Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

India—“Kugwirizana kwa Anthu Osiyana”

India—“Kugwirizana kwa Anthu Osiyana”

 Olengeza Ufumu Akusimba

India​—“Kugwirizana kwa Anthu Osiyana”

“KUGWIRIZANA Kwa Anthu Osiyana” ndiwo mawu amene amanenedwa kaŵirikaŵiri ku India pofuna kusonyeza kugwirizana kwa anthu ake. M’dziko lalikululi lazikhalidwe, zilankhulo, mafuko, mavalidwe osiyanasiyana, ndi zakudya zamitundumitundu, si nkhani yapafupi kukhalira pamodzi mogwirizana. Komabe, kugwirizana kumeneku kumaoneka pa ofesi yoyendetsa ntchito za Mboni za Yehova ku India, ngakhale kuti antchito odzifunira amene amakhala ndi kugwira ntchito pamenepo amachokera m’maboma ndi m’zigawo zambiri ndipo amalankhula zinenero zambiri zosiyanasiyana.

• Tidziŵane ndi Rajrani​—msungwana wochokera ku Punjab, kumpoto koma kumadzulo kwenikweni kwa dziko la India. Pamene Rajrani anali pasukulu, mmodzi wa anzake a m’kalasi anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Mtsikana ameneyu anayesa kukopa Rajrani kuti achite chidwi ndi Baibulo. Popeza kuti mnzake wa Rajrani ameneyo sanali kuchidziŵa bwino Chingelezi ndipo kunalibe Nsanja ya Olonda m’chinenero cha Chipunjabi panthaŵiyo, anapemphanso Rajrani kuti azim’tembenuzira nkhani za m’magaziniwo. Zimene Rajrani anaŵerenga mu Nsanja ya Olonda zinayamba kum’khudza mtima kwambiri moti ngakhale kuti makolo ake anam’tsutsa, iye anapitabe patsogolo mpaka anapatulira moyo wake kwa Yehova Mulungu. Panopo Rajrani akutumikira pa Beteli ya ku India, ndipo akuchita ntchito imodzimodziyo imene inam’tsegula maso kuti aone choonadi. Akutembenuzira zofalitsa zachikristu m’Chipunjabi!

• Nanga bwanji za Bijoe, amene kwawo ndi kuchigawo chinanso cha India​—kumwera koma kumadzulo, m’boma la Kerala. Bijoe anachotsedwa sukulu ali kusekondale chifukwa chokana kuchita nawo mapwando okondwerera dziko lawo. Utatha mlandu wautali wa m’khoti umene chigamulo chake chachikulu chinakomera kulambira koona, Bijoe anabwerera kusukulu. * Iye anapitiriza kuphunzira mpaka ku koleji. Komabe, chifukwa cha kuipitsitsa kwa khalidwe la anthu kukolejiko chikumbumtima chake chinam’vuta, ndipo analekeza maphunzirowo temu yoyamba. Tsopano atakhala zaka khumi pa Beteli, akuona kuti wapindula kwambiri mwa kukhala m’banja la Beteli la anthu osiyanasiyana koma ogwirizana kusiyana ndi mmene akanapindulira mwa kupitiriza maphunziro owonjezereka aja.

•Norma ndi Lily onse ali ndi zaka zoposa 70 zakubadwa ndipo akhala akazi amasiye kwa nthaŵi yaitali. Aliyense wa iwo ali ndi zaka zoposa 40 mu utumiki wa nthaŵi zonse. Lily wakhala akugwira ntchito panthambi kwa zaka pafupifupi 20 monga wotembenuza wa Chitamili. Norma anabwera ku Beteli zaka 13 zapitazo mwamuna wake atamwalira. Kuwonjezera pa kukhala zitsanzo zabwino za kugwira ntchito mwakhama ndi mokhulupirika, iwo amathandizira banja lonse la Beteli kukhala logwirizana. Amakonda kuchereza alendo, ndipo amasangalala kucheza ndi achinyamata a m’banjamo, kugaŵana nawo chimwemwe chawo cha zaka zambiri za moyo wachikristu. Achinyamatanso amawaitanira kuzipinda zawo kuti akacheze nawo ndi kuwathandiza akafuna thandizo. Zitsanzo zabwino zedi!

Pambuyo pogonjetsa malingaliro amene akuyambitsa ndewu ndi kusagwirizana m’madera ambiri, antchito odzifunira ameneŵa akugwira ntchito pamodzi mosangalala potumikira ena monga a m’banja la Beteli logwirizana ku India.​—Salmo 133:1.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Onani Nsanja ya Olonda, November 1, 1987, tsamba 21.

[Mawu a Chithunzi patsamba 8]

Chithunzi chachikulu: Mountain High Maps® Copyright © 1997 Digital Wisdom, Inc.