Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Chilengezo Chapadera

Chilengezo Chapadera

Chilengezo Chapadera

PAMAPETO a msonkhano wapachaka wa bungwe la Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania umene unachitika pa October 7, 2000, panaperekedwa chilengezo chapadera ndi tcheyamani, Mbale John E. Barr wa m’Bungwe Lolamulira. Chilengezo chimenecho chinakhudza nkhani zimene Mbale Theodore Jaracz ndi Mbale Daniel Sydlik anakamba kum’maŵa tsikulo.​—Onani masamba 12-16 ndi 28-31 m’magazini ino.

Potchula mfundo yofunika kwambiri, Mbale Barr anati: “‘Kapolo wokhulupirika ndi wanzeru’ ndi Bungwe lake Lolamulira anaikizidwa zinthu zapamwamba komanso zazikulu kwambiri kusiyana ndi zija zoikizidwa m’manja mwa mabungwe ake alamulo. Zolinga zolembedwa m’zikalata za mgwirizano za mabungwe oterowo ndi zokhudza nkhani zocheperapo. Koma Mbuye wathu, Yesu Kristu, wakhazika gulu la kapolo wokhulupirika kuti liyang’anire ‘zinthu’ zake zonse kapena kuti chuma cha Ufumu chonse padziko lapansi.”​—Mateyu 24:45-47.

Ponena za bungwe lalamulo la ku Pennsylvania, Mbale Barr anawonjezera kuti: “Chilikhazikitsireni bungwe la Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania, mu 1884, lachita mbali yofunika kwambiri m’mbiri yathu yamakono. Chikhalirechobe, ilo langokhala chabe bungwe lalamulo logwiritsidwa ntchito ndi ‘kapolo wokhulupirika ndi wanzeru’ pamene kuli kofunikira.”

M’nkhani zawo, Mbale Sydlik ndi Mbale Jaracz anafotokoza kuti, pamene “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” waikizidwa zinthu zonse za Mbuye zapadziko lapansi, sizitanthauza kuti gulu la kapololo silingalole amuna oyeneretsedwa pakati pa “nkhosa zina” kuti asamalire maudindo ena a kayendetsedwe ka ntchito. (Yohane 10:16) Komanso palibe chifukwa chilichonse cha m’Malemba choumiririra kuti onse kapena ena mwa madailekitala a mabungwe alamulo ogwiritsidwa ntchito ndi Mboni za Yehova ayenera kukhala Akristu odzozedwa.

Mbale Barr anauza omvetserawo kuti posachedwapa mamembala ena a Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova amene anali kutumikira monga madailekitala ndi maofesala a mabungwe a madailekitala, a mabungwe alamulo onse ogwiritsidwa ntchito ndi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” mu United States, anachoka pamaudindo awo modzifunira. Abale odalirika a gulu la nkhosa zina anasankhidwa monga oloŵa m’malo.

Chosankha chimenechi n’chopindulitsa zedi. Chidzalola mamembala a Bungwe Lolamulira kuthera nthaŵi yambiri pokonza chakudya chauzimu ndi kusamalira zosoŵa zauzimu za gulu la abale kuzungulira dziko lonse.

Pomalizira, tcheyamaniyo anauza omvetsera osangalalawo kuti: “Ngakhale kuti ntchito zina zalamulo ndi zakayendetsedwe ka ntchito zapatsidwa kwa oyang’anira achidziŵitso kwambiri, . . . onse akutumikira motsogoleredwa ndi mzimu pansi pa uyang’aniro wa Bungwe Lolamulira. . . . Tonsefe tikuyang’ana kwa Yehova mwapemphero kuti adalitse mgwirizano wathu poyesetsa kuchita chifuniro chake, ku ulemu ndi ulemerero wa dzina lake lalikululo.”