiyani?

 Kodi Uthenga Wabwino wa Ufumu N’chiyani?

Kodi ndi nkhani yanji imene anthu 6,035,564, ana ndi akulu omwe, m’mayiko 235 anatherapo maola 1,171,270,425 poifotokozera ena? Kuwonjezera pa kuifotokoza m’pakamwa, iwo anagaŵiranso anthu mabuku osiyanasiyana okwanira mamiliyoni 700 olengeza ndi kulongosola nkhaniyo. Anagaŵiranso makaseti a mu wailesi ndi mavidiyo kaseti masauzande ambirimbiri ofotokoza nkhani imodzimodziyi. Kodi ndi “nkhani” yanji?

NDI “nkhani” yonena za uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Kunena zoona, “uthenga uwu wabwino wa Ufumu” sunalalikidwepo pamlingo waukulu chonchi m’mbiri yonse ya anthu.​—Mateyu 24:14.

Amene akuchita ntchito yolalikira ndi yophunzitsa padziko lonse imeneyi ndi antchito odzifunira. M’maonekedwe apamwamba, angaoneke ngati kuti sangaithe ntchitoyo. Nangano n’chiyani chimawapangitsa kukhala olimba mtima ndi opambana? Choyambirira ndicho mphamvu ya uthenga wabwino wa Ufumu, popeza kuti ndi uthenga wonena za madalitso amene anthu adzalandira. Ameneŵa ndi madalitso amene anthu onse amawalakalaka​—chimwemwe, kumasuka ku mavuto a zachuma, boma labwino, mtendere ndi chisungiko, komanso chinachake chimene ochuluka sayesa n’kuchitchula komwe​—moyo wosatha! Umenewu ndi uthengadi wabwino kwa anthu amene akufunafuna tanthauzo la moyo ndi cholinga chake. Inde, madalitso onsewa ndi enanso ambiri mungawapeze ngati mulabadira uthenga wabwino wa Ufumu umene ukulengezedwawu.

Kodi Ufumuwo N’chiyani?

Koma kodi Ufumu umene ukulengezedwa monga uthenga wabwino ndiwo chiyani? Ndiwo Ufumu umene anthu mamiliyoni ambiri aphunzitsidwa kuupempherera m’mawu odziŵikawa: “Atate wathu wa Kumwamba, dzina lanu liyeretsedwe. Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano.”​—Mateyu 6:9, 10.

Ndiwo Ufumu umene mneneri wachihebriyo Danieli anatchula zaka zoposa mazana 25 zapitazo pamene analemba kuti: “Mulungu wa Kumwamba adzaika ufumu woti sudzawonongeka ku nthaŵi zonse, ndi ulamuliro wake sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse, nudzakhala chikhalire.”​—Danieli 2:44.

Chotero, uthenga wabwinowu ukunena za Ufumu, kapena kuti boma la Mulungu limene lidzachotsapo kuipa konse ndi mavuto onse kenako n’kudzalamulira dziko lonse mwamtendere. Lidzakwaniritsa chifuno choyambirira cha Mlengi kwa anthu ndi dziko lapansi.​—Genesis 1:28.

 “Ufumu wa Kumwamba Wayandikira”

Pafupifupi zaka 2,000 zapitazo, uthenga wabwino wa Ufumu unalalikidwa poyera choyamba ndi mwamuna amene maonekedwe ake ndi zochita zake zinali zochititsa chidwi. Mwamuna ameneyo anali Yohane Mbatizi, mwana wa wansembe Zakariya ndi mkazi wake, Elizabeti. Yohane anali kuvala chovala cha ubweya wa ngamila, ndi lamba wachikopa m’chiuno mwake, mofanana ndi mneneri Eliya, yemwe ankachitira chithunzi Yohane Mbatizi. Komano uthenga wake ndi umene unakopa chidwi cha anthu ambiri. Iye ankalengeza kuti: “Tembenukani mitima; chifukwa Ufumu wa Kumwamba wayandikira.”​—Mateyu 3:1-6.

Yohane anali kulengeza uthengawo kwa Ayuda, omwe ankati akulambira Mulungu woona, Yehova. Monga mtundu, iwo analandira pangano Lachilamulo kudzera mwa Mose zaka pafupifupi 1,500 kumbuyoko. M’Yerusalemu munali mudakali kachisi wokongola uja, kumene ankaperekera nsembe mogwirizana ndi Chilamulo. Ayuda anali otsimikiza kuti kulambira kwawo kunali kwabwino pamaso pa Mulungu.

Komano, atamvetsera mawu a Yohane, anthu ena anayamba kuona kuti chipembedzo chawo chinali chosiyana ndi mmene iwo ankachionera. Chikhalidwe chachigiriki ndi mafilosofi awo zinali zitasintha ziphunzitso zachiyuda. Chilamulo chimene anachilandira kwa Mulungu kudzera mwa Mose chinali chitasukuluka tsopano, mwinanso kuferatu, chifukwa cha zikhulupiriro ndi miyambo ya anthu. (Mateyu 15:6) Posocheretsedwa ndi atsogoleri achipembedzo ouma mtima ndi opanda chifundo, anthu ochuluka sanalinso kulambira Mulungu mwa njira imene Iye amaivomereza. (Yakobo 1:27) Anafunikira kulapa machimo awo amene anachimwira Mulungu ndi zimene analakwira pangano la Chilamulo.

Panthaŵiyo, Ayuda ambiri anali kuyembekeza kuona Mesiya wolonjezedwayo, kapena kuti Kristu, ndipo ena ankanena za Yohane kuti: ‘Kodi ameneyu sindiye Kristu?’ Koma Yohane anakana zoti ndiye Kristu ndipo m’malo mwake anawalozera wina wake, amene anam’longosola kuti: “Sindiyenera kumasula lamba la nsapato zake.” (Luka 3:15, 16) Posonyeza Yesu kwa ophunzira ake, Yohane analengeza kuti: “Onani Mwanawankhosa wa Mulungu amene achotsa tchimo lake la dziko lapansi!”​—Yohane 1:29.

Umenewo unalidi uthenga wabwino, chifukwa chakuti Yohane anali kwenikweni kusonyeza anthu onse njira yopezera moyo ndi chimwemwe​—Yesu, amene “achotsa tchimo lake la dziko lapansi!” Pokhala mbadwa za Adamu ndi Hava, anthu onse amabadwira mu ululu wa uchimo ndi imfa. Aroma 5:19 amafotokoza kuti: “Monga ndi kusamvera kwa munthu mmodzi [Adamu] ambiri anayesedwa ochimwa, chomwecho ndi kumvera kwa mmodzi [Yesu] ambiri adzayesedwa olungama.” Yesu, monga mwana wa nkhosa woperekedwa nsembe, anali ‘kudzachotsa uchimo’ ndi kuthetsa zovuta zonse m’moyo wa anthu. Baibulo limati: “Mphoto  yake ya uchimo ndi imfa; koma mphatso yaulere ya Mulungu ndiyo moyo wosatha wa mwa Kristu Yesu Ambuye wathu.”​—Aroma 6:23.

Monga munthu wangwiro, ndiponso munthu wamkulu zedi amene anakhalapo, Yesu anayamba ntchito yolalikira uthenga wabwino. Nkhani ya m’Baibulo pa Marko 1:14, 15 imatiuza kuti: “Ndipo ataperekedwa Yohane, Yesu anadza ku Galileya, nalalikira uthenga wabwino wa Mulungu, nanena, Nthaŵi yakwanira, ndipo Ufumu wa Mulungu wayandikira; tembenukani mtima, khulupirirani uthenga wabwino.”

Awo amene analabadira uthenga wa Yesu ndi kukhulupirira uthenga wabwino analandira madalitso aakulu. Yohane 1:12 akuti: “Onse amene anam’landira [Yesu], kwa iwo anapatsa mphamvu yakukhala ana a Mulungu, kwa iwotu, akukhulupirira dzina lake.” Pokhala ana, kapena ana aamuna, a Mulungu, iwo anali kuyembekeza kulandira mphoto ya moyo wosatha.​—1 Yohane 2:25.

Koma mwayi wolandira madalitso a Ufumu sunali wa anthu a m’zaka za zana loyamba okha ayi. Monga momwe tatchulira pamwambapo, uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu ukulengezedwa ndi kuphunzitsidwa padziko lonse lapansi lerolino. Chotero madalitso a Ufumu adakalipo. Kodi muyenera kuchitanji kuti mulandire nawo madalitso amenewo? Nkhani yotsatira idzalongosola.