Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

N’kukulitsiranji Khalidwe Labwino?

N’kukulitsiranji Khalidwe Labwino?

 N’kukulitsiranji Khalidwe Labwino?

MWAMUNA wina wachikulire wa ku Japan dzina lake Kunihito posachedwapa anasamukira ku United States. * M’milungu yoŵerengeka chabe atangofika kumeneko, anakumana ndi vuto limene likanam’tayitsa mwayi wake wa ntchito. Kunihito akusimba kuti: “Bwana wanga kuntchito atandifunsa ngati ndingakwanitse udindo winawake, ndinatsimikiza mtima kuulandira. Komabe, popeza kuti kuyambira ubwana wanga ndaphunzitsidwa kuona kudzichepetsa monga khalidwe labwino, ndinayankha kuti: ‘Sindikudziŵa ngati ndingakwanitse, komabe ndidzachita zonse zotheka.’ Atamva zimenezi, bwana wanga wachimereka uja anaona ngati kuti ndinali wosadziŵa ntchito ndi wopanda chidaliro. Nditadziŵa zimenezo, ndinazindikira kuti ndinafunikira kusintha.”

Maria, yemwe akukhala ku New York City, anali wophunzira wanzeru, ndipo nthaŵi zonse anali wofunitsitsa kuthandiza anzake m’kalasi. Juan ankaphunzira limodzi ndi Maria ndipo nthaŵi zina ankapempha Mariayo kuti am’thandize. Koma Juan ankam’funa Maria chibwenzi ndipo anayesa kumukopa. Ngakhale kuti Maria ankafunitsitsa kukhala woyera m’makhalidwe, anagonjera zofuna za Juan ndipo anagona naye.

Kusonyeza khalidwe labwino m’dziko lamakonoli losiyana chikhalidwe ndi lodzala makhalidwe oipa n’kovuta zedi. Tsono n’kukulitsiranji khalidwe labwino? Chifukwa chakuti makhalidwe abwino amakondweretsa Mulungu, ndipotu ambiri a ife timafunitsitsa kuti iye atiyanje.

Mawu a Mulungu, Baibulo, akulimbikitsa owaŵerenga kukulitsa khalidwe labwino. Mwachitsanzo, mtumwi Paulo analemba kuti: “Ngati kuli khalidwe lililonse labwino ndipo ngati kuli chinthu chilichonse choyamikirika, pitirizanibe kulingalira zinthu zimenezi.” (Afilipi 4:8, NW) Ndipo mtumwi Petro akutilimbikitsa kuchita ‘changu chonse, powonjezera ukoma [“khalidwe labwino,” NW] pa chikhulupiriro chathu.’ (2 Petro 1:5) Koma kodi khalidwe labwino n’chiyani? Kodi lingaphunzitsidwe m’kalasi? Kodi tingalikulitse motani?

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Tasintha mayina ena.