Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mungathe Kupitirizabe Polefulidwa!

Mungathe Kupitirizabe Polefulidwa!

 Mungathe Kupitirizabe Polefulidwa!

MUNTHU wanzeru analemba kuti: “Ukalefuka tsiku la tsoka mphamvu yako ichepa.” (Miyambo 24:10) Ngati munalefulidwapo, mungavomereze mawu ameneŵa.

Palibe amene sangalefulidwe. Kulefuka wamba kungakufooleni tsiku limodzi kapena aŵiri ndiyeno n’kutha. Koma ngati kukuphatikizapo kukhumudwa kapena mkwiyo, vutolo lingatenge nthaŵi. Akristu ena amene akhala okhulupirika kwa zaka zambiri, alefuka ndipo aleka kupezeka pamisonkhano ya mpingo ndi kusagwiranso nawo ntchito yolalikira.

Ngati mwalefulidwa, khazikani mtima pansi! Atumiki okhulupirika a m’nthaŵi zakale anapitirizabe ngakhale pamene analefulidwa, ndipo mwa thandizo la Mulungu, mungatero.

Pamene Ena Akukhumudwitsani

Musaganize kuti palibe amene angakuuzeni mawu okhumudwitsa kapena kukuchitani chipongwe. Komabe, mukhoza kukaniza kupanda ungwiro kwawo kuti kusakusokonezeni potumikira Yehova. Ngati munthu wina wakukhumudwitsani, kuganizira mmene Hana, mayi wake wa Samueli anachitira pamene anakhumudwitsidwa, kungakuthandizeni.

Hana anali kufunitsitsa ana, koma anali wosabereka. Mkazi wachiŵiri wa mwamuna wake, Penina, anali atabereka kale ana aamuna ndi aakazi. M’malo mom’mvera chifundo Hana pavuto lakelo, Penina anayesa Hana wopikisana naye ndipo khalidwe lake linachititsa Hana ‘kulira misozi, ndi kukana kudya.’​—1 Samueli 1:2, 4-7.

Tsiku lina Hana anapita ku chihema kukapemphera. Eli, mkulu wa ansembe wa Aisrayeli, anaona kuti milomo ya Hana inali kugwedera. Posazindikira kuti Hana anali kupemphera, Eli anaganiza kuti anali ataledzera. Ndipo Eli anati: “Udzaleka liti kuledzera? Chotsa vinyo wako.” (1 Samueli 1:12-14) Taganizirani mmene Hana anamvera. Iye anapita ku chihema kuti akalimbikitsidwe. Iye sanayembekezere kuti angaganiziridwe molakwa ndi mmodzi mwa anthu olemekezedwa kwambiri mu Israyeli!

Zimenezi zikanam’fooketsa kwambiri Hana mosavuta. Akanatha kungochokapo pa chihemapo mwamsanga, ndi kulumbira kuti sadzabweraponso kwa nthaŵi yonse ya utumiki wa Eli monga mkulu wa ansembe. Komabe, n’zoonekeratu kuti ubwenzi ndi Yehova ndiwo unali chinthu chamtengo wapatali kwa Hana. Anadziŵa kuti ngati angatero, sangam’sangalatse. Kuchihema ndiko kunali kuchimake kwa kulambira koyera. Yehova anaika dzina lake kumeneko. Ngakhale kuti Eli anali wopanda ungwiro, ndi amenebe anasankhidwa ndi Yehova kukhala womuimira.

Kuyankha mwaulemu kwa Hana zomwe Eli ananena, ndi chitsanzo chapamwamba kwa ife lero. Sanafune kuti aimbidwe mlandu molakwa, koma anayankha mwaulemu kwambiri. Poyankha, iye anati: “Iyayi, mbuyanga. Ine ndili mkazi wa mtima wachisoni; sindinamwa vinyo kapena chakumwa chowawa, koma ndinatsanulira mtima wanga pamaso pa Yehova. Musamandiyesa mdzakazi wanu mkazi woipa; chifukwa kufikira lero ndinalankhula mwa kuchuluka kwa kudandaula kwanga ndi kuvutika kwanga.”​—1 Samueli 1:15, 16.

Kodi Hana anamveketsa mfundo yake? Inde anaterodi. Komatu analankhula kwa Eli mwaulemu, mosasonyeza kuti akum’dzudzula chifukwa cha kum’ganizira molakwa. Chifukwa cha  zimenezo, Elinso anamuyankha mokoma mtima kuti: “Pita ndi mtendere; ndipo Mulungu wa Israyeli akupatse chopempha chako unachipempha kwa Iye.” Zonse zitatha, Hana “anamuka, nakadya, ndi nkhope yake siinakhalanso yachisoni.”​—1 Samueli 1:17, 18.

Kodi tikuphunziranji pa nkhaniyi? Mwamsanga Hana anathetsa kusam’vetsetsa, koma anatero mwa ulemu waukulu. Chotsatira chake chinali chakuti anasungabe unansi wabwino ndi Yehova komanso ndi Eli. Kaŵirikaŵiritu kulankhulana kwabwino ndiponso mwanzeru kumaletsa mavuto ang’onoang’ono kukhala akuluakulu!

N’kofunika kuzindikira kuti kuthetsa kusiyana maganizo pakati pa anthu, kumafunikira kuti onse akhale odzichepetsa ndi osaumirira malingaliro awo okha. Ngati wokhulupirira mnzanu sakufuna kuchitapo kanthu pa kuyesetsa kwanu kofuna kuthetsa kusiyana naye maganizo, mukhoza kungoisiya nkhaniyo m’manja mwa Yehova, ndi chikhulupiriro chakuti Iye adzaithetsa panthaŵi yake ndi m’njira yake.

Kodi Mwataya Mwayi wa Utumiki?

Ena avutika maganizo kwambiri chifukwa chakuti anachoka paudindo wa utumiki wa Mulungu umene amaukonda kwambiri. Anali kusangalala kutumikira abale awo, ndipo pamene mwayi umenewo unatha, anadzimva ngati sanalinso othandiza kwa Yehova ndi gulu lake. Ngati mukumva choncho, mungapeze nzeru pa chitsanzo cha wolemba Baibulo Marko, wotchedwanso kuti Yohane Marko.​—Machitidwe 12:12.

Marko anayenda limodzi ndi Paulo ndi Barnaba paulendo wawo woyamba wa umishonale, koma m’kati mwa ulendowo, iye anawasiya nabwerera ku Yerusalemu. (Machitidwe 13:13) Pambuyo pake, Barnaba anafuna kutenganso Marko paulendo wina. Komabe, Baibulo limati: “Sikunam’komera Paulo kum’tenga iye amene anawasiya nabwerera pa Pamfuliya paja osamuka nawo kuntchito.” Barnaba sanagwirizane ndi maganizo amenewo. Ndipo nkhaniyo ikupitiriza kuti, “panali kupsetsana mtima, kotero kuti analekana wina ndi mnzake; ndipo Barnaba anatenga Marko, naloŵa m’ngalawa, nanka ku Kupro. Koma Paulo anasankha Sila, namuka.”​—Machitidwe 15:36-40.

Marko ayenera kuti anamva chisoni kumva kuti mtumwi wolemekezeka Paulo, sanafune kugwira naye ntchito ndiponso kuti mkangano wa ziyeneretso zake unapangitsa kuti Paulo ndi Barnaba apatukane. Koma nkhaniyo sinathere pomwepo.

Paulo ndi Sila anafunikirabe wina woyenda naye. Atafika ku Lustra, anapeza munthu wina kuloŵa m’malo Marko, mnyamata wotchedwa Timoteo. Panthaŵiyi, Timoteo ayenera kuti anali atatha zaka ziŵiri kapena zitatu zokha kuchokera pamene anabatizidwa. Koma ponena za Marko, iye anali atagwirizana ndi mpingo wachikristu kuchokera pamene unayamba​—kwa nthaŵi yaitali kuposa ngakhale Paulo amene. Koma Timoteo ndiye analandira utumiki wapamwamba umenewo.​—Machitidwe 16:1-3.

Kodi Marko anatani atamva kuti walowedwa m’malo ndi munthu wamng’ono ndiponso wa chidziŵitso chochepa? Baibulo silinanene. Komabe, limasonyeza kuti Marko anapitirizabe kutumikira Yehova. Anagwiritsa ntchito mwayi umene anali nawo. Ngakhale kuti sanathe kutumikira ndi Paulo ndi Sila, iye anayenda ndi Barnaba kupita ku Kupro, komwe kunali kwawo kwa Barnaba. Marko anatumikiranso limodzi ndi Petro ku Babulo. Pambuyo pake, anadzakhala ndi mwayi wotumikira ndi Paulo ndi Timoteo ku Roma. (Akolose 1:1; 4:10; 1 Petro 5:13) M’kupita kwanthaŵi, Marko anauziridwa kulemba umodzi wa Mauthenga Abwino anayi!

Zonsezi zili ndi phunziro labwino. Marko sanakhudzidwe kwambiri ndi kutayika kwa mwayi wake mwakuti n’kulephera kugwiritsa ntchito mwayi wina womwe anali nawo. Iye anali wotanganidwa kutumikira Yehova, ndipo Yehova amam’dalitsa.

Choncho ngati mwataya mwayi, musalefuke. Ngati mupitirizabe kukhala ndi maganizo abwino ndi kukhala wotanganidwa, mungapezenso mwayi wina. Pali “[zo]kuchuluka mu ntchito ya Ambuye.”​—1 Akorinto 15:58.

 Mtumiki Wokhulupirika Alefulidwa

Si chapafupi kumenya zolimba nkhondo ya chikhulupiriro. Nthaŵi zina mungalefuke. Ndiyeno mungadziimbe mlandu chifukwa cha kufooketsedwa, poganiza kuti mtumiki wokhulupirika wa Mulungu sayenera kumva choncho. Taganizirani za Eliya, mmodzi mwa aneneri odziŵika kwambiri mu Israyeli.

Pamene Yezebeli Mfumukazi ya Israyeli, yemwe anali wodzipereka pa kulambira Baala anamva kuti aneneri a Baala aphedwa ndi Eliya, analumbira kupha Eliya. Eliya anali atakumanapo ndi adani oopsa kuposa Yezebeli. Koma mwadzidzidzi, iye anagwa mphwayi ndipo anangofuna kufa. (1 Mafumu 19:1-4) Kodi zimenezo zinatheka bwanji? Iye anali ataiŵala kanthu kena.

Eliya anali ataiŵala kudalira Yehova monga Gwero la mphamvu yake. Kodi ndani amene anapatsa Eliya mphamvu ya kuukitsa akufa ndi yothana ndi aneneri a Baala? Yehova. Mosakayikira, Yehova akanatha kum’patsa mphamvu yothana ndi mkwiyo wa Mfumukazi Yezebeli.​—1 Mafumu 17:17-24; 18:21-40; 2 Akorinto 4:7.

Aliyense akhoza kugwedera kwa kanthaŵi m’chikhulupiriro chake kwa Yehova. Monga Eliya, nthaŵi zina mungaone vuto lina ndi maso aumunthu m’malo mogwiritsa ntchito “nzeru yochokera kumwamba” pofuna kulithetsa. (Yakobo 3:17) Komabe, Yehova sanam’taye Eliya chifukwa cha kufooka kwake kwa kanthaŵiko ayi.

Eliya anathaŵira ku Beereseba kenako ku chipululu, komwe anaganiza kuti palibe munthu amene angam’peze. Koma Yehova anam’peza. Anatumiza mngelo kuti am’tonthoze. Mngeloyo anaonetsetsa kuti Eliya akhale ndi mkate watsopano kuti adye ndi madzi otsitsimula kuti amwe. Pambuyo pakuti Eliya wapuma, mngeloyo anam’tsogolera kuyenda ulendo wa makilomita pafupifupi 300 kukafika pa phiri la Horebu, komwe anali kukalimbikitsidwanso ndi Yehova.​—1 Mafumu 19:5-8.

Pa phiri la Horebu, Eliya anaona zionetsero zolimbitsa chikhulupiriro zoonetsa mphamvu za Yehova. Kenako, ndi mawu odekha, Yehova anam’tsimikizira kuti sanam’siye yekha. Yehova anali naye, ndiponso abale ake okwana 7,000 anali nayenso ngakhale kuti iye sanadziŵe zimenezi. Pomalizira pake Yehova anam’patsa ntchito. Sanasiye kum’gwiritsa ntchito monga mneneri wake!​—1 Mafumu 19:11-18.

Chithandizo Chilipo

Ngati nthaŵi zina mumavutika ndi kulefulidwa, mungapeze bwino mutapuma mowonjezereka ndi kudya chakudya chopatsa thanzi. Nathan H. Knorr, yemwe anali wa m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova mpaka pa imfa yake mu 1977, anaona kuti mavuto aakulu kaŵirikaŵiri amaoneka aang’ono kwambiri pambuyo pa kugona mokwanira usiku. Pamene vutolo likutenga nthaŵi, njira imeneyo ingakhale yosakwanira. Mungafunikire thandizo kuti mugonjetse kulefuka.

Yehova anatumiza mngelo kukalimbikitsa Eliya. Masiku ano, Mulungu amalimbikitsa kudzera mwa akulu ndi Akristu ena okhwima. Ndithudi, akulu “adzakhala monga pobisalira mphepo, ndi pousira chimphepo” (Yesaya 32:1, 2) Koma kuti akulimbikitseni, muyenera kuyamba ndinu kuchitapo kanthu. Eliya atalefuka, anapita ku phiri la Horebu kukalangizidwa ndi Yehova. Ife timalandira malangizo olimbikitsa kudzera mu mpingo wachikristu.

Pamene tivomera thandizo ndiponso kuthana molimba mtima ndi ziyeso monga, kukhumudwa kapena kutaya udindo wautumiki, timaona kuti kukhala kumbali ya Yehova ndi nkhani yofunika. Nkhani yanji? Satana ananenetsa kuti anthu amatumikira Yehova chifukwa cha dyera. Satana satsutsa kuti tidzatumikira Mulungu pamene chilichonse pamoyo wathu chikuyenda bwino, koma amati tidzasiya kutumikira Mulungu pamene takumana ndi mavuto. (Yobu, chaputala 1 ndi 2) Mwa kupitirizabe mosafooka kutumikira Yehova ngakhale titakumana ndi zofooketsa, tingathandize kuyankha chinenezo chanjiru cha Mdyerekezi.​—Miyambo 27:11.

Hana, Marko, ndi Eliya onseŵa anali ndi mavuto  omwe anaŵasowetsa mtendere kwa kanthaŵi. Komabe, anapirira mavuto awo nakhala ndi moyo wopindulitsa. Mothandizidwa ndi Yehova inunso mungapitirizebe ngakhale pamene ena akulefulani!