Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kugonjetsa Kufooka Kwaumunthu

Kugonjetsa Kufooka Kwaumunthu

 Kugonjetsa Kufooka Kwaumunthu

“Chisamaliro cha thupi chili imfa.”​—AROMA 8:6.

1. Kodi ena amaliona motani thupi la munthu, nanga ndi funso liti lofunika kulilingalira?

“NDIKUYAMIKANI chifukwa kuti chipangidwe changa n’choopsa ndi chodabwitsa.” (Salmo 139:14) Anaimba motero wamasalmo Davide pamene anali kusinkhasinkha za chimodzi mwa zinthu zomwe Yehova analenga​—thupi la munthu. Mosemphana ndi chitamando choyenereracho, pali aphunzitsi achipembedzo omwe amaliona thupi monga malo obisaliramo zoipa ndiponso monga chipangizo chauchimo. Alitcha ‘chophimba kupulukira, maziko a khalidwe lonyansa, nsinga za chivundi, chipinda cha zoipa, mtembo woyenda wokha.’ N’zoona kuti mtumwi Paulo anati: “M’thupi langa, simukhala chinthu chabwino.” (Aroma 7:18) Koma kodi zimenezi zikutanthauza kuti takodwa m’thupi lauchimoli popanda chiyembekezo chilichonse?

2. (a) Kodi “chisamaliro cha thupi” chimatanthauzanji? (b) Kodi ndi nkhondo yotani yapakati pa “thupi” ndi “mzimu” yomwe imachitika mwa anthu ofunitsitsa kukondweretsa Mulungu?

2 Nthaŵi zina Malemba amagwiritsa ntchito mawu akuti “thupi” kutanthauza munthu mumkhalidwe wake wopanda ungwiro monga mbadwa yauchimo ya Adamu wopandukayo. (Aefeso 2:3; Salmo 51:5; Aroma 5:12) Choloŵa chathu kuchokera kwa Adamu chadzetsa “kufooka kwa thupi.” (Aroma 6:19) Ndipo Paulo anachenjeza kuti: “Chisamaliro cha thupi chili imfa.” (Aroma 8:6) “Chisamaliro cha thupi” chikutanthauza kulamulidwa ndi kusonkhezeredwa ndi zilakolako za thupi lauchimoli. (1 Yohane 2:16) Chotero ngati tikuyesetsa kukondweretsa Mulungu, ndiye kuti pali nkhondo yosatha pakati pa uzimu wathu ndi mkhalidwe wathu wochimwawu womwe mosalekeza umatisonkhezera kuchita “ntchito za thupi.” (Agalatiya 5:17-23; 1 Petro 2:11) Atatsiriza kufotokoza za nkhondo yoŵaŵa imeneyi ya m’thupi lake, Paulo anafuula nati: “Munthu wosauka ine; adzandilanditsa ndani m’thupi la imfa iyi?” (Aroma 7:24) Kodi Paulo anali kuvutika ndi ziyeso popanda chitetezo china chilichonse? Baibulo limayankha mwamphamvu kuti ayi!

 Zoona Zake Ponena za Chiyeso ndi Tchimo

3. Kodi tchimo ndi chiyeso anthu ambiri amaziona motani, koma kodi Baibulo limachenjeza kuti chiyani za malingaliro otereŵa?

3 Anthu ambiri lerolino sakhulupirira kuti kuli uchimo. Ena amagwiritsa ntchito mawu akuti “tchimo” mopepuka monga mawu achikalekale pofuna kunena za kachizolowezi kachilendo ka munthu. Sazindikira kuti “ife tonse tiyenera kuonetsedwa ku mpando wa kuweruza wa Kristu, kuti yense alandire zochitika m’thupi, monga momwe anachita, kapena chabwino kapena choipa.” (2 Akorinto 5:10) Ena angasonyeze kuti chiyeso amachiona mopepuka zedi. Anthu ena akukhala m’chikhalidwe chokokomeza kukhutiritsa zofuna za panthaŵi yomweyo, kaya zofunazo zikukhudza chakudya, kugonana, maseŵero ndi zinthu zina zosangalatsa, kapena kuchita zinazake mopambana. Amafuna chinthu chilichonse, ndipotu amachifuna nthaŵi yomweyo! (Luka 15:12) Saona zakutsogolo kwa zosangalatsa za panthaŵiyo ndi kuona chimwemwe cham’tsogolo cha “moyo weniweniwo.” (1 Timoteo 6:19) Komabe, Baibulo limatiphunzitsa kuganiza mozama kwambiri ndi kuona patali, kupeŵa chilichonse chomwe chingativulaze mwauzimu kapena m’njira ina iliyonse. Mwambi wouziridwa umati: “Wochenjera aona zoipa, nabisala; koma wachibwana angopitirira, nalipitsidwa.”​—Miyambo 27:12.

4. Ndi chenjezo lotani lomwe Paulo anapereka pa 1 Akorinto 10:12, 13?

4 Paulo polembera Akristu okhala ku Korinto​—mzinda wodziŵika ndi mikhalidwe yake yoipa​—anapereka chenjezo loyenerera lokhudza chiyeso ndi mphamvu ya tchimo. Iye anati: “Chifukwa chake iye wakuyesa kuti ali chilili, ayang’anire kuti angagwe. Sichinakugwerani inu chiyeso koma cha umunthu; koma Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi chiyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.” (1 Akorinto 10:12, 13) Tonsefe​—mwana kapena wamkulu, mwamuna kapena mkazi​—timakumana ndi ziyeso zambiri kusukulu, kuntchito, kapena kwinakwake. Chotero, tiyeni tipende mawu a Paulowa ndi kuona tanthauzo lomwe alinalo kwa ife.

Musadzidalire Mopambanitsa

5. N’chifukwa chiyani kudzidalira mopambanitsa kuli koopsa?

5 Paulo anati: “Chifukwa chake iye wakuyesa kuti ali chilili, ayang’anire kuti angagwe.” Kudzidalira mopambanitsa kuti sitingagwere m’tchimo n’koopsa. Kumasonyeza kusazindikira mmene tchimo lilili komanso kusazindikira mphamvu zake. Popeza kuti anthu monga Mose, Davide, Solomo, ndi mtumwi Petro anagwapo m’tchimo, kodi tiyenera kulingalira kuti ife sizingatichitikire? (Numeri 20:2-13; 2 Samueli 11:1-27; 1 Mafumu 11:1-6; Mateyu 26:69-75) “Wanzeru amaopa nasiya zoipa; koma wopusa amanyada osatekeseka,” imatero Miyambo 14:16. Kuwonjezera pamenepo, Yesu anati: ‘Mzimu uli wofuna, koma thupi lili lolefuka.’ (Mateyu 26:41) Popeza kuti palibe munthu wopanda ungwiro amene zilakolako zauchimo zimam’phonya, tifunikira kulabadira chenjezo la Paulo mosamala kwambiri ndi kupeŵa chiyeso, apo ayi tidzagwa.​—Yeremiya 17:9.

6. Kodi ndi liti pamene tiyenera kukonzekera chiyeso ndipo tingachikonzekere motani?

6 N’chinthu chanzeru kukonzekera mavuto omwe angagwe mwadzidzidzi. Mfumu Asa anazindikira kuti nyengo ya mtendere ndiyo inali nthaŵi yabwino yokhwimitsa chitetezo. (2 Mbiri 14:2, 6, 7) Iye anadziŵa kuti mudzakhala mmbuyo mwa alendo kukonzekera adani atam’zinga. Mofananamo, maganizo ali m’malo panthaŵi yamtendere, ndi bwino kusankhiratu zomwe mudzachita chiyeso chikadzabuka. (Salmo 63:6) Danieli ndi anzake oopa Mulunguwo anasankha kukhala okhulupirika ku malamulo a Yehova asanayambe kuwakakamiza kudya chakudya cha mfumu. Chotero, sanazengereze kumamatira ku chikhulupiriro chawo ndi kukana kudya gawo la chakudya chodetsacho. (Danieli 1:8) Chiyeso chisanafike, tiyeni tilimbitse cholinga chathu chokhalabe oyera m’makhalidwe. Tikatero tidzakhala amphamvu pokana tchimo.

7. N’chifukwa chiyani kudziŵa kuti ena apambana pokana chiyeso kuli kolimbikitsa?

 7 Tikupezatu chitonthozo champhamvu m’mawu a Paulo akuti: “Sichinakugwerani inu chiyeso koma cha umunthu”! (1 Akorinto 10:13) Mtumwi Petro analemba kuti: “Mumkanize [Mdyerekezi], okhazikika m’chikhulupiriro, podziŵa kuti zowawa zomwezo zilimkukwaniridwa pa abale anu ali m’dziko.” (1 Petro 5:9) Inde, ena akumanapo ndi mayesero ngati amenewo ndipo chifukwa cha thandizo la Mulungu, awapirira mwachipambano, nafenso tingatero. Komabe, monga Akristu oona okhala m’dziko loipali, tonsefe tingayembekezere kuyesedwa nthaŵi iliyonse. Tsono tingatsimikizire motani kuti tidzagonjetsa kufooka kwaumunthu ndi chiyeso chakuti tichite tchimo?

Tingathe Kukana Chiyeso!

8. Kodi ndi njira yoyambirira iti yopeŵera chiyeso?

8 Njira yabwino yolekera kukhala “akapolo a uchimo” ndiyo kupeŵa chiyeso ngati n’kotheka. (Aroma 6:6) Miyambo 4:14, 15 ikuchenjeza kuti: “Usaloŵe m’mayendedwe ochimwa, usayende m’njira ya oipa. Peŵapo, osapitamo; patukapo, nupitirire.” Kaŵirikaŵiri timadziŵiratu pasadakhale ngati mikhalidwe inayake ingatigwetse m’tchimo. Chotero, choyenera kuchita monga Akristu ndicho ‘kupitirira,’ kutalikirana ndi aliyense ndi chilichonse ndi malo alionse omwe angadzutse zilakolako zoipa ndi kutisonkhezera zikhumbo zodetsa.

9. Kodi Malemba agogomezera motani kuthaŵa mkhalidwe woika pachiyeso?

9 Kuthaŵa mkhalidwe woika pachiyeso ndi sitepe linanso labwino lothandiza pogonjetsa chiyeso. Paulo anachenjeza kuti: “Thaŵani dama.” (1 Akorinto 6:18) Komanso analemba kuti: “Thaŵani kupembedza mafano.” (1 Akorinto 10:14) Mtumwiyu anachenjezanso Timoteo kuti athaŵe kukhumba chuma monyanyira, komanso athaŵe “zilakolako za unyamata.”​—2 Timoteo 2:22; 1 Timoteo 6:9-11.

10. N’zitsanzo ziŵiri ziti zosiyana zomwe zikusonyeza kufunika kothaŵa chiyeso?

10 Talingalirani zomwe Mfumu Davide ya Israyeli inachita. Pomwazamwaza maso ili pa tsindwi la nyumba yake yachifumu, inaona mkazi wokongola akusamba, ndipo zilakolako zoipa zinadzaza m’mtima wake. Ikanatha kuchoka patsindwipo ndi kuthaŵa chiyeso. M’malo mwake, inafunsafunsa za mkazi ameneyu​—Bateseba​—ndipo zotsatira zake zinali zosakaza. (2 Samueli 11:1–12:23) Kumbali ina, kodi Yosefe anachitanji mkazi wachiwerewere wa mbuye wake atam’kakamiza kugona naye? Nkhani yake imati: “Pakunenanena ndi Yosefe tsiku ndi tsiku, iye sanamvera mkazi kugona naye kapena kukhala naye.” Ngakhale kuti kunalibe malamulo a m’Chilamulo cha Mose, omwe panthaŵiyo anali asanaperekedwe, Yosefe anam’yankha mwakunena kuti: “Ndikachita choipa chachikulu ichi bwanji ndi kuchimwira Mulungu?” Tsiku lina mkaziyu anam’gwira Yosefe, akumati: “Gona ndi ine”! Kodi Yosefe anangokhala pomwepo ndi kuyesa kukambirana naye? Ayi. Iye “[a]nathaŵa, natulukira kubwalo.”  Yosefe sanapatse mpata chiyeso cha kugonana. Iye anathaŵa!​—Genesis 39:7-16.

11. N’chiyani chomwe chingakhale chotheka ngati tili m’chiyeso chosatha?

11 Nthaŵi zina wothaŵa amati n’ngwamantha, komatu kuchoka pamalopo kaŵirikaŵiri ndiko kuchita mwanzeru. Mwinamwake tikukumana ndi chiyeso chosatha kuntchito. Ngakhale kuti sitingathe kumangosinthasintha ntchito, pangakhale njira zina zambiri zochokera m’mikhalidwe yachiyeso. M’pofunika kuti tithaŵe chilichonse chomwe tikudziŵa kuti n’cholakwika, ndipo tiyenera kutsimikiza mtima kuchita chokhacho chomwe chili choyenera. (Amosi 5:15) Nthaŵi zina, kuthaŵa chiyeso kungafune kupeŵa mapulogalamu a pa Intaneti oonetsa zamaliseche ndi kupeŵa malo achisangalalo okayikitsa. Kungatanthauzenso kutaya magazini ena ake kapena kupeza mabwenzi atsopano​—mabwenzi okonda Mulungu komanso amene angathe kutithandiza. (Miyambo 13:20) Tidzachita bwino ngati motsimikiza mtima tidzanyalanyaza chilichonse chomwe chidzayesa kutigwetsa m’tchimo.​—Aroma 12:9.

Mmene Pemphero Lingathandizire

12. Kodi timapempha chiyani kwa Mulungu tikamati: “Musatitengere kokatiyesa”?

12 Paulo akupereka chitsimikizo cholimbikitsa chakuti: “Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi chiyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.” (1 Akorinto 10:13) Njira imodzi yomwe Yehova amatithandizira ndiyo mwa kuyankha mapemphero athu opempha kuti atithandize kupirira chiyeso. Yesu Kristu anatiphunzitsa kupemphera kuti: “Musatitengere kokatiyesa, koma mutipulumutse kwa woipayo.” (Mateyu 6:13) Mwa kuyankha mapemphero oterowo ochokera mumtima, Yehova sadzatilekerera m’chiyeso; adzatipulumutsa kwa Satana ndi zochita zake zamachenjera. (Aefeso 6:11) Tiyenera kum’pempha Mulungu kuti atithandize kuzindikira ziyeso ndikuti tikhale ndi mphamvu kuti tithe kuzipeŵa. Ngati tim’chondelera kuti asatilole kulephera pamene tikuyesedwa, adzatithandiza kuti tisagonje kwa Satana, “woipayo.”

13. Kodi tiyenera kuchitanji ngati tayang’anizana ndi chiyeso chosatha?

13 Tifunikira kupemphera mwakhama makamaka tikayang’anizana ndi chiyeso chosatha. Ziyeso zina zingalimbane mwamphamvu ndi maganizo komanso ndi mtima, zomwe zimatikumbutsa bwino lomwe kuti ndifedi ofooka. (Salmo 51:5) Mwachitsanzo, kodi tingachitenji ngati tavutika maganizo chifukwa chakuti takumbukira zonyansa zinazake zomwe tinkachita kale? Bwanji ngati tikuyesedwa kuti tibwerere ku zimenezo? M’malo mongoyesa chabe kunyalanyaza malingaliro amenewo, tulani nkhaniyo kwa Yehova m’pemphero​—mobwerezabwereza ngati n’koyenera. (Salmo 55:22) Ndi mphamvu za Mawu ake ndi mzimu woyera, angatithandize kuchotsa zizoloŵezi zodetsa m’malingaliro athu.​—Salmo 19:8, 9.

14. N’chifukwa chiyani pemphero lili lofunika popirira kufooka kwaumunthu?

14 Ataona kuti ophunzira ake alefuka m’munda wa Getsemane, Yesu anati: “Chezerani ndi kupemphera, kuti mungaloŵe m’kuyesedwa: mzimutu uli wakufuna, koma thupi lili lolefuka.” (Mateyu 26:41) Njira imodzi yogonjetsera chiyeso ndiyo kukhala watcheru ndi njira zosiyanasiyana zomwe chiyesocho chingafikire ndi kuzindikira mwamsanga machenjera ake. Kulinso kofunika kupemphera za chiyesocho mosazengereza kuti tikhale okonzeka mwauzimu kulimbana nacho. Popeza kuti chiyeso chimatifikira kumbali yathu yofooka, sitingathe kuchigonjetsa mwa ife tokha. Pemphero n’lofunika chifukwa chakuti mphamvu za Mulungu zingachirikize chitetezo chathu choletsa Satana. (Afilipi 4:6, 7) Tingafunenso thandizo lauzimu ndi mapemphero kuchokera kwa “akulu a Mpingo.”​—Yakobo 5:13-18.

Kanani Chiyeso Mwakhama

15. Kodi kukana chiyeso kumaphatikizapo kutani?

15 Kuwonjezera pa kupeŵa chiyeso ngati n’kotheka, tiyenera kuchikana mwakhama kufikira chitadutsa kapena mkhalidwewo utasintha. Pamene Yesu anali kuyesedwa ndi  Satana, anakana kufikira Mdyerekezi anachoka. (Mateyu 4:1-11) Wophunzira Yakobo analemba kuti: “Kanizani Mdyerekezi, ndipo adzakuthaŵani inu.” (Yakobo 4:7) Kukana kumayamba mwa kulimbitsa malingaliro athu ndi Mawu a Mulungu ndi kusankha molimba mtima kuti tidzamamatira ku miyezo yake. Tingachite bwino kuloŵeza pamtima ndi kusinkhasinkha pa malemba omwe akukamba za chofooka chathu chenichenicho mwachindunji. Tingachite bwino kupeza Mkristu wokhwima​—mwinamwake mkulu​—yemwe tingam’fotokozere nkhaŵa zathu komanso yemwe tingam’pemphe thandizo ngati chiyeso chitabuka mwadzidzidzi.​—Miyambo 22:17.

16. Kodi ndi motani momwe tingakhalirebe ndi makhalidwe olungama ?

16 Malemba amatilimbikitsa kuvala umunthu watsopano. (Aefeso 4:24) Zimenezi zikutanthauza kulola Yehova kutiumba ndi kutisintha. Polembera wantchito mnzake Timoteo, Paulo anati: ‘Utsate chilungamo, chipembedzo, chikhulupiriro, chikondi, chipiriro, chifatso. Limba nayo nkhondo yabwino ya chikhulupiriro, gwira moyo wosatha, umene adakuitanira.’ (1 Timoteo 6:11, 12) Ife ‘tingatsate chilungamo’ mwa kuphunzira Mawu a Mulungu mwakhama kuti tipeze chidziŵitso chakuya cha umunthu wake kenako mwa kuchita zinthu mogwirizana ndi zofuna zake. Ndandanda yosanja bwino ya ntchito zachikristu, monga kulalikira uthenga wabwino ndi kufika m’misonkhano, n’njofunikanso. Kuyandikira kwambiri kwa Mulungu ndi kugwiritsa ntchito mokwanira zogaŵira zake zauzimu kudzatithandiza kukula mwauzimu ndi kukhalabe ndi mikhalidwe yolungama.​—Yakobo 4:8.

17. Kodi tikudziŵa motani kuti Mulungu sadzatinyalanyaza m’nthaŵi ya chiyeso?

17 Paulo akutitsimikizira kuti chiyeso chilichonse chimene tingakumane nacho sichidzaposa mphamvu zathu zopatsidwa ndi Mulungu zokhoza kuthana nacho. Yehova ‘adzaika populumukirapo, kuti tidzakhoze kupirira.’ (1  Akorinto 10:13) Ndithudi, Mulungu salola kuti chiyeso chikhale chomkitsa mwakuti tisoŵe mphamvu zokwanira zauzimu zotithandiza kukhalabe okhulupirika ngati tipitirizabe kumudalira. Akufuna kuti tipambane pokana kwa mtu wa galu chiyeso chakuti tichite chomwe chili chosayenera kwa iye. Komanso, tingathe kukhulupirira lonjezo lake lakuti: “Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.”​—Ahebri 13:5.

18. N’chifukwa chiyani tingakhale otsimikizira kuti tidzagonjetsa kufooka kwaumunthu?

18 Paulo sanali kukayikira konse za zotsatirapo za kulimbana kwake ndi kufooka kwaumunthu. Sanadzilingalire kuti anali munthu womvetsa chisoni ndi wopanda thandizo lililonse wovutika ndi zilakolako zake zathupi. Mosiyana ndi zimenezo, iye anati: “Ine ndithamanga chotero, si monga chosinkhasinkha. Ndilimbana chotero, si monga ngati kupanda mlengalenga; koma ndipumpuntha thupi langa, ndipo ndiliyesa kapolo; kuti, kapena ngakhale ndalalikira kwa ena, ndingakhale wotayika ndekha.” (1  Akorinto 9:26, 27) Nafenso tingabutse nkhondo ndi kupambana polimbana ndi thupi lopanda ungwiroli. Kudzera m’Malemba, zofalitsa zofotokoza Baibulo, misonkhano yachikristu, ndi Akristu anzathu okhwima, Atate wathu wachikondi wakumwamba amatipatsa zikumbutso nthaŵi ndi nthaŵi zomwe zimatithandiza kulondola njira yolungama. Ndi thandizo lake, tingagonjetse kufooka kwaumunthu!

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi ‘kusamalira thupi’ kumatanthauzanji?

• Kodi chiyeso tingachikonzekere motani?

• Kodi tingachitenji kuti tipirire chiyeso?

• Kodi pemphero limachita mbali yofunika yotani pothana ndi chiyeso?

• Kodi tikudziŵa motani kuti n’zotheka kugonjetsa kufooka kwaumunthu?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 10]

Baibulo siliphunzitsa kuti ndife anthu okanthidwa ndi zilakolako za thupi opanda chitetezo chilichonse

[Chithunzi patsamba 12]

Kuthaŵa chiyeso ndi imodzi mwa njira zoyambirira zopeŵera tchimo