Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Samalirani Mzimu ndi Kukhala ndi Moyo!

Samalirani Mzimu ndi Kukhala ndi Moyo!

 Samalirani Mzimu ndi Kukhala ndi Moyo!

“Chisamaliro cha mzimu chili moyo.”​—AROMA 8:6.

1, 2. Kodi Baibulo limasiyanitsa bwanji “thupi” ndi “mzimu”?

SI CHAPAFUPI kukhalabe woyera kwa Mulungu mwa makhalidwe m’chipwirikiti cha anthu akhalidwe lonyansa amene amaona kukhutiritsa zilakolako zathupi kukhala kofunika kwambiri. Komabe, Malemba amasiyanitsa “thupi” ndi “mzimu,” kusonyeza bwino lomwe kusiyana pakati pa zotsatirapo zovulaza za kugonjera zofuna za thupi lochimwali ndi zotsatirapo za madalitso ochuluka omwe amadza chifukwa chomvera zitsogozo za mzimu woyera wa Mulungu.

2 Mwachitsanzo, Yesu Kristu anati: “Wopatsa moyo ndi mzimu; thupi silithandiza konse. Mawu amene ndalankhula ndi inu ndiwo mzimu, ndi moyo.” (Yohane 6:63) Polembera Akristu a ku Galatiya, mtumwi Paulo anati: “Thupi lilakalaka potsutsana naye Mzimu, ndi Mzimu potsutsana nalo thupi; pakuti izi sizilingana.” (Agalatiya 5:17) Paulo anatinso: “Wakufesera kwa thupi la iye yekha, chochokera m’thupi adzatuta chivundi; koma wakufesera kwa Mzimu, chochokera mu Mzimu adzatuta moyo wosatha.”​—Agalatiya 6:8.

3. Kodi chofunika n’chiyani kuti timasuke ku zilakolako ndi zizoloŵezi zoipa?

3 Mzimu woyera wa Yehova​—mphamvu yake yogwira ntchito​—ungazuliretu “zilakolako [zodetsa] za thupi” ndi zisonkhezero zovulaza za thupi lathu lauchimoli. (1 Petro 2:11) Kuti timasuke ku nsinga za zizoloŵezi zoipa, n’kofunika kuti mzimu wa Mulungu utithandize, pakuti mtumwi Paulo analemba kuti: “Chisamaliro cha thupi chili imfa; koma chisamaliro cha mzimu chili moyo ndi mtendere.” (Aroma 8:6) Kodi kusamalira mzimu n’kutani?

“Chisamaliro cha Mzimu”

4. Kodi ‘kusamalira mzimu’ kumatanthauzanji?

4 Polemba za “chisamaliro cha mzimu,” Paulo anagwiritsa ntchito mawu Achigiriki omwe amatanthauza “mmene munthu amaganizira, (kuika) maganizo, . . . cholinga, kukhumba, kuyesetsa mwakhama.” Verebu lofanana nalo limatanthauza “kuganiza, kulabadira mwa njira inayake.” Chotero, kusamalira mzimu kumatanthauza kulamuliridwa, kutsogozedwa, ndi kusonkhezeredwa ndi mphamvu yogwira ntchito ya Yehova. Kumasonyeza kuti mofunitsitsa timalola malingaliro athu, zizoloŵezi zathu, ndi zikhumbo zathu kusonkhezeredwa kotheratu ndi mzimu woyera wa Mulungu.

5. Kodi tiyenera kugonjera zisonkhezero za mzimu woyera mpaka pamlingo wotani?

5 Paulo anagogomezera muyezo umene tiyenera kugonjera nawo zisonkhezero za mzimu woyera pamene anali kufotokoza za ‘kutumikira mu mzimu.’ (Aroma 7:6) Pa maziko a chikhulupiriro chawo m’nsembe ya dipo ya Yesu, Akristu awomboledwa kuchoka muulamuliro wa uchimo ndipo mwanjira imeneyi ‘afa’ ku mkhalidwe wawo wakale wokhala akapolo auchimo. (Aroma 6:2, 11) Anthu omwe mophiphiritsira anafa m’njira yotereyi kwenikweni adakali amoyo ndipo tsopano ndi omasuka kutsatira Kristu monga “akapolo a chilungamo.”​—Aroma 6:18-20.

Kusintha Kochititsa Chidwi

6. Kodi n’kusintha kotani komwe awo amene akukhala “akapolo achilungamo” amapanga?

6 Kusintha kuchoka ku ‘ukapolo wa uchimo’ ndi kuyamba kutumikira Mulungu monga “akapolo a chilungamo” n’kochititsa chidwi zedi. Ponena za ena amene anasintha mwamtundu umenewu, Paulo analemba kuti: “Munasambitsidwa, koma munayeretsedwa, koma munayesedwa olungama, m’dzina la Ambuye Yesu Kristu, ndi mwa Mzimu wa Mulungu wathu.”​—Aroma 6:17, 18; 1 Akorinto 6:11.

7. N’chifukwa chiyani kuona zinthu monga momwe Yehova amazionera kuli kofunika?

7 Kuti tisinthe mochititsa chidwi choncho,  choyamba tifunikira kuphunzira momwe Yehova amaonera zinthu. Zaka zambiri zapitazo, wamasalmo Davide anapempha Mulungu ndi mtima wonse kuti: “Mundidziŵitse njira zanu, Yehova . . . Munditsogolere m’choonadi chanu, ndipo mundiphunzitse.” (Salmo 25:4, 5) Yehova anamvetsera Davide, ndipo Yehova angathenso kuyankha pemphero lotereli la atumiki ake amakono. Popeza kuti njira za Mulungu ndi choonadi chake n’zoyera ndi zopatulika, kusinkhasinkha pa zimenezo kudzatithandiza ngati tikusonkhezeredwa kukhutiritsa zilakolako zodetsa zathupi.

Mbali Yofunika Kwambiri ya Mawu a Mulungu

8. N’chifukwa chiyani kuli kofunika zedi kuti tidziphunzira Baibulo?

8 Mawu a Mulungu, Baibulo, ndi chipatso cha mzimu wake. Choncho, njira imodzi yofunika kwambiri yothandiza kuti mzimuwo uzigwira ntchito pa ife ndiyo mwa kuŵerenga ndi kuphunzira Baibulo​—tsiku ndi tsiku ngati n’kotheka. (1 Akorinto 2:10, 11; Aefeso 5:18) Kudzaza malingaliro athu ndi mitima yathu ndi choonadi cha Baibulo ndi mfundo zake zachikhalidwe kudzatithandiza kupirira chilichonse cholimbana ndi mkhalidwe wathu wauzimu. Inde, pamene chiyeso chakuti tichite khalidwe loipa chibuka, mzimu wa Mulungu ungatikumbutse zikumbutso za m’Malemba ndi mfundo zachikhalidwe zotsogoza zomwe zingasonkhezere kutsimikiza mtima kwathu kuchita mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu. (Salmo 119:1, 2, 99; Yohane 14:26) Chotero, sitidzanyengedwa kuti titsatire njira yolakwika.​—2 Akorinto 11:3.

9. Kodi kuphunzira Baibulo kumalimbitsa motani kufunitsitsa kwathu kuteteza ubwenzi wathu ndi Yehova?

9 Pamene tikupitirizabe kuphunzira Malemba ndi mtima wonse komanso mwakhama mothandizidwa ndi zofalitsa zofotokoza Baibulo, mzimu wa Mulungu umasonkhezera malingaliro ndi mtima wathu, kuchititsa kuti ulemu wathu pa miyezo ya Yehova uzame. Ubwenzi wathu ndi Mulungu umakhala chinthu chofunika kwambiri m’moyo wathu. Tikayang’anizana ndi chiyeso, sitilola kulingalira kwambiri za kusangalatsa kwa chinthu choipacho. M’malo mwake, nthaŵi yomweyo timalingalira za momwe tingakhalirebe okhulupirika kwa Yehova. Kuyamikira kwambiri ubwenzi wathu ndi Yehova kumatisonkhezera kulimbana ndi chizoloŵezi chilichonse chomwe chingawononge ubwenzi wathuwo.

“Ha! Ndikondadi Chilamulo Chanu”

10. N’chifukwa chiyani kumvera malamulo a Yehova kuli kofunika kuti tithe kusamalira mzimu?

10 Kungodziŵa Mawu a Mulungu n’kosakwanira kuti tithe kusamalira mzimu. Mfumu Solomo anaidziŵa bwino miyezo ya Yehova, koma chakumapeto kwa moyo wake analephera kuchita mogwirizana ndi miyezo imeneyo. (1 Mafumu 4:29, 30; 11:1-6) Ngati timalingalira zauzimu, tidzaona kufunika kwa kudziŵa zomwe Baibulo limanena komanso kwa kumvera malamulo a Mulungu ndi mtima wonse. Zimenezo zikutanthauza kupenda miyezo ya Yehova mogwirizana ndi chikumbumtima ndi kuyesetsa kuitsatira mwakhama. Wamasalmo anali ndi mtima wotero. Iye anaimba kuti: “Ha! Ndikondadi chilamulo chanu; ndilingiriramo ine tsiku lonse.” (Salmo 119:97) Ngatidi tatsimikiza mtima kutsatira malamulo a Mulungu, timayamba kuonetsa mikhalidwe yaumulungu. (Aefeso 5:1, 2) M’malo mokopeka kuchita tchimo popanda kudzitetezera kulikonse, timasonyeza chipatso cha mzimu, ndipo kufunitsitsa kwathu kukondweretsa Yehova kumatithandiza kupeŵa ‘ntchito zovunda za thupi.’​—Agalatiya 5:16, 19-23; Salmo 15:1, 2.

11. Kodi mungafotokoze motani mfundo yakuti lamulo la Yehova loletsa dama limatiteteza?

11 Kodi tingakulitse motani ulemu ndi chikondi chathu pa malamulo a Yehova? Njira imodzi  ndiyo mwa kupenda kufunika kwake mosamala kwambiri. Talingalirani za lamulo la Mulungu loletsa kugonana kwa osakwatirana ndi loletsa dama ndi chigololo. (Ahebri 13:4) Kodi kumvera lamulo limeneli kumatimanitsa chabwino chilichonse? Kodi Atate wachikondi wakumwamba angapange lamulo lotiletsa kuchita chinthu chopindulitsa? Ndithudi ayi! Taonani zomwe zikuchitika m’miyoyo ya anthu ambiri omwe sakuchita zinthu mogwirizana ndi miyezo ya Yehova ya makhalidwe abwino. Kaŵirikaŵiri amataya mimba zapathengo kapena nthaŵi zina amaloŵa m’mabanja asanakonzekere ndipo amasoŵa chimwemwe. Ena akulera okha mwana popanda mwamuna kapena mkazi. Kuwonjezera pamenepo, omwe amachita dama amatenga matenda opatsirana mwa kugonana. (1 Akorinto 6:18) Ndipo ngati mtumiki wa Yehova wachita dama, angavutike mumtima kwambiri. Kuyesa kupondereza kugunda kwa chikumbumtima chifukwa cha kulakwako kungachititse kuti asoŵe tulo usiku ndi kusoŵa mtendere m’maganizo. (Salmo 32:3, 4; 51:3) Chotero, kodi si zoonekeratu kuti lamulo la Yehova loletsa dama laikidwa kuti lititeteze? Inde, kukhalabe ndi makhalidwe oyera kulidi ndi phindu lalikulu kwabasi!

Pemphererani Thandizo la Yehova

12, 13. N’chifukwa chiyani kupemphera pamene tazingidwa ndi zilakolako zauchimo kuli koyenera?

12 Mosakayikira kusamalira mzimu kumafuna pemphero lochokera mumtima. N’kofunika kupempha thandizo la mzimu woyera wa Mulungu, popeza kuti Yesu anati: “Ngati inu . . . mudziŵa kupatsa ana anu mphatso zabwino, koposa kotani nanga Atate wanu wa Kumwamba adzapatsa Mzimu Woyera kwa iwo akumpempha Iye?” (Luka 11:13) M’pemphero, tingathe kusonyeza kudalira kwathu mzimu kuti utithandize pa zofooka zathu. (Aroma 8:26, 27) Ngati tazindikira kuti zilakolako zauchimo kapena makhalidwe auchimo akutiyambukira, kapena ngati wokhulupirira mnzathu watidziŵitsa zimenezo, chingakhale chinthu chanzeru kutchula vutolo mwachindunji m’mapemphero athu ndi kupempha Mulungu kuti atithandize kugonjetsa zizoloŵezi zimenezi.

13 Yehova angatithandize kuikira mtima pa zinthu zolungama, zoyera, zabwino, ndi zotamandika. Ndipotu m’pomveka kwabasi kuti tim’pemphe modzichepetsa kotero kuti “mtendere wa Mulungu” usunge mitima yathu ndi maganizo athu! (Afilipi 4:6-8) Chotero tipemphereretu thandizo la Yehova kuti “[ti]tsate chilungamo, chipembedzo, chikhulupiriro, chikondi, chipiriro, chifatso.” (1 Timoteo 6:11-14) Ndi thandizo la Atate wathu wakumwamba, nkhaŵa ndi mayesero sizidzakula kufikira pamlingo wosalamulirika. M’malo mwake, miyoyo yathu siidzasoŵa mtendere wopatsidwa ndi Mulungu.

Musamvetse Chisoni Mzimu

14. N’chifukwa chiyani mzimu woyera wa Mulungu uli mphamvu yachiyero?

14 Atumiki a Yehova okhwima maganizo, aliyense payekha amagwiritsa ntchito malangizo a Paulo akuti: “Musazime Mzimuyo.” (1 Atesalonika 5:19) Popeza kuti mzimu wa Mulungu ndiwo “mzimu wa chiyero,” uli woyera, wosadetsedwa, wopatulika. (Aroma 1:4) Pamene ukugwira ntchito pa ife, pamenepo mzimu umenewo umakhala mphamvu yopatulika, kapena kuti yachiyero. Imatithandiza kuti tikhalebe m’njira yoyera ya moyo yomwe imadziŵika ndi kumvera Mulungu. (1 Petro 1:2) Mchitidwe uliwonse wodetsa umatanthauza kunyalanyaza mzimu umenewu, ndipo zimenezo zingakhale ndi zotsatira zosakaza kwambiri. Motani?

15, 16. (a) Kodi mzimu wa Mulungu tingaumvetse motani chisoni? (b) Kodi tingapeŵe motani kumvetsa chisoni mzimu wa Yehova?

15 Eya, Paulo analemba kuti: “Musamvetse chisoni Mzimu Woyera wa Mulungu, amene munasindikizidwa chizindikiro mwa Iye, kufikira tsiku  la mawomboledwe.” (Aefeso 4:30) Malemba amayerekezera mzimu wa Yehova ndi chizindikiro, kapena kuti chikole chomwe Akristu okhulupirika odzozedwa adzalandira m’tsogolo. Ndipo chomwe adzalandira m’tsogolocho ndicho moyo wosafa wakumwamba. (2 Akorinto 1:22; 1 Akorinto 15:50-57; Chivumbulutso 2:10) Mzimu wa Mulungu ungatsogolere odzozedwa ndi anzawo amene ali ndi chiyembekezo cha padziko lapansi m’moyo wokhulupirika ndipo ungathe kuwathandiza kupeŵa ntchito zauchimo.

16 Mtumwi anachenjeza kuti tipeŵe zizoloŵezi za kunama, kuba, kuchita zomvetsa manyazi, ndi zina zotero. Ngati tingalole kukopeka ndi zinthu ngati zimenezo, ndiye kuti tidzakhala tikuchita motsutsana ndi uphungu wouziridwa ndi mzimu wa m’Mawu a Mulungu. (Aefeso 4:17-29; 5:1-5) Ku mlingo winawake, ngati titachita tero tidzakhala tikumvetsa chisoni mzimu wa Mulungu, ndipotu chimenecho n’chinthu chomwe tiyenera kupeŵa. Pa chifukwa chimenecho, ngati aliyense wa ife ayamba kunyalanyaza uphungu wa m’Mawu a Yehova, angayambe kukulitsa khalidwe kapena zizoloŵezi zomwe zotsatira zake zingakhale kuchimwa mwadala ndi kutayiratu chiyanjo cha Mulungu. (Ahebri 6:4-6) Ngakhale kuti panopo sitikuchita tchimo, mwina tikuloŵera chakomweko. Mwa kuchita zosemphana ndi chitsogozo cha mzimu, tidzaumvetsa chisoni. Tidzakhalanso tikukana ndi kumvetsa chisoni Yehova, gwero la mzimu woyera. Monga anthu okonda Mulungu, sitikufuna kuchita zimenezo. M’malo mwake, tiyeni tipempherere thandizo la Yehova n’cholinga chakuti tisamvetse chisoni mzimu wake koma kuti tikathe kudzetsera ulemu dzina lake lopatulika mwa kupitirizabe kusamalira mzimu.

Pitirizanibe Kusamalira Mzimu

17. Kodi zina mwa zolinga zauzimu zomwe tingapange ndi ziti, nanga n’chifukwa chiyani kuyesetsa kuzikwaniritsa kungakhale nzeru?

17 Njira yodziŵika bwino yakuti ife tipitirizire kusamalira mzimu ndiyo kukhala ndi zolinga zauzimu ndi kuchitapo kanthu kuti tizikwaniritse. Mogwirizana ndi zosoŵa zathu ndi mikhalidwe yathu, zolinga zathu zingaphatikizepo kuwongolera zizoloŵezi zathu za kuphunzira, kuŵirikiza ntchito yathu yolalikira, kapena kukalamira mwayi wa utumiki wakutiwakuti, monga utumiki wa upainiya wanthaŵi zonse, utumiki wa pa Beteli, kapena ntchito ya umishonale. Zimenezi zidzachititsa  maganizo athu kudzazidwa ndi zinthu zauzimu ndipo zidzatithandiza kupeŵa kugonjera zofooka zathu zaumunthu kapena kulamulidwa ndi chilakolako chokondetsa zinthu zakuthupi ndi zilakolako zosemphana ndi malemba zomwe n’zofala m’dongosolo lino la zinthu. Ndithudi kumeneku ndiko kuchita mwanzeru, pakuti Yesu anati: “Musadzikundikire nokha chuma padziko lapansi, pamene njenjete ndi dzimbiri ziwononga; ndi pamene mbala ziboola ndi kuba: koma mudzikundikire nokha chuma m’Mwamba, pamene njenjete kapena dzimbiri siziwononga, ndipo mbala siziboola ndi kuba; pakuti kumene kuli chuma chako, komwe udzakhala mtima wakonso.”​—Mateyu 6:19-21.

18. N’chifukwa chiyani kupitirizabe kusamalira mzimu kuli kofunika kwambiri m’masiku otsiriza ano?

18 Kusamalira mzimu ndi kupondereza zilakolako zakudziko ndithudi ndi chinthu chanzeru ‘m’masiku otsiriza’ ano. (2 Timoteo 3:1-5) Ndiiko komwe, “dziko lapansi lipita, ndi chilakolako chake; koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthaŵi zonse.” (1 Yohane 2:15-17) Mwachitsanzo, ngati Mkristu wachinyamata akhala ndi cholinga cha utumiki wa nthaŵi zonse, zimenezi zingakhale ngati muuni wotsogolera njira m’zaka zovuta za kusinkhuka kapena kuti m’zaka zaunyamata. Ngati wasonkhezeredwa kuchita zosayenera, munthu ameneyu adzazindikira bwino lomwe zomwe akufuna kukwaniritsa muutumiki wa Yehova. Munthu wauzimu wotereyu adzaona kuti n’kupanda nzeru, kapena kuti kupusa, kulephera kukwaniritsa zolinga zauzimu chifukwa chakuti akufuna kukhala ndi zinthu zakuthupi kapena zosangalatsa zilizonse zauchimo. Kumbukirani kuti Mose wofunitsitsa kuchita zauzimu ‘anasankha kuchitiridwa zoipa pamodzi ndi anthu a Mulungu, osati kukhala nazo zokondweretsa za zoipa za kwakanthaŵi.’ (Ahebri 11:24, 25) Kaya ndife achinyamata kapena achikulire, timasankha kuchita mofananamo pamene tikupitirizabe kusamalira mzimu m’malo mwa kusamalira thupi lauchimoli.

19. Kodi tidzasangalala ndi mapindu otani ngati tidzapitiriza kusamalira mzimu?

19 “Chisamaliro cha thupi chidana ndi Mulungu,” koma “chisamaliro cha mzimu chili moyo ndi mtendere.” (Aroma 8:6, 7) Ngati tipitirizabe kusamalira mzimu, tidzapeza mtendere wamtengo wapatali. Mitima yathu ndi maganizo athu adzakhala otetezeka kotheratu ku zisonkhezero za mkhalidwe wathu wauchimowu. Tidzakhoza bwino lomwe kupeŵa ziyeso zakuti tichite tchimo. Ndipo Mulungu adzatithandiza kupirira nkhondo yosatha yapakati pa thupi ndi mzimu.

20. N’chifukwa chiyani tingakhale otsimikizira kuti kupambana m’nkhondo yapakati pa thupi ndi mzimu n’kotheka?

20 Mwa kupitirizabe kusamalira mzimu, timasunga mgwirizano wabwino ndi Yehova, gwero la moyo ndi la mzimu woyera. (Salmo 36:9; 51:11) Satana Mdyerekezi ndi om’tsatira ake akuchita chilichonse chomwe angathe kuti awononge unansi wathu ndi Yehova Mulungu. Amayesa kulamulira malingaliro athu ndipo akudziŵa kuti ngati tigonjera zofuna zawo, pamapeto pake zimenezi zidzatipangira udani ndi Mulungu ndi kutitsogolera ku imfa. Koma tingathe kupambana m’nkhondo imeneyi yapakati pa thupi ndi mzimu. N’zimene zinachitikira Paulo, chifukwa chakuti polemba nkhani yokhudza nkhondo yake, choyamba anafunsa kuti: “Adzandilanditsa ndani m’thupi la imfa iyi?” Ndiyeno posonyeza kuti kulanditsidwa n’kotheka, iye anafuula nati: “Ndiyamika Mulungu, mwa Yesu Kristu Ambuye wathu.” (Aroma 7:21-25) Nafenso tingathokoze Mulungu kudzera mwa Kristu chifukwa chotipatsa njira yopiririra zofooka zaumunthu ndi kupitirizabe kusamalira mzimu ndi chiyembekezo chamtengo wapatali cha moyo wosatha.​—Aroma 6:23.

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi kusamalira mzimu kumatanthauzanji?

• Kodi tingalole motani mzimu wa Yehova kugwira ntchito pa ife?

• Fotokozani chifukwa chake, m’nkhondo yathu yolimbana ndi uchimo, kuli kofunika kuphunzira Baibulo, kumvera malamulo a Yehova, ndi kupemphera kwa iye.

• Kodi kukhala ndi zolinga zauzimu kungatithandize motani kukhalabe m’njira ya kumoyo?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 16]

Kuphunzira Baibulo kumatithandiza kupirira chilichonse cholimbana ndi mkhalidwe wathu wauzimu

[Chithunzi patsamba 17]

Kupempherera thandizo la Yehova kuti tigonjetse zilakolako zauchimo n’koyenera

[Zithunzi patsamba 18]

Zolinga zauzimu zingatithandize kupitirizabe kusamalira mzimu