Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Paradaiso Wauzimu N’chiyani?

Kodi Paradaiso Wauzimu N’chiyani?

 Kodi Paradaiso Wauzimu N’chiyani?

GUSTAVO anakulira mu mzinda waung’ono ku Brazil. * Kuyambira ali mwana, anauzidwa kuti anthu abwino amapita kumwamba akamwalira. Sanadziŵe kanthu za cholinga cha Mulungu chakuti anthu okhulupirika adzasangalala ndi moyo wangwiro m’paradaiso padziko lapansi nthaŵi ina. (Chivumbulutso 21:3, 4) Panalinso china chomwe sanachidziŵe. Sanazindikire kuti ngakhale pakalipano angakhale m’paradaiso wauzimu.

Kodi munamvapo za paradaiso wauzimu ameneyo? Kodi mukum’dziŵa, nanga chofunika n’chiyani kuti mukhalemo? Aliyense amene akufunadi kukhala wosangalala afunikira kudziŵa za paradaiso ameneyo.

Kupeza Paradaiso Wauzimu

Kunena kuti ngakhale lerolino munthu angakhale m’paradaiso, sikungamveke kukhala zoona. Dzikoli si paradaiso m’pang’ono pomwe. Pali anthu ochuluka kwabasi omwe amakumana ndi zimene mfumu yachihebri yakale inafotokoza kuti: “Taona, misozi ya otsenderezedwa, koma analibe wakuwatonthoza; ndipo akuwatsendereza anali ndi mphamvu koma iwoŵa analibe wakuwatonthoza.” (Mlaliki 4:1) Anthu osaŵerengeka amavutika ndi chinyengo cha zandale, chipembedzo, ndi zamalonda, ndipo alibe mpumulo, alibe “wakuwatonthoza.” Enanso ambiri amavutika kulera ana awo, ndiponso ochuluka amavutika kupeza zofunika pa moyo. Ameneŵanso angakonde wakuwatonthoza, amene angawapumuzeko. Onseŵa, sali m’paradaiso ngakhale pang’ono.

Nangano paradaiso wauzimuyo ali kuti? Chabwino, mawu achingelezi akuti “paradise” ndi ofanana ndi mawu achigiriki, achiperesiya, ndi achihebri okhala ndi lingaliro limodzi la malo okongola a zomera, malo a mtendere ndi otsitsimula. Baibulo limalonjeza kuti dziko lapansi lidzakhala paradaiso weniweni, malo okongola, mudzi wa anthu opanda uchimo. (Salmo 37:10, 11) Pokhala ndi malingaliro ameneŵa, tikuona kuti paradaiso wauzimu ndi wokongola ndi wothuza mtima, wolola munthu kukhala pa mtendere ndi munthu mnzake ndiponso ndi Mulungu. Lerolino, monga mmene Gustavo anaonera, paradaiso woteroyo alipo ndipo ali ndi anthu ambiri.

Pamene anali ndi zaka 12, Gustavo anaganiza za kukhala wansembe wa Roma Katolika. Pololedwa ndi makolo ake, anapita ku seminale ya zachipembedzo. Kumeneko, anayamba kuimba, kuchita maseŵero, ndi zandale. Zimenezi zinkalimbikitsidwa ndi tchalitchi pofuna kukopa achinyamata. Iye ankadziŵa kuti wansembe ayenera kudzipereka kwa anthu ndiponso kukhala wosakwatira. Komabe, ansembe ena ndi ophunzira enanso amene Gustavo anali kuwadziŵa anali amakhalidwe oipa. Pokhala ndi anthu oterowo, posapita nthaŵi Gustavo anayamba kumwa moŵa kwambiri. N’zoonekeratu kuti anali asanapeze paradaiso wauzimu.

Tsiku lina Gustavo anaŵerenga thirakiti lofotokoza Baibulo lomwe linanena za dziko lapansi la paradaiso. Linam’pangitsa kulingalira za cholinga cha moyo. Iye anati: “Ndinayamba kuŵerenga Baibulo kaŵirikaŵiri, koma sindinkalimvetsa. Ngakhale kuona kuti Mulungu ali ndi dzina sindinaone.” Anachokako ku seminale nakalankhula ndi Mboni za Yehova kuti zimuthandize  kulimvetsa Baibulo. Pambuyo pake, anapita patsogolo mofulumira ndipo mwamsanga anadzipatulira kwa Mulungu. Gustavo anali kuphunzira za paradaiso wauzimu.

Anthu a Dzina la Mulungu

Gustavo anaphunzira kuti dzina la Mulungu, Yehova, si loti wophunzira Baibulo angolidziŵa chabe ayi. (Eksodo 6:3) N’lofunika pa kulambira koona. Yesu anaphunzitsa otsatira ake kupemphera kuti: “Atate wathu wa Kumwamba, Dzina lanu liyeretsedwe.” (Mateyu 6:9) Polankhula za Akunja omwe anakhala Akristu, wophunzira Yakobo anati: “Mulungu anayang’anira amitundu, kuti atenge mwa iwo anthu a dzina lake.” (Machitidwe 15:14) M’zaka za zana loyamba, “anthu a dzina lake” anali mpingo wachikristu. Kodi pali anthu a dzina la Mulungu lerolino? Inde, ndipo Gustavo anazindikira kuti anthu amenewo ndi Mboni za Yehova.

Mboni za Yehova zikugwira ntchito m’mayiko 235. Iwo ndi alaliki oposa 6 miliyoni, ndipo anthu ena 8 miliyoni ochita nawo chidwi apezeka pamisonkhano yawo. Podziwika kwambiri ndi ulaliki wawo, amakwaniritsa mawu a Yesu aŵa: “Ndipo uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse.” (Mateyu 24:14) Koma n’chifukwa chiyani Gustavo anaona kuti wapeza paradaiso wauzimu poyanjana ndi Mboni za Yehova? Iye anati: “Ndinayerekezera zimene ndinaona m’dzikoli makamaka kuseminale ndi zimene ndimaona mwa Mboni za Yehova. Chosiyanitsa chachikulu ndi chikondi pakati pawo.”

Ena anenanso chimodzimodzi pofotokoza Mboni za Yehova. Miriam, mayi wachitsikana wa ku Brazil anati: “Sindinkadziŵa mmene ndingakhalire wosangalala ngakhale m’banja langa. Kuona chikondi chikugwira ntchito koyamba, kunali pakati pa Mboni za Yehova.” Munthu wina wotchedwa Christian anati: “Mwa apo ndi apo ndinali kuchita za mizimu, chipembedzo chinali chosafunika kwa ine. Chofunika kwambiri kwa ine chinali kudziŵika kwanga ndi ntchito yanga monga injiniya. Komabe, pamene mkazi wanga anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, ndinaona kusintha. Ndinachitanso chidwi ndi nsangala ndiponso kudzipereka kwa amayi achikristu omwe anali kudzacheza naye.” Kodi n’chifukwa chiyani anthu amafotokoza Mboni za Yehova motero?

Kodi Paradaiso Wauzimu N’chiyani?

Chinthu chimodzi chomwe chimapangitsa Mboni za Yehova kukhala zapadera, ndicho kuyamikira chidziŵitso cha Baibulo. Amakhulupirira kuti Baibulo n’loona ndiponso kuti ndi Mawu a Mulungu. N’chifukwa chake samakhutira ndi kungodziŵa chabe mfundo zoyambirira za chipembedzo chawo. Aliyense payekha amaphunzira ndiponso kuŵerenga Baibulo nthaŵi zonse. Ngati munthu ayanjana ndi Mboni za Yehova kwa nthaŵi yaitali, amaphunzira zambiri ponena za Mulungu ndi zolinga Zake monga mmene zavumbulidwira m’Baibulo.

Kuzindikira kumeneko kumamasula Mboni za Yehova ku zinthu zimene zimasoŵetsa anthu mtendere monga, miyambo ndi maganizo olakwika. Yesu anati: “Choonadi chidzakumasulani,” ndipo Mboni za Yehova zaona kuti izi n’zoona. (Yohane 8:32) Fernando, yemwe nthaŵi ina ankachita za mizimu, anati: “Kuphunzira za moyo wosatha kunali mpumulo waukulu. Ndinali ndi mantha kuti mwina makolo anga kapena ine ndingamwalire.” Choonadi chinamasula Fernando ku mantha ake oopa mizimu ndi ku chikhulupiriro cha moyo wa pambuyo pa imfa.

M’Baibulo, chidziŵitso cha Mulungu chimakhudzana ndi paradaiso. Mneneri Yesaya anati: “Sizidzaipitsa, sizidzasakaza m’phiri langa lonse loyera, chifukwa kuti dziko lapansi lidzadzala ndi odziŵa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.”​—Yesaya 11:9.

N’zoonadi kuti chidziŵitso chokha si chokwanira kuti chingadzetse mtendere womwe Yesaya analosera. Munthu ayenera kugwiritsa ntchito zomwe amaphunzira. Fernando  anathirirapo ndemanga kuti: “Pamene munthu akukulitsa zipatso za mzimu, amapititsa patsogolo paradaiso wauzimu.” Fernando anagwiritsa ntchito mawu a mtumwi Paulo, yemwe anatcha makhalidwe abwino omwe Mkristu ayenera kukulitsa kuti “chipatso cha Mzimu.” Iye anati zimenezi ndi “chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, chiletso.”​—Agalatiya 5:22, 23.

Kodi mukutha kuona chifukwa chomwe kuyanjana ndi anthu oyesetsa kukhala ndi mikhalidwe yotereyi, kungakhaliredi monga kukhala m’paradaiso? Paradaiso wauzimu woloseredwa ndi mneneri Zefaniya angapezeke pakati pa anthu ameneŵa. Iye anati: “Sadzachita chosalungama, kapena kunena mabodza; ndi m’kamwa mwawo simudzapezeka lilime lonyenga; pakuti adzadya nadzagona pansi, ndi palibe wakuwawopsa.”​—Zefaniya 3:13.

Kufunika kwa Chikondi

Muyenera kuti mwazindikira kuti choyamba mwa zipatso za mzimu zomwe Paulo anatchula ndi chikondi. Uwu ndi mkhalidwe umene Baibulo limaufotokoza kwambiri. Yesu anati: “Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.” (Yohane 13:35) N’zoona kuti Mboni za Yehova n’zopanda ungwiro. Nthaŵi zina pamakhala kusamvana pakati pa wina ndi mnzake monga mmene atumwi a Yesu anachitira. Koma amakondanadi ndipo amapempherera thandizo la mzimu woyera pamene akukulitsa mkhalidwe umenewu.

Chifukwa cha zimenezo, ubale wawo umakhala wapadera. Palibe kusankhana mitundu kapena mafuko pakati pawo. Ndipo m’madera omwe anthu a mtundu wina anali kuphedwa, ndiponso kuphana pakati pa mitundu komwe kunachitika kumapeto kwa zaka za m’ma 1900, Mboni zambiri zinatetezana ngakhale kuti kutero kunali kuika miyoyo yawo pachiswe. Ngakhale kuti atuluka “mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe,” akusangalala ndi mgwirizano womwe ndi wovuta kuumvetsa pokhapokha mutayanjana nawo.​—Chivumbulutso 7:9.

Paradaiso Pakati pa Ochita Chifuniro cha Mulungu

M’paradaiso wauzimu mulibe malo a umbombo, chiwerewere ndi kudzikonda. Akristu akuuzidwa kuti: “Musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chili chifuno cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.” (Aroma 12:2) Pamene tikukhala ndi makhalidwe oyera ndi kuchita chifuniro cha Mulungu, m’njira ina tikuthandiza kumanga paradaiso wauzimu ndiponso tikuwonjezera chimwemwe chathu chomwe. Carla anaona kuti zimenezi n’zoona. Iye anati: “Bambo anga anandiphunzitsa kulimbikira maphunziro kuti ndidzakhale wodzidalira pachuma. Komabe, ngakhale kuti maphunziro anga a ku yunivesite anandipangitsa kudzimva wosungika, sindinapeze mgwirizano wa pabanja ndi chisungiko chomwe chingapezeke mwa chidziŵitso cha Mawu a Mulungu chokha.”

N’zoona kuti kusangalala ndi paradaiso wauzimu sikuchotsa mavuto a moyo. Akristu amadwalabe.  M’dziko limene amakhala mungabuke nkhondo ya pachiŵeniŵeni. Ambiri ndi osauka. Komabe, kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova Mulungu, womwe ndi chinthu chofunika kwambiri m’paradaiso wauzimu, kumatanthauza kuti tingam’pemphe thandizo. Inde, akutiitana kuti ‘tim’senze nkhawa zathu,’ ndipo ambiri angachitire umboni za mmene wathandizira modabwitsa m’nthaŵi zovuta kwambiri pa moyo wawo. (Salmo 55:22; 86:16, 17) Mulungu analonjeza kukhala ndi atumiki ake ngakhale “m’chigwa cha mthunzi wa imfa.” (Salmo 23:4) Kudalira kuti Mulungu ndi wokonzeka kutithandiza kumatithandiza kusunga “mtendere wa Mulungu wakupambana chidziŵitso chonse” womwe ndiye chinsinsi chopezera paradaiso wauzimu.​—Afilipi 4:7.

Kupititsa Patsogolo Paradaiso Wauzimu

Anthu ambiri amasangalala kukacheza ku malo okongola a zomera. Amakonda kuyendayendamo kapena kukhala pansi ndi kusangalala ndi zimene akuona. M’njira yofananayo, ambiri amasangalala kuyanjana ndi Mboni za Yehova. Amaona kuti mgwirizanowo ndi wotsitsimula, wamtendere ndi wabata. Komabe, munda wokongola umafunikira kuusamalira kuti upitirizebe kukhala ngati paradaiso. Moteromo, paradaiso wauzimu akupezeka m’dziko lino lopanda mikhalidwe ya paradaiso chifukwa chakuti Mboni za Yehova zokha ndizo zikum’samalira, ndipo Mulungu akudalitsa khama lawo. Nanga ndi motani mmene munthu angathandizire kukulitsa paradaiso ameneyo?

Choyamba, muyenera kuyanjana ndi mpingo wa Mboni za Yehova, kuphunzira nawo Baibulo, ndiponso kulidziŵa Baibulo komwe ndi maziko a paradaiso wauzimu. Carla anazindikira kuti: “Popanda chakudya chauzimu, palibe paradaiso wauzimu.” Izi zikuphatikizapo kuŵerenga Mawu a Mulungu nthaŵi zonse ndi kulingalira zimene mwaŵerenga. Zomwe mungaphunzire zidzakupangitsani kuyandikira kwa Yehova Mulungu, ndipo mudzam’konda. Mudzaphunziranso kulankhula naye m’pemphero ndi kum’pempha kuti akutsogolereni ndiponso mzimu wake kuti ukuthandizeni pamene mukuchita chifuniro chake. Yesu anatiuza kuti tilimbikire kupemphera. (Luka 11:9-13) Mtumwi Paulo anati: “Pempherani kosaleka.” (1 Atesalonika 5:17) Mwayi wolankhula kwa Mulungu m’pemphero ndi chikhulupiriro chonse chakuti amakumvani, ndi mbali yofunika kwambiri m’paradaiso wauzimu.

M’kupita kwa nthaŵi, zimene mumaphunzira zidzayamba kusintha moyo wanu kukhala wabwinopo, ndipo potsiriza pake mudzafuna kuuzako ena za zimenezo. Ndiyeno mudzatha kumvera lamulo la Yesu lakuti: “Muŵalitse inu kuunika kwanu pamaso pa anthu, kuti pakuona ntchito zanu zabwino, alemekeze Atate wanu wa Kumwamba.” (Mateyu 5:16) Kugaŵirako ena zomwe tadziŵa ponena za Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu ndiponso kulimbikitsa chikondi chimene achisonyeza kwa anthu kumatipatsa chimwemwe chochulukirapo.

Ikudza nthaŵi imene dziko lonse lapansi lidzakhala paradaiso weniweni​—malo okongola osaipitsidwa, mudzi woyenera wa anthu okhulupirika. Paradaiso wauzimu ‘m’nthaŵi zoŵaŵitsa’ zino ndi chizindikiro cha mphamvu za Mulungu ndi chitsanzo cha zomwe angachite ndi zimene adzakwaniritsa m’tsogolo.​—2 Timoteo 3:1.

Amene akusangalala ndi paradaiso wauzimu, ngakhale tsopano, akuona kukwaniritsidwa kwauzimu kwa Yesaya 49:10: “Iwo sadzakhala ndi njala, pena ludzu; ngakhale thukuta, pena dzuŵa silidzawatentha; pakuti Iye amene wawachitira chifundo, adzawatsogolera, ngakhale pa akasupe a madzi adzawatsogolera.” José adzaona kuona kwake kwa mawuŵa. Anali kulakalaka kukhala woimba wotchuka, koma amakhutira ndi kutumikira Mulungu mu mpingo wachikristu. Iye anati: “Tsopano ndimasangalala ndi moyo watanthauzo. Ndimadzimva kuti ndine wosungika mu ubale wachikristu, ndipo ndimam’dziŵa Yehova monga Atate wachikondi yemwe tingam’dalire.” Chimwemwe cha José ndiponso cha mamiliyoni ena a anthu onga iye, chinafotokozedwa bwino pa Salmo 64:10 kuti: “Wolungama adzakondwera mwa Yehova, nadzakhulupirira Iye.” Ndi mmenedi paradaiso wauzimu alili!

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Anthu omwe atchulidwaŵa ndi anthu enieni, koma mayina ena asinthidwa.

[Chithunzi patsamba 10]

Pamene tikusangalala ndi paradaiso wauzimu, tiyenera kuthandiza kum’kulitsa!