Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukuchita Mogwirizana ndi Kudzipatulira Kwanu?

Kodi Mukuchita Mogwirizana ndi Kudzipatulira Kwanu?

 Kodi Mukuchita Mogwirizana ndi Kudzipatulira Kwanu?

“Chilichonse mukachichita, gwirani ntchito mochokera mumtima, monga kwa Ambuye, osati kwa anthu ayi.”​—AKOLOSE 3:23.

1. Kodi ndi kudzipereka kotani kumene kumaoneka m’maseŵera?

KODI ochita maseŵera osiyanasiyana amatha bwanji kuseŵera mwaukatswiri? M’maseŵera a tennis, mpira wa miyendo, basketball, baseball, othamanga, golf, kapena maseŵera ena alionse, woseŵera aliyense amakhala katswiri wotchuka ngati wadzipereka kotheratu kuzoloŵeretsa thupi ndi malingaliro ake kuti akhale ndi luso lokwanira m’maseŵera omwe wasankhawo. Choyamba amafunikira kuti akhale wathupi lathanzi ndi wa malingaliro okhazikika. Kodi tiyenera kulingalira za kudzipereka kwake kotereku pamene tikuganiza za kudzipatulira m’lingaliro la Baibulo?

2. Kodi “kudzipatulira” kumatanthauzanji m’Baibulo? Perekani chitsanzo.

2 Kodi “kudzipatulira” kumatanthauzanji m’lingaliro la Baibulo? Mawu achihebri omwe anawatembenuza kuti “kupatulira” ali ndi tanthauzo lakuti “kulekana; kukhala wosiyana; kupatuka.” * Mu Israyeli wakale, Mkulu wa Ansembe Aroni, anali kuvala “chizindikiro chopatulika cha kudzipatulira” pa nduŵira yake. Chizindikiro chimenechi chinali kanthu kaphanthiphanthi konyezimira ka golide weniweni kolembedwa mawu a m’Chihebri otanthauza kuti “Kupatulika n’kwa Yehova.” Chimenecho chinkakumbutsa mkulu wa ansembe kuti ayenera kupeŵa kuchita chilichonse chomwe chingaipitse malo opatulika “chifukwa chakuti chizindikiro cha kudzipatulira, mafuta odzozera a Mulungu wake, [anali] pa iye”​—Eksodo 29:6; 39:30, NW; Levitiko 21:12, NW.

3. Kodi kudzipatulira kuyenera kukhudza motani khalidwe lathu?

3 Titha kuona m’nkhani imeneyi kuti kudzipatulira si chinthu chamaseŵera. Kumafuna kudzidziŵikitsa monga mtumiki wa Mulungu, ndipo kumafuna khalidwe loyera. Choncho, tingathe kumvetsa chifukwa chake mtumwi Petro anagwira mawu Yehova akumati: “Muzikhala oyera mtima, pakuti Ine ndine woyera mtima.” (1 Petro 1:15, 16) Monga Akristu odzipatulira, tili ndi udindo waukulu wochita mogwirizana ndi kudzipatulira kwathu, kukhalabe okhulupirika mpaka mapeto. Koma kodi kudzipatulira kwachikristu kumaphatikizapo chiyani?​—Levitiko 19:2; Mateyu 24:13.

4. Kodi timafika motani pa sitepe la kudzipatulira, nanga kodi tingakuyerekezere ndi chiyani?

4 Titapeza chidziŵitso cholondola cha Yehova Mulungu ndi zifuno zake komanso cha Yesu Kristu ndi udindo wake m’zifuno zimenezo, tinadzisankhira kutumikira Mulungu ndi mtima wathu wonse, malingaliro athu onse, moyo wathu wonse ndi mphamvu zathu zonse. (Marko 8:34; 12:30; Yohane 17:3) Limeneli tingatinso ndi lumbiro laumwini, kudzipatulira kotheratu kwa Mulungu. Sitinadzipatulire mwaphuma ayi. Tinalingalira mosamalitsa ndi mwapemphero, tikumagwiritsa ntchito mphamvu za kulingalira. Pachifukwa chimenechi, sikuti chinali chosankha chakanthaŵi kochepa ayi. Sitingafanane ndi munthu amene wayamba kulima munda ndiye kenako n’kuleka atangotsala pang’ono kutsiriza ati chifukwa chakuti ndi ntchito yaikulu kapena chifukwa chakuti akuona ngati papita nthaŵi yaitali kuti adzakolole kapena sakukhulupirira nkomwe  kuti adzakolola. Talingalirani zitsanzo za ena omwe ‘anagwira chikhasu’ cha udindo wa teokalase m’nthaŵi ya nsautso.​—Luka 9:62; Aroma 12:1, 2.

Sanaiŵale Kudzipatulira Kwawo

5. Kodi Yeremiya anali motani chitsanzo chabwino kwambiri cha mtumiki wodzipatulira wa Mulungu?

5 Yeremiya anatumikira m’Yerusalemu monga mneneri kwa zaka zoposa 40 (647-607 B.C.E.), ndipotu sinali ntchito yamaseŵera. Ankadziŵa bwino zofooka zake. (Yeremiya 1:2-6) Anafunikira kulimba mtima ndi kupirira kuti azitha kukumana ndi anthu osalabadira a Yuda tsiku ndi tsiku. (Yeremiya 18:18; 38:4-6) Komabe, Yeremiya anakhulupirira Yehova Mulungu, yemwe anam’limbitsa moti anasonyeza kuti analidi mtumiki wodzipatulira wa Mulungu.​—Yeremiya 1:18, 19.

6. Kodi mtumwi Yohane anatipatsa chitsanzo chotani?

6 Bwanji nanga za mtumwi Yohane wokhulupirikayo, amene anam’pilikitsa kwawo ndi kukam’ponya pachisumbu choipa kwambiri cha Patmo m’masiku a ukalamba wake “chifukwa cha mawu a Mulungu ndi umboni wa Yesu”? (Chivumbulutso 1:9) Anapirira ndipo anasonyeza kudzipatulira kwake monga Mkristu kwa zaka pafupifupi 60. Anakhalabe ndi moyo pambuyo pa kuwonongedwa kwa Yerusalemu ndi magulu a nkhondo a Roma. Anali ndi mwayi wolemba Uthenga Wabwino, makalata atatu ouziridwa, komanso buku la Chivumbulutso, mmene anaoneratu nkhondo ya Armagedo. Kodi analeka atamva kuti Armagedo siidzafika m’nthaŵi yamoyo wake? Kodi anayamba kuzengereza? Ayi, Yohane anakhalabe wokhulupirika kufikira imfa yake, anadziŵa kuti ngakhale kuti ‘nthaŵi [“yoikika,”NW] inali itayandikira,’ kukwaniritsidwa kwa masomphenya ake kunali kwam’tsogolo.​—Chivumbulutso 1:3; Danieli 12:4.

Zitsanzo Zamakono za Kudzipatulira

7. Kodi mbale wina anali motani chitsanzo chabwino cha kudzipatulira kwachikristu?

7 M’nthaŵi zamakono zino, masauzande a Akristu okhulupirika agwiritsa zolimba kudzipatulira kwawo ngakhale kuti sanathe kukhalabe amoyo ndi kuona kuyambika kwa Armagedo. M’modzi mwa anthu ngati amenewo anali Ernest E. Beavor wa ku England. Anakhala Mboni m’chaka cha 1939 nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse itangoyamba kumene, ndipo anasiya bizinesi yake yotukuka yosindikiza zithunzi n’cholinga chakuti ayambe utumiki wa nthaŵi zonse. Chifukwa chosafuna kuloŵerera m’zandale monga Mkristu, anam’tsekera m’ndende kwa zaka ziŵiri. Banja lake linam’chirikiza mokhulupirika, ndipo m’chaka cha 1950 ana ake atatu anapita ku Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower kukaphunzira za umishonale, ku New York. Mbale Beavor anali wakhama kwabasi m’ntchito yake yolalikira moti anzake ankamutcha Armagedo Ernie. Mokhulupirika iye anachita mogwirizana ndi kudzipatulira kwake, ndipo analengeza kuyandikira kwa nkhondo ya Mulungu ya Armagedo kufikira m’nthaŵi ya ifa yake mu 1986. Sanaone kudzipatulira kwake monga pangano ndi Mulungu lakuti  agwira ntchitoyo kwanthaŵi yochepa! *​—1 Akorinto 15:58.

8, 9. (a) Kodi anyamata ambiri ku Spain anapereka chitsanzo chotani m’kati mwa ulamuliro wa Franco? (b) Kodi ndi mafunso ati omwe ali oyenera?

8 Chitsanzo chinanso cha changu chosazirala chikuchokera ku Spain. M’kati mwa ulamuliro wa Franco (1939-75), Mboni zachinyamata zodzipatulira mazanamazana, zinachirimika osaloŵerera m’zandale. Ambiri aiwo anathera zaka khumi kapena kuposerapo ali m’ndende za asilikali. Mboni imodzi, Jesús Martín, inali itaŵeruzidwa milandu yambirimbiri ndipo kuiphatikiza yonse pamodzi, anafunika kukhala m’ndende zaka 22. Anamenyedwa modetsa nkhaŵa m’ndende ya asilikali Kumpoto kwa Africa. Sizinali bwino m’pang’ono pomwe, komabe sanabwerere mmbuyo.

9 Nthaŵi zambiri, anyamata ameneŵa sankadziŵa nthaŵi yodzamasulidwa ngati zikanatheka nkomwe, chifukwa chakuti anali kulandira ziŵeruzo zambiri komanso mobwerezabwereza. Komabe, anapitiriza kukhala okhulupirika ndi kukhalabe achangu mu utumiki ali ku ukaidi komweko. Zinthu zitayamba kusintha mu 1973, ambiri mwa Mboni zimenezi, omwe panthaŵiyo anali a zaka za m’ma 30, anamasulidwa kundende ndipo nthaŵi yomweyo anapita kukachita utumiki wa nthaŵi zonse. Ena anachita upainiya wapadera ndipo ena anatumikira monga oyang’anira oyendayenda. Anasonyeza kudzipatulira kwawo m’ndende, ndipo ochuluka apitirizabe kuchita zomwezo kuchokera panthaŵi yomwe anamasulidwa. * Bwanji ife lerolino? Kodi tikusonyeza moona mtima kuti ndife odzipatulira monga momwe okhulupirika ameneŵa anachitira?​—Ahebri 10:32-34; 13:3.

Kuona Kudzipatulira Kwathu Moyenera

10.(a) Kodi kudzipatulira kwathu tiyenera kukuona motani? (b) Kodi Yehova amauona motani utumiki wathu?

10 Kodi kudzipatulira kwathu kwa Mulungu kuti tichite chifuniro chake timakuona motani? Kodi ndicho chinthu choyambirira m’moyo wathu? Mulimonse mmene zili kwa ife, kaya ndife mwana kapena wachikulire, wapabanja kapena mbeta, wathanzi kapena wodwala, tiyenera kuyesetsa kuchita mogwirizana ndi kudzipatulira kwathu malinga ndi mikhalidwe yathu. Mkhalidwe wamunthu ungam’lole kuchita utumiki wanthaŵi zonse ngati mpainiya, wantchito wodzifunira ku ofesi yanthambi ya Watch Tower Society, mmishonale, kapena muutumiki woyendayenda. Komabe, makolo ena angakhale ndi ntchito yaikulu yosamalira zosoŵa zakuthupi ndi zauzimu za banja lawo. Kodi maola awo ochepa omwe amathera mwezi uliwonse muutumiki n’ngopanda phindu kwenikweni kwa Yehova powayerekezera ndi maola ochuluka omwe mtumiki wanthaŵi zonse amathera muutumiki? Ayi. Mulungu sayembekezera kuti tim’patse chomwe tilibe. Mtumwi Paulo anatchula mfundo yakuti: “Ngati chivomerezocho chili pomwepo, munthu alandiridwa monga  momwe ali nacho, si monga chim’soŵa.”​—2 Akorinto 8:12.

11. Kodi chipulumutso chathu chimadalira chiyani?

11 Mulimonse mmene zingakhalire, chipulumutso chathu chimadalira osati pa chilichonse chomwe tingachite, koma pa chisomo cha Yehova kudzera mwa Kristu Yesu, Ambuye wathu. Paulo anafotokoza momveka bwino kuti: “Onse anachimwa, napereŵera pa ulemerero wa Mulungu; ndipo ayesedwa olungama kwaulere, ndi chisomo chake, mwa chiwombolo cha mwa Kristu Yesu.” Komabe, ntchito zathu ndi umboni wa chikhulupiriro chathu champhamvu m’malonjezo a Mulungu.​—Aroma 3:23, 24; Yakobo 2:17, 18, 24.

12. N’chifukwa chiyani sitiyenera kuyerekezera zochita zathu ndi za ena?

12 Palibe chifukwa choyerekezera nthaŵi yomwe tathera potumikira Mulungu, mabuku ofotokoza Baibulo omwe timagaŵira, kapena chiŵerengero cha maphunziro a Baibulo omwe timachititsa ndi mmene ena akuchitira. (Agalatiya 6:3, 4) Kaya timachita motani muutumiki wachikristu, tonsefe tiyenera kukumbukira mawu a Yesu osonyeza kudzichepetsa akuti: “Chotero inunso mmene mutachita zonse anakulamulirani, nenani, Ife ndife akapolo opanda pake, tangochita zimene tayenera kuzichita.” (Luka 17:10) Kodi tinganene kangati motsimikiza kuti tachita ‘zonse anatilamulira’? Chotero funso ndi lakuti, Kodi utumiki wathu kwa Mulungu uyenera kukhala wotani?​—2 Akorinto 10:17, 18.

Kupanga Tsiku Lililonse Kukhala Lopindulitsa

13. Kodi tifunika kukhala ndi mtima wotani pamene tikusonyeza kudzipatulira kwathu?

13 Atapereka malangizo kwa akazi, amuna, ana, makolo, ndi akapolo, Paulo analemba kuti: “Chilichonse mukachichita, gwirani ntchito mochokera mumtima, monga kwa Ambuye, osati kwa anthu ayi; podziŵa kuti mudzalandira kwa Ambuye mphoto ya choloŵa; mutumikira Ambuye Kristu mwaukapolo.” (Akolose 3:23, 24) Sitikutumikira kuti tisangalatse anthu ndi zomwe tikuchita muutumiki wa Yehova. Tikuyesa kutumikira Mulungu mwa kutsatira chitsanzo cha  Yesu Kristu. Anachita utumiki wake waufupiwo mwachangu.​—1 Petro 2:21.

14. Kodi Petro anapereka chenjezo lotani lokhudza masiku otsiriza?

14 Mtumwi Petro nayenso anasonyeza changu. M’kalata yake yachiŵiri, anachenjeza kuti m’masiku otsiriza kudzakhala onyoza​—ampatuko ndi okayikira​—omwe malinga ndi zofuna zawo, adzafunsa mafunso okhudza kukhalapo kwa Kristu. Komabe, Petro anati: “Ambuye sazengereza nalo lonjezano, monga ena achiyesa chizengerezo; komatu aleza mtima kwa inu, wosafuna kuti ena awonongeke, koma kuti onse afike kukulapa. Koma tsiku la Ambuye lidzadza ngati mbala.” Inde, tsiku la Yehova lidzafika ndithu. Chotero, tiyenera kudera nkhaŵa tsiku lililonse za kutsimikizika ndi kulimba kwa chikhulupiriro chathu m’lonjezo la Mulungu.​—2 Petro 3:3, 4, 9, 10.

15. Kodi tsiku lililonse m’moyo wathu tiyenera kuliona motani?

15 Kuti tichite mogwirizana ndi kudzipatulira kwathu mosamala kwambiri, tiyenera kugwiritsa ntchito tsiku lililonse kutamanda nalo Yehova. Kumapeto kwa tsiku lililonse, kodi tingathe kulingalira zomwe tachita m’tsikulo ndi kuona momwe tatengera mbali m’njira inayake pa kuyeretsa dzina la Mulungu ndi kulengeza uthenga wabwino wa Ufumu? Mwinamwake tachita zimenezo mwa khalidwe lathu loyera, makambitsirano athu olimbikitsa, kapena kudera kwathu nkhaŵa mwachikondi banja ndi mabwenzi athu. Kodi tagwiritsa ntchito mipata yopezeka kuuza ena za chiyembekezo chathu chachikristu? Kodi tathandiza winawake kulingalira mozama za malonjezo a Mulungu? Tiyeni tiyesetse kuchitapo kenakake kaphindu mwauzimu tsiku lililonse, kutsegula, titero kunena kwake, akaunti yauzimu ya kubanki.​—Mateyu 6:20; 1 Petro 2:12; 3:15; Yakobo 3:13.

Khalanibe Oona Zinthu Moyenerera

16. Kodi Satana amayesa motani kufoola kudzipatulira kwathu kwa Mulungu?

16 Tikukhala m’nthaŵi zomwe zikuvutiravutirabe  kwa Akristu. Satana ndi otsatira ake akuyesa kutchinga kuti tisaone kusiyana kwa chabwino ndi choipa, choyera ndi chodetsa, khalidwe labwino ndi khalidwe loipa, kuchita zabwino ndi kuchita zoipa. (Aroma 1:24-28; 16:17-19) Wachititsa kuti tithe kuipitsa mitima yathu ndi malingaliro athu mosavuta mwa kugwiritsa ntchito zomwe tasankha kuonera pa TV kapena pa intaneti. Maso athu auzimu atha kuchita khungu, kapena kuti sangaonenso bwino, ndipo tingalephere kuzindikira machenjera ake. Kutsimikiza mtima kwathu kuchita zinthu mogwirizana ndi kudzipatulira kwathu kungafooke ndipo sitingagwire “chikhasu” mwamphamvu ngati tinyalanyaza chuma chathu chauzimu.​—Luka 9:62; Afilipi 4:8.

17. Kodi uphungu wa Paulo ungatithandize motani kusungabe unansi wathu ndi Mulungu?

17 Choncho, mawu a Paulo ku mpingo wa Tesalonika alidi apanthaŵi yake, iye anati: “Pakuti ichi ndi chifuniro cha Mulungu, chiyeretso chanu, kuti mudzipatule kudama; yense wa inu adziŵe kukhala nacho chotengera chake m’chiyeneretso ndi ulemu, kosati m’chiliro cha chilakolako chonyansa, monganso amitundu osadziŵa Mulungu.” (1 Atesalonika 4:3-5) Anthu ena omwe ananyalanyaza kudzipatulira kwawo kwa Mulungu, achotsedwa mu mpingo wachikristu chifukwa cha chiwerewere. Analola kuti unansi wawo ndi Mulungu uzilale, kotero kuti sanalinso kumulabadira m’moyo wawo. Komabe, Paulo anati: “Mulungu sanaitana ife titsate chidetso, koma chiyeretso. Chifukwa chake iye wotaya ichi, sataya munthu, komatu Mulungu, wakupatsa Mzimu wake Woyera kwa inu.”​—1 Atesalonika 4:7, 8.

Kodi Mwatsimikiza Mtima Kuchitanji?

18. Kodi tiyenera kutsimikiza mtima kuchitanji?

18 Ngati tikuzindikira kuti kudzipatulira kwathu kwa Yehova Mulungu si chinthu chamaseŵera, kodi tiyenera kutsimikiza kuchitanji? Tiyenera kutsimikiza ndi mtima wonse kukhala ndi chikumbumtima chabwino chokhudza khalidwe lathu ndi utumiki wathu. Petro analimbikitsa kuti: ‘Khalani nacho chikumbumtima chabwino, kuti umo akunenerani, iwo akunenera konama mayendedwe anu abwino mwa Kristu, akachititsidwe manyazi.’ (1 Petro 3:16) Mwinamwake tingavutike ndi kuchitiridwa mosayenera chifukwa cha khalidwe lathu lachikristu, komatu Kristu zinam’chitikiranso zomwezo chifukwa cha chikhulupiriro ndi kukhulupirika kwake kwa Mulungu. Petro anati: “Popeza Kristu adamva zowawa m’thupi, mudzikonzere mtima womwewo; pakuti iye amene adamva zowawa m’thupi walekana nalo tchimo.”​—1 Petro 4:1.

19. Kodi tikufuna kuti ena anenenji za ife?

19 Ndithudi, kutsimikiza mtima kwathu kuchita zinthu mogwirizana ndi kudzipatulira kwathu kudzatiteteza ku misampha ya m’dziko la Satanali lomwe n’lodwala mwauzimu, mwamakhalidwe, ndi m’zochitika. Koma choposa zimenezo, tidzakhala otsimikiza kuti ndife oyanjidwa ndi Mulungu, chinthu chabwinotu kwabasi kuposa china chilichonse chimene Satana ndi om’tsatira ake angapereke. Chotero, ena asasimbetu za ife kuti tasiya chikondi chomwe tinali nacho poyambirira titangodziŵa kumene choonadi. M’malo mwake, anenetu za ife monga momwe zinalili kwa anthu a mumpingo wa m’zaka za zana loyamba ku Tiyatira kuti: “Ndidziŵa ntchito zako, ndi chikondi, ndi chikhulupiriro, ndi utumiki, ndi chipiriro chako, ndi kuti ntchito zako zotsiriza zichuluka koposa zoyambazo.” (Chivumbulutso 2:4, 18, 19) Inde, tisakhale ofunda ponena za kudzipatulira kwathu, koma tikhaletu “achangu mumzimu,” okangalika kufikira mapeto​—ndipotu mapeto ali pafupi.​—Aroma 12:11; Chivumbulutso 3:15, 16.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Onani Nsanja ya Olonda, yachingelezi ya April 15, 1987, tsamba 31.

^ ndime 7 Kuti mumve mbiri yonse ya Moyo wa Ernest Beavor, onani Nsanja ya Olonda yachingelezi ya March 15, 1980, masamba 8-11.

^ ndime 9 Onani 1978 Yearbook of Jehovah’s Witnesses, masamba 156-8, 201-18, yofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi kudzipatulira kumaphatikizapo chiyani?

• Kodi n’zitsanzo ziti zakale ndi zamakono za atumiki odzipatulira a Mulungu zomwe tiyenera kuzitsanzira?

• Kodi kutumikira kwathu Mulungu tiyenera kukuona motani?

• Kodi tiyenera kutsimikiza mtima kuchitanji ponena za kudzipatulira kwathu kwa Mulungu?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 15]

Yeremiya anakhalabe wokhulupirika ngakhale kuti anachitiridwa nkhanza

[Chithunzi patsamba 16]

Ernest Beavor anapereka chitsanzo kwa ana ake monga Mkristu wokangalika

[Chithunzi patsamba 17]

Mboni zachinyamata mazanamazana m’ndende za ku Spain zinakhalabe zokhulupirika

[Zithunzi patsamba 18]

Tiyeni tiyesetse kuchitapo kenakake kaphindu mwauzimu tsiku lililonse