Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

‘Wodala Munthu Wopeza Nzeru’

‘Wodala Munthu Wopeza Nzeru’

 ‘Wodala Munthu Wopeza Nzeru’

ANALI wolemba ndakatulo, katswiri wolemba mapulani a zomangamanga komanso mfumu. Pachaka, ankapeza ndalama zoposa madola 200 miliyoni, choncho anali wolemera kuposa mfumu ina iliyonse padziko lapansi. Analinso wodziŵika kwambiri chifukwa cha nzeru zake. Mfumukazi yomwe inadzamuchezera inachita chidwi kwambiri ndipo modabwa inati: “Taonani, anangondiuza dera lina lokha; nzeru zanu ndi zokoma zanu zakula pa mbiri ndinaimvayo.” (1 Mafumu 10:4-9) Ndi mmene inalili Mfumu Solomo ya Israyeli wakale.

Solomo anali ndi chuma ndiponso nzeru. Choncho anali wodziŵa bwino kusankha chofunika kwambiri pa ziŵirizi. Iye analemba kuti: “Wodala ndi wopeza nzeru, ndi woona luntha; pakuti malonda a nzeru aposa malonda a siliva, phindu lake liposa golidi woyengeka. Mtengo wake uposa ngale; ndipo zonse zikukondweretsa sizilingana naye.”​—Miyambo 3:13-15.

Kodi nanga nzeru ingapezeke kuti? N’chifukwa chiyani ili yoposa chuma? Kodi maubwino ake ndi otani? Chaputala 8 cha buku la m’Baibulo la Miyambo, lolembedwa ndi Solomo, chimayankha mafunsoŵa mochititsa chidwi. Mmenemo, nzeru ikutchulidwa monga munthu, ngati kuti ikulankhula ndi kuchita zinthu. Ndipo nzeruyo ikudzinenera yokha ubwino wake ndi mtengo wake.

“Ifuula”

Chaputala 8 cha Miyambo chikuyamba ndi funso losafuna yankho: “Kodi nzeru siitana, luntha ndi kukweza mawu ake?” * Inde, nzeru ndi luntha zimafuula, koma mosiyana ndi mkazi wachiwerewere yemwe amabisala m’malo a mdima kumanong’ona mawu okopa kwa mnyamata wachibwana wokhala yekhayekha. (Miyambo 7:12) “Liima pamwamba pamtunda, pamphambano za makwalala; pambali pa chipata poloŵera m’mudzi, poloŵa anthu pamakomo ifuula.” (Miyambo 8:1-3) Mawu amphamvu ndi okuwa a nzeru akumvekera bwino m’malo onse onga pazipata, m’makwalala ndi poloŵera mu mzinda. Anthu akumva mawuwo mosavuta ndipo akulabadira.

Ndani angatsutse mfundo yakuti pafupifupi aliyense padziko lapansi wofuna nzeru ya Mulungu yolembedwa m’Mawu ake ouziridwa, m’Baibulo, akhoza kuipeza? Buku lakuti The World Book Encyclopedia limati: “Baibulo ndi buku lomwe laŵerengedwa ndi anthu ambiri ndiponso lafalitsidwa kwambiri kuposa lililonse. Baibulo lamasuliridwa m’zilankhulo zambiri kuposa buku lina lililonse.” Baibulo lonse kapena mbali yake likupezeka m’zilankhulo zazikulu ndi  zazing’ono zoposa 2,100. Anthu oposa 90 peresenti padziko lonse angapeze mbali ya Mawu a Mulungu m’chilankhulo chawo.

Mboni za Yehova zimalengeza uthenga wa m’Baibulo paliponse. M’mayiko 235, izo zikulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu ndi kuphunzitsa anthu choonadi cha m’Mawu a Mulungu. Magazini awo ozikidwa pa Baibulo a Nsanja ya Olonda akufalitsidwa m’zinenero 140, ndipo Galamukani!, m’zinenero 83. Magazini a mtundu umodzi oposa 20 miliyoni amafalitsidwa nthaŵi zonse. Ndithudi, nzeru ikufuula ponseponse!

“Mawu Anga Ndilankhula kwa Ana a Anthu”

Nzeru ikuyamba kulankhula ngati munthu kuti: “Ndinu ndikuitanani, amuna, mawu anga ndilankhula kwa ana a anthu. Achibwana inu, chenjerani, opusa inu, khalani ndi mtima wozindikira.”​Miyambo 8:4, 5.

Nzeru ikuitana mosasankha. Ikuitana anthu onse. Ngakhale achibwana akuitanidwa kuti akhale ochenjera, kapena anzeru ndipo opusa akhale ndi mtima wozindikira. Inde, Mboni za Yehova zimakhulupirira kuti Baibulo ndi buku la anthu onse ndipo mopanda tsankho, zimayesetsa kulimbikitsa aliyense yemwe zakumana naye kuti aliŵerenge ndi kupezamo nzeru.

‘M’kamwa Mwanga Mudzalankhula Choonadi’

Nzeru ikupitiriza kuitanako: ‘Imvani, pakuti ndikanena zoposa, ndi zolungama potsegula pakamwa panga. Pakuti m’kamwa mwanga mudzalankhula choonadi, zoipa zinyansa milomo yanga. Mawu onse a m’kamwa mwanga alungama; mwa iwo mulibe zokhota ndi zopotoka.’ Inde, zomwe nzeru ikuphunzitsa n’zabwino ndi zowongoka, zoona ndi zolungama. Mulibe choipa kapena chokhota m’mawu ake. ‘Onsewo amveka ndi iye amene azindikira; alungama kwa akupeza nzeru.’​Miyambo 8:6-9.

Moyenera, nzeru ikulangiza kuti: “Landirani mwambo wanga, si siliva ayi; ndi nzeru kopambana ndi golidi wosankhika.” Kuitana kumeneku n’komveka “pakuti nzeru iposa ngale, ndi zonse tizifunitsa sizilingana nayo.” (Miyambo 8:10, 11) Chifukwa chiyani? N’chiyani chikupangitsa nzeru kukhala yoposa chuma?

“Chipatso Changa Chiposa Golidi”

Mphatso zimene nzeru imapatsa oimvetsera n’zamtemgo wapatali kuposa golidi, siliva, ngakhale ngale. Potchula mphatso zimenezi, nzeru ikuti: “Ine nzeru ndikhala m’kuchenjera, ngati m’nyumba yanga; ndimapeza kudziŵa ndi zolingalira. Kuopa Yehova ndiko kuda zoipa; kunyada, ndi kudzikuza, ndi njira yoipa, ndi m’kamwa mokhota, ndizida.”​Miyambo 8:12, 13.

Nzeru imapereka kuchenjera ndi luso la kulingalira kwa amene ali nayo. Munthu wanzeru zaumulungu alinso ndi ulemu waukulu  ndi mantha kwa Mulungu, pakuti “Chiyambi cha nzeru ndicho kuopa Yehova.” (Miyambo 9:10) Choncho amada chomwe Yehova amachida. Kudzikuza, kunyada, makhalidwe oipa, ndi m’kamwa mokhota sizipezeka mwa iye. Kudana ndi choipa kumam’teteza kuti asagwiritse ntchito mphamvu yake molakwa. N’kofunikatu kuti amene ali ndi maudindo mu mpingo wachikristu, ndi mitu ya mabanja afunefune nzeru!

Nzeru ikupitiriza kuti, “Ndine mwini uphungu ndi kudziŵitsa; ndine luntha; ndili ndi mphamvu. Mwa ine mafumu alamulira; akazembe naweruza molungama. Mwa ine akalonga ayang’anira, ndi akulu, ngakhale oweruza onse a m’dziko.” (Miyambo 8:14-16) Zipatso za nzeru monga kuzindikira, kumvetsetsa, ndi mphamvu, n’zofunika kwambiri kwa mafumu, akazembe, ndi olemekezeka. Nzeru ndi yofunika koposa kwa olamulira ndi amene amalangiza ena.

Aliyense akhoza kupeza nzeru yeniyeni. Koma si onse omwe amaipeza. Ena amaikana kapena kuipewa ngakhale pamene ili nawo ngati paphuno m’pakamwa. “Akundikonda ndiwakonda; akundifunafuna adzandipeza.” Ikutero nzeru. (Miyambo 8:17) Nzeru imapezeka ndi aliyense amene amaifunafuna moona mtima.

Nzeru njira zake ndi zolungama. Imapereka mphoto kwa amene amaifunafuna. Iyo ikuti: “Katundu ndi ulemu zili ndi ine, chuma chosatha ndi chilungamo. Chipatso changa chiposa golidi, ngakhale golidi woyengeka; phindu langa liposa siliva wosankhika. Ndimayenda m’njira ya chilungamo, pakati pa mayendedwe a chiweruzo, kuti ndionetse chuma akundikonda, chikhale choloŵa chawo, ndi kudzaza mosungira mwawo.”​Miyambo 8:18-21.

Kuphatikiza pa mikhalidwe yake yabwino kwambiri monga kuchenjera, kuganiza bwino, kudzichepetsa, kuzindikira, ndi kumvetsa zinthu, nzeru imaperekanso chuma ndi ulemu. Munthu wanzeru angapeze chuma mwachilungamo ndi kupita patsogolo mwauzimu. (3 Yohane 2) Komanso, munthu wanzeru amalemekezedwa. Kuwonjezera apo, amakhutira ndi zimene amapeza, ndipo amakhala ndi mtendere mu mtima mwake ndi chikumbumtima choyera pamaso pa Mulungu. Inde wodala munthu wopeza nzeru. Phindu la kukhala ndi nzeru n’loposadi golidi woyengeka ndi siliva wosankhika.

Langizo limeneli lafikadi panthaŵi yake kwa ife, chifukwa tikukhala m’dziko lokonda chuma kwambiri lomwe anthu amatsimikiza kupeza chuma m’njira iliyonse! Tiyeni tisaiwale kufunika kwa nzeru n’kuyamba kufunafuna chuma m’njira yosayenera. Tisanyalanyaze mphatso zomwe zimatipatsa nzeru monga misonkhano yathu yachikristu, kuŵerenga Baibulo patokha ndi zofalitsa zomwe “kapolo wokhulupirika ndi  wanzeru” amatipatsa chifukwa chongofuna kupeza chuma.​—Mateyu 24:45-47.

“Anandiimika Chikhalire Chiyambire”

Kutchula nzeru monga munthu m’chaputala 8 cha Miyambo, si kuti yangokhala njira chabe yofuna kufotokoza mkhalidwe wabwino umenewu. Kumaphiphiritsanso chilengedwe chofunika kwambiri cha Yehova. Nzeruyo ikupitirizabe kunena kuti: “Mulungu anali nane poyamba njira yake, Asanalenge zake zakale. Anandiimika chikhalire chiyambire, dziko lisanalengedwe. Pamene panalibe zozama ndinabadwa ine, pamene panalibe akasupe odzala madzi. Mapiri asanakhazikike, zitunda zisanapangidwe, ndinabadwa; Asanalenge dziko, ndi thengo, ngakhale chiyambi cha fumbi la dziko.”​Miyambo 8:22-26.

Zomwe Malemba amafotokoza ponena za “Mawu” zikugwirizana bwino kwambiri ndi nzeru yonga munthu yomwe yafotokozedwa kaleyi! Mtumwi Yohane analemba kuti: “Pachiyambi panali Mawu, ndipo Mawu anali ndi Mulungu, ndipo Mawuwo anali mulungu.” (Yohane 1:1, NW) Nzeru yonenedwa monga munthuyo, mophiphiritsa ikuimira Mwana wa Mulungu, Yesu Kristu, asanakhale munthu. *

Yesu Kristu ndiye “wobadwa woyamba wa chilengedwe chonse; pakuti mwa Iye, zinalengedwa zonse za m’mwamba, ndi za padziko, zooneka ndi zosaonekazo.” (Akolose 1:15, 16) Nzeru ija ikupitiriza kuti: “Pamene [Yehova] anakhazika mlengalenga ndinali pompo; pamene analemba pa zozama kwete kwete; polimbitsa Iye thambo lakumwamba, pokula akasupe a zozama. Poikira nyanja malire ake, kuti madzi asapitirire pa lamulo lake; polemba maziko a dziko, ndinali pambali pake ngati mmisiri; ndinam’sekeretsa tsiku ndi tsiku, ndi kukondwera pamaso pake nthaŵi zonse; ndi kukondwera ndi dziko lake lokhalamo anthu, ndi kusekerera ndi ana a anthu.” (Miyambo 8:27-31) Mwana woyamba kubadwa wa Yehova anali pambali pa Atate ake. Anali kugwira ntchito ndi Mlengi wosayerekezeka wa kumwamba ndi dziko lapansi. Pamene Yehova Mulungu anali kulenga munthu woyamba, Mwana Wake anagwira naye ntchitoyo monga Mmisiri Wamkulu. (Genesis 1:26) Ndiye chifukwa chake Mwana wa Mulungu ali ndi chidwi kwambiri ndi anthu mpaka kuwakonda!

“N’ngwodala Amene Andimvera”

Monga nzeru yonga munthu, Mwana wa Mulungu akuti: “Ndipo tsopano, ananga, mundimvere ine, n’ngodala akusunga njira zanga. Imvani mwambo, mukhale anzeru osaukana. N’ngwodala amene andimvera, nadikira pa zitseko zanga tsiku ndi tsiku, ndi kulinda pa mphuthu za makoma anga; pakuti wondipeza ine apeza moyo; Yehova adzam’komera mtima. Koma wondichimwira apweteka moyo wake; onse akundida ine akonda imfa.”​Miyambo 8:32-36.

Yesu Kristu ndiye chisonyezero cha nzeru ya Mulungu. “Amene zolemera zonse za nzeru ndi chidziŵitso zibisika mwa Iye.” (Akolose 2:3) Tiyenitu tsono, tim’mvere mosamala ndi kuyesetsa kulondola mapazi ake. (1 Petro 2:21) Kum’kana ndiko kupweteka moyo wathu ndi kukonda imfa, pakuti “palibe chipulumutso mwa wina yense.” (Machitidwe 4:12) Inde tiyeni tim’landire Yesu monga yemwe Mulungu watipatsa kuti tipulumuke. (Mateyu 20:28; Yohane 3:16) Tikatero, tidzasangalala ndi ‘moyo ndipo Yehova adzatikomera mtima.’

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 6 Liwu lachihebri lakuti “nzeru,” lili m’gulu la mawu osonyeza chinthu chachikazi. N’chifukwa chake otembenuza ena amagwiritsa ntchito mawu osonyeza mkazi potchula nzeru.

^ ndime 25 Ngakhale kuti mawu achihebri akuti “nzeru” nthaŵi zonse amasonyeza chinthu chachikazi, izi sizitsutsana ndi kuwagwiritsa ntchito kuimira Mwana wa Mulungu. Mawu achigiriki akuti “chikondi” m’mawu akuti “Mulungu ndiye chikondi,” amasonyezanso chinthu chachikazi. (1 Yohane 4:8) Komabe amagwiritsidwa ntchito kuimira Mulungu.

[Zithunzi patsamba 26]

Nzeru ndi yofunika kwambiri kwa audindo

[Zithunzi patsamba 27]

Musanyalanyaze mphatso zomwe zimatipatsa nzeru