Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuuka kwa Yesu Kukufufuzidwa

Kuuka kwa Yesu Kukufufuzidwa

 Kuuka kwa Yesu Kukufufuzidwa

“Ndikukuuzani moona mtima kuti ngakhale tikutsimikiza kuti Yesu anakhalakodi . . . , sitinganene motsimikiza chimodzimodzi kuti Mulungu anamuukitsa.” Anatero Akibishopu wa ku Canterbury wa Church of England.

MTUMWI wachikristu Paulo sanali wokayikira motero. M’chaputala 15 cha kalata yake youziridwa yoyamba yopita kwa Akristu anzake ku Korinto wakale, Paulo analemba kuti: “Ndinapereka kwa inu poyamba, chimenenso ndinalandira, kuti Kristu anafera zoipa zathu, monga mwa malembo; ndi kuti anaikidwa; ndi kuti anaukitsidwa tsiku lachitatu, monga mwa malembo.”​—1 Akorinto 15:3, 4.

Kunalitu kukhulupirira kuuka kwa Yesu Kristu komwe kunachititsa ophunzira ake kulalikira uthenga wabwino ku mayiko onse achigiriki ndi achiroma​—“cholengedwa chonse cha pansi pa thambo.” (Akolose 1:23) Ndiponso, kuuka kwa Yesu ndiko maziko achikhulupiriro chachikristu.

Komabe, kuyambira pachiyambi, ambiri anali kukayikira komanso kusakhulupirira kuuka kwa Yesu. Kwa Ayuda, chinali chipongwe chachikulu kuti otsatira a Yesu azinena kuti munthu wopachikidwayo anali Mesiya. Popeza kuti Agiriki ambiri ophunzira ankakhulupirira kuti moyo sumafa, mawu okhawo akuti kuuka ankadana nawo kwambiri.​—Machitidwe 17:32-34.

Okayikira Amakono

M’zaka zaposachedwapa, akatswiri ena omwe amadzitcha Akristu asindikiza mabuku komanso nkhani zonena kuti kuuka kwa Yesu ndi nthano chabe ndipo iwo ayambitsa mkangano waukulu pankhaniyi. M’kufufuza kwawo za ‘Yesu wotchukayo,’ akatswiri osiyanasiyana anena kuti nkhani za m’Mauthenga Abwino zosimba za manda opanda kanthu komanso kuonekera kwa Yesu pambuyo pa kuuka kwake ndi nthano zenizeni zomwe anazipeka patapita nthaŵi yaitali iye ataphedwa kale n’cholinga chochirikiza nkhani yoti iye ndi wolamulira kumwamba.

Mwachitsanzo, talingalirani za maganizo a katswiri wina wa ku Germany wotchedwa Gerd Lüdemann. Iyeyu ndi pulofesa wa Chipangano Chatsopano komanso yemwe analemba buku lakuti What Really Happened to Jesus​—A Historical Approach to the Resurrection. Iye ananena kuti, kuuka kwa Yesu ndi “nkhani yabodza” imene aliyense wodziŵa bwino “sayansi yadziko” ayenera kuitsutsa.

Pulofesa Lüdemann ananenanso kuti, munthu  yemwe mtumwi Petro anaona ndi kumkhulupirira kuti anali Yesu woukitsidwayo anali mazangazime chabe chifukwa cha kumva chisoni kwambiri komanso kudziimba mlandu chifukwa chokana Yesu. Lüdemann ananenanso kuti, kuonekera kwa Yesu ku khamu la okhulupirira okwana 500 panthaŵi ina, kunali ‘kutengeka maganizo chabe kwa anthuwo.’ (1 Akorinto 15:5, 6) Mwachidule, akatswiri ambiri amanena kuti nkhani za m’Baibulo zokhudza kuuka kwa Yesu zinali zopeka ndipo zinalimbikitsa ophunzira kukhala odzidalira mwauzimu ndiponso achangu pantchito yolalikira.

N’zoona kuti ambiri alibe chidwi chofufuza maganizo opotoka otereŵa. Komabe, nkhani ya kuuka kwa Yesu iyenera kukhala yofunika kwambiri kwa tonsefe. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti, ngati iye sanaukitsidwe, ndiye kuti maziko a Chikristu n’ngabodza. Koma, ngati kuuka kwa Yesu kunachitikadi, ndiye kuti maziko a Chikristu n’ngoona. Ngati n’choncho, ndiye kuti zomwe Kristu ananena komanso malonjezo ake zidzakwaniritsidwa. Komanso, ngati chiukiriro chilipo ndiye kuti imfa si yopambana koma ndi mdani yemwe atha kugonjetsedwa.​—1 Akorinto 15:55.

[Mawu a Chithunzi patsamba 3]

Chotengedwa m’Baibulo la “Self-Pronouncing Edition of the Holy Bible,” lokhala ndi Baibulo la King James ndi mabaibulo a Revised