Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Uthenga Wabwino wa Mtendere Ufika Kudera Lamapiri la Chiapas

Uthenga Wabwino wa Mtendere Ufika Kudera Lamapiri la Chiapas

 Uthenga Wabwino wa Mtendere Ufika Kudera Lamapiri la Chiapas

“M’kati mwa nkhondo yopulula kwambiri imene aliyense wam’boma la Chiapas sangaiwale, anthu wamba oti sangadziteteze okwana 45, ndi makanda 13, anaphedwa ndi kagulu ka . . . anthu okhala ndi zida.” Inatero nyuzipepala ya “El Universal” pofotokoza zimene zinachitika ku Acteal, m’boma la Chiapas, pa December 22, 1997.

CHIAPAS ndi boma lomwe lili kumwera kwenikweni kwa dziko la Mexico, kumalire ndi dziko la Guatemala. Chifukwa kwakhala kuli umphaŵi kwa nthaŵi yaitali, gulu la Aindiya a mtundu wotchedwa Maya linakonza zoukira boma mogwiritsa ntchito zida m’chaka cha 1994. Gululi linadzitcha dzina lakuti Ejército Zapatista de Liberación Nacional (EZLN, Gulu la Nkhondo la Zapatista Lomenyera Ufulu wa Dziko). Zokambirana zoti athetse kusagwirizanaku mwamtendere ankazichedwetsa dala. Asilikali aboma ndiponso zigaŵengazo anali kulanda madera ndiponso kuchita zipolowe, ndipo zimenezi zinaphetsa anthu ambiri. Chipwirikiti chimenechi chinachititsa kuti anthu wamba ambiri okhala m’derali athaŵire kwina.

Zinthu zili povuta chonchi, pali gulu limodzi la anthu okonda mtendere omwe sanaloŵererepo pa mkangano wandalewu. Iwo amadziŵitsa anthu mwakhama kuti Ufumu wa Mulungu wokha ndiwo ayenera kuuyembekeza kuti udzathetse mavuto amene anthu akupezana nawo, kwawoko komanso padziko lonse. (Danieli 2:44) Kodi ameneŵa ndani? Mboni za Yehova. Pomvera lamulo la Yesu, iwo akuyesetsa kupititsa uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu kumadera akutali kwambiri a ku mapiri a Chiapas. (Mateyu 24:14) Kodi kulalikira zinthu zili motero kunkayenda bwanji, ndipo kodi zotsatirapo zake zinali zotani?

“Ndine Wamboni za Yehova”

Tsiku lina, mnyamata wina wotchedwa Adolfo, amene anali atangokhala kumene wofalitsa wa Ufumu, anali kugwira ntchito panyumba ina youlutsira mawu ku Ocosingo. Mwadzidzidzi anamva kugogoda mwamphamvu pachitseko. Gulu la anthu ovala zinthu kumutu linangoti balamanthu n’kulozetsa mfuti zawo pamutu pake. Linathamangira m’chipinda choulutsira mawu, n’kulanda zida zoulutsira, ndi kuulutsa pawailesi kuti layamba kumenyana ndi boma.

Anthu a mfutiwo anamulamula Adolfo kuti aloŵe m’gulu lawo. “Ndine Wamboni za Yehova,” anayankha motero Adolfo, ngakhale kuti anali asanabatizidwe. Iye analongosola kuti Ufumu wa Mulungu ndiwo chinthu chokhacho tingayembekezere kubweretsa mtendere, ndipo anakanitsitsa kulandira yunifolomu ndiponso mfuti imene ankafuna kumupatsa. Poona kuti n’ngwotsimikiza kwambiri, anamuleka kuti azipita. Pokumbukira zimene zinachitikazi, Adolfo anati: “Zinandilimbikitsadi chikhulupiriro.”

M’kupita kwa nthaŵi zinthu zinasintha, koma deralo linakhalabe m’manja mwa asilikali. Ngakhale zinthu zinali choncho, akulu a kumpingo wa kwawoko atamupempha kuti  akatumikire pamodzi ndi kagulu ka Akristu komwe kanali pakokha kuderalo, Adolfo anavomera mosangalala. M’malo osechera amene anali kuwadutsa, asilikali anali kumupatsa ulemu akadzidziŵikitsa kuti ndi Wamboni za Yehova. Kenako anabatizidwa ndipo wakhala akugwira ntchito yokhutiritsa yothandiza kagulu kokhala kwakokhako kusanduka mpingo wa Mboni za Yehova. “Tsopano poti ndine wobatizidwa,” Adolfo anatero, “ndingathe kunena ndi mtima wonse kuti ndine Wamboni za Yehova!”

“Yehova Anatilimbitsa”

Gulu la EZLN litangoulutsa pa wailesi kuti layamba kumenyana ndi boma, anthu okhala m’tauni anathaŵa. Francisco, amene ali mlaliki wanthaŵi zonse, kapena mpainiya, analongosola mmene Yehova anam’limbitsira pamodzinso ndi mkazi wake pamavuto amene anakumana nawo.

“Tinaganiza zokabisala kudera lina lomwe linali ulendo wautali wokwana maola atatu mukuyenda wapansi. Kumeneku kunali mpingo, motero tinali kukakhala ndi abale. Posachedwa nthaŵi yokachita msonkhano wathu wadera ku Palenque inali itafika. Mkazi wanga ndi ine sitinafune kuphonya msonkhano wapadera wa apainiya, koma tinazindikira kuti njira yopitira kumsonkhano waderawo inali itatsekedwa ndi asilikali a  EZLN. Tinaganiza zongophotchola m’tchire, ndipo ulendowo tinauyenda maola asanu ndi anayi. Tinakafika nthaŵi yoyambira msonkhano wa apainiya isanakwane, ndipo tinasangalala nawo kwambiri pamodzinso ndi msonkhano wonsewo.

“Titabwerera, tinapeza nyumba yathu itawotchedwa ndiponso ziŵeto zathu zitabedwa. Chimene chinatsala chinali kachikwama ka zovala basi. Tinadandaula chifukwa chotaya zinthu zathu, koma abale a ku Ocosingo anatichitira chifundo n’kutiloŵetsa m’nyumba zawo. Anatisonyezanso kuchita zinthu zina zimene ife pokhala alimi tinali tisanachitepo. Mbale wina anandiphunzitsa kujambula zithunzi, ndipo wina anandiphunzitsa kukonza nsapato. Umu ndi mmene mkazi wanga ndi ine takhala tikudzithandizira mpaka pano, osasiya utumiki wanthaŵi zonse. Tikamayang’ana zinthu zimene zachitika, timaona kuti ngakhale kuti sikunali kwapafupi kuti tipirire, Yehova anali kutilimbitsa.”

Zipatso za Ntchito Yolalikira

Mboni za Yehova za m’boma la Chiapas sizinalole zovuta ndiponso zoopsazo kuti ziwafooketse pochita nawo ntchito yapadera yodziŵitsa anthu akuderalo za uthenga wabwino. Mwachitsanzo, m’miyezi ya April ndi May ya chaka cha 1995, iwo anagwirizana ndi Akristu anzawo padziko lonse pa ndawala yofalitsa Uthenga wa Ufumu Na. 34, wokhala ndi mutu woyenerera zedi wakuti N’chifukwa Ninji Moyo Uli Ndi Mavuto Ochuluka Motere?

M’kati mwa ndawalayo, pamalo otchedwa Pueblo Nuevo, mpainiya wina wokhazikika wotchedwa Ciro, anapeza banja limene linachita chidwi. Atapitakonso patatha masiku atatu, anayamba kuchita nalo phunziro la Baibulo. Koma Ciro ndi mnzake wina atapitanso kuti akapitirize kuphunzira ndi banjalo, bambo a panyumbayo kunalibe. M’malo mwake gulu la anthu ovala zinthu kumutu linali kumudikira kuti limuvulaze. Anamufunsa Ciro ndi mnzakeyo kuti akufuna chiyani ndipo anati akhoza kuwapha. Atapemphera kwa Yehova mwakachetechete, Akristu aŵiriwo analongosola molimba mtima kuti anabwerera kudzaphunzitsa banjalo Baibulo. Atanena choncho anthu ovala zinthu kumutu aja anawalola kuti azipita. Pazifukwa zina bambo wa m’nyumba ija sanapite kunyumba tsiku limenelo.

Tsiku lina patatha pafupifupi zaka zitatu, Ciro anadabwa bambo aja atafika panyumba pake. Ciro analidi wosangalala kwambiri kumva kuti banja lonse lija linali litabatizidwa ndi kuti panthaŵiyi linali mumpingo wina wa ku Guatemala! Moti mpaka mwana wawo wina wamkazi anali kuchita upainiya wokhazikika.

Kuyamikira Chakudya Chauzimu

Ngakhale kuti mavuto akupitirirabe ku Chiapas, woyang’anira chigawo wina anati Mboni za m’derali zimamvetsadi kufunika kwa kusonkhana pamodzi. (Ahebri 10:24, 25) Iye akulongosola  zimene zinachitika tsiku lina patsiku la msonkhano wapadera, umene unayenera kuyamba m’mamaŵa zedi kuti osonkhanawo athe kubwerera kunyumba kunja kudakayera. Ngakhale kuti ambiri anayenera kuyenda ulendo wam’tchire wopitirira maola atatu kuti akafike kumalo a msonkhano waderawo, aliyense anali atakhala pamalo pake pokwana 7 koloko m’maŵa. Pakati pawo panali anthu asanu ndi mmodzi a gulu la EZLN, ndipo anali kumvetsera n’kumawomba m’manja, kusonyeza kuti anali kusangalala ndi nkhanizo. Nawonso anayenda kwa maola atatu kuti abwere kumsonkhanowu. Anthu agululi 20 anabweranso ku Chikumbutso cha imfa ya Yesu, chimene chinachitikira m’Nyumba ya Ufumu ya kuderali.

Mnyamata wina wam’gulu lazigaŵengali anatumidwa ndi mabwana ake kuti akalondere dera linalake lam’tchire. Atafika pamudziwo, umenenso unali ndi Amboni za Yehova ochuluka, anapeza kuti anthu onse athaŵapo. Motero anayamba kukhala m’nyumba ina yothaŵidwa. Posoŵa chochita, anatenga mabuku ena amene anapeza panyumbapo n’kuyamba kuŵerenga. Mabukuwa anali mabuku a Watch Tower amene anasiyidwa ndi Mboni zija. Poti anali yekhayekha, mnyamatayu anapeza nthaŵi yosinkhasinkha zinthu zimene anali kuŵerenga. Anaganiza zosintha moyo wake ndi kukabweza zida zake. Anayesetsa kupeza Mbonizo mwamsanga, ndipo anayamba kuphunzira Baibulo. Patatha miyezi isanu ndi umodzi, anali kuuza anthu ena uthenga wabwino. Iyeyu kuphatikizaponso abale ake ena atatu amene anali kugwirizana ndi gulu lazigaŵenga lija tsopano ndi Akristu obatizidwa.

Kuona Zabwino Zake

Ngakhale kuti nkhondoyo inabweretsa mavuto adzaoneni, kwenikweni inachititsa anthu kumaiona bwino ntchito yolalikira. Mkulu wina wokhala mumzinda umene mkanganowu unabukira anati: “Patatha masiku asanu kumenyanako kutangoyamba, tinalinganiza ntchito yolalikira mu mzindamo ndiponso kunja kwake. Anthu anali ofunitsitsa kutimvetsera. Tinagaŵira mabuku ambiri olongosola Baibulo ndipo tinayambitsa maphunziro angapo a Baibulo. M’dera linalake, anthu ambiri anali kukana choonadi, koma chifukwa cha nkhondoyo, ayamba kumvetsera, kuphunzira Baibulo, ndi kupita kumisonkhano yampingo ndiponso misonkhano yaikulu.”

Abale n’ngosangalala chifukwa chakuti apitiriza kuchita ntchito zawo zaumulungu ngakhale mikhalidwe ili yovuta chonchi. Asilikali aboma ndiponso a gulu la EZLN akudziŵa, abalewo amachitabe misonkhano yawo ikuluikulu imene imawalimbikitsa mwauzimu. Kuyenderedwa ndi oyang’anira oyendayenda kwawalimbikitsanso kwambiri kuti apitirize kuchita ntchito yolalikira. N’zochititsa chidwi kuti ngakhale anthu amene akumenya nkhondoyo amalimbikitsa Mbonizo, ndipo nthaŵi zambiri amawauza kuti apitirize kuchita ntchito yawo yolalikira.

Ngakhale kuti ziyeso ndiponso zovuta zimene anthu a ku Chiapas akhala akukumana nazo zachepako nthaŵi inoyo, sikuti zatha ayi. Ngakhale zili choncho, chinthu chimodzi n’chotsimikizika​—ndicho chakuti Mboni za Yehova n’zofunitsitsa kupitiriza mosafooka m’ntchito yawo yokadziŵitsa anthu uthenga wabwino wamtendere wochokera m’Mawu a Mulungu, Baibulo. (Machitidwe 10:34-36; Aefeso 6:15) Iwo amazindikira zimene mneneri Yeremiya ananena zakuti “njira ya munthu siili mwa iye mwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.” (Yeremiya 10:23) Ndi Ufumu wa Mulungu wokha motsogozedwa ndi Mwana wake Yesu Kristu, umene ungabweretse njira yothetsera kupanda chilungamo ndiponso umphaŵi padziko lapansi.​—Mateyu 6:10.

[Mapu patsamba 9]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Gulf of Mexico

CHIAPAS

GUATEMALA

Nyanja ya Pacific

[Mawu a Chithunzi]

Mountain High Maps® Copyright © 1997 Digital Wisdom, Inc.

[Chithunzi patsamba 9]

Mboni za Yehova zikupita kokalalikira m’dera lamapiri la Chiapas